Kodi Ana Tiyenera Kuwalangiza Bwanji?
Kodi Ana Tiyenera Kuwalangiza Bwanji?
“Mavuto amabwera ngati ana amangouzidwa kuti achita bwino ngakhale atalakwitsa zinthu zina,” inatero nyuzipepala ya ku Canada yotchedwa National Post. Makolo ena amaona kuti ana kuwatero sakhala odzikayikira. Komabe katswiri wa zamaganizo dzina lake Roy Baumeister ananena kuti, “ndi bwino ngati munthu sadzikayikira chifukwa chochitadi zinthu zakupsa, motero makolo ayenera kulimbikira kuphunzitsa ana kuchita zinthu modziletsa.”
Kholo limene limaopa kudzudzula mwana wake akalakwa, ndiye kuti likumulakwira mwanayo. Ndipotu kudzudzula mwana ndi njira ina yom’langizira. Kumam’phunzitsa mwana wolakwayo kuti asadzachitenso zolakwazo. Inde n’zoona kuti makolo ayenera kupeŵa kudzudzula ana mwankhanza ndiponso mosagwirizana ndi zimene zalakwikazo. (Yeremiya 46:28) Ayenera kutsimikiza kuti sakudzudzula anawo mopitirira muyeso. Baibulo limati: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”—Akolose 3:21.
Baibulo, nthaŵi zonse limatchula za kudzudzula mogwirizana ndi chikondi ndiponso kufatsa, osati ndi mkwiyo kapena nkhanza. Mlangizi waluso ayenera akhale “woyenera, . . . woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.” (2 Timoteo 2:24, 25) Choncho, makolo akamadzudzula ana sayenera kutero n’cholinga chongoti aphwetse mkwiyo wawo. Baibulo sililola ngakhale pang’ono kugwiritsa ntchito njira zimene zingapweteke mwana kapenanso kum’sokoneza maganizo.
Anthu ochuluka zedi padziko lonse lapansi apindula nalo buku ili limene lili ndi masamba 192. M’bukuli, mitu ina yothandiza kwambiri polangiza n’njakuti “Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake” ndiponso “Thandizani Wachinyamata Wanu Kukula Bwino.” Kuti mulandire buku lanu, chonde lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino. Mudzapezamo maganizo abwino amene angakuthandizeni kuthetsa mavuto ndiponso kupangitsa moyo wabanja kukhala wosangalatsa monga mmene Mlengi ankafunira.
□ Nditumizireni buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.