Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Udani Wasanduka Mliri Wapadziko Lonse

Udani Wasanduka Mliri Wapadziko Lonse

Udani Wasanduka Mliri Wapadziko Lonse

KWABWERA chilombo choopsa chotchedwa udani. Ndipo chikungodziyendera padziko lonse.

M’mayiko otchedwa Balkans muli chigawo china chimene chikuvutikabe chifukwa cha nkhondo yaposachedwapa yofuna kuseseratu gulu linalake la anthu. Udani umene wakhalapo kwa zaka mazana ambiri wachititsa anthu ambiri kupululidwa, kugwiriridwa, ndi kuthamangitsidwa. Waotchetsa ndiponso kulanditsa katundu yense wam’nyumba ndi m’midzi, wawonongetsa mbewu zam’munda pamodzi ndi ziweto, ndiponso wabweretsa njala. Mabomba okwirira pansi akupezekabe ambiri.

M’dziko la East Timor, lomwe lili kumwera cha kum’maŵa kwa Asia, anthu 700,000 ogwidwa ndi mantha, anali balalabalala pothaŵa kuphedwa, kumenyedwa, kuwomberedwa mwachisawawa, ndiponso pothamangitsidwa kuchoka kwawo. Zigaŵengazo zinasakaziratu malowo moti anthuwo anawasiya malowo atasanduka bwinja. M’modzi wa anthuwo analira n’kumati: “Ndikungoona ngati ndine nyama imene ikusakidwa.”

Mumzinda wa Moscow, mdadada wina wanyumba zokhalamo unagumulidwa ndi bomba lalikulu limene linaphulitsidwa ndi zigaŵenga. Mitembo ya anthu 94 osalakwa, ena mwa iwo ana, inangoti mbwee chifukwa cha kuphulika kwa bombalo. Anthu opitirira 150 anavulala. Zinthu zoopsa ngati zimenezi zikachitika, anthu amadzifunsa kuti, ‘Kodi zigaŵengazi zikachoka pano ziloŵera kunyumba ya ndani?’

Mumzinda wa Los Angeles, ku California, munthu wina wodana ndi mafuko ena anawomba zipolopolo pofuna kuwombera kagulu ka ana achiyuda osayamba sukulu ndipo kenaka anawombera munthu wogwira ntchito yopereka makalata wochokera ku Phillipines.

Kunenadi zoona tingati udani ndi mliri wapadziko lonse. Pafupifupi tsiku lililonse, nkhani zimene timamva zimasonyeza zimene zimachitika anthu amene ali ndi udani wafuko, utundu, kapena chipembedzo akayambanso kuswa lamulo. Timaona mayiko, magulu a anthu, ndiponso mabanja akugaŵanika. Timaona mayiko atasokonezeka chifukwa chankhondo zofuna kupulula anthu agulu linalake. Timaona anthu ena akuchitira anzawo zinthu zauchinyama weniweni chifukwa chakuti “n’ngosiyana ndi iwowo.”

Kuti chilombo chimenechi chotchedwa udani chiletsedwe kumangodziyendera tiyenera kumvetsetsa chimene chimayambitsa udani wachiwawa. Kodi udani n’chibadwa cha anthu? Kodi ndi khalidwe lochita kuliphunzira? Kodi n’zotheka kuletsa udani kuti usapitirire?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Kemal Jufri/Sipa Press