Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pemphero Lingandithandize Bwanji?

Kodi Pemphero Lingandithandize Bwanji?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Pemphero Lingandithandize Bwanji?

“Pemphero ndilo linandithandiza kuti moyo wanga ubwerere mwakale,” anatero Brad. *

ACHINYAMATA ambiri akupemphera, mwinanso kuposa mmene mungaganizire. Bungwe la Gullup litafufuza achinyamata a zaka zoyambira 13 mpaka 17 ku United States, panapezeka kuti mwa achinyamata 100 alionse 56 amapemphera kaye asanadye chakudya. Atafufuza mwa achinyamata akuluakulu panapezeka kuti pa achinyamata 100 alionse 62 amapemphera tsiku lililonse.

Komabe kwa achinyamata ambiri pemphero ndi mwambo chabe kapena chizoloŵezi wamba. Achinyamata ochepa ndiwo ali ndi zimene Baibulo limati “chidziŵitso cha Mulungu.” (Akolose 1:9, 10) Ndiye n’chifukwa chake Mulungu samuona ngati wofunika kwambiri m’moyo wawo. Ofufuza ena anafunsa achinyamata ngati anapemphapo Mulungu kuti awathandize maganizo pamene anali kufuna kuchita chinthu china chofunika kwambiri. Mtsikana wina anayankha kuti: “Nthaŵi zonse ndimapempha Mulungu kuti andithandize kuti ndizichita zinthu zolondola.” Komabe iye anavomereza kuti: “Pakali pano sindingathe kukumbukira chinthu chilichonse chimene ndinam’pemphako.” Ndiye si zodabwitsatu kuti achinyamata ambiri sakhulupirira kuti pemphero lili ndi mphamvu kapena kuti lingawathandizedi.

Komabe achinyamata ambirimbiri adzionera okha mphamvu yapemphero ngati mmene zinakhalira ndi Brad yemwe ananena mawu apoyamba paja. Inunsotu mungatero! Nkhani yam’mbuyomu inasonyeza chifukwa chimene tingakhulupirire kuti Mulungu angamve mapemphero athu. * Tsopano funso n’lakuti, Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji? Choyamba, tatiyeni tione mmene Mulungu amayankhira mapemphero athu.

Mmene Mulungu Amayankhira Mapemphero

M’nthaŵi za m’Baibulo amuna ena achikhulupiriro anayankhidwa mapemphero awo mwachindunji, ngakhalenso mozizwitsa. Mwachitsanzo mfumu Hezekiya atadwala kwambiri, anapemphera kwa Mulungu kuti am’chiritse. Mulungu anam’yankha kuti: “Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa.” (2 Mafumu 20:1-6) Amuna ndi akazi ena owopa Mulungu nawonso anathandizidwa ndi Mulungu.—1 Samueli 1:1-20; Danieli 10:2-12; Machitidwe 4:24-31; 10:1-7.

Komabe ngakhale m’nthaŵi za m’Baibulozi, Mulungu sanali kuthandiza anthuŵa mwachindunji nthaŵi zonse. Nthaŵi zambiri Mulungu ankayankha mapemphero a atumiki ake osati mozizwitsa ayi, koma powathandiza kuti “akadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.” (Akolose 1:9, 10) Inde, Mulungu anawathandiza mwakuwalimbikitsa anthu akewo mwauzimu ndiponso mwamaganizo, kuwapatsa nzeru ndi chidziŵitso kuti aganize bwino. Akristu ankati akagwa m’mavuto, si kuti tingati Mulungu ankawachotsera chiyesocho. Mmalo mwake ankawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa,” kuti apirire chiyesocho.—2 Akorinto 4:7, NW; 2 Timoteo 4:17.

Masiku anonso mwina yankho la pemphero lanu silingachite kukhala chinthu choonekeratu. Koma monga mmene Mulungu anachitira m’mbuyomu, angakupatseni mzimu wake woyera n’kukulimbitsani kuti muthane ndi mavuto ena alionse amene mungakumane nawo. (Agalatiya 5:22, 23) Mwachitsanzo tatiyeni tione mmene pemphero lingatithandizire m’njira zinayi izi.

Lingakuthandizeni Poganizira Zinthu Zoyenera Kuchita

Karen anali pachibwenzi ndi mnyamata wina wooneka ngati ali ndi zolinga zauzimu zabwino kwambiri. Iye anati, “Nthaŵi zonse mnyamatayu ankandiuza kuti akufuna kudzakhala mkulu mumpingo.” Zimenezi zinali zabwino ndithu. Komano “ankakambakambanso zabizinesi imene ankafuna kuyambitsa, n’kumatchulanso zinthu zambirimbiri zimene azidzandigulira. Ndinayamba kukayikira ngati anali woona mtima.” Karen anapemphera za nkhani imeneyi. “Ndinam’pempha Yehova kuti ndizindikire ndiponso kuti ndione zoyenera kudziŵa mwa mnyamatayu.”

Nthaŵi zina kupemphera kokhako kumapindulitsa chifukwa kungakuthandizeni kuganizira za mavuto anu n’kuona mmene Yehova akuwaonera. Koma Karen anafunikanso malangizo oti awagwiritse ntchito. Kodi akanayankhidwa mozizwitsa? Taganizirani kaye za nkhani ya m’Baibulo ya mfumu Davide. Atadziŵa kuti mnzake wapamtima Ahitofeli anali kulangiza mwana wake woukira Abisalomu, Davide anapemphera kuti: “Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.” (2 Samueli 15:31) Koma Davide anachitanso mogwirizana ndi pemphero lake. Anam’tuma mnzake Husai pomuuza kuti: “udzanditsutsira uphungu wa Ahitofeli.” (2 Samueli 15:34) Mofananamo, Karen anachita mogwirizana ndi pemphero lake pouza mkulu wokhwima maganizo wachikristu yemwe ankadziŵa chibwenzi chakecho. Mkuluyo anamuuza kuti zimene anali kukayikirazo n’zoona: Mnyamata amene anali naye pachibwenziyo sankalimbikiradi n’komwe kuti akhale wotsogola pa zinthu zauzimu.

Karen ananena kuti: “Nkhani imeneyo inandionetseratu mphamvu yapemphero.” N’zachisoni kuti chibwenzi chake chakalecho chinakonda kwambiri chuma ndipo chinaleka kutumikira Mulungu. “Ndikanakwatiwa naye, bwenzi ndikumapita ndekha kumisonkhano yachikristu,” anatero Karen. Pemphero linam’thandiza Karen kusankha zochita zabwino.

Lingakuthandizeni Kulamulira Maganizo Anu

Pa Miyambo 29:11 Baibulo limati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; Koma wanzeru auletsa nautontholetsa.” Vuto n’lakuti masiku ano anthu ambiri amakumana ndi zinthu zambiri zowasokoneza maganizo ndipo nthaŵi zambiri amalephera kuugwira mtima. Choncho nthaŵi zina zotsatira zake zimakhala zoopsa kwambiri. Mnyamata wina wotchedwa Brian akukumbukira kuti: “Mnzanga wakuntchito ankandivuta. Tsiku lina ananditulutsira mpeni.” Mukanakhala inu mukanatani? Brian anapemphera. Iye anati: “Yehova anandithandiza kuti ndisapupulume ndipo ndinakambirana naye moti sanandibaye. Anasiya mpeniwo n’kumapita.” Kukhazikitsa mtima pansi kunam’thandiza Brian kuti asachite ukali ndipo potero anadzipulumutsa.

Si kuti nthaŵi zonse anthu angakuopsezeni ndi mpeni. Koma pali nthaŵi zambiri pamene mungafunike kuugwira mtima. Pemphero lingakuthandizeni kuti musapupulume.

Lingakuthandizeni Pamene Muli ndi Nkhaŵa

Barbara akukumbukira “nthaŵi ina pamene anavutika kwambiri” zaka zingapo zapitazo. Iye ananena kuti: “Kuyambira ntchito yanga, akwathu, anzanga, palibe chomwe chinali kuyenda bwino. Ndinasoŵa chochita.” Barbara anangozindikira kuti wayamba kupemphera kuti athandizidwe. Koma panali vuto. Iye anati, “Sindinadziŵe choti ndim’pemphe Yehova. Kenaka ndinapempha kuti mtima wanga ukhazikike. Usiku uliwonse ndinkapempha kuti andithandize kuti ndisakhale ndi nkhaŵa ina iliyonse.”

Kodi pemphero limenelo linam’thandiza bwanji? Iye anati: “Patapita masiku ochepa ndinaona kuti ngakhale kuti mavuto anga anali asanachoke, sankandipweteketsanso mutu kapena kundisoŵetsa mtendere.” Baibulo limalonjeza kuti: “Zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

Lingakuthandizeni Kum’konda Kwambiri Mulungu

Taganizirani zimene zinam’chitikira mnyamata wina dzina lake Paul. Iye ananena kuti: “Ndinali nditangosamuka kumene n’kumakhala ndi abale anga ena. Tsiku lina usiku, ndinavutika maganizo kwambiri. Ndinali nditangomaliza kumene maphunziro akusekondale motero anzanga onse ndinawasoŵa kwambiri. Misozi inalengeza m’maso mwanga pokumbukira zinthu zosangalatsa zimene tinkachitira pamodzi.” Kodi Paul akanatani? Anapemphera mochokera pansi pamtima kwa nthaŵi yoyamba. Iye ananena kuti: “Ndinatsegula mtima wanga n’kupempha Yehova kuti andilimbitse ndiponso andikhazike mtima m’malo.”

N’chiyani chinadzachitika? Paul akukumbukira kuti: “Mmaŵa mwake ndinadzuka mtima wanga utatsika kuposa kale lonse m’moyo wanga. Mtima wanga unasiya kuwawa ndipo ndinakhala ndi ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.’” Popeza kuti tsopano mtima wa Paul unali utatsika, anayamba kuchita zinthu mosapupuluma. Ndipo anazindikira mwamsanga kuti “masiku akale” aja sikuti analidi abwino. (Mlaliki 7:10) Ndipotu “anzake” amene anawasoŵa kwambiriwo sanali kum’thandiza kukhala munthu wabwino.

Chofunika kwambiri n’chakuti Paul anadzionera yekha mmene Yehova amathandizira. Anakhulupirira mawu a pa Yakobo 4:8 akuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” Nthaŵi imeneyi ndiyo imene Paul anasinthiratu kwambiri. Zinam’limbikitsa kutsogoza Yehova pochita chilichonse ndiponso kuti apereke moyo wake kwa Yehovayo.

Lankhulani ndi Mulungu!

Nkhani zolimbikitsa zimenezi zikutsimikizira kuti pemphero lingakuthandizeni. Inde, zingakhale choncho pokhapokha ngati mukufunitsitsa kum’dziŵa bwino Mulungu polimbikira kugwirizana naye. Tsoka lake, achinyamata ambiri amazengereza kutero. Carissa anakulira m’banja lachikristu. Koma anavomereza kuti: “Ndikukhulupirira kuti ndi m’zaka zochepa chabe zapitazi pamene ndinayambadi kuzindikira ubale wathu wapadera kwambiri ndi Yehova.” Brad yemwe tam’tchula poyamba paja, analeredwa ngati mkristu koma analeka kulambira koona kwa zaka zingapo ndithu. Iye ananena kuti, “Sindinkafuna kulambira, koma pamene ndinadzazindikira mwayi umene ndinataya ndinam’kumbukira Yehova. Tsopano ndikudziŵa kuti moyo umakhaladi wachabechabe ngati sugwirizana ndi Yehova.”

Komabe musachite kudikira kuti muvutike kaye kuti muyambe kum’konda Mulungu. Yambani panopo kulankhula naye nthaŵi zonse! (Luka 11:9-13) “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake.” (Salmo 62:8) Mukatero simuchedwa kuona kuti pemphero lingakuthandizenidi!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Mulungu Angamve Mapemphero Anga?” mu Galamukani! ya July 8, 2001.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

Pemphero Lingakuthandizeni

● Kuganiza zochita zabwino

● Kuugwira mtima mukavutika maganizo

● Kuziziritsa mtima mukakhala ndi nkhaŵa

● Kum’konda kwambiri Mulungu