Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pamene Mwakumana ndi Zoopsa

Pamene Mwakumana ndi Zoopsa

Pamene Mwakumana ndi Zoopsa

“Ndilitu ndi mpeni! Ukhale chete, apo ayi ndikupha!”

KUNJA kunacha bwino ndipo anali masana m’nyengo yachilimwe pamene mtsikana wina wa zaka 17 dzina lake Jane, * amene ali m’gulu la Mboni za Yehova, anali kuyenda atavala nsapato zamatayala mu paki ina ya ku Virginia, m’dziko la United States. Kenaka anangozindikira kuti kupakiko kwati zii, ndipo naye anaganiza zomapita kwawo. Ndiye atakhala pansi pafupi ndi galimoto yakwawo akuvula nsapatozo, panafika munthu wosam’dziŵa. Munthuyu anam’chititsa nthumanzi Jane pomuuza mawu ali pamwambaŵa n’kumatinso akufuna kumugona ndipo anam’mbwandira n’kumam’kankhira m’kati mwa galimotoyo. Jane anakuwa kwambiri ndi mawu ake onse, koma munthuyo sanam’lekebe.

Pambuyo pake Jane anati, “Panthaŵiyo ndinasoŵeratu chochita, ndinkangodziona ngati kanyerere kamene kakulimbana ndi chilombo chachikulu. Koma sindinasiye kukuwa ndiponso kulimbana naye munthuyo. Kenaka ndinapemphera kwa Mulungu mokuwa kuti, ‘Yehova, chonde musalole kuti zimenezi zindichitikire!’” Zikuoneka kuti mawu ameneŵa anachidzidzimutsa chigaŵengacho, ndipo chinam’siya mwamsanga n’kuthaŵa.

Chigaŵenga chimene chimafuna kum’gwirirachi chitaloŵa m’galimoto yake, Jane anadzitsekera m’galimoto yawo ija akunjenjemera kwambiri. Ndiye podzilimbitsa anatenga telefoni yam’manja n’kuimbira apolisi n’kuwalongosolera molondola maonekedwe onse a galimoto yachigaŵengacho kuphatikizaponso nambala yake. Zimenezi zinapangitsa kuti achigwire chigaŵengacho pasanapite nthaŵi n’komwe.

Kodi Tingati Nkhaniyi Inatha Bwino?

Inde, koma osati nthaŵi yomweyo. Uku kunali kuyamba chabe kwa mavuto a Jane. Ngakhale kuti apolisi ndiponso nyuzipepala zinam’yamikira kwambiri chifukwa choganiza msanga ndiponso kuchita zinthu mokhazikika maganizo, Jane sanali wokhazikikanso maganizo pambuyo pa zoopsa zimenezi. Iye akukumbukira kuti: “Patatha milungu ingapo maganizo anayamba kundivutitsa kwambiri. Ndinkangodzidzimuka nthaŵi iliyonse, mwakuti sindinkapeza tulo. Zimenezi zitandichitikira kwa milungu ingapo, sindinkathanso kuŵerenga kapena kuganiza bwinobwino. Mtima wanga unkangokhala m’mwamba. Ndili kusukulu mnyamata wina wa m’kalasi lathu wofanana ndi munthu amene ankafuna kundigwirira uja anandikodola pamsana kuti andifunse nthaŵi ndipo pang’onong’ono n’kanaoneka ngati wopenga.”

Jane akutinso: “Ndinkangoti ndwii. Sindinalinso kugwirizana ndi anzanga, ndipo kusukidwaku kunangondiwonjezera maganizo. Ndinkadziimba mlandu chifukwa chodziika dala m’mavuto, ndipo ndinkamva chisoni poganizira kuti kale ndinali munthu wosangalala, komanso munthu woti ena n’kumadalirapo. Ndinkangoona ngati kuti ndine munthu wina.”

Apatu Jane anali kuvutika ndi mantha amene amayamba chifukwa chokumbukira zoopsa. Vutoli ndi post-traumatic stress disorder (PTSD). Kodi vuto la PTSD n’nlotani kwenikweni, ndipo kodi amene ali ndi vutoli angathandizidwe bwanji? Nkhani yotsatira iyankha mafunsoŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dzinali talisintha.