Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudalira Mulungu Kunandilimbitsa

Kudalira Mulungu Kunandilimbitsa

Kudalira Mulungu Kunandilimbitsa

YOSIMBIDWA NDI RACHEL SACKSIONI-LEVEE

PAMENE MSILIKALI WINA WOTILONDERA ANALI KUNDIMENYA KUMASO MOSALEKEZA CHIFUKWA CHOKANA KUGWIRA NAWO NTCHITO YOPANGA ZIPANGIZO ZA NDEGE ZOPONYA MABOMBA ZA CHIPANI CHA NAZI, MSILIKALI MNZAKE ANAMUUZA KUTI: “IWE, INGOMULEKA AMENEYO. OPHUNZIRA BAIBULO AMENEŴA AMALOLERA KUWAMENYA MPAKA KUFA CHIFUKWA CHA MULUNGU WAWO.”

ZIMENEZI zinachitika mwezi wa December m’chaka cha 1944 ku Beendorff, komwe kunali kampu yozunzira azimayi kufupi ndi migodi ya mchere cha kumpoto kwa dziko la Germany. Taimani ndikuuzeni mmene ndinapezekera kumeneko ndiponso mmene ndinapulumukira patangotsala miyezi yochepa kuti nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse ithe.

Ndinabadwira m’banja la Chiyuda mumzinda wa Amsterdam, ku Netherlands, m’chaka cha 1908 ndipo ndine wachiŵiri kubadwa pa atsikana okhaokha atatu. Bambo anga ankagwira ntchito yosalaza miyala ya diamondi, ntchito imene Ayuda ambiri ku Amsterdam anali kugwira nkhondo ya padziko lonse yachiŵiri isanaulike. Iwo anamwalira ndili ndi zaka 12, ndipo zitatero agogo aamuna anadzakhala nafe. Agogowo anali m’Yuda weniweni wosam’suntha wamba, ndipo ankaonetsetsa kuti tikutsatiradi miyambo yonse yachiyuda.

Potsatira luso la ababa, ndinaphunzira ntchito yawo yosalaza miyala ya diamondi ndipo m’chaka cha 1930, ndinakwatiwa ndi munthu wina wa ntchito yomweyo. Tinabereka ana aŵiri. Woyamba dzina lake anali Silvain, yemwe anali mnyamata wochangamuka ndiponso wokonda kudziŵa zinthu zatsopano ndipo winayo anali Carry, yemwe anali kamtsikana kabwino kwambiri, komanso ka phee. Tsoka ilo, mwamunayu sindinakhale naye m’banja kwa nthaŵi yaitali. M’chaka cha 1938 titangosudzulana kumene, ndinakwatiwanso ndi Louis Sackisioni, yemwe nayenso anali kugwira ntchito yosalaza miyala ya diamondi. M’mwezi wa February chaka cha 1940, mwana wathu wamkazi dzina lake Johanna anabadwa.

Ngakhale kuti Louis anali Myuda sankatsatira zochita za chipembedzo chakecho. Choncho sitinkakondwereranso mapwando a Chiyuda amene ndinkawakonda kwambiri ndili mwana. Ndinkawalakalaka kwambiri mapwandowo, koma ndinapitiriza kukhulupirira Mulungu mumtima mwanga.

Mmene Ndinasinthira Chipembedzo

Cha kumayambiriro kwa m’ma 1940, chaka chimene anthu a ku Germany anayamba kulanda dziko la Netherlands, mkazi wina anafika pakhomo pathu n’kukambirana nane za m’Baibulo. Sindinamvetsetse zinthu zambiri zimene ananena, koma ndinkalandira mabuku amene ankandipatsa nthaŵi iliyonse akandiyendera. Komabe, sindinkaŵerenga mabuku amene ankasiyawo chifukwa chakuti sindinkafuna kumva chinthu chilichonse chokhudza Yesu. Ndinali nditaphunzitsidwa kuti Yesu anali Myuda wopanduka.

Kenaka tsiku lina pakhomo panga panafika bambo winawake. Ndinam’funsa mafunso onga akuti: “Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu sanalenge anthu ena Adamu ndi Hava atachimwa? N’chifukwa chiyani anthu akuvutika kwambiri chonchi? N’chifukwa chiyani anthu amadana komanso kuyambitsa nkhondo?” Ananditsimikizira kuti ngati nditafatsa, iye atha kundiyankha kuchokera m’Baibulo. Choncho tinakonza zoyamba phunziro la Baibulo lapanyumba.

Komabe, sindinamvere zakuti Yesu anali Mesiya. Koma posakhalitsa, nditapemphera kuti ndimvetse nkhaniyi, ndinayamba kuŵerenga maulosi a Mesiya m’Baibulo, mosaganizira zimene ndinali kudziŵa kale. (Salmo 22:7, 8, 18; Yesaya 53:1-12) Yehova anandithandiza kuona kuti maulosi amenewo anakwaniritsidwa pa Yesu. Mwamuna wanga analibe nazo ntchito zimene ndinali kuphunzira, komabe sanandiletse kuti ndikhale m’gulu la Mboni za Yehova.

Ndinkalalikirabe Ngakhale Kuti Ndimakhala Mobisala

Nthaŵi imene dziko la Germany linalanda dziko la Netherlands inali yoopsa kwambiri kwa ine, chifukwa chakuti ndinali Myuda, mtundu umene anthu a ku Germany ankaugwira n’kuuika m’misasa yachibalo, komanso ndinali m’gulu la Mboni za Yehova, lomwe linali gulu la chipembedzo chimene chipani cha Nazi chinkayesetsa kuchithetseratu. Komabe ndinalimbikira, ndipo ndinkalalikira kwa maola 60 mwezi uliwonse pouza anthu ena za chiyembekezo chachikristu chatsopano chimene ndinali nditapeza.—Mateyu 24:14.

Tsiku lina madzulo mwezi wa December, m’chaka cha 1942, mwamuna wanga sanabwerere kunyumba kuchokera kuntchito. Ndinadzazindikira pambuyo pake kuti anali atam’manga kuntchito pamodzi ndi anzake. Sindinadzamuonenso. Mboni zinzanga zinandilangiza kuti ndipite kukabisala ndi ana anga. Ndinakakhala ndi mlongo wina wachikristu kudera lina la mzinda wa Amsterdam. Chifukwa chakuti kunali koopsa kuti tonse anayi tizikhala malo amodzi, ana anga ndinawasiya ndi anthu ena.

Nthaŵi zambiri ndinkangopulumukira mkamwa mwambuzi. Tsiku lina usiku mboni ina inkandipititsa kumalo ena okabisalako panjinga yake. Koma getsi la njinga yakeyo silinkayaka, ndipo apolisi aŵiri a Chidatchi anatiimitsa. Anandiunika kumaso ndi nyali zawo zoyaka mothobwa m’maso ndipo anazindikira kuti ndine Myuda. Mwayi wake, anangoti: “Pitirizani ulendo wanu mofulumira, koma muyende wapansi.”

Anandigwira Ndipo Ananditsekera

Tsiku lina mmaŵa m’chaka cha 1944 nditangotsala pang’ono kuti ndiyambe kulalikira, anandigwira, osati chifukwa chakuti ndinali Mboni ayi koma chifukwa chakuti ndinali Myuda. Anapita nane kundende ina ya mumzinda wa Amsterdam, komwe ndinakhalako kwa masiku khumi. Kenaka anandikweza sitima ya pamtunda pamodzi ndi Ayuda ena kupita kukampu yongoyembekezera ya Westerbork cha kumpoto koma kummaŵa kwa dziko la Netherlands. Akachoka nawo kumeneko Ayudawo ankawapititsa ku Germany.

Ku Westerbork n’kumene ndinakumana ndi mlamu wanga wamwamuna pamodzi ndi mwana wake wamwamuna, omwe nawonso anali atawagwira. Pakati pa Ayuda onsewo Mboni ndinali ndekha ndipo ndinalimbikira kupemphera kwa Yehova kuti andilimbitse. Patapita masiku aŵiri ine ndi mlamu wanga pamodzi ndi mwana wake uja, tinakwera m’sitima ya pamtunda yonyamula ng’ombe imene inangotsala pang’ono kuuyamba ulendo wopita ku Auschwitz kapena ku Sobibor, yomwe inali misasa yopherako anthu ya ku Poland. Mwadzidzidzi, ndinangomva dzina langa ndipo ananditenga n’kukakwera sitima ina, yomwe nthaŵi zonse imanyamula anthu.

Anthu amene anali mmenemo anali anzanga akale amene ndinkagwira nawo ntchito yamiyala ya diamondi. Anthu okwana mwina 100 amene anali kugwira ntchito ya diamondi anali kuwapititsa ku Bergen-Belsen cha kumpoto kwa dziko la Germany. Kenaka ndinadzazindikira kuti ntchito yanga inandipulumutsa, chifukwa chakuti Ayuda amene anapita ku Auschwitz ndiponso ku Sobibor ankangofikira kunyumba zimene ankapheramo anthu ndi mpweya wa gasi. N’zimene anamuchita mwamuna wanga, ana anga aŵiri ndiponso achibale anga ena. Koma panthaŵi imeneyo, sindinadziŵe kuti n’chiyani chinawachitikira.

Titafika ku Bergen-Belsen ife amene tinkaphwanya miyala ya diamondi anali kutisunga kunyumba zinazake zapadera zosaoneka bwino. Pofuna kuti tipumitse manja athu pa ntchito yathuyo imene inkafunika kusamala kwambiri, sitinkagwiranso ntchito ina. Mboni ndinali ine ndekha pagulu lathu ndipo ndinkawauza molimba mtima Ayuda anzanga za chikhulupiriro changa chatsopano. Koma iwo ankandiona ngati munthu wopanduka, kungokhala ngati mmene anthu ena a m’zaka za zana loyamba ankamuonera mtumwi Paulo.

Ndinalibe Baibulo, ndipo ndinkalakalaka kwambiri nditapeza chakudya chauzimu. Dokotala wina wachiyuda pakampupo anali nalo Baibulo, ndipo anandipatsa nditasinthana naye ndi mapisi angapo a buledi ndiponso sitoko. Ndinakhala pamodzi ndi ‘gulu la diamondi’ limeneli kwa miyezi isanu ndi iŵiri tili ku Bergen-Belsen. Ifeyo ankatikhazikako bwino ndithu ndipo zimenezi zimatipangitsa kudedwa ndi akaidi anzathu achiyuda. Komabe pamapeto pake, panapezeka kuti miyala ya diamondi yonse imene inkatipatsa ntchito yatha. Choncho pa December 5 m’chaka cha 1944, mwina akazi okwana 70 pagulu lathu anatitumiza kukagwira ntchito kukampu ya azimayi ku Beendorff.

Ndinakana Kupanga Zida Zankhondo

Akaidi ankawapatsa ntchito yopanga zipangizo za ndege zoponya mabomba m’migodi yozama pafupifupi mamita 400, imene inali pafupi ndi kampuyo. Nditakana kugwira ntchito imeneyi, anandikang’antha nazo zibakera. (Yesaya 2:4) Msilikaliyo analirima ponena kuti ngati ndikufuna kuti zindiyendere bwino, ndiyenera kukhala wokonzeka kudzagwira ntchitoyo tsiku lotsatira.

Tsiku lotsatira mmaŵa sindinakaonekere panthaŵi yoitana mayina a amene abwera kuntchito, koma ndinangokhala m’nyumba zimene tinkagonamo. Ndinali wotsimikiza kuti basi andiwombera, choncho ndinapemphera kuti Yehova adzandifupe chifukwa cha chikhulupiriro changa. Ndinkangobwerezabwereza kutchula mumtima mwanga salmo la m’Baibulo lakuti: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa; munthu adzandichitanji?”—Salmo 56:11.

Anafufuza m’nyumba zonse zogonamo, ndipo anandisokolotsa. M’pamene msilikali wina anandimenya mosalekeza, kwinaku akufunsa kuti: “Ndani amene sakulola kuti ugwire ntchito imeneyi?” Nthaŵi iliyonse, ndinkangoyankha chimodzimodzi kuti ndi Mulungu. Apa m’pamene msilikali mnzake anamuuza mzimayiyu kuti: “Iwe, ingomuleka ameneyo. Ophunzira Baibulo * amenewo amalolera kuwamenya mpaka kufa chifukwa cha Mulungu wawo.” Mawu akewo anandilimbikitsa kwambiri.

Pakuti kutsuka m’zimbudzi inali ntchito imene anthu anali kupatsidwa powalanga ndipo inali ntchito yonyansa kwambiri imene sindinkaifuna ngakhale pang’ono, ndinadzipereka kuti ndizigwira ntchito imeneyo. Ndinali wokondwa kulandira ntchito imeneyo chifukwa chakuti inali ntchito imene ndikanatha kugwira popanda kuvutika ndi chikumbumtima. Tsiku lina mmaŵa mkulu wa pakampupo amene anthu onse ankamuopa anatulukira. Anaima patsogolo panga n’kufunsa kuti: “Iwe ndiwe Myuda amene ukukana kugwira ntchito, eti?”

“Mwaona nokha kuti ndikugwira ntchito pano,” ndinam’yankha choncho.

“Koma ikakhala ntchito yokhudza nkhondo sungagwire, eti?”

“Ayi sindingagwire. Mulungu safuna zimenezo,” ndinayankhanso.

“Koma kodi ukapanga nawo zidazo ndiye kuti ukupha nawo?”

Ndinam’longosolera kuti ngati nditapanga nawo zida zankhondo, ndiye kuti chikumbumtima changa chachikristu chindivuta.

Anatenga tsache langa n’kunena kuti: “Ndikhoza kukupha ndi tsacheli, ukutsutsa kapena?”

“Ayi sindingatsutse n’komwe. Kungoti tsache sanalipange kuti lizigwira ntchito imeneyo koma mfuti.”

Tinakambirana zakuti Yesu anali Myuda ndiponso kuti ngakhale kuti poyamba ineyo ndinali m’chipembedzo chachiyuda, ndinaloŵa m’gulu la Mboni za Yehova. Atachoka, akaidi anzanga anabwera ali odabwa kuti ndinalimba mtima kulankhulana ndi mkulu wa pakampupo mosatutumuka ndi chilichonse. Ndinawauza kuti siinali nkhani ya kungolimba mtima basi koma kuti zinatheka kutero chifukwa chakuti Mulungu wanga anali atandipatsa mphamvu yakuti nditero.

Ndinapulumuka Mpaka Nkhondoyo Inatha

Pa April 10, 1945, pamene magulu ankhondo ogwirizana ankafika ku Beendorff, panthaŵi yoitana mayina a amene abwera kuntchito tinangoima pabwalo pafupifupi kwa tsiku lonse. Kenaka mwina azimayi okwana 150 anatipanikiza m’sitima zapamtunda zonyamula ng’ombe, koma popanda chakudya kapena madzi. Sitimazo zinanyamuka ulendo wopita komwe sitinkakudziŵa, ndipo tinkangopita uku ndi uku pakati pa magulu a asilikali ankhondo oopsa. Ena ankapha akaidi anzawo powapotola makosi n’cholinga chakuti apeze malo okhalako motakasuka m’mabogimo ndipo mapeto ake, azimayi ambiri anazungulira mitu. Chimene chinandithandiza kupirira chinali kudalira kuti Yehova andisamala.

“Tsiku lina sitima yathu inaima pafupi ndi kampu ya amuna ndipo anatilola kutsika. Ena ochepa mwa azimayife anatipatsa ndowa kuti tikatunge madzi kukampuyo. Nditafika pampope, ndinayamba kaye ndamwa madzi ambiri kenaka n’kudzazitsa ndowa yanga. Nditabwerako, azimayiwo anandikanganira ngati nyama zakutchire ponjenjemerera madziwo. Madzi onse amene anali m’ndowamo anawataya polimbirana. Mmodzi wa apolisi amphamvu a Hitler amene ankawatcha kuti ma SS anangoima poteropo n’kumangoseka. Patatha masiku 11, tinakafika kukampu ina yotchedwa Eidelstedt imene inali kunja kwa mzinda wa Hamburg. Pafupifupi theka la anthu a pagulu lathu anali atamwalira chifukwa cha mavuto a paulendowo.

Tsiku lina tili ku Eidelstedt, ndinkaŵerengera Baibulo azimayi ena angapo. Tinangozindikira kuti mkulu wa pakampupo ali chilili pawindo. Tinasoŵa poloŵa chifukwa cha mantha popeza kuti Baibulo linali buku loletsedwa pakampupo. Mkuluyo analoŵa n’kutenga Baibulolo n’kungoti: “Limeneli ndi Baibulo, eti?” Ndinakhazika mtima pansi pamene anandibwezera Baibulolo n’kunena kuti: “Ngati mayi wina atamwalira, ndiye uyenera kuŵerenga mawu enaake kuchokera mmenemu mwakuti aliyense amve.”

Kukumananso Ndi Mboni Zinzanga

Patatha masiku 14 atatimasula, bungwe la Red Cross linatipititsa kusukulu yapafupi ndi mzinda wa Malmö, m’dziko la Sweden. Tili kumeneko, anatikhazika kwatokha kwa kanthaŵi ndithu. Ndinafunsa mkazi wina amene anali m’gulu la anthu otithandiza ngati akanatha kuuza Mboni za Yehova kuti ndikukhala kumene kuli anthu othaŵa kwawo. Patapita masiku angapo, ndinamva wina akuitana dzina langa. Nditamuuza mzimayi amene ankandifunayo kuti ndinali Mboni, anayamba kusisima. Nayenso anali Mboni! Mtima wake utakhala mmalo, anandiuza kuti nthaŵi zonse Mboni za Yehova m’dziko la Sweden zinkapempherera abale ndi alongo awo achikristu amene anali m’misasa yachibalo ya chipani cha Nazi.

Kungoyambira tsiku limenelo kupita m’tsogolo, kunkabwera mlongo amene ankandibweretsera khofi ndi kena kake kotsitsira tsiku lililonse. Nditachoka pamalo a anthu othaŵa kwawopo, ananditumiza kwinakwake kufupi ndi mzinda wa Göteborg. Nditafika kumeneko, Mboni zinakonza kaphwando kapamwamba chakumadzulo kondilandirira. Ngakhale kuti sindinkatha kumvana nawo, zinali zonyaditsa kwambiri kukhalanso pakati pa abale ndi alongo anga.

Ndili ku Göteborg, ndinalandira kalata yochokera kwa Mboni ina ku Amsterdam yondidziŵitsa kuti ana anga Silvain ndi Carry ndiponso achibale anga onse anagwidwa ndipo sanabwererenso. Amene anapulumuka anali mwana wanga wamkazi dzina lake Johanna ndi mchemwali wanga wachitsirizira basi. Chaposachedwa mpamene ndaona maina a ana anga, wamwamuna ndi wamkazi m’kaundula wa Ayuda amene anawaikira poizoni m’misasa ya Auschwitz ndiponso Sobibor.

Zochitika Nkhondo Itatha

Ndinabwerera ku Amsterdam ndipo ndinakumananso ndi Johanna, yemwe tsopano anali ndi zaka zisanu ndipo sindinachedwe kuyambiranso kulalikira. Nthaŵi zina ndinali kukumana ndi anthu amene anali m’gulu la NSB lomwe linali gulu la ndale la a Datchi limene linkagwirizana ndi anthu a ku Germany. Anthuŵa anathandiza nawo kupha mwakhanza pafupifupi anthu onse a m’banja langa. Pofuna kuwalalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndinkachita kudziletsa kuti ndisaipidwe nawo. Ndinkaganizira kuti Yehova ndiye amaona mtima ndiponso kuti pamapeto pake iye ndi amene amaweruza anthu, osati ineyo ayi. Ndipo chifukwa chokhala ndi maganizo ameneŵa ndinadalitsidwa kwambiri!

Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi mkazi wina amene mwamuna wake anali m’ndende chifukwa chogwirizana ndi chipani cha Nazi. Ndikamakwera masitepesi opitira kunyumba yawo, ndinkamva anthu oyandikana nawo akuti: “Tamuoneni Myuda uja, akukachezanso ndi anthu oipa aja a gulu la NSB!” Koma ngakhale kuti mwamuna wamkaziyu yemwe ankadana kwambiri ndi Ayuda ankamuletsa kwambiri kutero, mkaziyu pamodzi ndi ana ake aakazi atatu anakhala Mboni za Yehova onse.

Ndinasangalala kwambiri pambuyo pake pamene mwana wanga wamkazi Johanna anapereka moyo wake kwa Yehova. Iyeyo pamodzi ndi ine tinapita kukatumikira kumene kunkafunika kwambiri anthu olengeza Ufumu. Tinalandira madalitso auzimu ambiri. Panopa ndikukhala m’tauni inayake yaing’ono cha kum’mwera kwa dziko la Netherlands, kumene ndimagwira nawo ntchito yolalikira limodzi ndi mpingo nthaŵi iliyonse yomwe ndingathe kutero. Ndikakumbukira kale langa, chimene ndinganene n’chakuti sindinaganizepo zakuti Yehova wanditaya. Nthaŵi zonse ndakhala ndikuganiza kuti Yehova ndiponso Mwana wake wokondedwa, Yesu ali nane ngakhale m’mavuto otani.

Nthaŵi ya nkhondo, mwamuna wanga, ana anga aŵiri ndiponso achibale anga ambiri anamwalira. Koma ndimakhulupirira kuti ndidzawaonanso m’dziko latsopano la Mulungu. Ndikakhala ndekha n’kumakumbukira zomwe zinandichitikira, ndimaganizira mwachimwemwe ndiponso mokondwa mawu a wamasalmo akuti: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.”—Salmo 34:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Mboni za Yehova kale ankazitchula choncho.

[Chithunzi patsamba 24]

Ayuda akuwapititsa ku Germany kuchokera kukampu ya ku Westerbork

[Mawu a Chithunzi]

Herinneringscentrum kamp Westerbork

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi ana anga Carry ndi Silvain omwe anaphedwa onse ndi chipani cha Nazi

[Chithunzi patsamba 26]

Atatisunga kwatokha ku Sweden

[Chithunzi patsamba 26]

Khadi loyembekezera londivomereza kubwerera kwathu

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili ndi mwana wanga Johanna panopa