Vuto Losamalira Ana
Vuto Losamalira Ana
Britain ndi dziko lotukuka la azungu. Koma akuti ana oposa 100,000 a m’dzikoli, omwe n’ngochuluka moŵirikiza kuposa mmene anthu ankaganizira kale, amathaŵa panyumba pawo. Motero, mwana m’modzi mwa ana 7 ameneŵa amachitidwa chiwawa kapena kugwiriridwa.
“Ana akamaona kuti akupatulidwa ndiponso kukanidwa, amaona kuti ndibwino kungothaŵa,” anatero Ian Sparks, amene ndi mkulu wa bungwe loona za ana la Children’s Society. Iyeyu ananenanso kuti: “Nkhani imeneyi ikukhudza mabanja olemera ndi osauka omwe. Ana angathe kuthaŵa m’madera olemera kapenanso m’madera osauka a m’mizinda.”
Kusamalira ndiponso kuphunzitsa ana ndi udindo waukulu kwambiri. Kodi thandizo likupezeka kuti? Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja linalembedwa kuti lithandize pankhaniyi. Ina mwa mitu yake 16 n’njakuti: “Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake,” “Thandizani Wachinyamata Wanu Kukula Bwino,” ndiponso “Tetezani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga.” Mitu yonse 16 m’bukuli ili ndi malangizo othandiza ndiponso makamaka imagwiritsa ntchito Baibulo monga gwero la nzeru zoposa zathu.
Mungathe kuitanitsa buku lanu la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja polemba zofunikira m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi yosonyezedwapoyo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ino.
□ Munditumizire buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.