Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziŵa Zoyambitsa Zake

Kudziŵa Zoyambitsa Zake

Kudziŵa Zoyambitsa Zake

“Kaŵirikaŵiri sichikhala chinthu chimodzi chokha chimene chimachititsa achinyamata kuvutika maganizo, koma pamakhala zoyambitsa zingapo,” anatero Dr. Kathleen McCoy.

KODI n’chiyani chimene chimavutitsa maganizo a achinyamata? Pali zinthu zingapo. Chinthu china n’chakuti kusintha kwa thupi ndi maganizo kumene kumachitika munthu akakula msinkhu kumavutitsa achinyamata posadziŵa zomwe ziwachitikire ndiponso pochita mantha, motero iwo amakonda kudandauladandaula. Chinanso n’chakuti, nthaŵi zambiri achinyamata amalephera kuugwira mtima wawo akaona kuti anzawo akukana kugwirizana nawo kapena akaona kuti akukanidwa ndi wina yemwe akanakonda kukhala naye pachibwenzi. Komanso chinthu china n’chimene nkhani yathu yoyamba yatchula kuti achinyamata amasiku ano akukulira m’dziko limene palokha lili ndi zochita zovutitsa maganizo. Ndithudi, tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa.’—2 Timoteo 3:1.

Chimaipitsanso zinthu n’chakuti achinyamata akukumana ndi zovuta za m’moyo kwa nthaŵi yoyamba, ndipo sadziŵa zinthu komanso alibe nzeru ngati za akulu. Motero, nthaŵi zambiri achinyamata amakhala ngati anthu okaona malo amene akufufuza njira yodutsa m’dera lachilendo, amenenso asokonezeka mutu chifukwa cha malo amene aliwo ndipo nthaŵi zambiri, osafuna n’komwe kufunsa kuti athandizidwe. Zinthu zimenezi zingayambitse vuto la maganizo.

Koma pali zinthu zina zambiri zimene zingachititsenso kuti achinyamata avutike maganizo. Tatiyeni tionepo zochepa chabe.

Kusoŵa Chinthu Chinachake Kumavutitsa Maganizo

Nthaŵi zina vuto la maganizo limabwera chifukwa cha kusoŵa kwambiri chinthu chinachake, mwina imfa ya wina wokondedwa kapena kusoŵa amayi kapena abambo amene anachoka ukwati wawo utatha. Ngakhalenso kufa kwa nyama ya pakhomo kungapangitse achinyamata ena kuvutika maganizo.

Palinso mitundu ina yakusoŵa zinthu imene sidziŵika kwenikweni. Mwachitsanzo, mukasamukira kumalo ena atsopano ndiye kuti mumasiya malo amene munazoloŵera ndiponso anzanu apamtima. Ngakhale kukwaniritsa cholinga chimene mumalakalaka kwambiri, monga kumaliza sukulu, kungapangitse wina kukhala ndi maganizo oti akusoŵa chinachake. Muyenera kudziŵa kuti mukayamba moyo wina ndiye kutinso muyenera kusiyana ndi zosangalatsa ndiponso zabwino zina zomwe munali nazo kale. Ndiye pali achinyamata amene akulimbana ndi matenda ena ake okhalitsa. Zikakhala choncho, zimawawa mukamaganiza kuti ndinu wosiyana ndi anzanu, kapenanso kuti anzanu akukuthaŵani motero zingapangitse wachinyamata kuona ngati si munthunso wabwinobwino.

N’zoona kuti achinyamata ambiri amakumana ndi mavuto otere koma sasoŵeratu chochita. Amamva chisoni, amalira, amadandaula, amavutika mumtima, koma panthaŵi yoyenera amasintha. Nanga n’chifukwa chiyani zimatheka kuti achinyamata ambiri amapirira nawo bwinobwino mavuto awo, koma ena amawapatsa maganizo? Mayankho ake ndi ovuta kutchula, chifukwa chakuti vuto la maganizo ndi lovuta kwambiri kulilongosola. Koma achinyamata ena amaoneka kuti angavutike maganizo mosavuta.

Zokhudzana ndi Madzi a M’Thupi

Madokotala ambiri a anthu amisala amakhulupirira kuti madzi a m’bongo akachuluka kapena kuchepa ndiwo makamaka amayambitsa vuto la maganizo. * Vutoli lingathenso kukhala la kumtundu, chifukwa chakuti ofufuza apeza kuti achinyamata amene ali ndi kholo limene limavutika maganizo angathe kukhalanso ndi vutoli mosavuta. Buku lakuti Lonely, Sad and Angry limati, “Nthaŵi zambiri pamapezeka kuti ana ovutika maganizo amakhala ndi kholo limodzi limene likuvutikanso maganizo.”

Zimenezi zikubutsa funso lakuti, Kodi ana amachitadi kuyamwira matenda amaganizo, kapena amangochita kuphunzira kukhala ndi maganizo kuchokera kwa kholo limene lili nawo matendaŵa? Funso limeneli ndi lovuta kuliyankha, chifukwa ubongo ndi wovuta kwambiri kuumvetsetsa monganso zinthu zina zambiri zimene zimachititsa wachinyamata kuvutika maganizo.

Zochitika za M’banja Zimavutitsa Maganizo

Anthu ena akuti vuto la maganizo ndi nkhani ya m’banja, ndipo n’zomveka ndithu. Monga taona kale, n’kutheka kuti pangakhale kachibadwa kena kochokera kumtundu kamene kamatenga chizoloŵezi chinachake kumbadwo wina kumka nacho ku mbadwo wotsatira. Koma zochitika za m’banja zingathenso kuvutitsa maganizo. Dr. Mark S. Gold analemba kuti, “Ana amene makolo awo amawazunza angathe kuvutika maganizo mosavuta. N’chimodzimodzinso ana amene makolo awo amangowakalipira zilizonse ndiponso amene amangoyang’ana zolakwa za mwana wawo.” Munthu angavutikenso maganizo chifukwa chom’sasatitsa ndiponso chifukwa chom’tchinjiriza monyanyira. Komabe chochititsa chidwi n’chakuti wofufuza wina anapeza kuti ana amavutikanso maganizo mosavuta kwambiri ngati makolo sakuchita nawo chidwi kwenikweni.

Komabe, apa sizikutanthauza kuti achinyamata onse amene amavutika maganizo amatero chifukwa chosaleredwa bwino ayi. Kuganiza mothamanga choncho kungaphimbe zinthu zina zambiri zimene zimachititsanso kuti wina avutike maganizo. Komabe, nthaŵi zina zochitika za m’banja ndizo zimabweretsa kwambiri vutoli. Dr. David G. Fassler analemba kuti, “Ana amene akukhala m’nyumba zimene makolo awo amangokhalira kuvutana angavutike maganizo mosavuta kuposa ana amene ali m’mabanja osavutana kaŵirikaŵiri. Chifukwa china n’chakuti makolo amene amakhalira kukangana amangoganizira milandu yawoyo motero amanyalanyaza zofuna za ana awo. Chinanso n’chakuti nthaŵi zambiri makolo amakangana chifukwa cha anawo, zimene zingachititse anawo kudziimba mlandu, kukwiya, ndiponso kuipidwa kwambiri.”

Izi ndi zinthu zina chabe zimene zingavutitse achinyamata maganizo. Palinso zina. Mwachitsanzo, akatswiri ena amati zinthu zina (monga kusoŵa zakudya zina m’thupi, poizoni ndiponso kuledzera kapena kusuta) zingayambitse kuvutika maganizo. Anthu ena amati mankhwala ena akuchipatala (monga amtundu wa antihistamine ndiponso tranquilizer) amene amakhudza maganizo angathenso kuvutitsa munthu maganizo. Komanso zikuoneka kuti ana amene sakhoza kusukulu amavutikanso maganizo mosavuta, mwina chifukwa chakuti amayamba kudzidelera akazindikira kuti sangafananenso ndi anzawo a m’kalasi.

Komabe, ngakhale kuti pali zambiri zimene zimayambitsa vutoli, ndi bwino kuganizira za funso lakuti, Kodi achinyamata amene akuvutika maganizo angathandizidwe motani?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Anthu ena amaganiza kuti ngakhale kuti ambiri amabadwa nalo vutoli, palinso ena amene amabadwa ali abwinobwino ndipo kenaka akakumana ndi zoopsa zina ubongo wawo umasokonezeka motero angathe kuvutika maganizo mosavuta.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kaŵirikaŵiri mavuto a m’banja ndiwo amayambitsa wina kuvutika maganizo