Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Othandiza Ali Kwina Kulikonse

Anthu Othandiza Ali Kwina Kulikonse

Anthu Othandiza Ali Kwina Kulikonse

MNYAMATA wina wa zaka 15 wotchedwa Baxter, yemwe ali pasukulu yasekondale, amachita ntchito yochititsa chidwi madzulo aliwonse Loŵeruka. Amapita kunyumba yosungira anthu okalamba kukawaimbira ndiponso kukawaimbitsa nyimbo. Mphunzitsi wa Baxter ananena kuti, “Iye amawaseketsa, ndi kuwasangalatsa.” Nayenso Lucille yemwe ali ndi zaka 78 amachita ntchito yokoma mtima yangati yomweyi. Amagaŵira anthu osoŵa chakudya ndipo amayendera odwala omwe ali okhaokha m’chipatala. Ponena za Lucille mnzake anati: “Ngati kwina anthu akusoŵa thandizo limene iye angapereke, amapita kukawathandiza.”

Tanthauzo la Kudzipereka

Anthu ambiri padziko lonse amatsatira mfundo imeneyi yakuti, ‘Muzidzipereka ngati pakufunika thandizo.’ Amathandiza komwe kuli zomangamanga ndi m’maofesi, m’mafakitale, m’malo osamala anthu amene sangathe kudzisamala, m’zipatala, m’makampu a anthu othaŵa kwawo, m’malo a anthu osoŵa pokhala, m’madipatimenti ozimitsa moto, m’maofesi omwe anthu amakatula madandaulo awo, m’malo omwe anthu amakasiyako ziŵeto zosochera ndi m’malo enanso. Amapezeka pafupifupi kwina kulikonse! Amagwiritsa ntchito maluso awo pothandiza ntchito zagulu monga kumanga nyumba mpaka kupeza ndalama zothandizira ndiponso kusamala ana onyanyalidwa ndi kusamala anthu odwala mwakayakaya. Amene amachita zonsezi ndi anthu ongodzipereka omwe amathandiza anthu ofunika thandizo.

Ena anati ntchito yongodziperekayi ndi “nzeru yapamwamba kwambiri imene munthu amachitadi.” Imafuna kuti munthuyo akhale ndi cholinga chodzipereka, mzimu wongofuna kuthandiza, wosafuna malipiro ndipo wokonzeka kuvutikira ena. Anthu aŵiri omwe akhala ongodzipereka kwa nthaŵi yaitali anati, “Ntchito yodzifunira imatanthauza kudzipereka kwathu pogwiritsa ntchito nthaŵi yathu, manja ndi miyendo yathu, nzeru zathu, luso lathu pothandiza anthu, maluso athu othetsera mavuto komanso nzeru zathu pantchito yathu.” Ubwino wake n’ngwakuti kungodzipereka koteroko, kumawapindulitsanso ongodziperekawo.—Onani bokosi lakuti “Nawonso Anthu Ongodzipereka Amapindula.”

Anthu Akamachuluka, Ofuna Thandizo Amachulukanso

Ku United States akuti anthu 100 miliyoni amagwira ntchito yongodzipereka, ndipo akumka nachulukabe. Kathleen Behrens yemwe ndi mkulu woyang’anira bungwe loona za anthu ogwira ntchito yongodzipereka lotchedwa New York Cares, posachedwapa anauza mtolankhani wa Galamukani! kuti, “M’bungwe lathu anthu akuchuluka mofulumira kwambiri. Chaka chatha chokha ongodzipereka atsopano oposa 5,000 analoŵa m’gulu lathu.” Anthu akuchulukanso m’magulu a anthu ongodzipereka ku Ulaya. Mwachitsanzo ku France pazaka 20 zapitazi, chaka chilichonse anthu 6 ongodzipereka amawonjezeka pa anthu 100 alionse. Komabe anthu ongodzipereka akufunikabe ambiri. Ndiye n’chifukwa chake poganizira za vutoli padziko lonse, a bungwe la anthu ongodzipereka la United Nations Volunteers ananena kuti, “thandizo la anthu ambiri ongodzipereka likufunika kwambiri masiku ano kuposa kale lonse.” Woyang’anira malo osungirako zinthu zamakedzana ananena kuti: “Anthu ongodzipereka ndiwo mizati yathu yeniyeni kuno.”

Komabe zimadabwitsa kuti akuluakulu ambiri, mamanijala ndiponso atsogoleri ambiri amene amagwira ntchito pamodzi ndi anthu ongodzipereka, amaona kuti ongodziperekawo ndi “ofunika kwambiri,” koma ntchito yaikulu yomwe ongodziperekawo amagwira sioneka ngati yaphindu m’maso mwa anthu ena. Choncho pofuna kuti asinthe zimenezi, a bungwe la United Nations anaganiza zoti chaka cha 2001 chikhale choganizira anthu ogwira ntchito yodzipereka. M’bokosi lakuti “Chaka Choganizira Anthu Ongodzipereka Padziko Lonse” mwalembedwa zolinga zina zimene a bungwe la United Nations ali nazo.

Pakalipano ntchito ya anthu ongodzipereka ikusintha ndipo kusinthaku kukubweretsa mavuto kwa anthu ongodziperekawo ndi akuluakulu omwe amatsogolera ntchito yawo. Ngakhale zili choncho, anthu ambirimbiri alipobe padziko lonse omwe akufunitsitsa kungodzipereka m’malo mwa anzawo. Kodi n’chiyani chomwe chimawapangitsa kuchita zimenezi? Kodi amachita zotani? Ndipo kodi zochita zawo zingakukhudzeni bwanji inuyo?

[Bokosi patsamba 14]

Nawonso Anthu Ongodzipereka Amapindula

Michael, yemwe akugwira ntchito yongodzipereka kwa maola oŵerengeka ananena kuti “Kuyesetsa kuthandiza ena kwandipindulitsa kwambiri kuposa mmene ndikanapindulira ndikanakhala kuti ndikungogwira ntchito yanga.” Si Michael yekha yemwe amaganiza choncho. Sharon Capeling-Alakija, yemwe ndi mkulu woyang’anira bungwe la anthu ongodzipereka la United Nations Volunteers, ananena kuti: “Padziko lonse anthu amene . . . amangodzipereka amadziŵa bwino mmene amapindulira akangodzipereka.” Dr. Douglas M. Lawson, yemwe ndi katswiri wa nkhani za ntchito yongodzipereka, anatsimikiza kuti ofufuza apeza kuti “nthaŵi zambiri munthu ukangodzipereka kuchita ntchito inayake kwa maola ochepa chabe, umamva bwino kwambiri m’thupi ndiponso m’maganizo ako moti ena ananena kuti kumeneku ndiko ‘kukoma kumene wongodzipereka amamva.’” Ndipo “kukoma kumene ongodzipereka amamva” si kwakanthaŵi kochepa chabe. Ofufuza a payunivesite ya Cornell ku United States anafufuza gulu la anthu kwa zaka zoposa 30 ndipo anapeza kuti “anthu amene anangodzipereka pantchito, anali anthu achimwemwe ndiponso athanzi kuposa amene sanatero.” N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limati “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35; Miyambo 11:25.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

Chaka Choganizira Anthu Ongodzipereka Padziko Lonse

Pa November 20, 1997, bungwe la General Assembly of the United Nations linalengeza kuti chaka cha 2001 chikhale “Chaka Choganizira Anthu Ongodzipereka Padziko lonse.” Bungwe la UN linanena kuti pali zolinga zinayi zoti zichitike m’chaka chimenechi.

Kuzindikira bwino ntchitoyi Maboma akulimbikitsidwa kuzindikira kufunika kwa anthu ongodzipereka mwa kufufuza ndi kulemba ntchito zawo zopambana ndi kuwafupa pa ntchito zabwino kwambiri zimene achita.

Kuika malamulo othandiza Mayiko akulimbikitsidwa kuti alimbikitse ntchito zongodzipereka, mwachitsanzo polola ntchito yongodzipereka kukhala ntchito imene munthu angasankhe m’malo mwausilikali kapena powachotsera msonkho anthu ongodzipereka.

Kuuzana nkhani Olemba nkhani akupemphedwa kuthandiza kwambiri polengeza ntchito zopambana za anthu ongodzipereka. Zikatero, ntchito zoterozo zingachitidwenso kwina, “n’kupeŵa zoti anthu onse komwe ali azidzichitira zaokha.”

Kudziŵitsa anthu Mabungwe a anthu ongodzipereka akuwalimbikitsa kukonza njira zodziŵitsira anthu zaphindu limene anthu onse akupeza chifukwa cha ntchito yongodzipereka.

Bungwe la United Nations likukhulupirira kuti Chaka Choganizira Anthu Ongodzipereka Padziko Lonse cha 2001 chithandiza kuti anthu apemphe ntchito zambiri zoti anthu ongodzipereka achite, popempha anthu ambiri kuti agwire ntchito monga ongodzipereka ndiponso popereka ndalama zambiri ndi malo ogwirira ntchito kuti mabungwe a anthuŵa athandize pa zinthu zambiri zimene anthu akusoŵa. Mayiko 123 ayamba kuthandiza nawo pokwaniritsa zolinga za bungwe la United Nations zimenezi.