Kodi Adzadyetse Dziko Ndani?
Kodi Adzadyetse Dziko Ndani?
KODI anthu m’tsogolo muno adzayamba kutetezako mitundu yosiyanasiyana ya zachilengedwe m’malo moiwononga? Malingana ndi mawu a wa sayansi wina John Tuxill, kuti anthu adzatero m’pofunika “kusintha kwambiri mfundo zawo.” Komabe iye anawonjezera mawu akuti kusintha kumeneku “n’zokayikitsa kuti kungatheke ngati anthu atapanda kuzindikira ubwino wa mitundu yosiyanasiyana ya mbewu, ngati safuna kusintha zimene akuchita panopo, ndiponso ngati safuna kuchita zinthu m’njira zatsopano.”
Anthu ambiri sakhulupirira n’komwe kuti zinthu zingadzasinthedi kwambiri. Ndipo ambiri amatsutsa mfundo ya Tuxill imeneyi. Ndiye palinso akatswiri ena a sayansi ya zachilengedwe amene amaona kuti mpaka pano anthu sazindikira kwenikweni kufunika kwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe ndiponso amaona kuti akatswiri ena akhala akufotokoza nkhaniyi mowonjezera. Ngakhale kuti asayansi sakugwirizana pankhaniyi, ndi bwinobe kumvetsera zodetsa nkhaŵa zimene akatswiri ena ankhaniyi anenapo. Zikuoneka kuti chikuwavutitsa maganizo si kutha kwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe kokha ayi komanso umbombo ndiponso kusayang’ana zam’tsogolo kumene akuti n’komwe kukusoŵetsa zinthuzi. Taonani ndemanga izi zimene zinanenedwa ndi olemba nkhani osiyanasiyana.
Wolemba za sayansi wina Jeremy Rifkin anati: “Zaka 100 zokha zapitazi, alimi ochuluka zedi m’madera osiyanasiyana padziko lonse, ankakhala ndi mbewu zawozawo. . . . Masiku ano, makampani padziko lonse ndiwo anayambitsa mbewu zambiri mwa kuzisintha, ndipo ndi zawozawo. Choncho wina aliyense alibe ufulu wobzala mbewuzo popanda iwo kum’lola. . . . Chifukwa chomangoganizira mapindu a nthaŵi yomweyo, malonda a umisiri wa zamoyo akuoneka kuti angawonongeretu mbewu zimene m’tsogolo zingadzafunike kwambiri polimbana ndi matenda ena ake atsopano kapena tizilombo tina tosamva mankhwala.”
David Suzuki, katswiri wa sayansi ya chibadwa cha zinthu anati: “Mfundo imene yafalitsidwa mobwerezabwereza n’njakuti chofunika kwambiri
pankhaniyi ndi misika, kuchita malonda mwaufulu ndi mayiko ena ndiponso kuyendetsa chuma padziko lonse. Chifukwa cholamulidwa ndi chuma ndiponso mapindu amene mabungwe aakulu amapeza, ofalitsa nkhani amakhulupirira mfundo ya zachuma imeneyi ngati kuti n’chiphunzitso chachipembedzo ndipo nthaŵi zambiri saikayikira n’komwe.”M’buku lake lakuti Seeds of Change—The Living Treasure, wolemba wina wotchedwa Kenny Ausubel ananenapo za mayiko olemera amene amanamizira kuti “maboma awo ndiponso makampani awo akudandaula chifukwa cha kusoŵa kwa ‘choloŵa cha anthu onse’ chimene chili mbewu.” Iye anati ameneŵanso ndiwo mayiko amene akuchepetsa mitundu yosiyanasiyana ya zachilengedwe polimbikitsa njira zaulimi wamakono ndiponso ulimi wa mbewu zamtundu umodzi.
Kaya akatswiri a zachilengedwe akungoopa njokaluzi kaya akuopadi zenizeni, mwina zingakuvuteni
kudzilimbitsa mtima mukamaganizira tsogolo la dzikoli. Kodi dzikoli lingakhalepo mpaka liti pakuti anthu akuoneka kuti n’ngaumbombo zedi? Posoŵa yankho, anthu ambiri amangoti mwina sayansi ndiyo ingatipulumutse m’vutoli.Kodi Sayansi Ndiponso Umisiri Zingatipulumutse M’vutoli?
Bungwe la Royal Society of Edinburgh posachedwapa linanena kuti likuda nkhaŵa kuti asayansi akutulukira zinthu zambiri ndiponso zovuta kwambiri kuzimvetsa mwakuti n’kutheka kuti sangathe kudziŵa bwinobwino zotsatirapo zake. David Suzuki analemba kuti, “Sayansi imatithandiza kumvetsa zinthu zochepa kwambiri zokhudza chilengedwe. Tikudziŵa zinthu zochepa kwambiri zokhudza sayansi ya zinthu zachilengedwe za padziko, ndiponso mmene zinthuzo zimadalirana.”
Monga mmene magazini yotchedwa Science inalongosolera kuti, ‘kuopsa ndiponso ubwino wa zinthu zachilengedwe zosinthidwa sikukudziŵika bwinobwino ndiponso sizikhudza chinthu china chilichonse chosinthidwa chibadwa. . . . Sitingathe kudziŵiratu ndendende mmene zachilengedwe zochokera kudera lina, ngakhalenso zimene zasinthidwa zingakhudzire malo.’
Zinthu zambiri zimene amati n’chitukuko zangokhala ngati mpeni wakuthwa konsekonse. Zimathandiza m’njira zina koma zimasonyezanso kuti anthu alibe nzeru zokwanira ndiponso nthaŵi zambiri zasonyeza kuti n’ngadyera. (Yeremiya 10:23) Mwachitsanzo, ngakhale kuti ulimi wamakono unachititsa chakudya kuchuluka, unachepetsanso mitundu yosiyanasiyana ya mbewu. Dr. Mae-Wan Ho analemba kuti, polimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo ndiponso njira zina zokwera mtengo zaulimi, ulimi wamakonowu kwenikweni unali kupindulitsa “makampani opanga mbewu ndiponso mayiko amene sali osauka kwenikweni koma kwinaku anthu wamba n’kumavutika.” Zimenezi zikupitirirabe pakuti ulimi wa umisiri wa zachilengedwe watchuka ndipo akuudalira kwambiri komanso m’tsogolo muno ulimiwu uchititsa kuti sayansi ndiyo ikhale njira yodalirika kwambiri yopezera chakudya chokwanira.
Komabe zimenezi zisatidetse nkhaŵa. Ndithudi, zikungotiuza chinthu chimodzi chachikulu. Baibulo limatithandiza kuona kuti tisamadalire kwambiri anthu opanda ungwiro amene akuyendetsa dzikoli ndi zinthu zimene lili nazo. Pakali pano, anthu ayeneradi kulephera ndiponso kusayendetsa bwino zinthu. Motero, Salmo 146:3 amatilangiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Koma tikhulupirire Mulungu ndi mtima wathu wonse. (Miyambo 3:5, 6) Iye ali ndi mphamvu ndiponso amafunitsitsa kutithandiza.—Yesaya 40:25, 26.
Dziko Labwino, la Mwanaalirenji Layandikira
Musanayambe kukonzanso nyumba yowonongeka mumachotsa kaye zinyalala zonse. Chonchonso, Yehova Mulungu posachedwa adzachotsa padziko lapansi anthu onse oipa, kuphatikizaponso anthu amene amayesa dziko lathuli, zinthu zake zachilengedwe, ngakhalenso anthu anzawo, kuti ndi zinthu zomwe angachite nazo zimene akufuna kuti iwo ndi mabungwe awo apezerepo phindu. (Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 11:18) Koma Yehova adzasiya anthu okha amene amam’konda ndipo amayesetsadi kuchita zimene iye amafuna.—1 Yohane 2:15-17.
Kenaka, dziko lapansi ndiponso zamoyo zake zosaŵerengeka, kuphatikizapo anthu, lidzalamulidwa ndi boma loikidwa ndi Mulungu, Ufumu Waumesiya. (Danieli 7:13, 14; Mateyu 6:10) Kodi dzinthu zimene dzikoli lidzabale muulamuliro wanzeru umenewo n’zoti n’kuzisimba ngati? Masalmo 72:16 amati: “Mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.” Inde, chakudya sichidzakhalanso nkhani yokanganitsa kapena yodetsa nkhaŵa. Koma chidzakhala chakudya chabwino ndiponso chochuluka zedi.
Motero, ngakhale kuti dziko panthaŵi ino likudandaulitsa ndiponso kudetsa nkhaŵa kwambiri, amene amakhulupirira Yehova amayembekezera tsogolo losangalatsa kwambiri pompano padziko lapansi. Zimene amayembekezerazi ndizo zimasimbidwa mu ‘uthenga wabwino wa ufumu,” umene Mboni za Yehova zimauzako anthu onse amene amafuna dziko labwino ndiponso lolungama. (Mateyu 24:14) Chifukwa cha chiyembekezo chosakayikitsa chimenechi, ndiponso chifukwa chakuti Mulungu amasamalira bwino anthu ake, ngakhale tsopano tingathe, ‘kukhala osatekeseka, ndi kukhala phe osaopa zoipa.’—Miyambo 1:33.
[Chithunzi patsamba 10]
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, chakudya chidzakhala chabwino ndiponso chambiri zedi
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Chithunzi cha FAO /K. Dunn
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Tourism Authority of Thailand