Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chakudya Chanu N’chosakayikitsa?

Kodi Chakudya Chanu N’chosakayikitsa?

Kodi Chakudya Chanu N’chosakayikitsa?

KODI mumadya katatu patsiku? Ngati mumatero ndiye kuti mukadzakwanitsa zaka 70, mudzakhala mutadya mopitirira ka 75,000. Nzika yeniyeni ya ku Ulaya ndiye kuti mwa zina, idzakhala itadya mazira okwana 10,000, buledi wokwana 5,000, matumba a mbatata okwana 100, ng’ombe zitatu ndiponso nkhosa ziŵiri. Kodi tingati kudya zonsezo n’chintchito chachikulu? Ayi ndithu! Chifukwa timakondwa tikamva wina akuti “yandikirani kutebuloko” kapena kuti “kalibu”! Mphunzitsi wamkulu pa sukulu ina ya zophikaphika anafika mpaka ponena kuti: “Chakudya n’chinthu chofunika kwambiri m’moyo.”

Nthaŵi zambiri timatayirira n’kumaganiza kuti chakudya chonse chimene timadya n’chosakayikitsa ndiponso n’chopatsa thanzi. Komatu ngati tinadya chakudya choipa kamodzi kokha pa nthaŵi 75,000 zija, tikhoza kudwala kwambiri. Kodi tingakhale otsimikiza kuti chakudya chimene timadya chilibe zinthu zina zoipa? Masiku ano anthu ambiri akuoneka kuti akukayikira ngati amadya chakudya chopanda zinthu zina zoipa. M’mayiko ena anthu ambiri ayamba kuda nkhaŵa poganiza kuti mwina chakudya chawo n’chokayikitsa. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Zifukwa Zake

Chaka chilichonse, anthu a ku Ulaya okwana 15 pa 100 alionse amadwala matenda owatenga ku chakudya. Mwachitsanzo m’dziko la Spain, kumayambiriro kwa m’ma 1980 mafuta ophikira a poizoni anapha anthu okwana 1,000 ndipo anthu ena okwana 20,000 anadwala kwambiri chifukwa cha mafutawo. Mu 1999 anthu a ku Belgium anachita mantha atamva kuti n’kutheka kuti zinthu monga mazira, tchizi ndiponso sitoko zinali ndi poizoni. Chaposachedwapa anthu ogula malonda a ku Britain anakhumudwa, ndipo misika yawo ya nyama ya ng’ombe anaiphwasula pamene ng’ombe zinagwidwa ndi matenda a misala. Kenaka kunagwanso matenda a chigodola amene anachititsa kuti anthu aphe n’kutaya ng’ombe, nkhosa, nkhumba ndiponso mbuzi zochuluka zedi.

Ngakhale kuti zinthu zimenezi n’zoopsa, pali zinthu zinanso zimene anthu akuda nazo nkhaŵa pankhani ya chakudya. Anthu akudandaula chifukwa cha umisiri watsopano umene akuugwiritsa ntchito paulimi ndiponso pokonza zakudya. Mu 1998 bungwe la The European Commission linalemba kuti: “Zinthu zaumisiri wamakono monga kuumika zakudya ndi moto wamphamvu ya magetsi ndiponso kusintha chibadwa cha mbewu zapangitsa kuti anthu akangane kwambiri.” Kodi njira za sayansi zamakonozi zimakonza chakudya chathu kuti chikhale chabwino kapena zimangochiipitsa? Nanga tingatani kuti chakudya chathu chikhale chosakayikitsa?