Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Cholakwika Ngati Utabwezera?

Kodi Pali Cholakwika Ngati Utabwezera?

Achinyamata Akufunsa Kuti  . . .

Kodi Pali Cholakwika Ngati Utabwezera?

“Ananditukwana,” anatero Conneel, wa zaka 15, amene ali m’ndende chifukwa cha kupha munthu.

Andrew, wa zaka 14, amene anapha mphunzitsi pa dansi ya kusukulu, anati amadana ndi aphunzitsi ndiponso makolo ake komanso atsikana chifukwa choti amamukana.

MAGAZINI ya Time inati limeneli ndi “khalidwe loopsa.” Wachinyamata wina atakalipa anatenga mfuti yoopsa n’kupita nayo mobisa kusukulu kenaka n’kuyamba kuwombera ana asukulu anzake ndiponso aphunzitsi. Zoopsa ngati zimenezi zikuoneka kuti zayamba kufala kwambiri ku United States mwakuti wailesi ina yakanema youlutsa nkhani inati uku “n’kuwanda kwa chiwawa.”

Mwayi wake, zowomberana kusukulu sizinayambebe kuchitika kaŵirikaŵiri. Komabe milandu yambiri yaposachedwapa yochitika chifukwa cha ukali ikusonyeza kuti achinyamata ena ali ndi ukali kwambiri. Kodi n’chiyani chimene chikuoneka kuti chimawakwiyitsa chonchi? Zikuoneka kuti ena mwa achinyamataŵa anakwiya chifukwa chakuti akuluakulu ena anawachitira zinthu zopanda chilungamo kapena zowapezerera poti ndi ana. Ena anakwiya chifukwa chomangovutitsidwa ndi anzawo. Mnyamata wina wa zaka 12 amene anawombera mnzake wam’kalasi ndipo kenaka n’kudziwombera yekha, anali kusekedwa chifukwa chonenepa kwambiri.

N’zoona kuti achinyamata ambiri sangaganizeko kuti achite zinthu zoopsa ngati zimenezi. Komabe, n’kovuta kuti usapse mtima ngati ena akukusankha mtundu, kukuzunza, kapena kukuvutitsa mwankhanza. Poganizira zakale adakali kusukulu, Ben anati: “Nthaŵi zonse pagulu la ana onse amsinkhu wanga ine ndiye ndinali wamfupi zedi. Ndipo chifukwa chakuti ndinkameta mpala, anzangawo ankangondiseka n’kumandimenya nkhonya m’mutu. Izi zinkandikwiyitsa zedi. Chinkandipweteka kwambiri n’chakuti ndikapita kukawaneneza kwa akuluakulu, akuluakuluwo sankalabadira n’komwe. Ndiye zikatere, ine sikukwiya kwake!” Ben anatinso: “Ndikanakhala ndi mfuti, anthu ameneŵa ndikanawawombera koma mwayi wake, ndinalibe mfutiyo.”

Kodi muyenera kuwaona motani achinyamata amene amafuna kubwezera anthu amene anawapweteketsa mtima? Ndipo kodi inuyo muyenera kutani anthu ena akamakuvutani? Kuti tiyankhe mafunsoŵa tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena.

Kudziletsa Kumasonyeza Uchamuna!

Kuzunzana ndiponso kusoŵa chilungamo sizachilendo ayi. Wolemba Baibulo wina anapereka malangizo aŵa: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) Nthaŵi zambiri, mkwiyo umachititsanso kusadziletsa ndipo munthu akamachita zinthu atakalipa saganizira mapeto ake a zimene akuchitazo. Kudzilola “kupsa mtima” kungachititse munthu kukalipa kwambiri! Kodi ndiye atatero chingachitike n’chiyani?

Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo cha Kaini ndi Abele. “Kaini ndipo anakwiya kwambiri,” kukwiyira mbale wake Abele. Mapeto ake, “pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.” (Genesis 4:5, 8) Chitsanzo china cha kusaugwira mtima n’chokhudza Mfumu Sauli. Chifukwa chochita nsanje ndi kupambana kwa Davide pankhondo, iye anaponya mikondo pofuna kupha Davide, komanso ngakhale mwana wake yemwe Jonatani!—1 Samueli 18:11; 19:10; 20:30-34.

N’zoona kuti nthaŵi zina munthu umayenera kupsa mtima. Komatu ngakhale kupsa mtima moyenera kungachititse munthu zoipa ngati atapanda kuugwira mtima. Mwachitsanzo Simeoni ndi Levi anayeneradi kum’psera mtima Sekemu atamva kuti wagwirira mlongo wawo Dina. Koma m’malo mochita zinthu mofatsa, iwo anakwiya monyanyira, monga mmene mawu amene ananena pambuyo pake akusonyezera. Mawuwo ndi akuti: “Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?” (Genesis 34:31) Ndipo atalunda mosati n’kugwirika, “anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima naloŵa m’mudzi napha amuna onse” okhala m’mudzi wa Sekemu. Ukali wawo unakhudzanso ena chifukwa ‘ana ena aamuna a Yakobo’ analoŵerera pa kupha anthu kumeneku. (Genesis 34:25-27) Ngakhale zaka zambiri pambuyo pake, Yakobo, abambo awo a Simeoni ndi Levi, anatsutsa khalidwe lawo lokwiya mosadziletsa.—Genesis 49:5-7.

Pamenepa timaphunzirapo mfundo yofunika kwambiri yakuti kukwiya mosadziletsa sikusonyeza uchamuna koma kumasonyeza kulephera. Lemba la Miyambo 16:32 limati: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.”

Uchitsiru wa Kubwezera

Motero Malemba amapereka malangizo otsatiraŵa: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Musabwezere choipa.” (Aroma 12:17, 19) Mulungu sakondwera ndi kubwezera pochita zachiwawa kapena kungolalata. Komanso kubwezera kotere n’kosathandiza n’komwe ndiponso si kwanzeru. Ndiponsotu kubwezera pochita zachiwawa kumangobala chiwawa chinanso. (Mateyu 26:52) Ndipo mawu olalata amangochititsanso ena kuti alalate. Kumbukiraninso kuti nthaŵi zambiri anthu amakwiya asanadziŵe bwino nkhani yonse. Mwachitsanzo kodi mungadziŵedi kuti munthu amene wakulakwirani amakudani? Kodi sizingatheke kuti mwina munthuyo wakulakwirani mosaganizira bwinobwino kapena anangochita mwano? Ndipo ngati anachitadi zadala, kodi ndiye kuti kubwezera kungakhaledi njira yabwino?

Taganizirani mawu a m’Baibulo pa Miyambo 7:21, 22 akuti: “Mawu onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera; pakuti kaŵirikaŵiritu mtima wako udziŵa kuti nawenso unatemberera ena.” Inde, zimawawa anthu ena akamatinenera zoipa. Koma Baibulo limati ndimo mmene moyo ulili. Kodi si zoona kuti mwina nanunso munanenerapo ena mawu oipa amene simunayenera kuwanena? Choncho nanga inu mukwiyiranji kwambiri munthu wina akakulankhulirani udyo? Nthaŵi zambiri chinthu chothandiza kwambiri mukamasekedwa ndicho kungonyalanyaza zomwe zikuchitikazo.

Chonchonso si kwanzeru kukulitsa nkhani ngati mukuona kuti wina wakulakwirani. Mnyamata wina wotchedwa David akukumbukira zimene zinam’chitikirapo akuseŵera mpira wamanja umene amati basketball ndi anzake ena achikristu. “Munthu wina wa gulu lina anandimenya ndi mpira,” anatero David. Iye anafulumira kuganiza kuti munthuyu anachita dala, motero anam’bwezera pomumenyanso ndi mpirawo. David anavomereza kuti “Ndinakalipadi kwambiri.” Koma zinthu zisanaipe kwambiri, David anapemphera kwa Yehova. Iye anadzifunsa kuti, ‘Vuto langa n’chiyani makamaka, n’zoona ndingafune kumenya mbale wanga wachikristu?’ Pambuyo pake anapepesana.

Zoterezi zikachitika ndi bwino kukumbukira chitsanzo chabwino cha Yesu Kristu. “Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa.” (1 Petro 2:23) Inde, mukasokonezeka maganizo, m’malo mopsa mtima pempherani kwa Mulungu ndi kum’pempha kuti akuthandizeni kuugwira mtima. Iye mooloŵa manja “adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye.” (Luka 11:13) M’malo mobwezera wina akakuputani, chomwe muyenera kuchita ndicho kukambirana naye nkhani imeneyo. (Mateyu 5:23, 24) Kapena ngati mukuvutitsidwa kwambiri, mwina ndi mwana wasukulu wina wovutitsa anzake, musayese kukangana naye. M’malo mwake, muyenera kuyesetsa kuchita zinthu zothandiza kuti mudziteteze. *

Mtsikana Amene Anaugwira Mtima

Achinyamata ambiri agwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zimenezi ndipo apindula nazo. Mwachitsanzo Catrina ali mwana anasiyidwa n’kuleredwa ndi makolo osakhala ake. Iye anati: “Ndinali ndi vuto lokwiya pafupipafupi chifukwa chakuti sindinkamvetsa chifukwa chimene amayi anga ondibala anandisiyira. Motero ukali wonse unkathera pa amayi anga ondilera. Ndinkaganiza mopusa kuti ndikamachita zinthu zowapweteka mtima, ndiye kuti ndikubwezera amayi anga ondibereka m’njira inayake. Motero ndinkayerekedwa m’njira zosiyanasiyana, monga kutukwana, kumenyetsa mwendo pansi chifukwa cha ukali ndiponso kungonyanyuka. Chimene ndinkakonda kwambiri ndicho kutseka zitseko momenyetsa kwambiri. Ndipo ndinkakondanso kuwauza kuti, ‘Mumandinyansa!’ koma zonsezo chinali chifukwa chopsa mtima basi. Ndikamakumbukira zimenezi sindikhulupirira kuti ndineyo amene ndinkatero.”

Kodi chinam’thandiza Catrina kuti achepetse mkwiyo wake n’chiyani? Iye anayankha kuti: “N’kuŵerenga Baibulo! Kutero n’kofunika kwambiri chifukwa Yehova amadziŵa mmene tikumvera.” Catrina anatsikanso mtima pamene iye ndi a m’banja lakewo ankaŵerenga nkhani za mu Galamukani! makamaka zokhudza banja langati lawolo. * Iye akukumbukira kuti, “Tonse tinkatha kukambirana mavuto athu n’kumvetsetsana maganizo.”

Nanunso mungaphunzire kuugwira mtima mukakwiya. Ena akamakusekani, kukuzunzani kapena kukuvutitsani, kumbukirani mawu a m’Baibulo opezeka pa Salmo 4:4 akuti: “Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.” Mawu amenewo angakuthandizeni kuti musapse mtima mpaka kuchita zoopsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Kuti mudziŵe njira zothandiza kuti musavutike mtima ndi aphunzitsi opanda chilungamo, ana asukulu ozunza anzawo, ndiponso anthu ovutitsa, onani nkhani za “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ” zopezeka m’magazini ya Galamukani! ya June 8, 1986 ndi August 8, 1989 ndiponso maganizi a Chingerezi a February 8, 1984.

^ ndime 21 Onani nkhani zotsatizana zakuti “Kodi Muyenera Kulera Ana a Ena,” za m’magazini ya Galamukani! ya May 8, 1996.

[Chithunzi patsamba 15]

Nthaŵi zambiri chinthu chothandiza kwambiri mukamasekedwa ndicho kungonyalanyaza zomwe zikuchitikazo