Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mwina Tsopano Asintha”

“Mwina Tsopano Asintha”

“Mwina Tsopano Asintha”

ROXANA * ndi mayi wansangala ndiponso wokongola, wa ana anayi ndipo mwamuna wake ndi dokotala wotchuka pa ntchito yake ya opaleshoni ku South America. Iye anati, “Akazi amaona kuti mwamuna wanga ndi munthu wosangalatsa zedi, ndipo amuna nawo amam’konda kwambiri.” Koma mwamuna wa Roxana ali ndi vuto limene ngakhale anzake apamtima salidziŵa. “Akakhala kunyumba ankasanduka chilombo choopsa. Ndi wansanje kwambiri.”

Pamene akupitiriza nkhani yake, Roxana akuonekeratu kuti ali ndi nkhaŵa. “Vutoli linayamba titakwatirana kwa milungu yochepa chabe. Azichimwene anga ndi amayi anga anabwera kudzatichezera ndipo ndinasangalala ndiponso kuseka nawo kwambiri. Koma atachoka, mwamuna wanga anandikankha mwamphamvu n’kundigwetsera pa sofa, atakalipa kwambiri. Sindinathe kumvetsa kuti akuchitiranji zimenezi.”

N’zomvetsa chisoni kuti uku kunali kuyamba chabe kwa mavuto a Roxana, chifukwa wakhala akumenyedwa molapitsa kwa zaka zambiri tsopano. Roxana amadziŵiratu zimene mwamunayo anazoloŵera kuchita akam’menya. Amati akam’menya, amamupepesa kwambiri ndipo amalonjeza kuti sadzachitanso. Akatero amasintha khalidweli kwa kanthaŵi. Kenaka amayambiranso kuchita zoopsazi. Roxana anati, “Ndimangoti mwina tsopano asintha. Ngakhale ndikam’thaŵira, nthaŵi zonse ndimabwereranso.”

Roxana amaopa kuti tsiku lina khalidwe la mwamuna wakeli lidzafika poipa. Iye anati, “Anandiopsezapo kuti adzandipha, adzapha ana athu ndipo kenaka adzadzipha yekha. Tsiku lina anandipana pakhosi ndi sizasi. Tsiku linanso anandiopseza ndi mfuti, anailozetsa pa khutu panga, n’kuikhetchemula! Mwayi wake inalibe zipolopolo, koma pang’onong’ono n’kanafa ndi mantha.”

Ambiri Saulula

Monga Roxana, akazi ambiri padziko lonse akuvutitsidwa ndi amuna omenya. * Ambiri saulula zimenezi ayi. Amaganiza kuti kuwaneneza amuna awo si kungathandize n’komwe. Ndiponsotu amuna ambiri savomera zakuti amamenyadi akazi awo ponena kuti “Mkazi wanga amaganiza mothamanga” kapena kuti “Mkaziyu amakonda kuwonjezera nkhani.”

N’zomvetsa chisoni kuti panyumba pawo penipeni, akazi ambiri amakhala mtima uli m’mwamba poopa kumenyedwa, m’malo moti azikhala mosatekeseka. Koma n’zodandaulitsa kuti nthaŵi zambiri anthu amamvera chisoni omenya mnzakeyo m’malo mwa omenyedwayo. N’zoonadi, anthu ena sakhulupirira n’komwe kuti munthu wooneka ngati waulemu wake angamenye mkazi wake. Taganizirani zimene anakumana nazo mkazi wina dzina lake Anita pamene anaulula kuti mwamuna wake waulemu wake ndithu anali kum’menya. “Mnzathu wina anandiuza kuti: ‘N’zoona iwe ungam’nenere zoipa zotere mwamuna wabwino ngati ameneyu?’ Mnzathu winanso ananena kuti mwina ineyo ndinali kum’puta dala! Ndipo ngakhale pamene mwamuna wangayu anadziŵikadi khalidwe lake, anzanga ena anayamba kundithaŵa. Akuti bwenzi nditangopirira chifukwa chakuti paja ‘amuna ndi achoncho.’”

Zimene anaona Anitazi zikusonyeza kuti ambiri zimawavuta kumvetsa mmene zimapwetekera ukamamenyedwa ndi mwamuna wako. Kodi n’chiyani chimachititsa mwamuna kuchitira mkazi amene amati amamukonda nkhanza zotere? Kodi omenyedwawo angathandizidwe bwanji?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina tawasintha m’nkhani zino.

^ ndime 7 Tikudziŵa kuti amuna ambiri amamenyedwanso. Koma ofufuza amati akazi ndiwo amavulazidwa modetsa nkhaŵa kwambiri. Motero nkhani zino zikulongosola za nkhani ya kumenya akazi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]

Akazi Amavutitsidwa M’njira Zambiri Panyumba

Malingana ndi mfundo ya bungwe la United Nations Yoletsa Kuwachitira Nkhanza Akazi, “kuchitira nkhanza akazi” kungatanthauze ‘kuchita chinthu chilichonse chovutitsa munthu chifukwa chakuti ndi wamkazi, chimene mapeto ake chingathe kum’vulaza.’ Kuvutitsaku kukuphatikizaponso ‘kungotchula zinthu zimenezi moopseza ndiponso kukakamiza mkazi kuchita chinachake kapena kusam’patsa ufulu uliwonse, kaya pamaso pa anthu ena kapena pa aŵiri.’ Zina zimene zili m’gulu lomweli ndi zinthu monga, “kuchita zinthu zovulaza akazi, zowavutitsa pankhani ya kugonana, ndiponso zowavutitsa maganizo, kaya n’zochitidwa m’banja kapena zochitidwa ndi anthu wamba, ngakhalenso kuwachita zopusa ana aakazi, kuvutitsa mkazi chifukwa cha malowolo, kugona mkazi wako mom’kakamiza, mdulidwe wa akazi ndiponso miyambo ina yovulaza akazi.”