Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Vuto Lokhala Wamantha Mukamakumbukira Zoopsa Ndi Lotani Kwenikweni?

Kodi Vuto Lokhala Wamantha Mukamakumbukira Zoopsa Ndi Lotani Kwenikweni?

Kodi Vuto Lokhala Wamantha Mukamakumbukira Zoopsa Ndi Lotani Kwenikweni?

ZAKA ZAPITAZO, vuto limeneli lotchedwa post-traumatic stress disorder (PTSD) nthaŵi zambiri linkagwira asilikali opuma pantchito. Masiku ano zinthu zasintha kwambiri. Munthu sayenera kukhala msilikali kuti apezeke ndi vutoli. Munthu angam’peze ndi vutoli malinga ngati anapulumuka chinachake choopsa.

Choopsacho chitha kukhala nkhondo kapena kufuna kugwiriridwa ngakhalenso kuchita ngozi yagalimoto. Chikalata china cholembedwa ndi bungwe la National Center For PTSD, ku United States, chinalongosola motere: “Amene angapezedwe ndi vuto la PTSD ndi munthu yekhayo amene anakumanako ndi zoopsa.” Munthuyu “akhale kuti anakumana kapena anangotsala pang’ono kukumana ndi chinthu chinachake CHOM’VULAZA kapena chom’vutitsa.”

Jane, amene tam’tchula m’nkhani yoyamba ija ananena kuti: “Ndazindikira kuti kukumana ndi zoopsa zokututumutsa kumakuchititsa kukhala ndi nthumanzi kwambiri ndipo zimenezi zimakuchititsa kuti usamachedwe kudzidzimuka ndi chilichonse chokuopseza. Mwachibadwa mtima umabwerera m’malo mwamsanga zoopsazo zikapita, koma kwa anthu odwala PTSD, mtima umangokhalabe m’mwamba.” Zoopsazi zinachitika kalekale, koma nthumanzi ya zimene zinachitikazo inkaoneka ngati siidzachoka m’maganizo a Jane, monga mlendo wobwera yekha amene akukana kuchoka panyumba panu.

Ngati munapulumuka zoopsa ndipo zinthu zovutazi zikukuchitikirani, ndibwino kudziŵa kuti simuli nokha. M’buku lina lokhudza nkhani zogwirira limene analemba Linda E. Ledray analongosolamo kuti kudwala PTSD “n’kwachibadwa ndipo aliyense amene anakumanapo ndi zoopsa mwakuti sakanatha kuchita chilichonse kuti adziteteze angakhale ndi vutoli.”

Komabe, kunena kuti kudwala PTSD n’nkwachibadwa sikukutanthauza kuti aliyense amene anakumanako ndi zoopsa angakhale ndi vutoli. Ledray ananena kuti: “Pakufufuza kwina mu 1992 anapeza kuti, anthu amene anafunsidwa patatha mlungu umodzi atawagwirira, anthu 94 mwa 100 alionse anali ndi vutoli ndipo pakutha milungu 12, anthu 47 mwa 100 alionse anali kudwalabe. Akazi 50 mwa 100 alionse amene anapimidwa pachipatala cha anthu ogwiriridwa cha Sexual Assault Resource Service mumzinda wa Minneapolis m’chaka cha 1993 anapezedwabe ndi vutoli patatha chaka chimodzi atawagwirira.”

Zimenezi zikusonyeza kuti vuto la PTSD n’nlofala kuposa mmene anthu ambiri amaganizira. Ndipo anthu okhala ndi vutoli n’ngosiyanasiyana, ndipo amavutikanso pazifukwa zosiyanasiyana. Anthu ena olemba mabuku, Alexander C. McFarlane ndi Lars Weisaeth anathirira ndemanga ponena kuti: “Kufufuza kwaposachedwa kwasonyeza kuti nthaŵi zambiri zinthu zoopsa zimawachitikira anthu wamba panthaŵi yamtendere komanso zimawachitikira asilikali kapena anthu ovutitsidwa pankhondo, ndiponso kuti opulumuka pazinthu zoopsazi amadwala PTSD.” Ngakhalenso mitundu inayake yachithandizo chamankhwala kapenanso matenda amtima zimachititsa anthu ena kudwala PTSD.

“Zikuoneka kuti vuto la PTSD lafala kwambiri,” anatero olemba mabuku tawatchula pamwambaŵa. Iwo anapitiriza kunena kuti: “Atafufuza mwachisawawa pakati pa achinyamata a ku America, okwana 1,245 anapeza kuti 23 mwa 100 alionse anavutitsidwapo kapena kugwiriridwa, ngakhalenso kuonerera ena akuvutitsidwa. Wachinyamata mmodzi pa achinyamata asanu alionse otere anayamba kudwala PTSD. Zimenezi zikusonyeza kuti pafupifupi achinyamata oposa miliyoni a ku United States ali ndi vuto la PTSD tikunena pano.

Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti m’dziko limodzi lokhali muli achinyamata ambiri amene ali ndi vutoli! Kodi anthu otereŵa ndiponso odwala ena mamiliyoni ambiri padziko lonse angathandizidwe motani?

Kodi Angathandizidwe Motani?

Ngati mukuganiza kuti inuyo kapena munthu wina amene mumam’dziŵa akudwala PTSD, mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni.

Yesetsani kukhala ndi chizoloŵezi chochita zinthu zauzimu. Jane akulongosola kuti “Nthaŵi zonse ndinali kupita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya m’dera lathu. Ngakhale pamene ndinkakanika kumvetsera bwinobwino zimene zikukambidwa, ndinali kudziŵa kuti Yehova Mulungu akufuna kuti ndizipezeka kumeneko. Anthu onse a mumpingo mwathu ankandikonda kwambiri ndiponso anandilimbikitsa, ndipo kundikonda kwawo komanso kundiganizira kwawo kunandithandiza kwambiri panthaŵi yonse imene ndinali kuvutika.” Jane anapitiriza kunena kuti: “Chinanso chinandithandiza ndicho kuŵerenga masalmo. Ndikamaŵerenga mapemphero a anthu osauka ankangondimvekera ngati akupempherera ineyo. Ndikamapemphera ndiye n’kuona kuti ndikulephera kunena zimene ndikufuna ndinkangoti “Amen.’”

Musachite mphwayi kumulimbikitsa wodwalayo. Ngati munthu wina amene mumakonda akuvutika maganizo akamakumbukira zoopsa zimene zinam’chitikira, mvetsetsani kuti si kuti iyeyu akuchita kuwonjeza kapena kuti akuvuta. Chifukwa chosokonezeka maganizo, nkhaŵa, kapena kukwiya, iye angakanike kusintha monga mmene mungafunire pamene mukuyesa kumuthandiza maganizo. Koma musalekere pomwepo! Baibulo limanena kuti, “bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

Wovutikayo ayenera kudziŵa ndiponso kupeŵa njira zina zopusa zothetsera vuto lake zimene zimayambitsa mavuto ena. Zina mwanjirazi ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kumwa mowa mwauchidakwa. Ngakhale kuti mowa ndiponso mankhwala osokoneza bongo angam’chititse munthu kumva ngati ali bwino kwakanthaŵi, posakhalitsa munthuyo zingamuike m’mavuto ena aakulu. Nthaŵi zambiri amachititsa kuti munthu akhale ndi vuto la kudzipatula, kuthaŵa anthu amene akufuna kumuthandiza, kugwira ntchito mosalekeza, mtima wapachala, kudya kwambiri kapena kudya pang’ono, kapenanso kuchita makhalidwe ena ofuna kudzipha.

Kaonaneni ndi dokotala wodziŵadi ntchito. N’kutheka kuti munthuyo alibe vuto la PTSD, koma ngati ali nalo, thandizo lilipo. * Ngati mukulandira chithandizo, musam’bisire kanthu dokotala amene akukuthandizaniyo ndipo funsani mmene mungathetsere makhalidwe alionse atchulidwa pamwambaŵa.

Kumbukirani kuti: Nthaŵi zambiri zilonda ndizo zimayamba kuchiritsidwa, koma anthu odwala PTSD amavulazidwa m’njira zambiri, monga m’thupi, m’maganizo, ndiponso mumtima. Nkhani yotsatirayi ilongosola njira zinanso zimene wodwala ndiponso anthu amene amakhala naye angachite kuti achire ndiponso ilongosola chiyembekezo cha anthu onse omwe amakhala ndi mantha chifukwa chokumbukira zoopsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Mboni za Yehova sizisankhira anthu mtundu uliwonse wachithandizo, kaya chamankhwala kapena chokhudza maganizo.

[Bokosi patsamba 22]

Zizindikiro za Vuto la PTSD

Anthu ambiri amene anakumanapo ndi zoopsa amangozindikira kuti zoopsazo zikuwabwererabe m’maganizo. Nthaŵi zambiri anthuŵa satha kupewa kapena kuletseratu kuti zimenezi zisawachitikire. Mapeto ake angamaone zinthu zotsatirazi:

• Kumangoona ngati kuti zoopsazo zikuchitikanso

• Maloto oopsa

• Kumangotutumuka pakamveka phokoso lalikulu kapena munthu akadutsa kumbuyo kwawo mwadzidzidzi.

• Kusakhazikika maganizo ndiponso kumangotuluka thukuta

• Mtima umagunda kwambiri kapena amavutika popuma

• Kukwiya akawona, akamva, akakhudza, akanunkhiza kapena akalaŵa chinthu chowakumbutsa zoopsazo

• Nkhaŵa kapena mantha—kumva ngati pali chinanso choopsa chomwe chawapeza

• Kulephera kuugwira mtima chifukwa chakuti zinthu zimene zimawakumbutsa zoopsazo zimawadetsa nkhaŵa ndiponso kuwapsetsa mtima mwadzidzidzi

• Kulephera kuchita zinthu kapena kuganiza bwinobwino

• Kuvutika kuti apeze tulo kapena kuti agone bwinobwino

• Kusakhazikika maganizo ndiponso kukhala watcheru paliponse poopa kupezana ndi zoopsa

• Kulepheleratu kuganiza kapena osaganizanso monga mwakale

• Kusatha kukonda ena kapena kusonyeza khalidwe lililonse lokoma

• Kumangoona ngati kuti zimene akuona zasintha kapena kuti si zenizeni

• Kusakhalanso ndi chidwi ndi zinthu zimene poyamba ankakonda

• Kulephera kukumbukira zinthu zofunika kuzidziŵa zimene zinachitika pamene anakumana ndi zoopsazo.

• Kuona ngati sakukhudzidwa ndi zimene anthu ena akuchita ndiponso zimene zikuwachitikira

[Zithunzi pamasamba 20, 21]

Pali zoopsa zosiyanasiyana zimene zingayambitse vuto la PTSD