Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ankakondwera ndi Malonda a Ukapolo?

Kodi Mulungu Ankakondwera ndi Malonda a Ukapolo?

Lingaliro Labaibulo

Kodi Mulungu Ankakondwera ndi Malonda a Ukapolo?

ANTHU akuda akungokha thukuta ndipo angoti werawera atathyoka nawo mabelo ambiri a thonje uku akuyenda mokwakwaza miyendo kuti akakwere zombo zapamadzi. Atsogoleri awo ankhanza akuwaumiriza kugwira ntchito powakwapula ndi zikoti zachikopa cha nyama. Ana omwe akulira mokuwa kwambiri akulandidwa m’manja mwa amayi awo, nawonso amayiwo akulira ndipo akugulitsidwa kwa amponda matiki. Izi n’zina zomvetsa chisoni kwambiri zimene zimabwera m’maganizo mukaganizira zaukapolo.

Koma chodabwitsa n’chakuti, akuti anthu ambiri amene ankagula ndi kugulitsa akapolo anali anthu okonda zachipembedzo kwambiri. Wolemba mbiri wotchedwa James Walvin analemba kuti: “Panali anthu ambirimbiri amene ankatero, a ku Ulaya ndiponso a ku America, ankatamanda Ambuye kuti akuwadalitsa, ndipo anali kuthokoza chifukwa cha malonda opindulitsa ndiponso oyenda bwino a mu Africa pobwerera kwawo kuwoloka nyanja yaikulu kupita ku America.”

Anthu ena afika mpaka ponena kuti Mulungu ankakondwera ndi malonda a ukapolo. Mwachitsanzo, polankhula pamsonkhano wa General Conference of the Methodist Protestant Church m’chaka cha 1842, Alexander McCaine ananena kuti lamulo la ukapolo “linaikidwa ndi Mulungu Mwiniwake.” Kodi McCaine ananenadi zoona? Kodi Mulungu ankagwirizana nako kuba ndi kugwiririra atsikana, kulekanitsa mabanja mwankhanza ndiponso kumenya anthu mopanda chifundo kumene kunali kuchitika panthaŵi yaukapolo m’nthaŵi ya McCaine? Nanga tinganeneponji masiku ano pankhani ya anthu mamiliyoni ambiri amene akuumirizidwa kuti azigwira ntchito ngati akapolo powazunza moipa kwambiri? Kodi Mulungu amakondwera nazo zinthu zauchinyama zimenezi?

Ukapolo M’nthaŵi ya Aisrayeli

Baibulo limati “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Mwina mfundo imeneyi inaonekera kwambiri poyera nthaŵi yaukapolo wosiyanasiyana wankhanza umene anthu akhala akuuchita. Sikuti Yehova Mulungu saganizira mavuto amene ukapolo unabweretsa.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinawaonekera Aisrayeli. Baibulo limatiuza kuti Aigupto “anawawitsa moyo wawo ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zawo zonse zimene anawagwiritsa n’zosautsa.” Aisrayeli “anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wawo, nalira, ndi kulira kwawo kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.” Kodi Yehova sanali kuwaganizira pamavuto awoŵa? Nkhaniyo sili choncho ayi. “Mulungu anamva kubuula kwawo, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.” Kuwonjezera pamenepo, Yehova anauza anthu ake kuti: “ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu.”—Eksodo 1:14; 2:23, 24; 6:6-8.

N’zoonekeratu kuti Yehova sanavomereze kuti ‘wina alamulire mnzake’ kudzera muukapolo wankhanza. Koma kodi kenaka Mulungu sanalole ukapolo pakati pa anthu ake? Analoladi. Komabe ukapolo umene unalipo ku Israyeli unali wosiyana kwambiri ndi ukapolo wonse wankhanza umene wakhalapo m’mbiri yonse.

Chilamulo cha Mulungu chinanena kuti kuba ndi kugulitsa munthu ndi milandu yoyenera kuphedwa. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anapereka malamulo otetezera akapolo. Mwachitsanzo, kapolo wina akavulazidwa modetsa nkhaŵa ndi mbuye wake, anali kum’masula. Ngati kapolo wina wamwalira chifukwa chomenyedwa ndi mbuye wake, mbuyeyo anayenera kuphedwa. Akazi ogwidwa anali kukhala akapolo, kapena anali kuwakwatira. Koma sanali kuwatenga n’cholinga chomangowagona basi. Komabe mfundo yaikulu ya m’Chilamulo iyenera kuti inathandiza Aisrayeli amtima wabwino kuti aziwalemekeza ndiponso kuwachitira chifundo akapolo, ngati mmene akanachitira ndi antchito owalipira.—Eksodo 20:10; 21:12, 16, 26, 27; Levitiko 22:10, 11; Deuteronomo 21:10-14.

Ayuda ena anadzipereka kukhala akapolo a Ayuda anzawo n’cholinga chakuti abweze ngongole. Kuchita zimenezi kunawateteza kuti asafe ndi njala ndipo kwenikweni kunathandiza ambiri kuti asakhale aumphaŵi. Komanso panthaŵi zina zofunika kwambiri pa kalendala ya Ayuda, akapolo anali kuwamasula ngati akufuna. * (Eksodo 21:2; Levitiko 25:10; Deuteronomo 15:12) Pothirira ndemanga pa zamalamulo ameneŵa okhudza akapolo, katswiri wina wachiyuda wamaphunziro wotchedwa Moses Mielziner ananena kuti “kapolo ankakhalabe munthu basi, iye anali kutengedwa monga munthu wokhala ndi ufulu wachibadwidwe wina wake ndithu, woti ngakhale mbuye wake analibe nawo mphamvu yoti aloŵererepo.” Zinalitu zosiyana kwabasi ndi ukapolo wankhanza wopundula anthu umene unkachitika m’mbiri!

Ukapolo M’nthaŵi ya Chikristu

Mu Ufumu wa Roma umene Akristu a m’zaka za zana loyamba anakhalamo, ukapolo unali m’gulu la ntchito zopindulitsa. Choncho Akristu ena anali akapolo, ndipo ena anali ndi akapolo awo. (1 Akorinto 7:21, 22) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti ophunzira a Yesu anali eni akapolo ankhanza? Ayi ndithu! Kaya lamulo la Aroma linalola zinthu zotani, n’zosakayikitsa kuti Akristu sanachitire nkhanza anthu amene anali kuwalamulira. Ndipotu mpaka mtumwi Paulo anam’limbikitsa Filemoni kuti azimuona Onesimo kapolo wake amene anadzakhala Mkristu, ngati “mbale.” *Filemoni 10-17.

Baibulo silisonyeza kuti chinali cholinga choyambirira cha Mulungu chakuti anthu azikhala akapolo kwa anzawo. Kuwonjezera pamenepo, palibe ulosi uliwonse wa m’Baibulo umene umasonyeza kuti anthu ena adzakhala akapolo a anthu anzawo m’dziko latsopano la Mulungu. M’malo mwake, m’Paradaiso amene akudzayo, olungama “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Mika 4:4.

N’zoonekeratu kuti Baibulo siligwirizana nazo zozunza ena m’njira ina iliyonse. Mosiyana ndi zimenezo, limalimbikitsa anthu kuchitirana ulemu ndiponso kukhala olingana. (Machitidwe 10:34, 35) Limalimbikitsa anthu kuchitira anzawo zinthu zimene iwo angakonde kuchitiridwa. (Luka 6:31) Ndiponso, Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti azidzichepetsa n’kumaona ena monga owaposa, ngakhale ali onyozeka. (Afilipi 2:3) Mfundo zimenezi n’zosagwirizana n’komwe ndi ukapolo wankhanza umene mayiko ambiri achita, makamaka m’zaka mazana zaposachedwapa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mfundo yakuti zinkatheka kulola akapolo ena kukhalabe ndi ambuye awo ikusonyezeratu poyera kuti ukapolo wa Aisrayeli sunali wankhanza.

^ ndime 13 N’chimodzimodzinso masiku ano, Akristu ena amalemba anzawo ntchito; ena amalembedwa ntchito. Mongadi mmene Mkristu wolemba mnzake ntchito sangazunze anthu amene akum’gwirira ntchito, ophunzira a Yesu m’zaka za zana loyamba akanachitiranso akapolo mogwirizana ndi mfundo za Chikristu.—Mateyu 7:12.