Nyamakazi Ndi Matenda Opundula Anthu
Nyamakazi Ndi Matenda Opundula Anthu
“SIMUNGAMVETSE ULULU WA NYAMAKAZI NGATI SI INAKUGWIRENIPO. IMFA NDICHO CHINTHU CHOKHACHO CHIMENE NDINKAONA NGATI CHINGANDIPATSE MPUMULO.” ANATERO NDI SETSUKO WA KU JAPAN.
“NDIMAONA KUTI MATENDAŴA ANANDIWONONGERA UNYAMATA WANGA CHIFUKWA ANANDIYAMBA NDILI NDI ZAKA 16.” ANATERO NDI DARREN WA KU GREAT BRITAIN.
“ZAKA ZIŴIRI ZINATHERA PADERA M’MOYO WANGA CHIFUKWA CHONGOKHALA NDILI CHIGONERE.” ANATERO NDI KATIA WA KU ITALY.
“NDITAYAMBA KUMVA ULULU M’MFUNDO ZONSE ZA MAFUPA ANGA, MOYO NDINAYAMBA KUUMVA KUPWETEKA KWAMBIRI.” ANATERO NDI JOYCE WA KU SOUTH AFRICA.
AŴA ndi ena mwa madandaulo a anthu odwala matenda a nyamakazi. Anthu ambiri chaka n’chaka amapita kuchipatala kukafuna chithandizo chakuti matenda a nyamakazi asamawamvetse ululu, asawalepheretse kuyenda, komanso asawapundule.
Ku United States kokha, matendaŵa amagwira anthu oposa 42 miliyoni ndipo munthu m’modzi pa anthu asanu ndi m’modzi aliyense amene ali nawo matendaŵa amapunduka. Tingoti nyamakazi ndiyo imapundula anthu ambiri m’dzikolo. Bungwe la ku America loona za matenda lotchedwa National Centers for Disease Control and Prevention linanena kuti “matendaŵa akufanana ndi zinthu zina zimene zimawonongetsa chuma,” chifukwa chakuti anthu a ku America amawononga ndalama zokwana madola 64 biliyoni chaka chilichonse pogulira mankhwala a matendaŵa komanso polepheretsa anthu ambiri kugwira bwino ntchito yawo. Bungwe la World Health Organization linati atafufuza m’mayiko osatukuka kwenikweni, monga Brazil, Chile, China, India, Indonesia, Malaysia, Mexico, Pakistan, Philippines, ndi Thailand, anapeza kuti matenda osiyanasiyana a nyamakazi m’mayiko ameneŵa akuvutitsa anthu “mofanana ndi m’mayiko olemera.”
Si zoona kuti matenda a nyamakazi amagwira anthu achikulire okha. Inde, n’zoona kuti anthu akamakula m’pamene amadwaladwala matendaŵa kwambiri. Koma pali matenda ena okhalitsa a nyamakazi yofala kwambiri amene amagwira anthu ambiri a zaka 25 kapena mpaka 50. Ku United States, pafupifupi anthu atatu pa anthu asanu alionse odwala nyamakazi sanakwanitse zaka 65. Nakonso ku Great Britain, pa anthu 8 miliyoni amene akudwala matendaŵa, anthu oposa 1 miliyoni sanakwanitse zaka 45 ndipo anthu oposa 14,500 pa gululi ndi ana.
Chaka chilichonse, anthu ambiri amayamba kudwala nyamakazi. Ku Canada, m’zaka khumi zikubwerazi, anthu enanso okwana miliyoni adzayamba kudwala matendaŵa. Ngakhale kuti ku Ulaya kuli anthu ambiri odwala nyamakazi kusiyana ndi ku Africa ndiponso ku Asia, matendaŵa ayambanso kuchuluka m’mayikoŵa. Motero kuchuluka kwa matenda a nyamakazi kwachititsa kuti bungwe la World Health Organization likhazikitse zaka zoyambira 2000 mpaka 2010 monga zaka khumi zolimbana ndi matenda a mafupa ndiponso mfundo za mafupa. Panthaŵiyi madokotala ndiponso ogwira ntchito ya zaumoyo a padziko lonse agwirizana poyesa kuthandiza anthu odwala matenda ogwira minofu ndi mafupa, monga matenda a nyamakazi, kuti akhaleko bwino.
Kodi n’chiyani chimene chikudziŵika pa za matenda opwetekaŵa? Kodi ndani amene angadwale matendaŵa? Kodi anthu amene amadwala nyamakazi angathane nawo bwanji matenda opundulaŵa? Kodi m’tsogolo muno padzapezeka njira yowathetsera? Nkhani zimene zikubwerazi ziyankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
X ray: Taloledwa kugwiritsa ntchito chithunzichi ndi bungwe la Arthritis Research Campaign, United Kingdom (www.arc.org.uk)