Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Si la Achinyamata Ang’onoang’ono Okha

Si la Achinyamata Ang’onoang’ono Okha

Si la Achinyamata Ang’onoang’ono Okha

Mtsikana wina wazaka 25 dzina lake Jolanta anafotokoza m’kalata yake imene analembera likulu la Mboni za Yehova ku Poland kuti ankavutika maganizo kwambiri. Iye n’ngolumala moti satha kuyenda, ndipo m’miyezi isanu ndi umodzi yokha, amayi ndi agogo ake aakazi anamwalira. Koma kenaka anayamba kuŵerenga buku la Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Analemba kuti:

“Ndinkaganiza kuti bukuli linali lothandiza achinyamata ang’onoang’ono osati ine, koma ndinkalakwitsa bwanji! Nditaphunzira mitu 12 mpaka 16 m’bukuli, mafunso anga anayankhidwa bwino. Mafunso akuti: ‘Kodi n’chifukwa ninji ndimachita tondovi kwambiri ndi kusukidwa?’ ‘Kodi n’chifukwa ninji sindimadzikonda?’ ndiponso kuti ‘Kodi n’chifukwa ninji ndakhala ndi chisoni chonchi abale anga okondedwa atamwalira?’”

Anapitiriza kuti: “Mfundo ziŵiri izi zimene zili patsamba 130 zinandisangalatsa: ‘Kudziŵa kuti kuchita chisoni n’chibadwa n’kothandiza kwambiri. Koma, kupitirizabe kusakhulupirira zimene zachitikazo kumangotalikitsa chisonicho.’ Nditaŵerenga mawu ameneŵa ndinalimba mtima n’kukhala ndi chiyembekezo chodzawaona anthu amene agona mu imfa, ndipo zimenezi zinandipatsa mphamvu kwambiri.”

Ngati mukufuna kuthetsa madandaulo anu ndiponso kuti moyo wanu ukhale wosangalatsa, tikukhulupirira kuti inunso mungapindule mutaŵerenga buku limeneli la Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Kuti mulandire buku lanu, lembani zoyenera m’mizere ili pamunsiyi n’kutumiza ku adiresi imene yaperekedwayo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni buku la Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Lembani chilankhulo chimene mukufuna.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.