Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuletsa Udani Kuti Usapitirire

Kuletsa Udani Kuti Usapitirire

Kuletsa Udani Kuti Usapitirire

“Kondanani nawo adani anu.”—MATEYU 5:44.

KWA masiku angapo, atsogoleri amayiko odana aŵiri anakambirana kwambiri nkhani zamtendere. Mtsogoleri wina wadziko lamphamvu komanso lolemera analipo pazokambiranazo, poyesa kugwiritsa ntchito luso lake lonyengerera kuti agwirizanitse atsogoleri aŵiriwo. Koma mapeto antchito yovutayi kwenikweni anali kungowonjezera mavutowo. Patangotha milungu iŵiri mayiko aŵiriwo anayamba kumenyana koopsa ndipo magazini ya Newsweek inati mayikoŵa “anali asanamenyanekonso motero kwa zaka makumi aŵiri.”

Padziko lonse, udani sukutha pakati pa mitundu ndiponso mayiko osiyanasiyana, ngakhale kuti atsogoleri amayiko akuyesetsa kwambiri kuuthetsa. Vuto la udani limakulirakulira chifukwa cha kusadziŵa, kudziona ngati oposa ena, ndiponso chifukwa cha mabodza. Koma ngakhale kuti atsogoleri amasiku ano amangodzivutitsa n’kuyesa kupeza njira zatsopano zothetsera vutoli, satha kuona kuti njira yabwino kwambiri imene ilipo ndi njira yakale kwambiri, yomwe inaperekedwa kalekale pa Ulaliki wa pa Phiri. Pa ulaliki umenewo Yesu Kristu analimbikitsa omumvetsera kuti azitsatira njira za Mulungu. Pankhani imeneyi iye ananena mawu ali pamwambaŵa akuti, “Kondanani nawo adani anu.” Malangizo amenewo ndi abwino kwambiri pothetsera vuto la udani ndiponso la tsankhu, komanso ndi malangizo okhawo amene ali othandizadi!

Anthu okonda kukayikira zinthu amangoti n’zosatheka kuti munthu akonde mdani wake. Komabe, ngati udani uli khalidwe lochita kuphunzira, kodi sizomvekanso kunena kuti munthu angathe kuphunzira kuleka mkhalidwewu? Choncho mawu a Yesu n’ngopatsa chiyembekezo chenicheni kwa anthu. Akusonyeza kuti n’kotheka kuthetseratu ngakhale maudani akalekale.

Taganizirani mmene zinthu zinalili m’nthaŵi ya Yesu kwa Ayuda amene ankamumvetsera. Adani awo sanali kutali ayi. Asilikali achiroma anali kulamulira chigawocho, n’kumakhometsa Ayudawo msonkho wochuluka mosayenera, ndale zawo zinali zowadyera ena masuku pamutu, ankawazunza, ndi kuwapondereza. (Mateyu 5:39-42) Komabe panali ena amene ankaona Ayuda anzawo monga adani awo chifukwa cha timilandu timene anatilekelera ndipo tinakula. (Mateyu 5:21-24) Kodi Yesu ankaganizadi kuti anthu amene ankamumvetsera angakonde anthu amene anawakhumudwitsa ndi kuwapsetsa mtima?

Tanthauzo la “Chikondi”

Choyamba, zindikirani kuti ponena kuti “chikondi,” Yesu sanali kutanthauza chikondi chimene mabwenzi apamtima amakhala nacho. Mawu achigiriki otanthauza chikondi amene anatchulidwa pa Mateyu 5:44 amachokera kumawu akuti a·gaʹpe. Mawu ameneŵa amatanthauza chikondi chimene munthu amakhala nacho potsatira mfundo yachikhalidwe. Si kuti kwenikweni n’chikondi cholira kuti munthu akhale wapamtima wanu. Chifukwa chakuti chikondichi chimatsogoleredwa ndi mfundo zachikhalidwe zolungama, chimam’pangitsa munthu kuti aziona ubwino wa ena, ngakhale khalidwe lawo litachita kuipa motani. Motero chikondi cha a·gaʹpe chingagwirizanitse anthu amene amadana. Yesu mwini anasonyeza chikondi choterechi. M’malo motemberera asilikali achiroma amene anam’pachika, iye anapemphera kuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”—Luka 23:34.

Kodi n’kwanzeru kuganiza kuti dziko lonse lingatsatire zimene Yesu anaphunzitsazi ndipo kuti anthu angayambe kukondana? Ayi, chifukwa chakuti Baibulo limati dziko lino likupitirirabe kuipa. “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa,” analosera motero 2 Timoteo 3:13. Komabe, munthu payekha angathe kuletsa udani wake ndi ena kuti usapitirire pophunzira bwinobwino mfundo zachikhalidwe zolungama m’Baibulo. Pali umboni wosonyeza poyera kuti anthu ambiri aphunzira kuletsa udani. Taonani zitsanzo zingapo izi zimene zinachitikiradi anthu ena.

Kuphunzira Kukonda Ena

Ali ndi zaka 13, José anamenya nawo nkhondo m’gulu la zigaŵenga. * Anam’phunzitsa kudana ndi anthu amene iye anauzidwa kuti ndiwo ankayambitsa mavuto onse amene anali kuona. Ngati zidakatheka, cholinga chake chinali chakuti anthuwo asadzaonekenso. Poona anzake ambiri akuphedwa, José anakwiya kwambiri ndipo ankangofuna kubwezera. Ali m’kati mokonza mabomba oponya ndi manja iye ankadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu ambiri akuvutika chonchi? Ngati kunjaku kuli Mulungu, kodi saona n’komwe zonsezi?’ Nthaŵi zambiri ankangokhalira kulira, chifukwa chothedwa nzeru ndiponso kuganiza kwambiri.

Mkupita kwanthaŵi José anapeza mpingo wa Mboni za Yehova kumene ankakhalako. Atakasonkhanako koyamba, anaona nthaŵi yomweyo kuti kunali mzimu wachikondi. Aliyense anam’patsa moni mwachikondi ndiponso mwansangala. Kenaka kunakambidwa nkhani yakuti “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika?” ndipo nkhaniyi inamuyankha mwachindunji mafunso akewo. *

Mkupita kwanthaŵi, kudziŵa zambiri za m’Baibulo kunam’pangitsa José kusintha moyo wake ndi maganizo ake. Anaphunzira kuti “Iye amene sakonda akhala muimfa. Yense wakudana . . . ali wakupha munthu; ndipo . . . wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.”—1 Yohane 3:14, 15.

Komabe kusiyana ndi zigaŵenga zinzakezo kunali kovuta. Nthaŵi iliyonse akapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, ankam’londalonda. Anzake ena mpaka anapita kumisonkhano ingapo kuti adziŵe bwino chimene chinam’pangitsa José kuti asinthe chonchi. Atakhutitsidwa kuti iye sanali kazitape kapena wofuna kuwaika m’mavuto, anam’siya. Atakwanitsa zaka 17, José anabatizidwa n’kuloŵa m’gulu la Mboni za Yehova. Posakhalitsa anayamba kulalikira mokhazikika. M’malo mowapangira anthu chiŵembu chofuna kuwapha, iye tsopano amakawapatsa uthenga wachikondi ndiponso wachiyembekezo!

Kugonjetsa Udani wa Mafuko

Kodi anthu amafuko osiyanasiyana angathetse udani umene umawalekanitsa? Taganizirani zagulu la Mboni za Yehova la ku London, m’dziko la England, loyankhula chilankhulo chotchedwa Amharic. Gululi lili ndi anthu 35, ndipo mwa ameneŵa 20 ndi a ku Ethiopia pamene 15 ndi a ku Eritrea. Iwo amapempherera pamodzi mwamtendere ndiponso mogwirizana ngakhale kuti kwawo ku Africa, anthu a ku Eritrea ndi ku Ethiopia posachedwapa anamenyana nkhondo yodetsa nkhaŵa.

Mboni ina ya ku Ethiopia inauzidwa ndi am’banja lake kuti: ‘Usamawakhulupirire anthu a ku Eritrea!’ Koma panopo iye amawakhulupirira Akristu anzake a ku Eritrea ndipo amawatcha mbale kapena mlongo! Ngakhale kuti anthu a ku Eritrea ameneŵa amalankhula chilankhulo chotchedwa Tigrinya, anakonda kuphunzira Chiamharic chomwe amalankhula abale awo a ku Ethiopia, kuti aziphunzira pamodzi Baibulo. Umenewutu ndi umboni wosangalatsa kwambiri wakuti chikondi chaumulungu n’champhamvudi pokhala “chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:14.

Kuiwala Zakale

Kodi bwanji ngati munthu anazunzidwapo mwauchinyama? Kodi si kwachibadwa kuti adane ndi amene anamuzunzawo? Taganizirani zimene zinam’chitikira Manfred amene ndi Mboni ya ku Germany. Iye anakhala zaka zisanu ndi chimodzi m’ndende ya chikomyunizimu chifukwa choti anali m’gulu la Mboni za Yehova. Kodi anayamba wadanapo ndi amene anam’zunzawo kapena kulakalaka zowabwezera? Iye anayankha kuti “Ayi.” Malingana ndi nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Saarbrücker Zeitung, Manfred analongosola kuti: “Kuchita kapena kubwezera zoipa . . . kumangoyambitsanso vutolo ndipo mumangobwereza kuchitirana zoipa.” Mwachionekere Manfred anali kugwiritsa ntchito mawu a m’Baibulo akuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:17, 18.

Dziko Lopanda Udani!

Mboni za Yehova sizinena kuti zilibiretu vuto pankhani imeneyi. Nawonso amaona kuti nthaŵi zambiri kusiya udani umene wakhalapo kwa nthaŵi yaitali kumavuta. Munthu ayenera kulimbikira mosaleka kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo. Koma kumbali yaikulu, chitsanzo chomwe chilipo chosonyeza mphamvu zimene Baibulo lili nazo zoletsa udani kupitirira n’cha Mboni za Yehova. Kudzera m’ntchito yophunzitsa anthu Baibulo panyumba, Mboni zikuwathandiza anthu ambiri chaka chilichonse kuti aleke kusankhana mitundu ndiponso kudziona ngati oposa ena. * (Onani bokosi lakuti “Malangizo a M’Baibulo Amathandiza Kuletsa Udani.”) Kuyenda bwino kwa ntchitoyi kukungosonyeza pang’ono chabe zotsatirapo zake zantchito yakuphunzitsa anthu padziko lonse imene posachedwapa idzathandize kuchotseratu udani ndi zimene zimauyambitsa. Ntchito yophunzitsayi imene idzachitike m’tsogolomu idzayendetsedwa ndi Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lapadziko lonse. Yesu anatiphunzitsa kupempherera Ufumu umenewo m’Pemphero la Ambuye, pamene anati: “Ufumu wanu udze.”—Mateyu 6:9, 10.

Baibulo limalonjeza kuti pansi pa ufumu wakumwamba umenewu, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova.” (Yesaya 11:9; 54:13) Panthaŵiyi mawu aŵa a Yesaya amene amagwidwa mawu kaŵirikaŵiri adzakwaniritsidwa padziko lonse: “[Mulungu] adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Motero Mulungu mwini wake ndiye adzachotseretu vuto la udani kwamuyaya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Si dzina lake lenileni.

^ ndime 12 Onani Mutu 8, wakuti “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika” m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 21 Mungakonze zomaphunzira Baibulo kwaulere mutapezana ndi Mboni za Yehova kumene mukukhala kapena polembera kwa ofalitsa magazini ino.

[Bokosi patsamba 11]

Malangizo A M’baibulo Amathandiza Kuletsa Udani

“Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu?” (Yakobo 4:1) Nthaŵi zambiri tingachepetse mikangano ndi ena ngati titaphunzira kuletsa zikhumbo zosaganizira ena.

“Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Kuganizira kaye zofuna za ena tisanaganizire zathu ndi njira ina yothetsera mikangano yosadziŵika bwino.

“Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) Tingathe kuletsa chizoloŵezi chamtima wapachala ndipo tiyeneradi kutero.

“Mulungu . . . analenga mitundu yonse ya anthu [mwa munthu mmodzi, NW], kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:24, 26) Si kwanzeru kuona ngati mtundu wathu n’ngoposa mitundu ina, chifukwa chakuti tonse ndife a m’banja limodzi la anthu onse.

‘Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, muziona anzanu ngati okuposani.’ (Afilipi 2:3) Kunyoza ena n’kupanda nzeru chifukwa nthaŵi zambiri anthu ena amakhala m’pokomera pawo pamene ife tilibe. Palibe fuko kapena mtundu wa anthu umene uli nazo zokoma zonse.

“Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma.” (Agalatiya 6:10) Kungoyamba chabe inuyo kukhala wansangala ndiponso wothandiza ena, mosaganizira fuko kapena mtundu wawo, kungathetse kusamvetsetsana ndipo kungachititse kuti muzikhala momasuka ndi ena.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Mboni za ku Ethiopia ndi za ku Eritrea zikupempherera pamodzi mwamtendere

[Chithunzi patsamba 10]

Manfred, amene anapulumuka m’ndende yachikomyunizimu, sanalole kuti udani umugonjetse

[Chithunzi patsamba 10]

Baibulo lingathandize kugonjetsa udani umene umagaŵanitsa anthu