Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zikondwerero Zotchuka Zilibe Vuto Lililonse?

Kodi Zikondwerero Zotchuka Zilibe Vuto Lililonse?

Kodi Zikondwerero Zotchuka Zilibe Vuto Lililonse?

M’KATI mwa mwezi wa October, zinthu zimasintha kwambiri m’mizinda ina ya ku France. M’mawindo a sitolo mumadzaza ndi maungu, mafupa ndiponso ulusi wa akangaude. M’sitolo zikuluzikulu zakumeneko, olandira ndalama amavala zipewa zakuda zosongoka. Chikondwererochi chikafika pachimake, ana amavutitsa m’misewu, amagogoda m’nyumba za anthu ndipo amaopseza eninyumba kuti akapanda kuwapatsa masiwiti awakhaulitsa.

Zinthu zodabwitsa zonsezi zimachitika pa chikondwerero chotchedwa Halloween. Poyamba chikondwererochi chinkaonedwa ngati cha ku America kokha koma tsopano chafala padziko lonse, ndipo chatchuka pakati pa ana ndi akulu omwe. Ku France, zikuoneka kuti anthu ayamba kukonda chikondwerero chimenechi ndi mtima wonse. Malingana ndi mmene ena anafufuzira, akuti pafupifupi khomo limodzi mwa makomo atatu alionse a ku France anachita chikondwerero chimenechi chaka chatha. Nyuzipepala yatsiku ndi tsiku ya ku Italy yotchedwa La Repubblica inanena kuti chikondwerero chatsopanochi chatchuka kwambiri pachilumba chonse cha Italy. Nyuzipepala yotchedwa Nordkurier inanena kuti “kuposa kale lonse, nzika zambiri za ku [Germany] sizifuna kumanidwa zosangalatsa za pachikondwererochi.”

Sikuti ndi ku Ulaya kokha kumene chikondwerero cha Halloween chatenga malo. Kungoyambira ku Bahamas mpaka ku Hong Kong, anthu akutengeka mtima kwambiri ndi chikondwerero cha Halloween. Nyuzipepala yotchedwa International Herald Tribune inati chaka chatha nyumba ina youlutsa mawu pawailesi ku Sri Lanka inakonza mpikisano wofuna kupeza “amene angalembe njira yophikira chakudya choipa kwambiri chogwirizana ndi Halloween ndiponso amene angakuwe mochititsa nthumanzi kwambiri.” Chikondwerero cha Halloween chayambanso kutchuka ku Japan, ndipo anthu ochuluka zedi akhala akuchita perete wokondwerera tsikuli ku Tokyo.

Ngakhale kumadera apadziko lonse kumene chikondwerero cha Halloween sichotchuka, nthaŵi zambiri kumakhalanso zikondwerero ndiponso zochitika zina zotchuka zomwe zili zofanana nacho. Pa chikondwerero china chausiku cha ku Britain chotchedwa Guy Fawkes Night, mungathe kuona magulu a ana ali piringupiringu kumapempha ndalama ndiponso kuchita zinthu zina zoyerekedwa zangati za pa Halloween. Ku Taiwan, kuli chikondwerero china chokopa chotchedwa Lantern Festival. Ana aang’ono amayendayenda m’misewu atanyamula nyali zomwe amajambulapo mbalame ndi zilombo zoopsa. Ku Mexico kuli chikondwero chotchedwa Día de los Muertos, kapena kuti Tsiku la Akufa ndipo chikondwererochi chadutsa malire a dzikoli mpaka chafika ku United States. Malingana ndi wolemba wina wotchedwa Carlos Miller, akuti anthu ena a ku America amene anachokera ku Mexico mpaka pano “amavalabe zigoba zathabwa zotchedwa calacas kumutu kwawo ndipo amavina polemekeza achibale awo amene anafa.”

Anthu ambiri amaona kuti zikondwerero zoterezi n’zongosalangatsa anthu basi ndipo zilibe vuto lililonse chifukwa zimangochititsa kuti ana ndiponso achikulire akhale omasuka povala zilizonse zimene angafune. Komatu, kuwona nkhaniyi mopepuka chotere n’kusaganizira mfundo yakuti zikondwerero zimenezi n’zachikunja. Mwachitsanzo, chikondwerero cha ku Taiwan cha Lantern Festival, chinayamba pamene anthu ankayatsa nyali pofuna kuona mizimu yakumwamba imene ankakhulupirira kuti inali kuuluka m’mwambamo. Tsiku la Akufa la ku Mexico linayamba chifukwa cha mwambo wolemekeza akufa wa anthu amtundu wotchedwa Aztec.

Anthu ena anganene kuti zilibe kanthu kuti zikondwerero zoterezi zinayamba bwanji. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi zikondwerero zoyamba m’njira zoipa ngati zimenezi zingakhaledi zopanda vuto lililonse? N’zachidziŵikire kuti nkhani imeneyi siiwakhudza n’komwe anthu olimbikitsa malonda a zinthu zokhudza zikondwererozi. Ponenapo za chikondwerero cha Halloween, mkulu wina woimira bungwe la Cultural Institute of Barcelona, ku Spain anati: “Chikondwererochi amachitchukitsa chifukwa cha malonda.” Taganizirani kuti chaka chatha, malisiti okhudza chikondwererochi anali okwana madola mabiliyoni 6.8 ku United States kokha. Ku France, kampani imene imapanga zovala za pa nthaŵi ya Halloween m’zaka zitatu zokha bizinesi yake yawonjezeka kuposa nthaŵi 100.

Koma kodi inuyo muyenera kuchita nawo zikondwerero zimenezi chifukwa chongoti n’zotchuka kapena kuti n’zopindulitsa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyamba talongosola mwatsatanetsatane za chikondwerero cha Halloween.

[Chithunzi patsamba 18]

Zigoba zopangidwa ndi shuga zimene amazigwiritsa ntchito pa Tsiku la Anthu Akufa ku Mexico

[Mawu a Chithunzi]

SuperStock, Inc.

[Chithunzi patsamba 19]

Ku Britain, pa chikondwerero cha Guy Fawkes Night amakoleza chimoto panja

[Mawu a Chithunzi]

© Hulton Getty Archive/gettyimages