Matenda Opatsirana Amaopsa Koma Amapeŵeka
Matenda Opatsirana Amaopsa Koma Amapeŵeka
ZIVOMEZI zowononga ndiponso kusefukira kwa madzi kochititsa mantha amazilemba patsamba loyamba la nyuzipepala, koma kuwanda kwa matenda opatsirana sakutchukitsa m’nyuzipepala. Ngakhale zili choncho, “anthu amene amamwalira chifukwa cha matenda opatsirana (monga EDZI, malungo, zifuwa ndiponso kutsegula m’mimba) anaposa anthu amene anamwalira chaka chatha chifukwa cha tsoka lachilengedwe moŵirikiza nthaŵi 160 ndipo vutoli likukula kwambiri.” Inatero nkhani ina ya bungwe la Red Cross/Red Crescent yolengezedwa mu June 2000.
Akuti pali zinthu ziŵiri makamaka zimene zikuchititsa kuti zinthu ziopse choncho. Choyamba n’kufala kwa EDZI, nthenda imene imapha anthu 300 ola lililonse. Peter Walker, mkulu wa bungwe loona za ngozi padziko lonse la International Federation of Red Cross and Red Crescent Societies ananena kuti, “EDZI si matendanso masiku ano, koma ndi mliri.” “Nthenda yofala kwambiri chonchi imapha anthu ogwira ntchito ndipo imagwetsa chuma chadziko.” Chachiŵiri n’kuloŵa pansi kwa kusamalira anthu odwala kumene kwabweretsanso matenda akale monga chifuwa chachikulu, chinzonono ndiponso malungo. Mwachitsanzo, m’dziko lina la ku Asia akuti panopo pakumakhala anthu atsopano odwala chifuwa chachikulu okwana 40,000 chaka chilichonse. M’zaka khumi zapitazo, matenda a chinzonono aŵirikiza ka 40 m’dziko lina kum’maŵa kwa Ulaya.
Komabe kudabwitsa kwake n’kwakuti ngakhale matenda opatsiranaŵa asanduka miliri, iwo ali m’gulu la ngozi zopeŵeka kwambiri. Ndipotu akuti anthu ambiri mwa anthu mamiliyoni 13 omwe anamwalira mu 1999 chifukwa cha matenda opatsirana akanatha kupeŵa matendawo pogwiritsa ntchito madola asanu pa munthu mmodzi aliyense.” Kukanakhala kuti maboma padziko lonse akufunitsitsa kuwonongera munthu mmodzi ndalama zokwana madola asanu pa zaumoyo, zimene zikukwana madola 30 biliyoni pamodzi, ndiye tangoganizani kuti ndi anthu ambiri bwanji amene akanawapulumutsa!
Ngakhale zimenezi zili ndalama zambiri, tikayerekezera ndi ndalama zimene zimawonongedwa padziko lonse pa zinthu zina, zimenezo n’zochepa kwambiri. Mwachitsanzo, chaka china cha posachedwapa, ndalama zimene dziko lonse linawonongera pankhondo zinakwana madola mabiliyoni 864. Zimenezi zikutanthauza kuti anawononga madola 144 pa munthu mmodzi. Tangoganizani ndalama zimene zikuwonongedwa pokonzekera nkhondo kuposa zimene zikuwonongedwa pofuna kuteteza kufala kwa matenda! N’kutheka kuti anthu sangathe kuthetsa kufala kwa matenda opatsirana, osati chifukwa chosoŵa ndalama koma pazifukwa zovuta kwambiri kuzimvetsa. Maboma aanthu akukanika ngakhale kuyamba kaye achita zinthu zofunikira asanachite zina.
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
X ray: New Jersey Medical School—National Tuberculosis Center
Chithunzi chamunthu yemwe akutsokomola: WHO/Thierry Falise