Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziŵa Zizindikiro Zake

Kudziŵa Zizindikiro Zake

Kudziŵa Zizindikiro Zake

“Kumva chisoni n’kwachibadwa, ndiponso kumasonyeza kuti munthu ali bwino, koma kukhala ndi maganizo ofoola ndi vuto. Vuto lagona pomvetsetsa ndi kudziŵa kusiyana kwake,” anatero Dr. David G. Fassler.

MOFANANA ndi matenda ena onse, kuvutika maganizo kuli ndi zizindikiro zodziŵikiratu. Koma m’povuta kudziŵa vutoli mwakungoona mmene munthuyo akuonekera. N’chifukwa chiyani kuli kovuta? Chifukwa chakuti pafupifupi achinyamata onse amakhala achisoni nthaŵi ndi nthaŵi, ngati mmene amachitira akuluakulu. Kodi kusiyana kwa kumva chisoni ndi kuvutika maganizo n’chiyani? Kwenikweni ndi kukula ndiponso kukhalitsa kwa vutolo.

Kukula kwake ndi zinthu monga mmene maganizo ofoola akum’vutitsira wachinyamata. Kuvutika maganizo si kuti n’kuthedwa nzeru kwa nthaŵi yochepa chabe, koma ndi vuto lofooleratu maganizo limene limam’lepheretsa wachinyamata kuchita zinthu bwinobwino. Dr. Andrew Slaby anafotokoza kupweteka kwa vutoli motere: “Taganizirani ululu waukulu kwambiri umene munaumvapo, mwina kunali kuthyoka fupa, kuwawa kwa dzino, kapena ululu wa pobereka, ndiye muŵirikize ululuwu ka khumi. Ndiye muyerekezere kuti simukudziŵa chimene chadzetsa ululuwu. Ngati mwatero ndiye kuti mwatha kuganizira chabe kusautsa kwake kwa kuvutika maganizo.”

Kukhalitsa kwake kukukhudza nthaŵi imene munthu wakhala ndi vuto lofoolali. Pulofesa wa zachipatala Leon Cytryn ndi pulofesa mnzake Donald H. McKnew ananena kuti, “mwana amene sakuoneka kukhazikika maganizo kapena kuti ali bwino ngati patha mlungu umodzi atakhumudwa (pachifukwa china chilichonse) kapena patatha miyezi isanu ndi umodzi atasoŵa chinthu chimene iye angaone kuti n’chofunika kwambiri, angathe kuvutika maganizo.”

Zizindikiro Zodziŵika Kwambiri

Wachinyamata angapezedwe ndi vuto limeneli pokhapokha ngati akuonetsa zizindikiro zake zambiri kaŵirikaŵiri tsiku lina lililonse, kwa milungu iŵiri. Kuvutika maganizo kwanthaŵi yochepa, amakutcha kuti vuto la maganizo losakhalitsa. Munthu angam’peze ndi vuto la maganizo lokhalitsa ngati ali ndi zizindikiro zake kwa chaka chathunthu koma osapezako bwino ngakhale kwa miyezi yoposa iŵiri. Kodi pa mitundu yonse iŵiri ya kuvutika maganizo kumeneku pali zizindikiro zina zotani zodziŵika kwambiri? *

Khalidwe ndi zochita zimasintha mwadzidzidzi. Wachinyamata yemwe poyamba amakhala womvera amasintha mwadzidzidzi kukhala wamwano. Achinyamata ovutika maganizo amakonda khalidwe loukira ndiponso lothaŵa panyumba.

Kudzipatula. Wachinyamata wovutikayu amadzipatula pakati pa anzake. Kapena kuti nthaŵi zina anzakewo amam’thaŵa, poona kusintha kwina koipa pa zochita ndiponso khalidwe lake.

Chidwi chimachepa pafupifupi pa zochita zina zilizonse. Kaŵirikaŵiri wachinyamatayo amangokhala ndwii. Zinthu zimene posachedwa zinali kum’sangalatsa kwambiri zimasanduka zom’nyong’onya.

Kusintha pa kadyedwe. Akatswiri ambiri amati nthaŵi zambiri mavuto ena monga matenda odana n’kudya ndiponso matenda omangodya kenaka n’kumasanza komanso kudya mosalekeza nthaŵi zambiri zimatsatana (ndipo nthaŵi zina zingayambe chifukwa cha) kuvutika maganizo.

Mavuto a tulo. Wachinyamatayo mwina amangogona pang’ono kapenanso amagona kwambiri zedi. Ena amasokonezeka nthaŵi yogona, n’kumakhala ali maso usiku wonse koma n’kumagona masana onse.

Mavuto a kusukulu. Wachinyamata wovutika maganizo amavutana ndi aphunzitsi ndiponso anzake, ndipo amayamba kulephera. Posakhalitsa wachinyamatayo safunanso n’komwe kupita kusukuluko.

Khalidwe loika moyo pachiswe kapena lofuna kudzipha. Makhalidwe oika moyo pachiswe angasonyeze kuti wachinyamatayo watopa nawo moyo. Chizindikiro china chingakhalenso kudzivulaza dala (monga kudzicheka thupi).

Kumangoona ngati ndi munthu wopanda pake kapena kudziimba mlandu kosayenera. Wachinyamatayo amayamba kudzida kwambiri, n’kumaona ngati palibe chilichonse chimene angathe kuchita ngakhale zimenezi zitakhala kuti si zoona.

Matenda ena obwera chifukwa choganiza kwambiri. Ngati palibe chizindikiro chooneka, kuwawa kwa mutu, msana, m’mimba ndiponso matenda ena otero kungasonyeze kuti vuto lenileni ndi maganizo.

Kumangoganiza za imfa kapena kudzipha. Kumangoganizira zinthu zoopsa kungakhale vuto la maganizo. N’chimodzimodzinso kutchulatchula zofuna kudzipha.—Onani bokosi lili pansipa.

Kuvutika Maganizo Modukizadukiza

Zina mwa zizindikiro zomwezi zitha kuonekanso munthu akakhala ndi vuto lina losautsa lotchedwa bipolar disorder. Malinga n’kunena kwa Dr. Barbara D. Ingersoll ndi Dr. Sam Goldstein, akuti vutoli (limenenso limatchedwa kuti manic-depressive disorder) ndi “matenda ovutitsa maganizo modukizadukiza. Nthaŵi zina zingaipiretu pena n’kusintha kukhala munthu wokondwa kwambiri ndiponso wamphamvu zake, inde kukondwa kochita kupitirira nako muyeso.”

Nthaŵi yokondwa mopitirira muyeso imeneyi imatchedwa mania. Zizindikiro zake zina n’kuganiza mothamanga kwambiri, kulankhulalankhula kwambiri ndiponso kusakonda kugona. Kwenikweni, munthu wodwala matendaŵa atha kukhala masiku angapo osagona koma n’kumaonekabe wamphamvu. Chizindikiro china cha matendaŵa ndi khalidwe losaopa kuchita chinthu china chilichonse. Bungwe la U.S. National Institute of Mental Health linalemba lipoti lakuti, “Nthaŵi zambiri mania imawononga kuganiza, nzeru ndiponso khalidwe labwino mwakuti imabweretsa mavuto aakulu ndiponso ochititsa manyazi.” Kodi kukondwa kopitirira muyeso kumeneku kumakhala nthaŵi yaitali bwanji? Nthaŵi zina kumakhala masiku ochepa chabe; nthaŵi zinanso vutoli limakanirira kwa miyezi yambiri lisanasanduke vuto lenileni la maganizo.

Anthu amene m’mabanja mwawo muli ena amene amavutika maganizo ndiwo makamaka angakhale ndi vutoli mosavuta. Nkhani yabwino n’njakuti pali chiyembekezo kwa odwala matendaŵa. Buku lakuti The Bipolar Child limati, “Atayezedwa msanga ndiponso atalandira mankhwala oyenerera, ana ameneŵa ndiponso am’banja mwawo akhoza kukhala bwino kwambiri osasinthasintha.”

Ndi bwino kudziŵa kuti chizindikiro chilichonse pachokha sichisonyeza kuti munthuyo ali ndi vuto la maganizo kapena kuti amavutika maganizo modukizadukiza. Nthaŵi zambiri, pamakhala zizindikiro zambiri zimene zimaoneka kwa nthaŵi yaitali zimene zingachititse kuti wachinyamatayo apezeke ndi vutoli. Komabe funso limene lilipobe n’lakuti, N’chifukwa chiyani vuto losoŵetsa mtendere limeneli limakhala ndi achinyamata?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Cholinga cha zizindikiro zimene tatchula pano n’kungopereka chithunzithunzi chabe osati kupereka njira yoyezera munthu ngati ali ndi vutoli.

[Bokosi patsamba 6]

MWANA AKAFUNA KUFA

Bungwe loyang’anira za matenda la U.S. Centers for Disease Control linati, chaka china posachedwapa achinyamata ambiri ku United States anamwalira podzipha kuposa amene anamwalira chifukwa cha matenda onse titchuleŵa: kansa, mtima, EDZI, matenda ena obadwa nawo, matenda ofa ziwalo, chibayo, chimfine ndiponso matenda okhalitsa a m’mapapo. Chodandaulitsanso kwambiri n’chakuti: Achinyamata a zaka zoyambira 10 mpaka 14 amene amadzipha akuti akuchuluka mochititsa nthumanzi.

Kodi kudzipha pakati pa achinyamata kungapeŵedwe? Inde, nthaŵi zina kungapeŵedwe. Dr. Kathleen McCoy analemba kuti, “Umboni ukusonyeza kuti kwenikweni ambiri amene amadzipha amayamba ayesa kaye kutero kapena amauza kaye ena ndiponso kuwachenjeza. Mwana wanu akangoyamba kutchula zodzipha, muyambe kumuonetsetsa ndiponso mwina kufunafuna anthu odziŵa zimenezi kuti akuthandizeni.”

Kuchuluka kwa vuto la maganizo pakati pa achinyamata kukusonyezanso kuti makolo ndi anthu ena akuluakulu akufunika kuti aziganizira mozama kanthu kena kalikonse kosonyeza kuti wachinyamata winawake akufuna kudzipha. Dr. Andrew Slaby analemba m’buku lake lakuti No One Saw My Pain kuti, “Pafupifupi nkhani ina iliyonse yokhudza kudzipha imene ndinaifufuza, ikusonyeza kuti zonena za wachinyamata amene anadziphayo zakuti adzadzipha anali kuzinyalanyaza kapena sanali kuzitenga moyenerera. Am’banja la wachinyamatayo ndi anzake sanazindikire kuti munthuyo wasintha kwambiri. Ankangoona pamwamba chabe pa vutolo osati vuto lenilenilo, choncho ankangoti wachinyamatayu ali ndi ‘mavuto am’banja’ kapena ‘amamwa mankhwala osokoneza bongo’ kapenanso ‘amangosala kudya.’ Nthaŵi zina ankalimbana ndi kuthetsa ukali, kusokonezeka ndiponso kunyanyuka maganizo koma osati ndi vutolo. Vuto lenileni silinasinthe, linangopitiriza kum’pweteka kwambiri.”

Apatu ndiye nkhaniyi yamveka bwino ndithu: Chilichonse chosonyeza kuti munthu akufuna kudzipha muchiganizire mozama!

[Chithunzi patsamba 7]

Nthaŵi zina, khalidwe loukira limakhala chizindikiro cha vuto la maganizo

[Chithunzi patsamba 7]

Nthaŵi zambiri achinyamata ovutika maganizo sakondanso kuchita zinthu zimene poyamba zinkawasangalatsa