Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nthaŵi Zina Ndimangoona Ngati N’kutulo Ndithu!”

“Nthaŵi Zina Ndimangoona Ngati N’kutulo Ndithu!”

“Nthaŵi Zina Ndimangoona Ngati N’kutulo Ndithu!”

Lourdes akusuzumira pa windo ali m’nyumba yake n’kumayang’ana mzindawo ndipo wagwira pakamwa pake pamene pakunjenjemera ndi mantha. Iyeyu ndi mayi wa ku Latin-America amene anavutitsidwa kwambiri ndi mwamuna wake womenya Alfredo kwa zaka zoposa 20. Chinachake chinam’chititsa Alfredo kusintha khalidwe lakelo. Koma panopa zimam’vutabe kwambiri Lourdes kuti alongosole mmene anazunzidwira.

Ndi mawu ofooka, Lourdes anasimba motere: “Vutoli linayamba titangokwatirana kwa masabata aŵiri. Nthaŵi ina anandimenya n’kundichotsa mano aŵiri. Nthaŵi inanso ataponya nkhonya yake ndinazinda ndipo anamenya kabati ya zovala. Koma chinkandipweteka kwambiri chinali kumanditchula mayina ondinyoza. Ankanditcha ‘chitsiru chosatha ntchito’ ndipo ankangonditenga ngati wosaganiza bwino. Ndinkafuna kuchoka, koma kodi ana atatu n’kanaloŵera nawo kuti?”

Alfredo akusisita pheŵa la Lourdes mwachikondi. Iye akuti: “Ndili ndi udindo waukulu kuntchito kwanga ndipo ndinachita manyazi nditapatsidwa chisamani komanso chikalata cha ku boma chondiletsa kumenya mkazi wanga. Ndinayesetsa kusintha, koma pasanathe nthaŵi ndinayambiranso.”

Nanga zinthu zinasintha bwanji? Lourdes amene tsopano akuoneka kuti wakhazikika maganizo akulongosola motere: “Mkazi wa pa sitolo ina yake ali m’gulu la Mboni za Yehova ndipo anandiuza kuti n’tafuna angathe kundithandiza kumvetsa Baibulo. Ndinaphunzira kuti Yehova amaŵerengera akazi kuti ndi ofunika. Ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova, ngakhale kuti poyamba Alfredo zinkam’psetsa mtima kwambiri. Nditapita ku Nyumba ya Ufumu kanali koyamba kuti ndichezeko ndi anzanga. Ndinadabwa kuona kuti ndinali ndi ufulu wokhala ndi chikhulupiriro changachanga, chimene ndikanatha kuuza ena mwaufulu. Ndinazindikira kuti Mulungu amandiona kuti ndine wofunika. Zimenezi zinandilimbitsa mtima.

“Pali chinthu chimodzi chachikulu chimene sindidzaiŵala. Alfredo anali kupitabe ku Misa yachikatolika Lamlungu lililonse, ndipo ankadana nazo zimene ndinali kuchita ndi Mboni za Yehova. Ndinamuyang’anitsitsa n’kunena mwachifatse koma molimba mtima kuti: ‘Alfredo, maganizo ako ndi osiyana ndi anga.’ Ndipo sanandimenye! Pasanapite nthaŵi yaitali ndinabatizidwa ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo patha zaka zisanu asanandimenye.”

Koma apa anali atangoyamba chabe kusintha. Alfredo analongosola kuti: “Patatha zaka zitatu Lourdes atabatizidwa, mnzanga wina wa m’gulu la Mboni za Yehova anandiitana kunyumba kwake, ndipo anandilongosolera zinthu zosangalatsa kwambiri zochokera m’Baibulo. Ndiye ndinayamba kuphunzira naye Baibulo koma mkazi wanga sindinamuuze. Posapita nthaŵi ndinayamba kutsagana naye mkazi wanga Lourdes ku misonkhano. Nkhani zambiri zimene ndinamva kumeneko zinali zokhudza banja, ndipo nthaŵi zambiri ndikamvetsera nkhanizi manyazi ankandigwira kwambiri.”

Alfredo anagoma kuona anthu amumpingo, ndi amuna omwe, akusesa misonkhano ikatha. Atapita kunyumba zawo, anakaona amuna akuthandiza akazi awo kutsuka mbale. Zinthu zazing’ono ngati zimenezi zinam’thandiza Alfredo kuona mmene chikondi chenicheni chimakhalira.

Posapita nthaŵi, Alfredo anabatizidwa ndipo panopa iye ndi mkazi wake akuchita ntchito ya utumiki wolalikira wa nthaŵi zonse. Lourdes anati “Nthaŵi zambiri amandithandiza kukonza patebulo tikamaliza kudya ndiponso kuyala pabedi. Amandiyamikira n’kaphika chakudya, ndipo amandilola kusankha zimene ndikufuna, monga nyimbo zimene ndikufuna kumvetsera komanso katundu wa m’nyumba amene tikufuna kugula. Likanakhala kale Alfredo sakanandilola n’komwe kutero! Posachedwapa, kwa nthaŵi yoyamba, anandigulirako maluŵa posonyeza kuti amandikonda. Nthaŵi zina ndimangoona ngati n’kutulo ndithu!”

[Chithunzi patsamba 10]

“Ndinazindikira kuti Mulungu ankandiona kuti ndine wofunika. Choncho ndinalimba mtima”

[Chithunzi patsamba 10]

Anaona amuna akuthandiza akazi awo kutsuka mbale

[Chithunzi patsamba 10]

Alfredo anagoma kuona anthu a mumpingo, ndi amuna omwe, akusesa misonkhano itatha

[Chithunzi patsamba 10]

“Posachedwapa, kwa nthaŵi yoyamba, anandigulirako maluŵa posonyeza kuti amandikonda”