Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Wokana Kristu Ndani?

Kodi Wokana Kristu Ndani?

Lingaliro Labaibulo

Kodi Wokana Kristu Ndani?

“MUDAMVA KUTI WOKANA KRISTU AKUDZA.”—1 YOHANE 2:18.

KODI mutauzidwa kuti chigaŵenga choopsa chinaoneka chikuloŵera cha kwanu, mungatani? N’kutheka kuti mungafunitsitse kudziŵa mmene chimaonekera ndiponso zimene chimachita. Mungakhale osamala kwambiri.

Ndi mmene zililinso masiku ano. Mawu a mtumwi Yohane akutichenjeza kuti: “Mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Kristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m’dziko lapansi tsopano lomwe.” (1 Yohane 4:3) Kodi alipo wokana Kristu wotero yemwe ndi mdani wa Mulungu ndiponso wonyenga anthu, yemwe tsopano akuopseza anthu onse?

Yohane anagwiritsa ntchito mawu oti “wokana Kristu” kasanu m’makalata ake aŵiri. Mawuwo amanena za anthu amene amatsutsa zimene Baibulo limaphunzitsa za Yesu Kristu. Amanenanso za anthu amene amadzionetsa ngati Kristu kapena otumidwa ndi iye. Baibulo limatiuza zoona zake za wokana Kristu ameneyu. Koma monga zimakhalira nthaŵi zina kwa anthu opalamula milandu yaikulu, anthu amalabadira kwambiri nkhani zopanda umboni zokhudza gulu losadziŵika bwinoli kuposa nkhani zoona.

Kuganizira Munthu Wolakwika

Kuyambira m’masiku a mtumwi Yohane, anthu akhala akunena kuti mawu a Yohane onena za wokana Kristu amaimira munthu mmodzi. Anthu akhala akuganizira anthu osiyanasiyana kuti ndiwo okana Kristu. Zaka mazana angapo zapitazo anthu ankaganiza kuti Mfumu Yaikulu ya Roma, dzina lake Nero ndiye anali wokana Kristu. Kenaka Adolf Hitler atadanitsa anthu kwambiri ndiponso n’kuwachititsa nthumanzi, ambiri anakhutira kuti iye ndiye anali wokana Kristu. Wafilosofi wina wa ku Germany, Friedrich Nietzsche anatchedwaponso kuti “Wokana Kristu.” Komanso ena amakhulupirira kuti wokana Kristu adzabwerabe ndiponso kuti adzaoneka ngati munthu wochenjera, wandale wankhanza wokhala ndi cholinga cholamulira dziko lonse. Iwo amakhulupirira kuti chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso mutu 13 chimatanthauza wokana Kristu weniweni amene Yohane anatchula. Amanena kuti chizindikiro chake cha 666 penapake chimasonyeza ndithu kuti munthu yemwe adzakhale wandale woipa ameneyo ndiye wokana Kristu amene Yohane ananena.

Anthu amene amagwirizana ndi maganizoŵa akuti Yohane ankanena za wokana Kristu mmodzi yekha. Koma kodi mawu ake akusonyezanji? Taganizirani mawu a pa 1 Yohane 2:18 amene amati: “Mudamva kuti wokana Kristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri.” Inde, kalekale m’zaka za zana loyamba “okana Kristu ambiri,” osati mmodzi ndiwo anayambitsa vuto lauzimu. Masiku ano pali okana Kristu osati mmodzi koma ambiri. Onseŵa apanga gulu limene lawononga kwambiri anthu onse mwauzimu. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Kodi kwenikweni ndi ayani amene ali m’gulu la okana Kristu?

Tiyeni titenge chilombo cha m’Chivumbulutso kukhala wokana Kristuyo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalungwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a fisi, [chimbalangondo, NW] ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango.” (Chivumbulutso 13:2) Kodi zimenezi zikuimira chiyani?

Ophunzira Baibulo aonapo kugwirizana pa Chivumbulutso 13 ndi Danieli 7. Mulungu anaonetsa Danieli masomphenya a zilombo zophiphiritsa. Zilombozo zinali nyalugwe, chimbalangondo ndi mkango. (Danieli 7:2-6) Kodi mneneri wa Mulunguyo anati zikutanthauzanji? Analemba kuti zilombo zimenezo zinaimira mafumu a padziko lapansi, kapena maboma. (Danieli 7:17) Choncho titha kunenadi kuti chilombo cha pa Chivumbulutso chimaimira maboma aanthu. Popeza kuti maboma ameneŵa amatsutsa Ufumu wa Mulungu, ndiye kuti nawonso ndi mbali ina ya wokana Kristu.

Kodi Enanso Amene Ali M’gulu la Wokana Kristu Ndani?

Pamene Mwana wa Mulungu anali padziko, anali ndi adani ambiri. Masiku ano aliponso om’tsutsa ngakhale kuti tsopano sangathenso kum’peza. Taonani omwe ali m’gululi.

Mtumwi Yohane anati: “Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu sali Kristu? Iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.” (1 Yohane 2:22) Ampatuko pamodzi ndi atsogoleri a kulambira konyenga amakhotetsa ziphunzitso za Yesu zomveka bwino n’kuzisandutsa mabodza osokeretsa onyengera anthu m’zipembedzo. Anthu otereŵa amakana choonadi cha m’Baibulo ndipo amafalitsa mabodza m’dzina la Mulungu ndi Kristu. Amakana ubale weniweni umene ulipo pakati pa Atate ndi Mwana pogwiritsa ntchito chiphunzitso chawo cha Utatu. Choncho nawonso ali m’gulu la wokana Kristu.

Yesu anachenjezeratu otsatira ake pa Luka 21:12 kuti: “Anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende . . . chifukwa cha dzina langa.” Kuyambira m’zaka za zana loyamba, Akristu oona apirira kuzunzidwa kodetsa nkhaŵa. (2 Timoteo 3:12) Anthu amene amalimbikitsa khalidwe lozunza limeneli amatsutsa Kristu. Ameneŵanso ali m’gulu la wokana Kristu.

“Iye wosavomerezana ndi ine atsutsana ndi ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi ine amwaza.” (Luka 11:23) Apa Yesu akulengeza kuti onse amene amam’tsutsa ndiponso kutsutsa zolinga za Mulungu zimene iye amatsatira, ali m’gulu la wokana Kristu. Kodi pomalizira pake n’chiyani chidzawachitikire anthu ameneŵa?

Kodi N’chiyani Chidzachitikire Okana Kristu?

Salmo 5:6 limati: “[Mulungu] adzawononga iwo akunena bodza: Munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.” Kodi zimenezi zikukhudza okana Kristu? Inde. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Onyenga ambiri adatuluka kuloŵa m’dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Kristu anadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.” (2 Yohane 7) Mulungu Wamphamvuyonse adzawawononga okana Kristu chifukwa cha mabodza awo ndi kunyenga kwawo.

Pamene chiweruzo chimene chidzaperekedwa chikuyandikira, Akristu oona asalole kunyengedwa ndi kukakamizidwa makamaka ndi ampatuko kuti chikhulupiriro chawo chifooke. Chenjezo la Yohane n’lofunika kwambiri. Chenjezoli n’lakuti: “Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphoto yokwanira.”—2 Yohane 8.

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Chinthunzi cha Nero pamasamba 2 ndi 30: mwachilolezo cha Visitors of the Ashmolean Museum, Oxford