Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Odwala Nyamakazi Asataye Mtima

Odwala Nyamakazi Asataye Mtima

Odwala Nyamakazi Asataye Mtima

“NYAMAKAZI si matenda amene amapha anthu ambiri monga amachitira matenda amtima kapena a kansa, koma amam’sautsa kwambiri munthu,” anatero Dr. Fatima Mili. Matenda a nyamakazi angasokoneze chilichonse chimene munthu amachita. Kodi ndi mavuto otani makamaka amene odwala nyamakazi amapezana nawo? Kodi angathe kulimbana nawo bwinobwino?

Katia, * amene ali ndi zaka 28 ndipo kwawo n’ku Italy anati: “Atandipeza ndi matenda a nyamakazi ndili ndi zaka 20, moyo wanga wonse unasinthiratu. Ndinakakamizika kusiya ntchito yanga ndiponso utumiki wa nthaŵi zonse chifukwa chomva ululu.” Anthu onse amene akudwala nyamakazi amamva ululu. Alan amene ali ndi zaka 63 ndipo kwawo n’ku England anati: “Nthaŵi zonse penapake pamaŵaŵa, ngakhale kuti nthaŵi zina si ukhala ululu waukulu.” Vuto linanso ndilo kutopatopa. Sarah, wa zaka 21 anati, “Ngakhale utazoloŵera kumangomva ululu ndiponso kutupatupa, umasoŵa mtendere kwambiri chifukwa cha kutopa.”

N’zopatsa Maganizo

Setsuko wa ku Japan, yemwe ali ndi zaka 61 anati munthu akamavutika ndi ululu wosatha tsiku n’tsiku, zingathenso “kum’patsa maganizo.” Ngakhale kugwira pensulo yeniyeniyi kapena telefoni kumatha kukhala kovuta kwambiri! Kazumi, yemwe ali ndi zaka 47 anadandaula motere: “Ndayamba kulephera kuchita zinthu zosavuta zimene ngakhale mwana angathe kuchita.” Janice, wa zaka 60 yemwe sangathenso kukhala ali chilili kapena kuyenda kwa nthaŵi yaitali anati: “Zimandikhudza kwambiri kuona kuti sindithanso kuchita zimene ndinkachita kale.”

Mavuto otere angam’foole munthu n’kuyamba kumadziganizira zinthu zoipa. Gaku amene ali ndi zaka 27 ndipo ali m’gulu la Mboni za Yehova anati: “Poti ndimakanika kuchita nawo bwinobwino ntchito ya kufalitsa uthenga wabwino kapena ntchito zina zakum’pingo, ndimaona kuti ndine munthu wopanda ntchito.” Francesca amene wakhala akudwala nyamakazi kuyambira ali ndi zaka ziŵiri, ananena kuti “wakhala akuvutika maganizo kwambiri chifukwa cha matendaŵa.” Maganizo otere angathe kum’sokoneza munthu kwambiri mwauzimu. Joyce, amene ali Mboni ku South Africa, anavomereza kuti anayamba kujomba kumisonkhano yachikristu. Iye anafotokoza kuti: “Sindinkafunanso kuonana ndi munthu aliyense.”

Wodwalayo angakhalenso ndi nkhaŵa zambiri zokhudza tsogolo lake, monga kuopa kuti sadzathanso kuyenda motero azidzangodalira ena, adzasoŵa munthu wom’samalira, angadzagwe n’kuthyoka mafupa, ndipo angamaopenso kuti sadzathanso kusamalira banja lake. Yoko ali ndi zaka 52 ndipo anavomereza kuti: “Ndinkati ndikaona pa mfundo inayake ya mafupa patayamba kuoneka chilema, ndinkaopa poganiza kuti papitirira kutero.”

Achibale angathenso kuvutika ndi maganizo chifukwa tsiku lililonse amaona mbale wawo wokondedwa akuvutika. Mabanja ena amayamba kusoŵa kwambiri mtendere wa m’banja. Mkazi wina ku England, dzina lake Denise, anati: “Nditakhala m’banja kwa zaka 15, mwamuna wanga ananenetsa poyera kuti, ‘Ndatopa nayo nyamakazi yako tsopano!’ Anandisiya ukwati n’kundisiyira mwana wamkazi wa zaka zisanu.”

Motero matenda a nyamakazi amabweretsa mavuto aakulu kwa odwala komanso mabanja awo. Komabe anthu ambiri akulimbana nawo matendaŵa bwinobwino! Tatiyeni tione mmene ena akuchitira zimenezi.

Osalimbana ndi Zinthu Zimene Simungathenso Kuchita

Kupuma mokwanira n’kofunika kwambiri ngati mukudwala nyamakazi, chifukwa kungathandize kuti musamatope kwambiri. Koma si kuti muyenera kusiiratu kuchita zinthu zina ndi zina. Timothy analongosola kuti: “Muyenera kumachita tintchito tosiyanasiyana kuti nyamakazi isakufooketseni maganizo, chifukwa ikakufooketsani, ndiye kuti muzingokhala n’kumangomverera ululuwo.” Katswiri wina wa nthenda ya nyamakazi, William Ginsburg yemwe ndi dokotala wa pa chipatala chotchedwa Mayo Clinic anati: “Pali kusiyana ndithu pakati pa kugwira ntchito kwambiri ndi kungokhala. Nthaŵi zina anthu otere ayenera kukumbutsidwa kuti azipumako ndi kuchita zinthu moganizira matenda awo.”

Zimenezi zikukhudza kusachita zinthu zimene mumaona kuti simungathenso kuzichita. Daphne, wa ku South Africa, anati: “Ndinayenera kuchita zinthu modziŵa kuti ndingathebe kuchita zinthu zinazake kungoti ndiyenera kuzichita mwapang’onopang’ono. M’malo moda nkhaŵa kapena kukhumudwa, ndimangochita zinthu zochepa n’kupuma kaye.”

Ndibwinonso kudziŵa bwino zida zosiyanasiyana zimene zingakuthandizeni, mwinanso kukambirana ndi dokotala wanu za nkhaniyi. Keiko analongosola kuti: “M’nyumba mwathu tinaika chikepe chokwerera m’mwamba ndi kutsikira pansi. Ndikamatsegula zitseko za m’nyumba mwathu mikono yanga inkawawa kwambiri motero tinasintha zotsegulira zake. Tsopano ndimatha kutsegula zitseko zonse pozikankha ndi mutu. Mipopi yonse ya m’nyumba mwathu tinaiikira zotsegulira zosavuta potsegula kuti ndizitha kuchita nawo ntchito zina ndi zina zapanyumba.” Munthu wina wodwala nyamakazi dzina lake Gail anati: “Makiyi a galimoto ndiponso a nyumba yanga anawamamatiza ku chogwirira chachitali, motero ndimatha kuwagwiritsa ntchito mosavuta. Zipeso zanga anazilumikiza kuzinthu zazitali ndipo zimatheka kuzipendeketsera mbali iliyonse popesa.”

Anthu a M’banjalo Akamathandiza “Zimalimbikitsa Kwambiri”

Carla, wa ku Brazil, anati: “Mwamuna wanga wakhala akundithandiza kwambiri. Chifukwa chakuti ankandiperekeza popita kuchipatala, ndinalimba mtima. Tinadziŵira pamodzi zimene matendaŵa akundichita m’thupi mwanga, zizindikiro zake, ndiponso mankhwala ake oyenerera. Ndinkapezako bwino chifukwa chakuti iye ankamvetsa kuti ndikuvutika kwambiri.” Indedi, anthu amene amazindikira kuti amuna kapena akazi awo sangakwanitse kuchita zinthu zina ndiponso amene amafunadi kudziŵa bwino matendawo angalimbikitse kwambiri wodwalayo.

Mwachitsanzo, matenda a nyamakazi atam’lepheretsa mwamuna wake kupitiriza kugwira ntchito yake ya zomangamanga Bette anayamba ntchito yokonza m’nyumba. Mwamuna wa Kazumi ankayang’anira mkazi wake pamene ankadwala komanso ankachita ntchito za pakhomo zimene mkaziyo sakanatha kuzichita. Komanso anaphunzitsa ana awo kuthandizapo pa ntchito zina zimene akanatha. Kazumi anati: “Mwamuna wanga wakhala akundilimbikitsa kwambiri. Chipanda iye kundithandiza bwenzi matenda anga atakula kwambiri.”

Mkazi wina wotchedwa Carol, wa ku Australia, ananena mawu ochenjeza aŵa: “Samalani kuti musamachulutse zinthu zimene mukufuna kuchita. Ndikalephera kuchita nawo zinthu zimene a m’banja mwanga amachita sindichedwa kuganiza kuti ndine wopanda ntchito.” Ngati zili zochokeradi pansi pamtima ndiponso ngati zikuchitidwa moganizirana, ndiye kuti a m’banja angakhale anthu olimbikitsadi odwalawo.

Kuthandiza Mwauzimu

Katia anati: “Munthu akadwala matenda ngati ameneŵa, amakhulupirira kuti palibenso aliyense amene akudziŵa mmene akumvera. Motero m’pofunika kwambiri kuganizira Yehova Mulungu, podziŵa kuti iye amamvetsetsadi mmene tikumvera m’thupi ndiponso m’maganizo. (Salmo 31:7) Chifukwa chakuti iyeyo ndi mnzanga, ndili ndi mtendere m’maganizo mwanga umene umandithandiza kusaganiza zambiri chifukwa cha matenda angaŵa.” Baibulo limanenadi molondola kuti Yehova ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Motero pemphero lingam’limbikitse kwambiri munthu amene akumva ululu wosatha. Kazumi anasimba kuti: “Nthaŵi zina ndikamalephera kugona usiku wonse chifukwa cha ululu, ndimapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pamtima misozi ili m’maso ndipo ndima’mpempha kuti andilimbikitse kuti ndithe kupirira ululuwu ndiponso kuti ndikhale ndi nzeru zondithandiza kuthana ndi mavuto anga onse. Yehova wandiyankhadi.” Nayenso Francesca waona thandizo la Mulungu lachikondi. Iye anati: “Ndaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Afilipi 4:13 akuti: ‘Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.’”

Nthaŵi zambiri, Yehova Mulungu amathandiza anthu pogwiritsa ntchito mpingo wachikristu. Mwachitsanzo Gail, anasimba za mmene anathandizidwira ndi abale ndi alongo a mumpingo wake wa Mboni za Yehova. Iye anati: “Chikondi chawo chinandithandiza kuti ndisavutike maganizo.” Chimodzimodzinso, Keiko atam’funsa kuti “Kodi pali chinthu chabwino chilichonse chimene ungathe kukumbukira m’moyo wako?,” iye anayankha kuti: “Inde, n’chikondi ndiponso chifundo chimene anthu onse a mumpingo amandichitira!”

Mumipingo ya Mboni za Yehova, akulu ndiwo amatsogolera pothandiza m’njira imeneyi. Setsuko anati: “Sindikudziŵa kuti ndingalongosole bwanji mmene munthu wodwala kwambiri amamvera akulu akamam’mvera mavuto ake ndi kum’limbikitsa.” Komabe Daniel amene akudwala nyamakazi anati tisaiwale kuti, “abale ndi alongo athu auzimu angatithandize kokha ngati titawalola kuti atero.” Motero m’pofunika kwambiri kuti odwala asamatalikirane ndi Akristu anzawo poyesetsa kufika kumisonkhano ya mpingo. (Ahebri 10:24, 25) Kumeneko angathe kukalimbikitsidwa mwauzimu kuti athe kupirira.

Kuvutika Kudzatha

Odwala nyamakazi amathokoza a zachipatala chifukwa chopeza njira zotsogola zothandiza odwalawo. Komabe, ngakhale mankhwala apamwamba kwambiri samachiritsiratu matendaŵa. Motero chimene chingawalimbitse mtima kwambiri odwalaŵa ndicho kukhulupirira lonjezo la Mulungu la dziko latsopano. * (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4) M’dziko limenelo “wopunduka adzatumpha ngati nswala.” (Yesaya 35:6) Matenda a nyamakazi ndiponso matenda ena onse amene akuvutitsa anthu adzatheratu mpaka kalekale! Ndiye chifukwa chake Peter, amene akudwala nyamakazi yamsana, anati: “Ndikuona kuti ngakhale ndikuvutika chonchi, palibe chifukwa chotayira mtima.” Mayi wina wachikristu dzina lake Giuliana ananenanso chimodzimodzi kuti: “Tsiku lililonse likatha ndimaona kuti ndapambana chifukwa ndiye kuti ndapungulapo masiku amene ndiyenera kuvutika chimaliziro chisanabwere!” Inde, nthaŵi yayandikira yoti nyamakazi ndiponso kuvutika kulikonse kudzatheretu!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.

^ ndime 24 Ngati mungakonde kuti munthu wina wam’gulu la Mboni za Yehova adzakuchezereni n’kudzakulongosolerani malonjezo a m’Baibulo, kafunseni kumpingo wa Mboni za Yehova wa kumene mukukhala kapena lemberani kalata kwa ofalitsa magazini ino.

[Chithunzi patsamba 10]

Pali zida zosiyanasiyana zothandiza odwala kumachita zinthu zowapindulitsa m’moyo

[Chithunzi patsamba 12]

Mungathandizidwe mwachikondi kumisonkhano yachikristu