Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vuto la Mantha Lidzatha!

Vuto la Mantha Lidzatha!

Vuto la Mantha Lidzatha!

MWINA munapitapo kunkhondo ndiye mumalota kapena mumakumbukira zoopsa zimene zimakuchititsani kumva ngati kuti nkhondoyo siinathe kwa inuyo. Mwinanso munakumanapo ndi khalidwe lauchinyama monga kugwiriridwa ndipo mumamva ngati kuti kungoyambira nthaŵi imeneyo munasinthiratu. Mwinanso n’kutheka kuti munthu wina amene munkamukonda anafa kutagwa tsoka kapena pangozi ndiye kukhala popanda iyeyo kukupwetekani mtima kwambiri.

Kodi mumadzifunsa ngati kuli kotheka kuiwalako zimenezi? Tingathe kuyankha mosakayika kuti, inde n’kotheka! Pakali pano, anthu onse amene amavutika maganizo chifukwa cha zoopsa angathe kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu, Baibulo.

Tingathandizidwe Kupirira Vutoli

Zaka pafupifupi zikwi ziŵiri zapitazo, mtumwi Paulo anakumana ndi zinthu zoopsa kwambiri zimene zikanatha kumupha. Zina mwa izo anazilongosola m’Baibulo. Paulo analemba kuti, “Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziŵa za chisautso chathu tinakomana nacho m’Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhaŵa ngakhale za moyo wathu; koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha.”—2 Akorinto 1:8, 9.

Ngakhale kuti zimene zinachitika panthaŵiyo sizidziŵika, mosakayika zinali zoopsadi. (2 Akorinto 11:23-27) Kodi Paulo anathana nazo bwanji?

Poganizira mavuto amene anakumana nawo ku Asiya, iye analemba kuti: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Inde, anthu onse amene anakumana ndi zoopsa angathandizidwe ndi “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” Kodi mungapeze bwanji chitonthozo choterocho?

Mmene Mungathandizidwire

Choyamba, pemphani kuti muthandizidwe. Ngati mwathedwa nzeru, kumbukirani kuti aliponso ena amene anamvapo chimodzimodzi. Nthaŵi zambiri amene anagonjetsapo maganizo otere amafunitsitsa kuthandiza ena. Monga mtumwi Paulo, nthaŵi zambiri iwo amaona kuti chitonthozo chimene analandira kwa Mulungu pamene anali m’mavuto ayenera kugaŵirako ‘iwo okhala m’nsautso iliyonse.’ Musazengereze kukumana ndi aliyense wa Mboni za Yehova amene mungamasuke naye ndi kum’pempha kuti akuthandizeni kupeza thandizo kwa Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse.”

Limbikirani kupemphera. Ngati mukulephera kupemphera chifukwa chaukali, funsani munthu wina amene ali woyenerera m’zinthu zauzimu kuti apemphere nanu. (Yakobo 5:14-16) Mukamalankhulana ndi Yehova Mulungu, kumbukirani ‘kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse pakuti iye asamalira inu.’ (1 Petro 5:7) Nthaŵi ndi nthaŵi Malemba amagogomezera kuti Mulungu payekha amawaganizira kwambiri atumiki ake.

N’kutheka kuti wolemba Salmo 94 anakumanapo ndi zoopsa kwambiri chifukwa analemba kuti: “Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova, moyo wanga ukadakhala kuli chete. Pamene ndinati, litereka phazi langa, chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”—Salmo 94:17-19.

Anthu ena okhala ndi vutoli amavutika kwambiri ndi “zolingalira” zimene nthaŵi zina zimatha kusanduka maganizo osachedwa kuphulitsa ngozi. Komabe, pemphero lochokera pansi pamtima lingathe ‘kukuchirikizani’ mpaka malingaliro amenewo atatha. Yehova muzimuona ngati kholo lokukondani ndipo inuyo muzidziona ngati mwana wamng’ono amene khololi limam’teteza mwachikondi. Kumbukirani lonjezo la m’Baibulo lakuti “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:7.

Kuchiza matenda, kaya akhale okhudza thupi kaya maganizo kapena auzimu sikuchitika kamodzin’kamodzi. Choncho sikwanzeru kuganiza kuti pemphero lingapereke mtendere nthaŵi yomweyo kwa anthu amene anasokonezekeratu chifukwa chokumana ndi zoopsa. Komabe m’pofunika kupemphera mosaleka. Kutero kungam’thandize wodwalayo kuti asatayiretu mtima chifukwa cha kuganizira zoopsa zimene zinam’chitikira.

Ŵerengani ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu. Ngati mukukanika kuganiza bwino, funsani munthu wina kuti aŵerenge nanu pamodzi nkhani zolimbikitsa za m’Baibulo. Mungasankhe malemba amene amasonyeza kuti Yehova amadera nkhaŵa kwambiri anthu ake okhulupirika, ngakhale atavutika kwambiri maganizo kapena atatayiratu mtima.

Jane, amene tam’tchula m’nkhani zam’mbuyo uja, analimbikitsidwa ndi malemba ambiri a m’Baibulo ochokera m’Masalmo. Ena mwa malembaŵa ndi Salmo 3:1-8; 6:6-8; 9:9, 10; 11:1-7; 18:5, 6; 23:1-6; 27:7-9; 30:11, 12; 31:12, 19-22; 32:7, 8; 34:18, 19; 36:7-10; 55:5-9, 22; 56:8-11; 63:6-8; 84:8-10; 130:1-6. Osalimbana n’kuŵerenga malemba ambirimbiri a m’Baibulo panthaŵi imodzi. Koma aganizireni kaye mofatsa ndiponso pempherani.

Kuvutika Maganizo Kosaneneka Tsopano

N’zomvetsa chisoni kuti, sitiyenera kudabwa kuti kugwiririra chigololo, kupha anthu, nkhondo, ndiponso chiwawa choyamba pazifukwa zazing’ono zafala masiku ano. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yesu Kristu ananena kuti nthaŵi yathu idzadziŵika chifukwa cha “kuchuluka kwa kusayeruzika.” Iye anawonjeza kunena kuti: “Chikondano cha aunyinji chidzazirala.”Mateyu 24:7, 12.

M’zaka zaposachedwapa kusokonezeka maganizo chifukwa cha zoopsa kwafala kwambiri makamaka chifukwa cha zinthu zomwezi zimene Yesu analosera kuti zidzachitika. Monga mmene Baibulo linanenera pa Mateyu chaputala 24, Marko chaputala 13, ndiponso Luka chaputala 21, Yesu ananena kuti panthaŵi yamapeto adziko lino, kudzakhala nkhondo padziko lonse, masoka achilengedwe, kuswa malamulo kochuluka, ndiponso kusoŵa chikondi. Komabe, monga mmene Yesu anasonyezera, chithandizo chatsala pang’ono kubwera.

Atalongosola zoopsa zimene zidzakhalepo padziko lonse ndiponso atalongosola kuyamba kwa “chisautso chachikulu” pambuyo pa zoopsazi, taonani zimene Yesu ananena kuti anthu ayenera kuchita: “Weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.” (Mateyu 24:21-31; Luka 21:28) Inde, pamene dziko lino likumka liipiraipira, tingakhale otsimikiza kuti chisautso chachikulu chimene dziko lamavutoli lidzakumane nacho chidzafika pachimake pamene kuipa konse kudzathetsedwe ndipo dziko latsopano lolungama lidzakhalapo.—1 Yohane 2:17; Chivumbulutso 21:3, 4.

Tisadabwe ayi kuti tidzaomboledwa pokhapokha kuipa ndiponso chiwawa zitafika pachimake. Kale Mulungu analanga anthu a m’nthaŵi ya Nowa ndiponso anthu akhalidwe loipa a m’Sodomu ndi Gomora m’njira yofananayi. Zilango za Mulungu zakalezi zikusonyeza zimene zidzachitike m’tsogolo.—2 Petro 2:5, 6.

Mapeto a Vuto la Mantha

Ngati mumavutika ndi PTSD mwina mungamakayike zoti maganizo anu adzasiya kukuvutitsani. Koma mfundo yosakayikitsa n’njakuti: Inde, adzasiyadi! Pa Yesaya 65:17, Yehova Mulungu analengeza kuti: ‘Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.’ Ngakhale kuti mabala a mumtima a zoopsa zimene zinachitika m’mbuyo angaoneke ngati kuti sadzatha, lembali likutitsimikizira kuti nthaŵi ikudza pamene sadzativutitsanso n’komwe.

Pakali pano patha masiku oposa chaka chimodzi Jane atakanika kum’gwirira ndipo iye akutumikira monga mpainiya (mlaliki wanthaŵi zonse) wa Mboni za Yehova. Posachedwapa ananena kuti: “Sindinali wokhazikika mtima mpaka pamene mlanduwo unatha n’kuchitsekera chigaŵengacho, ndipo panatenga miyezi isanu ndi itatu kuti mtima wanga ubwerere m’malo mwake. Chaka chatha nthaŵi ngati inoyo sindinkaganizako zakuti ndingadzakhale ndi mtendere ndiponso chimwemwe chimene ndili nacho panopo. Ndimathokoza Yehova chifukwa cha chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha ndiponso chifukwa chamwayi wouza ena chiyembekezochi.”—Salmo 27:14.

Ngati mwataya mtima ndiponso kuthedwa nzeru chifukwa chovutika ndi PTSD, chiyembekezo chimenechi chingathe kukuthandizani inunso.

[Chithunzi patsamba 24]

Kupita kumisonkhano yachikristu kungakuthandizeni kupirira

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kuŵerenga Mawu a Mulungu ndiponso kupemphera kungakulimbikitseni

[Chithunzi patsamba 26]

Posachedwapa zoopsa zonse zidzasanduka mbiri chabe