Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo

Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo

Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo

KODI akazi amene amamenyedwa ndi amuna awo angathandizidwe bwanji? Choyamba, muyenera kumvetsetsa mavuto amene akukumana nawo. Nthaŵi zambiri amuna otere si kuti amangowamenya chabe akaziwo. Amawaopsezanso ndi kuwanyoza motero amangodziona ngati ndi achabechabe.

Tatiyeni tione nkhani ya Roxana imene taisimba m’nkhani yoyamba ija. Nthaŵi zina mwamuna wake amam’nyoza mopweteketsa mtima kwambiri. Roxana anaulula mavuto ake motere: “Amanditchula mayina ondinyoza. Amandiuza kuti: ‘Mbuli iwe, sunamalize n’komwe sukulu. Ungathe bwanji kusamala ana popanda ine? Ndiwe mayi waulesi ndiponso wosathandiza. Ukuganiza kuti ngakhale aboma angakulole kusamalira anaŵa popanda ineyo?’”

Mwamuna wa Roxana amasunga ndalama zonse kuti mkazi wake asakhale ndi mphamvu zilizonse. Sam’lola kuyendetsa galimoto yawo, ndipo tsiku lililonse sipatenga nthaŵi asanaimbe telefoni kuti adziŵe zimene mkazi wake akuchita. Akati anenepo maganizo ake pa nkhani inayake, mwamunayo amayamba kukalipa moopsa. Motero Roxana amadziŵiratu kuti sayenera kunenapo maganizo ake pa nkhani iliyonse.

Apatu tingathe kuona kuti nkhani ya kuvutitsa mkazi ndi yovuta. Kuti mum’thandize mkaziyo muyenera kumvetsera mokhudzidwa mtima. Musaiwale kuti nthaŵi zambiri zimawavuta kwambiri akazi kulongosola zimene zakhala zikuwachitikira. Cholinga chanu chikhale cholimbikitsa mkaziyo pamene akuthana pang’onopang’ono ndi vutolo.

Akazi ena omenyedwa angafune kupempha chithandizo ku boma. Nthaŵi zina kuchita chinthu china chachikulu, monga kupita ku polisi, kungachititse mwamuna womenya kudziŵa kuti imeneyi si nkhani yamaseŵera ayi. Koma n’zoona kuti nkhaniyo ikangotha basi maganizo onse osiya khalidweli amaiwalika.

Kodi mkazi womenyedwayo ayenera kum’siya mwamunayo? Baibulo silinena kuti nkhani ya kupatukana n’njaing’ono. Komanso silikakamiza mkazi womenyedwa ndi mwamuna wake kukhalabe ndi mwamunayo amene angathe kudzam’vulaza kwambiri mwinanso kumupha kumene. Mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: ‘Ngati am’siya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo.’ (1 Akorinto 7:10-16) Chifukwa chakuti Baibulo sililetsa kupatukana ngati pali vuto lalikulu kwambiri, zimene mkazi angaganize kuchita pankhaniyi munthu wina sangam’pangire. (Agalatiya 6:5) Munthu wina aliyense sayenera kum’nyengerera kuti asiye mwamuna wake, komanso sayenera kum’kakamiza kuti akhalebe ndi mwamunayo ngati akuopera kuti avulala kapena kufa kapenanso kuti am’sokoneza pa zauzimu.

Kodi Amuna Omenya Akazi Awo Angasinthe?

Kuvutitsa mkazi n’kuphwanya poyera mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo. Pa Aefeso 4:29, 31, timaŵerenga kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu . . . Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.”

Mwamuna aliyense amene amatsatira Yesu sanganene kuti amakonda mkazi wake ngati amam’zunza. Ngati mwamuna amazunza mkazi wake, ndiye kuti zabwino zonse zimene mwamunayo amachita zili n’ntchito yanji? Munthu ‘wandewu’ si woyenera maudindo apadera mumpingo wachikristu. (1 Timoteo 3:3; 1 Akorinto 13:1-3) Inde, aliyense wodzitcha Mkristu amene amachita zinthu mopsa mtima kaŵirikaŵiri komanso wosalapa angathe kuchotsedwa mumpingo wachikristu.—Agalatiya 5:19-21; 2 Yohane 9, 10.

Kodi amuna andewu angathe kusintha khalidwe? Ena asintha. Komabe nthaŵi zambiri amuna omenya akazi awo samasintha pokhapokha (1) ngati atavomereza kuti khalidwe lawolo n’loipa, (2) ngati akufunadi kuleka khalidwe lawolo, ndiponso (3) ngati akufunafuna kuthandizidwa. Mboni za Yehova zapeza kuti Baibulo ndilo lingathe kum’sintha kwambiri munthu. Anthu ambiri achidwi amene amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ayamba kufunitsitsa kumusangalatsa Mulungu. Anthu ongoyamba kumene kuphunzira Baibulo ameneŵa amaphunzira kuti Yehova Mulungu ‘amada aliyense wokonda chiwawa.’ (Salmo 11:5) N’zoona kuti mwamuna womenya ayenera kusinthanso zinthu zina osangosiya kumenya kokhako. Mwamunayo amafunika kuti aphunzirenso kuona mkazi wake m’njira yosiyana kwambiri.

Mwamuna akadziŵa Mulungu, amaphunzira kuona mkazi wake monga “wom’thangatira” osati monga wantchito kapena wonyozeka koma monga woyenera kumupatsa “ulemu.” (Genesis 2:18; 1 Petro 3:7) Amaphunziranso kukhala wachifundo ndiponso kumvetsera maganizo a mkazi wake. (Genesis 21:12; Mlaliki 4:1) Ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene Mboni za Yehova zimachita yathandiza mabanja ambiri. M’banja lachikristu si muyenera kupezeka munthu wankhanza kapena womenya anzake.—Aefeso 5:25, 28, 29.

“Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Motero, nzeru zopezeka m’Baibulo zingathandize mabanja kuona bwino mavuto awo ndi kuwalimbitsa mtima kuti athane ndi mavutowo. Chofunikanso kwambiri n’chakuti m’Baibulo muli chiyembekezo chotsimikizika ndiponso cholimbitsa mtima chakuti m’dzikoli simudzakhalanso kuzunzana Mfumu yakumwamba yosankhidwa ndi Yehova ikamadzalamulira anthu onse omvera. Baibulo limati: “Adzapulumutsa waumphaŵi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”—Salmo 72:12, 14.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

M’banja lachikristu si muyenera kupezeka munthu wankhanza kapena womenya anzake

[Bokosi patsamba 8]

Kukonza Mabodza

Akazi amene amamenyedwa amawayamba dala amuna awo.

Amuna ambiri savomera mlandu womenya akazi awo chifukwa amati akaziwo amachita kuwaputa dala. Nthaŵi zina ngakhale anzawo abanjalo angavomereze kuti n’zoonadi mkaziyo ndi wovuta, ndipo mpake kuti nthaŵi zambiri mwamuna wake amalephera kupirira. Komatu kutero kumakhala kulungamitsa wolakwayo n’kuimba mlandu womenyedwayo. Kunena zoona, akazi omenyedwa amayesetsa kwambiri kuziziritsa mtima amuna awo. Komatu palibiretu chifukwa chilichonse chokwanira kuti munthu amenye mkazi wake. Buku lina lonena za khalidwe la amuna omenya lotchedwa The Batterer—A psychological Profile limati: “Amuna amene mabwalo amilandu amawalamula kuti akalangidwe chifukwa chovutitsa akazi awo amakhala kuti anazoloŵera kwambiri kuchita za ndewu. Amachita zimenezi pofuna kuphwetsa ukali ndi kukhazikitsa maganizo, kusonyeza mphamvu ndi kuthetsa nkhani, komanso pofuna kuziziritsa mtima. . . . Nthaŵi zambiri sangathe kuvomereza kuti ali ndi vuto kapena siziwakhudza n’komwe zoti ali ndi vutoli.”

Moŵa umachititsa kuti munthu azimenya mkazi wake.

Inde, n’zoona kuti amuna ena amakhala andewu kwambiri akamwa moŵa. Koma kodi n’kwanzeru kunena kuti moŵawo ndi umene umawachititsa zimenezi? “Munthu womenya mkazi wake ataledzera amapeza ponamizira, m’malo movomera kuti iyeyo ndiye ali ndi khalidwe loipa,” analemba choncho, K. J. Wilson m’buku lake lakuti When Violence Begins at Home. Iye anapitiriza kunena kuti: “Zikuoneka kuti kwa anthufe, ambiri timaona kuti ngati mwamuna wamenya mkazi wake ataledzera m’pomveka. Mkazi womenyedwayo safuna kuvomereza kuti mwamuna wake ndi wovuta, koma amangoti ndi chidakwa.” Wilson anati maganizo otere, angapusitse mkaziyo n’kumayembekeza kuti “ngati mwamunayo atangosiya kumwa moŵa, basi sadzam’menyanso.”

Pakali pano, ofufuza ambiri amaona kuti vuto la uchidakwa ndi kumenya mkazi ndi mavuto aŵiri osiyana. Ndiponsotu amuna ambiri omwa mwauchidakwa kapena amene amagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo samenya akazi awo. Anthu amene analemba buku lakuti When Men Batter Women anaona kuti: “Chimapangitsa amuna kusasiya kumenya akazi awo n’chakuti kumenyako kumatheketsa kuti azilamulira akaziwo, kuwaopseza ndiponso kuwagonjetsa. . . . Amuna otere amakhala kale ndi khalidwe lauchidakwa ndiponso logwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma n’kulakwa kuganiza kuti moŵa kapena mankhwala osokoneza bongo n’zimene zimawapangitsa kukhala andewu.”

Amuna omenya akazi awo amachitira nkhanza munthu aliyense.

Nthaŵi zambiri munthu womenya mkazi wake amatha kukhala munthu wabwino kwambiri kwa ena. Iye amasinthasintha zochita kukhala ngati birimankhwe. Ichi n’chifukwa chake anzawo a banjalo sakhulupirira akamauzidwa kuti mwamunayo n’ngwa ndewu. Koma zoona zake zimakhala zakuti mwamunayo amakhala chilombo kwa mkazi wake.

Akazi sadandaula n’kuzunzidwa.

N’kutheka kuti anthu amaganiza zimenezi chifukwa chosamvetsa kuti mkazi womenyedwa amalephera kuthaŵa chifukwa chosoŵa kothaŵira. Mkazi womenyedwayo angathe kukhala ndi anzake amene angam’sunge mwina kwa mlungu umodzi kapena iŵiri, koma akachoka pakhomopo kodi angatani payekha? Amatheratu mphamvu akamaganiza kuti ayenera kupeza ntchito ndiponso kulipira nyumba ya lendi kwinakunso akusamalira ana. Ndipo malamulo a m’dzikolo angam’letse kuthaŵa nawo anawo. Ena anathaŵapo koma amuna awo anawafunafuna n’kuwapeza kenaka n’kubwerera nawo kunyumba, mowakakamiza kapena mowanyengerera. Anzawo amene sangamvetse kuti chachitika n’chiyani angaganize molakwa kuti akazi otere sadandaula n’kuzunzidwa.