Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Bwino Kuti Mulungu Azigwiritsa Ntchito Mphamvu?

Kodi Ndi Bwino Kuti Mulungu Azigwiritsa Ntchito Mphamvu?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Ndi Bwino Kuti Mulungu Azigwiritsa Ntchito Mphamvu?

CHINTHU chimene anthu akhala akuchita m’mbiri yonse ndicho kugwiritsa ntchito mphamvu m’njira yoipa kwambiri. Ofufuza ena akuti n’kutheka kuti anthu 170,000,000 anaphedwa m’zaka za 1900 ndi maboma awo omwe. Zikugwirizanadi ndi zimene Baibulo linanena molondola kuti anthu akhala akupweteka anzawo powalamulira.—Mlaliki 8:9.

Chifukwa choona anthu akugwiritsa ntchito mphamvu mwankhanza, anthu ena anganene kuti Mulungu naye sagwiritsa ntchito bwino mphamvu akamawononga adani ake. Iwo angamati, Kodi si Mulungu amene anatuma Ayuda kuti aukire ndi kupha Akanani eni a Dziko Lolonjezedwa? (Deuteronomo 20:16, 17) Ndipo kodi Mulunguyo sananene kuti adzaphwanya ndi kutha maufumu onse oipa? (Danieli 2:44) Anthu ena okhulupirika akhala akukayikira ngati nthaŵi zonse Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu moyenera.

Kugwiritsa Ntchito Mphamvu Molakwika

Ndi bwino kwambiri kumvetsa kuti ndi chinthu chofunika kuti boma lizitha kugwiritsa ntchito mphamvu. Kunena zoona, akuluakulu amene sagwiritsa ntchito mphamvu pa malamulo awo, ndi olephera pa ntchito yawo. Mwachitsanzo, ngakhale kuti pali nkhani zambiri zonena kuti apolisi amalakwira anthu, kodi ndi anthu angati amene angafune kukhala popanda kutetezedwa ndi apolisi? Ndipo kodi ndi munthu wamtundu wanji wabwinobwino amene anganene kuti m’posafunika kuti anthu azikhala ndi gulu lina lokhala ndi mphamvu zoonetsetsa kuti lamulo likutsatiridwa?

Mohandas Gandhi yemwe anali wotchuka chifukwa chodana ndi chiwawa ananenapo kuti: “Tayerekezerani kuti munthu wina wasokonezeka mutu ndipo sakugwirika, akungoyendayenda molusa atanyamula chikwanje m’manja mwake, ndipo akupha munthu wina aliyense amene akukumana naye, koma palibe munthu amene akulimba mtima kuti amugwire wamoyo. Aliyense amene angathe kupha chigaŵengachi, anthu angakondwere naye ndipo angamuone monga munthu wabwino kwambiri.” Inde, ngakhale Gandhi anaona kuti nthaŵi zina pamafunika kugwiritsa ntchito mphamvu.

Choncho n’zosachita kufunsa kuti kugwiritsa ntchito mphamvu ndi chinthu chofunika pakati pa anthu onse. Nthaŵi zambiri anthu akamadandaula chifukwa cha mmene ena akugwiritsira ntchito mphamvu, ndiye kuti mphamvuzo akuzigwiritsa ntchito molakwika.—Mlaliki 4:1-3.

“Njira Zake Zonse Ndi Chiweruzo”

Palibe umboni uliwonse wam’mbuyomo wakuti Mulungu anayamba wagwiritsapo ntchito mphamvu zake molakwika. Iye salamulira anthu mowapondereza ayi. Amafuna kuti tizim’lambira chifukwa chakuti timam’konda. (1 Yohane 4:18, 19) Kwenikweni, Mulungu sagwiritsa ntchito mphamvu ngati pali njira ina yabwino yochitira zimene akufunazo. (Yeremiya 18:7, 8; 26:3, 13; Ezekieli 18:32; 33:11) Ndipo akafuna kugwiritsa ntchito mphamvu, nthaŵi zonse amapereka machenjezo ochuluka kuti aliyense amene akufuna adziŵiretu chochita kuti zimuyendere bwino. (Amosi 3:7; Mateyu 24:14) Kodi Mulungu wopondereza ndiponso wankhanza angachite zinthu zotere?

Sitingayerekezere n’komwe mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake ndi mmene anthu amagwiritsira ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo. Potchula za Yehova, Mose anati, “Njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.” (Deuteronomo 32:4) Mosiyana ndi maboma ankhanza a anthu, boma la Mulungu siliyendera zakuti winawake wokhala ndi mphamvu zambiri ndiye ayenera kuyendetsa zinthu. Pa nkhani ina iliyonse imene Mulungu anagwiritsapo ntchito mphamvu, iye anatero mogwirizana ndi ungwiro wake pa chikondi, nzeru ndiponso chilungamo.—Salmo 111:2, 3, 7; Mateyu 23:37.

Mwachitsanzo, pamene Mulungu anawononga ndi Chigumula cha madzi anthu oipa, iye anali atawachenjeza kwa zaka zambiri. Aliyense akanatha kudzipereka yekha kuti atetezedwe m’chingalawa n’kupulumuka. Anthu asanu ndi atatu okha ndiwo anachita zimenezo. (1 Petro 3:19, 20; 2 Petro 2:5) M’masiku a Yoswa, Mulungu analamula mtundu wa Israyeli kulanga mtundu wa khalidwe loipa wa Akanani, ndipo chilangocho chinalengezedwa zaka 400 chisanachitike. (Genesis 15:13-21) N’zosatheka kuti nthaŵi yonseyo, Akanani anali asanamvepo nkhani zotsimikizika ndithu zakuti Aisrayeli anali anthu osankhidwa ndi Mulungu. (Yoswa 2:9-21; 9:24-27) Komatu palibe mtundu wa Akanani uliwonse kupatulapo Agibeoni, umene unapempha kuchitiridwa chifundo kapena umene unadzipereka wokha kuti upeze mtendere. M’malo mwake Akananiwo anachita makani pokana kumvera Mulungu.—Yoswa 11:19, 20.

Mulungu Ali ndi Mphamvu

Tikafuna kumvetsa mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu, tiyenera kudziŵa kaye kuti kodi ifeyo timaoneka bwanji pamaso pa Mulungu. Mneneri Yesaya anavomereza modzichepetsa kuti “Ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu.” (Yesaya 64:8) N’zachionekere kuti monga Mlengi wa chilengedwe chonse, Mulungu angagwiritse ntchito mphamvu mwa njira ina iliyonse imene iye akufuna. Pozindikira mphamvu ya Mulungu, tinganene monga Solomo kuti: “Mawu a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?”—Mlaliki 8:4; Aroma 9:20, 21.

Chifukwa chakuti Mulungu ndi Mlengi wa mphamvu yonse, iye ali ndi ufulu wopereka kapena kuchotsa moyo padziko lapansi. Kunena zoona, anthu alibe nzeru zokwanira ndiponso sadziŵa zinthu zambiri mwakuti anganenepo kanthu kotsutsa mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake. Anthu ayenera kuphunzira kuti aziganiza mogwirizana ndi maganizo a Mulungu. Nthaŵi inayake Yehova anafunsa kuti: ‘Kodi njira zanu si ndizo zosayenera?’—Ezekieli 18:29; Yesaya 45:9.

Chifukwa chakuti Yehova n’ngwachilungamo ndiponso amakonda anthu, adzachotsa m’dziko anthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu mosayenera n’kumapondereza kwambiri anzawo. Mulungu akadzagwiritsa ntchito mphamvu motere adzapangitsa zinthu kukhala zabwino kwambiri padziko lapansi kwa anthu onse okonda mtendere. (Salmo 37:10, 11; Nahumu 1:9) Motero boma la Mulungu lidzadziŵika kuti n’lolungama ndiponso kuti n’lolondoladi kwamuyaya.—Chivumbulutso 22:12-15.