Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Aliyense Adzakhala Nacho Chakudya Chosakayikitsa

Munthu Aliyense Adzakhala Nacho Chakudya Chosakayikitsa

Munthu Aliyense Adzakhala Nacho Chakudya Chosakayikitsa

KUDYA chakudya chopatsa thanzi n’kosangalatsa. Koma monga taonera, nthaŵi zambiri kumakhala kovuta kupeza chakudya chotere. Ndipo chomvetsa chisoni kwambiri n’chakuti pali anthu ambiri amene sangakwanitse kuganizira zopeza chakudya chosakayikitsa n’komwe kapena chopatsadi thanzi mwakuti amangodya chakudya chilichonse. Iwo amangoganiza zopeza chakudya chokwanira kungoti akhale ndi moyo basi. Kodi tingati Mulungu anafuna kuti zinthu zikhale motere?

Taganizirani izi. Kodi pamene Mulungu anaika mwamuna ndi mkazi padziko lapansi, panali chinthu china chilichonse chowapangitsa anthu kudera nkhaŵa za chakudya? Ayi ndithu, panalibiretu ngakhale n’chimodzi chomwe! Nkhani ya m’Baibulo m’buku la Genesis imati: “Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.” (Genesis 2:9) Choncho Adamu ndi Hava anali ndi mitundu yosiyanasiyana ya zakudya zokoma komanso inali yambiri ndipo yosatha. Mulungu amene anawalenga ankadziŵa bwinobwino zinthu zopatsa thanzi zimene iwo akanafunikira; ndiponso ankadziŵa zinthu zimene zikanawakondweretsa. Inde n’zoona kuti ifeyo panopa sitili m’munda wa Edene. Koma kodi Mulungu wasintha cholinga chake choyamba chimene anapangira anthu ndi dziko lapansi?

Tili ndi chifukwa choyenera chokhulupirira kuti posachedwapa munthu aliyense padziko lapansi adzakhala ndi thanzi labwino ndiponso chakudya chopatsa thanzi chochuluka! Kukhulupirira zimenezi kungatithandize kwambiri panopo kuona nkhani yokhala ndi chakudya chokwanira m’njira yoyenera. Ngati tikutsimikiza ndiponso kukhulupiriradi zimenezi, zingatithandize kupeŵa kuyamba kukhala anthu oona zinthu monyanyira.

Kodi n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kwambiri kuti posachedwapa moyo usintha? Anthu amene amakonda kwambiri kuphunzira Mawu a Mulungu akudziŵa kuti panopa tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a nthaŵi ino. Pakalipano dziko likuyendetsedwa ndi nzeru za anthu, zimene zili zosatsimikizika ndiponso zongodalira kuyesa pofuna kuchita zinthu zosiyanasiyana. Tikanena nkhani ya zaumisiri wokonza zakudya, anthu akukayikira ndithu kuti kaya umisiriwo n’ngwabwino kapena n’ngoopsa. Kukayikira kotereku kumabweretsa mantha ndiponso kusagwirizana.—2 Timoteo 3:1-5.

Mlengi wa anthu onse walonjeza kuti adzachotseratu zinthu za m’nthaŵi inozi ndipo m’malo mwake adzabweretsa zina zatsopano. Iye adzakwaniritsa cholinga chake cha poyamba chakuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso ngati munda wa Edene, ndipo kuti mukhale anthu athanzi. Kenaka nzeru ya Mulungu imene ili yogwirizanitsa anthu idzadzaza dziko lonse lapansi. (Yesaya 11:9) Nzeru zokayikitsa za anthu sizidzakhalakonso. Dziko latsopano limene Mulungu adzapanga lidzakhala loti anthu sadzafunikanso kukayikira ngati chakudya chili chabwino. Kodi sizomveka kunena kuti Mulungu amene analenga anthu angadziŵenso bwino zinthu zofunika kuti tikhale athanzi?

Mlengi Adzapereka Chakudya Chopanda Matenda

Baibulo lili ndi maulosi omveka bwino okhudza mmene zinthu zidzakhalire m’dziko limene likubwera. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Mulungu adzapatsa mvula ya mbewu yako, ukaidzale m’nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuruka; tsiku limenelo ng’ombe zako zidzadya m’madambo aakulu. Momwemonso ng’ombe ndi ana a bulu olima nthaka adzadya chakudya chochezera, chimene chapetedwa ndi chokokolera ndi mkupizo.”

Kenaka ulosiwo unati: “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.”—Yesaya 25:6; 30:23, 24.

Kodi n’zokukondweretsani zimenezo? Ulosi wa Yesaya umatitsimikizira kuti munthu aliyense amene adzakhale m’dziko latsopano la Mulungu adzakhala ndi zakudya zamwanaalirenji. Kodi zakudyazo zidzakhala zabwino? N’zosachita kufunsa. Ulosi wina umatitsimikizira kuti anthu a Mulungu “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.” (Mika 4:4) Mawu olimbitsa mtima amenewo adzakwaniritsidwa ndi Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Mesiya, umene uyambe posachedwapa kulamulira padziko lonse lapansi.—Yesaya 9:6, 7.

Anthu sadzakayikiranso kuti kaya chakudya n’chopanda matenda kapena n’cha matenda. Koma tizidzaitanira anzathu mokondwa kuti: “Yandikirani kutebuloko” kapena kuti “Kalibu.”

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Posachedwapa munthu aliyense padziko lapansi adzakhala ndi chakudya chopatsa thanzi chamwanaalirenji

[Chithunzi patsamba 20]

Mulungu akulonjeza anthu onse kuti adzakhala ndi chakudya chosakayikitsa ndiponso chopatsa thanzi