Kodi Ndingatani Kuti Ndisamade Nkhaŵa Kwambiri?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani Kuti Ndisamade Nkhaŵa Kwambiri?
“Chinthu china chopatsa maganizo kwambiri kwa wachinyamata ndicho kuganizira zatsogolo lako. Umangoda nkhaŵa, n’kumadzifunsa kuti, Kodi ndichoke panyumba? Ndipite kusukulu? Ndiyambe utumiki wanthaŵi zonse? Kapena kodi ndiloŵe m’banja? Umakhala n’zambiri zimene umaganiza kuti ungachite mwakuti zimangokuopsa,” anatero Shane, mnyamata wa zaka 20.
KODI mumangokhala ndi nkhaŵa nthaŵi zonse? Achinyamata ambiri amakhala ndi nkhaŵa pazifukwa zosiyanasiyana. Nyuzipepala ina yolembedwa n’cholinga cholangiza makolo inati: “Posachedwapa atafufuza achinyamata a zaka 15 mpaka 18 a m’mayiko 41 anapeza kuti achinyamata ambiri masiku ano amada nkhaŵa akamaganiza za mmene angapezere ntchito yabwino.” Chachiŵiri chinali kudera nkhaŵa zathanzi la makolo awo. Chinanso chimene chinkawadetsa nkhaŵa kwambiri chinali nkhani yakulekana ndi munthu amene anam’konda.
Unduna wa zamaphunziro wa ku United States utafufuza unapeza kuti achinyamata ambiri ku United States ankada nkhaŵa kwambiri chifukwa cha “kufunitsitsa kukhoza bwino m’kalasi.” Pa kufufuza komweku anapezanso kuti achinyamata ambiri amamva mmene Shane (amene tam’tchula pamwambapo) ankamvera. Mtsikana wina wotchedwa Ashley, anati: “Ndimada nkhaŵa n’kamaganiza za tsogolo langa.”
Koma achinyamata ena amada nkhaŵa akamaganiza kuti ndi osatetezeka. Malingana ndi kufufuza kwa m’chaka cha 1996, pafupifupi theka la achinyamata onse a ku United States anali kuona kuti zachiwawa zinali kuchuluka kusukulu kwawo. Achinyamata oposa 18 miliyoni (amene ali 37 peresenti) anati akudziŵapo munthu winawake amene anawomberedwa!
Komatu si nkhaŵa zonse zimene zili zoopsa. Achinyamata ambiri chimene chimawadetsa nkhaŵa kwambiri ndi mmene amakhalira ndi ena. Magazini ina ya pa intaneti yolembera makolo inati: “Achinyamata amada nkhaŵa ngati alibe chibwenzi, koma nthaŵi zambiri amada nkhaŵa ngati alibe mnzawo aliyense.” Mtsikana wotchedwa Meagan anadandaula kuti: “Kodi ndingatani kuti ndizioneka motsogola ndiponso kuchita zinthu mochangamuka? Ndiyenera kukhala ndi anzanga.” Pa chifukwa chomwecho, mnyamata wina wachikristu wa zaka 15 dzina lake Natanael anati: “Anzanga a kusukulu amada nkhaŵa ndi masitayelo a zovala. Amada nkhaŵa ndi mmene amayendera, mmene amalankhulira, ndiponso mmene amaonekera kwa anthu ena. Amaopa kuoneka ngati opusa.”
Mavuto Ndiwo Moyowo
Zikanakhala bwino ngati tikanakhala opanda mavuto. Komabe Baibulo limati: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Motero, mavuto ndiponso nkhaŵa ndiwo moyowo. Koma mukalola kuti muzingokhala odandaula ndiponso ankhaŵa, mungodzipweteka nokha. Baibulo limachenjeza kuti: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu.”—Miyambo 12:25.
Njira ina yopeŵera kudandaula ndi zilizonse ndiyo kudziletsa pochita zinthu. Mtsikana wotchedwa Ana, yemwe ali ndi zaka 16 anati: “Atsikana ambiri a m’kalasi lathu amada nkhaŵa chifukwa choopa kutenga mimba kapena matenda ena opatsirana m’njira yachiwerewere.” Komatu mungathe kupeŵa nkhaŵa yotere potsatira makhalidwe abwino a m’Baibulo. (Agalatiya 6:7) Ngakhale zili choncho, si mavuto anu onse amene ali odziŵika bwinobwino ndiponso amene angathetsedwe mosavuta. Kodi mungaleke bwanji kukhala ndi nkhaŵa kwambiri?
‘Mukhale Wanzeru Poda Nkhaŵa’
Anthu ambiri amalola kuti nkhaŵa iwalepheretse kuchita chilichonse. Koma nkhani imene inafalitsidwa m’magazini ina ya achinyamata inapereka malingaliro akuti munthu angathe “kukhala wanzeru poda nkhaŵa” mwa kulola nkhaŵazo kuwathandiza kuchita zinthu zaphindu! Baibulo lili ndi mfundo zambiri zimene zingakuthandizeni kutero. Taganizirani zimene lemba la Miyambo 21:5 limanena zakuti: “Zoganizira za wakhama zichurukitsadi katundu.” Mwachitsanzo tiyeni tingoyerekezera kuti mukufuna kuitana anzanu angapo a mumpingo wanu kuti muchite phwando. Kuganizira bwino kungakuthandizeni kupeŵa zodandaulitsa zambiri. Dzifunseni kuti, ‘Kwenikweni ndi anthu ati amene ndiwaitane? Kodi ndikufuna kuti abwere nthaŵi yanji? Nanga ndikufuna kuti achoke nthaŵi yanji? Kodi pakufunika zakumwa ndi zakudya zochuluka bwanji? Kodi ndi maseŵera otani amene aliyense angasangalale nawo?’ Mukaganizira mozama zinthu zimenezi ndiye kutinso mwina phwando lanu lingadzayende bwino kwambiri.
Komabe, mungathe kuyambitsa nkhaŵa polimbana n’zinthu zambiri. Yesu Kristu anapereka malangizo awa kwa mkazi wina amene ankalimbana n’kupatsa alendo ake zinthu zapamwamba kwambiri: “Koma chisoŵeka chinthu chimodzi.” (Luka 10:42) Motero dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chikufunikadi kuti phwandoli lidzayende bwino?’ Kusalimbana n’zinthu zambiri kungakuthandizeni kuchepetsa nkhaŵa yanu.
Chinthu china chodetsa nkhaŵa chingakhale nkhani ya kutetezeka kwanu kusukulu. Ndi zinthu zochepa chabe zimene mungachite kuti mudziteteze kusukulu. Koma mungathe kuchitapo zinthu zothandizadi kuti mudziteteze. “Wochenjera aona zoipa, nabisala,” amatero Miyambo 22:3. Kungopeŵa chabe malo oopsa, osati kokha amene sikupezeka anthu komanso malo osayang’aniridwa amene kumakonda kukhala anthu opulukira, kungakuthandizeni kuti musapeze mavuto.
Ntchito ya kusukulu ingakhale chinthu chinanso choyambitsa nkhaŵa. N’kutheka kuti muli ndi ntchito zambiri zokachitira kunyumba ndipo mukuda nkhaŵa kuti simukwanitsa kuchita ntchito zonsezo panthaŵi imene zikufunika. Zikatere mfundo ya pa Afilipi 1:10, NW n’njothandiza. Mfundoyi n’njakuti: “Mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri.” Inde, phunzirani kuyamba kaye mwachita zinthu zofunika kwambiri! Ganizirani ntchito imene ikufunika mwamsanga kwambiri, ndipo mukatero yambirani imeneyo. Kenaka, chitani ntchito yotsatira. Pang’onom’pang’ono mudzayamba kuona kuti mukukwanitsa kuchita ntchito zanu zonse.
Funsirani Nzeru
Pamene Aaron anali mnyamata, ankada nkhaŵa kwambiri pofuna kukhoza mayeso omaliza mwakuti anayamba kumva kuwawa pamtima. Iye akukumbukira kuti: “Ndinauza makolo anga ndipo anandipititsa kwa dokotala. Dokotalayo anaona nthaŵi yomweyo kuti mtima wanga unalibe vuto ndipo anandilongosolera mmene nkhaŵa imawonongera thupi. Kenaka makolo anga anandithandiza kuzindikira kuti ndinali nditakonzekera mayeso mokwanira ndipo kuti tsopano ndinayenera kuganizira za thanzi langa. Nkhaŵa yanga inatha, pamtima paja panasiya kuwawa, ndipo ndinakhoza mayesowo.”
Ngati mukuvutika ndi nkhaŵa, uzani ena. Lemba la Miyambo 12:25, limene mbali yake ina taigwira kale mawu, lonse limanena motere: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu; Koma mau abwino aukondweretsa.” Kokha ngati muuza ena “nkhaŵa” zanu m’pamene mungauzidwe “mawu abwino” okulimbikitsani!
Choyamba mungafune kukambirana ndi makolo anu, ndipo angathe kukulangizani zoyenera kuchita. Anthu achikulire mwauzimu a mumpingo wachikristu angathenso kukuthandizani. Janelle, mtsikana wa zaka 15 akusimba kuti: “Ndinkada nkhaŵa ndikamaganiza zopita kusukulu yasekondale, chifukwa zonse zimene ndikanakakumana nazo kumeneko, monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kugonana, ndiponso ndewu zinkandiopsa. Nkhaŵa yanga inatha nditalankhula ndi mkulu wina mumpingo. Iye anandilangiza zinthu zambiri zothandiza. Nthaŵi yomweyo ndinayamba kusangalala chifukwa ndinazindikira kuti ndikathana nawo mavutowo.”
Osazengereza Pochita Zinthu
Nthaŵi zina timakhala ndi chinthu choti tichite, koma timazengereza chifukwa chakuti sichosangalatsa. Mwachitsanzo mtsikana wina wa zaka 19 wotchedwa Shevone, anayambana ndi Mkristu mnzake. Ankadziŵa kuti anayenera kukambirana naye nkhaniyo, koma ankangozengereza. Iye anavomereza kuti: “Chifukwa cha kuzengerezaku nkhaniyi inayamba kundiwawa kwambiri.” Kenaka Shevone anakumbukira mawu a Yesu a pa Mateyu 5:23, 24, amene amalimbikitsa Akristu kuthetsa mavuto otere mwamsanga. Shevone akukumbukira kuti, “Kenaka nditaithetsa nkhaniyi, mtima wanga unakhala m’malo.”
Kodi chilipo chinthu china chimene mukuchinyalanyaza, monga ntchito inayake yosasangalatsa kapena mkangano umene munali nawo ndi winawake? Ndiyetu chitanipo kanthu mwamsanga ndipo mukatero ndiye kuti mwapungula zinthu zina zokudetsani nkhaŵa.
Mavuto Aakulu
Si mavuto onse amene amangothetsedwa mosavuta. Taganizirani nkhani ya mnyamata wina wotchedwa Abdur. Amayi ake ali ndi matenda a kansa, ndipo motero iye amawasamalira komanso amasamaliranso mng’ono wake. Mwachibadwa, Abdur amada nkhaŵa ndi kudwala kwa amayi ake. Koma iye anati: “Ndimangokumbukira mawu a Yesu akuti, ‘Ndani wa inu ndi kudera nkhaŵa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?’ M’malo mofooka nkhongono ndimayesetsa kuganizira bwinobwino vutolo n’kuona chimene chingandithandizedi.”—Mateyu 6:27.
Kukhazikika maganizo panthaŵi yamavuto si kwapafupi. Ena amadandaula kwambiri mwakuti samadzisamaliranso, n’kumakana chakudya. Komabe buku lakuti Helping Your Teenager Deal With Stress limachenjeza kuti mukamadzimana chakudya chofunika m’thupi, ndiye kuti “m’povutanso kwambiri kuti muthane ndi vuto la maganizo ndipo matenda ena aakulu angathe kukugwirani mosavuta.” Choncho samalirani thupi lanu. Muzigona ndiponso kudya mokwanira.
Mungathe kutsitsimulidwa kwambiri potsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Shane amene tam’tchula poyamba paja, ankada nkhaŵa akamaganizira za tsogolo lake. Iye akukumbukira kuti, “Ndinayamba kuganizira kwambiri Mawu a Mulungu ndiponso cholinga chake.” Pasanapite nthaŵi anazindikira kuti angadzakhale osangalala m’tsogolo ngati atagwiritsa ntchito moyo wake potumikira Mulungu. (Chivumbulutso 4:11) Shane anati, “Ndinasiya kumadzidera nkhaŵa, chifukwa ndinapeza chinthu chofunika kwambiri choyenera kuchiganizira.”
Choncho mukaona kuti mwayamba kukhala ndi nkhaŵa kwambiri, funafunani njira zothandiza zothetsera vuto lanulo. Funsirani nzeru. Ndipo chachikulu kwambiri n’chakuti muyenera kuuza Yehova nkhaŵa zanuzo “pakuti iye asamalira inu.” (1 Petro 5:7) Iye akakuthandizani, n’kutheka kuti mungaleke kukhala ndi nkhaŵa kwambiri.
[Chithunzi patsamba 13]
Kambiranani zimene zikukudetsani nkhaŵa ndi makolo anu
[Chithunzi patsamba 14]
Mukathetsa mavuto mwamsanga, nkhaŵanso imatha msanga