Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kente—Nsalu ya Mafumu

Kente—Nsalu ya Mafumu

Kente—Nsalu ya Mafumu

Yolembedwa ndi Wolemba GALAMUKANI! ku Ghana

WOOMBA nsaluyo akungoyendetsa manja ake mofulumira pamwamba pa nsaluyo. Manjawo akuyenda mogwirizana ndi kaphokoso kamene kakumveka kuchokera ku mawilo ndiponso zokokera ulusi zikamakhulana, koma wolukayo akungolimbana ndi nsalu yokongola imene akuwombayo. Wapana zingwe ndi zala zakumiyendo ndipo zingwezi zikukoka mawaya amene amagaŵa ndi kuyendetsa ulusi wautali mamita asanu ndi imodzi umene umakhala kutsogolo kwa makina owombera nsalu. * Ndi zala zake zakumanja, akutenga mofulumira zingwe zamitundu yosiyanasiyana chimodzi n’chimodzi ndi kuziloŵetsa m’zingwe zinzakezo n’kuwomba nsalu ya maonekedwe ena ake imene amailimbitsa poikankhira ku mbali imene watha kaleyo.

Nsalu imene imatuluka akatere imangokhala masentimita khumi okha mlifupi. Koma imakhala yokongola ndiponso yochititsa kaso. Mmisiriyo akamayang’ana luso lake, amasangalala ndi luso limene waonetsa powomba nsalu yeniyeni ya kente.

Umisiri Wakalekale

Kwa zaka zambiri zedi, amisiri aluso akhala akuchita luso lakale limeneli lowomba nsalu. Ulusi wochokera ku mtengo wa bwazi, thonje, ndiponso silika ndiwo wakhala ukugwiritsidwa ntchito mosavuta powomba nsalu. Utoto anali kuutenga m’mitsitsi ndiponso masamba a zomera zinazake, ndipo owomba nsaluŵa ankapanga maluŵa ndiponso zokongoletsa zina pansalu zimene ankawombazo.

Anthu a ku Africa osakhazikika malo amodzi anakonza zida zowombera nsalu zazing’ono zimene anali kuyenda nazo mosavuta. Zida zimenezi anali kuwombera nsalu imene mlifupi inali masentimita pafupifupi asanu ndi atatu kapena khumi ndi limodzi basi. Tinsalu tatitali timeneti anali kutilumikiza potisokerera pamodzi m’mbali mwake, n’kupanga nsalu yaikulu imene ankaivala. Zida zotha kunyamulika zowombera nsalu zotere anali kuzinyamula pa nyama zonyamula katundu n’kudutsa nazo m’zipululu, mitsinje, ndiponso mapiri aataliatali. Zidazi zinali kuthandiza kwambiri anthu amene anali kuzigwiritsa ntchito ndipo anali kudutsa nazo m’njira zakale za amalonda.

Kulakalaka Nsalu

Kwa zaka zambiri mafumu a kumadzulo kwa Africa ndiwo anali kuyendetsa dziko lodzala ndi miyala yamtengo wapatali limene ofufuza a ku Ulaya analitcha kuti Gold Coast [Gombe la Golide]. * M’dzikoli munali kukumbidwa golide wambiri, motero mfumu zake za fuko la Ashanti pamodzi ndi mabanja awo zinalemera kwambiri. Mfumuzi zinali kudzikongoletsa povala zibangiri zagolide zolemera ndiponso malaya owombedwa mwapadera, motero izo pamodzi ndi mafumu awo ang’onoang’ono anali kuonetsera chuma, mphamvu ndiponso ulemerero wawo kwa anthu omwe ankawalamulira. Nsalu zapadera zimene olamuliraŵa anali kuvala zinayamba kutchedwa kuti kente, dzina limene mwina linkatanthauza kuti kawombedwe ka nsaluyi n’kofanana ndi malukidwe a dengu. Mafuko enanso a ku Gold Coast anali kuwomba nawo nsalu, koma mafumu a chishanti anayamba kuona nsalu ya kente monga nsalu yoimira ulemerero ndiponso ufumu.

Owomba nsalu a ku Gold Coast anali kugwiritsa ntchito thonje lokonzedwa komweko. Kunkapezeka utoto wosinthitsa ulusi kukhala wa mtundu wa buluu basi. Ulusi wa buluu umenewu unkalukidwa pamodzi ndi ulusi wathonje woyera mongoti mbuu n’kupanga nsalu yovala anthu akumeneko ya mizeremizere ndi mandalasi.

Nsalu ya kente yovala mfumu anali kuiluka mwapamwamba ndipo sankalola kuti anthu ena alionse aluke nsalu yotere. Anaika magulu a anthu aluso owomba nsalu za mfumu kuti ndiwo aziwomba nsaluzi mwapamwamba zedi. Sankalolanso kuti anthu adziŵe kawombedwe kansaluzi ndipo chinali chinsinsi chachikulu. Anthu ena onse owomba nsalu anali kuletsedwa kuwomba nsalu zokometsedwa monga nsalu za mfumu ndiponso anthu okhala kubanja lachifumu. Mfumu inkakhala ndi nsalu zambiri, ndipo nsalu iliyonse inkakhala ndi mapangidwe ndiponso kaonekedwe kosiyana. Mwachikhalidwe chawo, mafumu sanali kuvala nsalu imodzimodzi mobwereza akamaonekera kwa anthu.

Kusankha Mtundu Woyenera

M’zaka za m’ma 1500, ku Ghana kunabwera mtundu wina wansalu. Nsalu yatsopanoyi siinali kuwombedwa ndi zida za ku Africa zoombera nsalu koma inali kupangidwa kutali ndipo amalinyero oyamba ochokera ku Ulaya ndiwo ankaifikitsa kumeneko podzafunako minyanga ya njovu, golide, ndiponso akapolo. Nsalu zochokera kunjazi zinali ndi ulusi wowala ndiponso wochititsa kaso zedi. Posakhalitsa, ulusi wochokera kunja umenewu, umene unali wokometsedwa ndi utoto wofiira, wachikasu, ndiponso wobiriŵira, unasanduka malonda ofunika zedi. Anthu ochepa ndiwo anali ndi ndalama zogulira nsalu zokwera mtengo zimenezi kuchokera kwa anthu amalonda a ku Ulaya ameneŵa. Amene ankakwanitsa kugula nsaluzi anali Ashanti olemera okha amene anali kuyang’anira golide, minyanga ya njovu, ndi akapolo akamapita nazo ku sitima zapamadzi zimene zinali kudikirira padoko. Koma mfumu yaikulu ya Ashanti ndiponso mafumu ake aang’ono sanali kukonda nsalu zimenezi.

Ankati akapeza nsalu, owomba nsaluwo anali kuchita ntchito yovuta yosolola ulusi wonse wokongolawo wokhala ndi utoto, n’kutaya nsalu yotsalayo. Kenaka ulusi wamtengo wapataliwu anali kuuwombanso pa zida zowombera nsalu za amisiri amfumuwo. Chifukwa cha kuchuluka kwa mitundu yokongola ya ulusiwo, kunabuka maluso ena ndiponso njira zina zatsopano ndipo izi zinachititsa kuti amisiriŵa agwiritse ntchito nzeru ndi maluso awo powomba nsalu zochititsa kaso kuposa kale lonse. Owomba nsalu aluso ochokera m’mafuko ena ankalembedwa ntchito ndi mafumu afuko la Ashanti, choncho ankapanga nsalu za kente zabwino koposa.

Maluŵa ooneka bwino okhala ngati nsomba, mbalame, zipatso, masamba, kuloŵa kwa dzuŵa, utawaleza, ndiponso zinthu zina zachilengedwe, ankakongoletsa kwambiri nsaluzo ndipo anali ndi matanthauzo ophiphiritsira. Nsalu zowombedwa pamodzi ndi ulusi wamtundu wagolide zinali kuimira chuma, mtundu wobiriŵira unali kusonyeza kuti chinthucho n’chatsopano, wakuda unkaimira kukhumudwa, wofiira unkasonyeza kukwiya, ndipo wonyezimira unkaimira zinthu zabwino kwambiri ndiponso chimwemwe.

Owomba nsalu anali kugwira ntchito yawo mwa phee komanso mosapupuluma, ndipo nsalu imodzi inkawatengera miyezi yambiri podziŵa kuti nsaluyo ikatha anthu adzazindikira kuti ndi akatswiri pantchito yawoyo. Ndi anthu ochepa chabe amene anali kufuna kugula nsalu zaluso lapamwamba zedi zimenezi chifukwa chakuti ambiri sankakwanitsa kugula nsalu ya kente yovuta kupezayo komanso yokwera mtengo.

Nsalu ya Kente ya Makono

Kenaka patapita nthaŵi ndithu, mafumu aakulu ndi aang’ono otchuka anayamba kuchepa mphamvu. Panalibenso chifukwa choti nsalu ndiyo izisiyanitsa anthu a m’banja la mfumu ndi anthu wamba. Anthu ambiri anayamba kugula nsaluyi, pakuti anthu ena onse anayamba kuigwiritsa ntchito. Nsaluyi anayamba kuiwomba mothamanga poti anthu ambiri ankaifuna, motero inafwifwa, ndiponso inatsika mtengo.

Masiku ano nsalu zambiri za kente zimawombedwa ndi ulusi wochita kupanga ndi zinthu zosiyanasiyana ndipo akaziwomba amapangira zikwama, matayi, malamba, zipewa, ndi zovala zambiri. Pali owomba nsalu ochepa chabe amene amapangabe nsalu ya kente pogwiritsa ntchito zida zakale zija zomwe n’zotopetsa ndiponso zimadya nthaŵi yambiri. Nsalu zakale za kente zimakondedwa kwambiri masiku ano ndipo n’zosiyirana kuchokera kwa makolo mpaka kwa zidzukulu zawo. Indedi, nthaŵi inapita imene anthu ankaomba nsalu za kente zimene zinali zapamwamba zedi pogwiritsa ntchito zida zosalira zambiri zamitengo, n’kumati ndi nsalu za mafumu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ulusi umenewu umakhalapo mitundu iŵiri. Wina umakhala moimika, winawo mopingasa.

^ ndime 9 Kumene masiku ano amati ku Ghana

[Zithunzi patsamba 16]

Zida zowombera nsaluzi n’zopepuka ndipo n’zosavuta kunyamula

[Chithunzi patsamba 17]

Wolukayo amagwiritsa ntchito miyendo yake poyendetsa mawaya amene amakoka ulusi