Thandizo Ndiponso Kukoma Mtima kwa Anthu a M’madera Osiyanasiyana
Thandizo Ndiponso Kukoma Mtima kwa Anthu a M’madera Osiyanasiyana
ANTHU ongodzipereka anachokera m’madera osiyanasiyana a dziko la United States ndiponso m’mayiko ena. Munthu wina wongodzipereka anali Tom (uyo ali pamwambayo), yemwe ali ndi zaka 29 ndipo amagwira ntchito yozimitsa moto mumzinda wa Ottawa, ku Canada. Iye anauza mtolankhani wa Galamukani! kuti: “Ndinaona nkhaniyi pa TV ndipo ndinafuna kuthandiza ozimitsa moto anzanga a ku New York. Ndinabwera Lachisanu pagalimoto ndipo Loŵeruka ndinapita pamalo pamene panachitika ngozipo kuti ndithandize nawo. Anandiika m’gulu limene analitcha kuti gulu lonyamula zidebe, ndipo tinkachotsa zogumuka pomazitapa ndi zidebe.
“Tinkazichotsa pang’onopang’ono ndi fosholo chifukwa tinkafuna kupeza zinthu zimene zingatithandize kudziŵa ozimitsa moto amene anakwiririka. Ndinapeza chida china chotsegulira zitseko ndi zinthu zina ngakhale atazikhoma ndi kiyi. Inali ntchito yofunika khama ndiponso kusamala kwambiri. Pa anthu 50 amene tinadzipereka kugwira ntchito imeneyi, pankatha maola aŵiri kuti tidzazitse galimoto yonyamula zinyalala.
“Lolemba pa September 17, tinafukula mitembo ya ozimitsa moto ena amene anathamangira kunyumbazi Lachiŵiri lapitalo. Sindidzaiwala zimene ndinaona pamenepo. Onse ogwira ntchito yopulumutsa anthu anasiya kaye kugwira ntchito yawo, n’kuvula zipewa zawo zotetezera kumutu, kenaka n’kungoima njoo pochitira ulemu antchito anzathu amene anafa.
“Nditaima n’kumayang’ana zimene zinkachitika pamalo angoziwo, zinandikhudza mtima poganizira kuti moyo wa masiku ano n’ngosachedwa kutha. Zinandipangitsa kuti ndiganizire za moyo wanga, ntchito yanga, ndiponso banja langa. Ngakhale kuti ntchito yanga n’njoopsa, ntchitoyi n’njopindulitsa kwambiri chifukwa ndimatha kuthandiza anthu ngakhalenso kuwapulumutsa kumene.”
Mboni za Yehova Zinagwira Ntchito Yothandiza Kwambiri
Kwa masiku aŵiri oyambirira ngoziyi itangochitika, anthu pafupifupi 70 anathaŵira ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Ena amene zipinda zawo za ku hotela zinali zitagumuka komanso amene anali atataya katundu wawo anapatsidwa malo okhala ndiponso zovala zina. Anawapatsanso chakudya. Ndipo mwina chofunika kwambiri n’chakuti akulu achikristu odziŵa kulimbikitsa anawathandiza kuti asamadandaule kwambiri.
Mboni za Yehova zinatumizanso zida zofunika pangozi ndiponso katundu wina ku gulu lopulumutsa anthu lija limene linali kugwira ntchito pa malo angoziwo. Zinaperekanso magalimoto ku bungwe lozimitsa moto kuti azinyamuliramo anthu ozimitsa moto opita kumeneko. Ricardo (uyo ali pamwamba chakumanjayo), yemwe ndi Mboni ya zaka 39 ndipo amagwira ntchito yotaya zinyalala, anali m’gulu la anthu ochuluka amene tsiku lililonse ankachotsa zogumuka zolemera matani ambiri. Iye anauza mtolankhani wa Galamukani! kuti: “Malowo anali ofoola nkhongono kwambiri, makamaka kwa ozimitsa moto,
amene anali kufunafuna anzawo amene anafa. Ndinawaona akusolola munthu wina wozimitsa moto amene anali moyo. Wina anali atangophedwa ndi mtembo wamunthu umene unam’gwera kuchokera m’mwamba. Anthu ambiri ozimitsa moto ankangolira. Ndinalephera kudzilimbitsa ndipo ndinayamba kulira nawo. Patsikulo panalibenso munthu wina amene analimba mtima koposa anthu ameneŵa.”‘Nthaŵi ndi Zochitika Zongotigwera Mwadzidzidzi’
Anthu zikwizikwi anafa pa zoopsazi. Mwa anthu ameneŵa pali Mboni za Yehova zosachepera 14, zimene zinali pamene panachitika ngoziyo kapena chapafupi. Joyce Cummings, wa zaka 65, anachokera ku Trinidad, ndipo anapita kukaonana ndi dokotala wa mano cha pafupi ndi nyumba zosanjazo. Tsoka ilo panthaŵiyi m’pamene kunkachitika ngoziyo. Zikuoneka kuti anabanika kwambiri ndi utsi ndipo anathamangira naye ku chipatala chapafupi ndi pomwepo. Koma analephera kum’pulumutsa. Iye ndi mmodzi mwa anthu ambiri ovutika chifukwa cha ‘nthaŵi ndi zochitika zongotigwera mwadzidzidzi.’ (Mlaliki 9:11) Mayiyu anali kudziŵika chifukwa cha khama lake pa kulalikira uthenga wabwino.
Calvin Dawson (onani kabokosi) ankagwira ntchito ku kampani inayake ya zamalonda imene inali m’nsanja ya nambala 84 m’nyumba yosanja imene inali chakumwera. Iye anali muofesi yake ndipo ankatha kuona bwinobwino nyumba yosanja imene inali chakumpoto itangowombedwa kumene ndi ndege. Bwana wake sanali muofesi panthaŵiyi ndipo anaimba telefoni kuti adziŵe chimene chinachitika. Bwanayo anati: “Calvin amayesa kundilongosolera zimene anaona. Anandiuza kuti, ‘Anthu akudumpha!’ Ndinamuuza kuti atulukemo ndiponso kuti auze anthu ena onse kuti nawonso atuluke m’maofesiwo.” Calvin sanakwanitse kutuluka m’nyumbayo. Bwanayo anapitiriza kunena kuti: “Calvin anali munthu wabwino kwambiri ndipo aliyense ankamuyamikira, ngakhale ifeyo amene sitikonda kuchita zinthu zauzimu. Tinkam’sirira chifukwa ankakonda kwambiri Mulungu komanso anali wokoma mtima.”
Mboni ina imene inafa ndi James Amato (amene ali pamunsiyo patsamba 10 chakumanja), amene anali bambo wa ana anayi ndipo anali wotsogolera anthu ozimitsa moto m’bungwe lozimitsa moto mumzinda wa New York. Anthu amene ankamudziŵa anati anali munthu wolimba mtima kwambiri mwakuti
“ankaloŵa m’nyumba imene ikuyaka ngakhale pamene anthu akuthaŵamo.” James anam’kweza pa udindo iye kulibe n’kukhala bwana wamkulu woyang’anira ozimitsa moto.Mboni ina yogwira ntchito yozimitsa moto, anali George DiPasquale, amene wakhala akugwira ntchitoyi kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Mkazi wake anali Melissa ndipo anali ndi mwana wamkazi wa zaka ziŵiri dzina lake Georgia Rose. Anali mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova wa pa chilumba cha Staten ndipo nyumba yosanja ya kumwera inagwa iye ali momwemo ali m’nsanja ya nambala 10. Nayenso anafa ali m’kati moyesetsa kupulumutsa ena.
Ameneŵa ndi anthu aŵiri okha mwa anthu ambirimbiri ozimitsa moto, apolisi, ndiponso ogwira ntchito yopulumutsa anthu pangozi amene anafa uku akuyesetsa mwachamuna kuti apulumutse anthu. Kulimba mtima kwa anthu ameneŵa n’kosasimbika. Mkulu woyang’anira mzinda wa New York a Rudolph Giuliani pambuyo pake anauza gulu la ozimitsa moto amene tsopano anali atakwezedwa maudindo kuti: “Mwatipatsa mphamvu chifukwa chofunitsitsa kulimbana ndi vutoli kwinaku mukukumana ndi mikwingwirima yoopsa . . . Ndipo palibenso . . . chitsanzo china cha amunamuna olimba mtima choposa gulu la ozimitsa moto a mumzinda wa New York.”
Ntchito Yolimbikitsa Anthu
Masiku angapo nkhani ya ngoziyi idakali mkamwamkamwa, Mboni za Yehova pafupifupi 900,000 m’dziko lonse la United States zinayesetsa kuchita zotheka polimbikitsa anthu amene anali kulira maliro. Kukonda anzawo kunawapangitsa kulimbikitsa olira maliro. (Mateyu 22:39) Muutumiki wawo iwo ayesetsanso kuuza anthu za chiyembekezo chimodzi chokha chodalirika kwa anthu onse amene akusautsidwa.—2 Petro 3:13.
Mbonizo zinkawalankhula anthuwo mwachifundo. Cholinga chawo chinali kuwalimbikitsa ndi Malemba ndiponso kutsanzira Kristu, amene anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Akulu magulumagulu ochokera m’mipingo ya Mboni za Yehova ya ku Manhattan anawalola kufika pa malo angoziwo kuti alankhule ndiponso alimbikitse anthu amene amagwira ntchito pamenepo. Anthuwo anali kumvetsera mwachidwi. Atumiki ameneŵa ananena kuti: “Pamene tinali kuwaŵerengera malemba, azibambo ogwira ntchitowo misozi inangoti ndee m’maso mwawo.” Opulumutsa anthu anali kupumulira m’boti lokochezedwa pa gombe. “Anthuŵa ankaoneka kuti atheratu mphamvu ndipo anangoti zyolizyoli, kulephera kumvetsa zimene anaona. Tinakhala nawo pansi ndi kuwaŵerengera malemba a m’Baibulo. Iwo anatithokoza kwambiri chifukwa chodzawayendera, ndipo ananena kuti ankafunikadi kuwalimbikitsa mmene tinachitira.”
Anthu ambiri amene anawalankhula ngoziyi itachitika ankafuna chinachake choti aŵerenge, ndipo anapatsidwa mabulosha masauzande ambiri kwaulere. Ena mwa mabulosha ameneŵa ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Will There Ever Be a World Withour War? ndiponso Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Komanso, nkhani zoyambira pachikuto za m’magazini aŵiri aŵa a Galamukani! anazifalitsa mwapadera: “Uchigaŵenga Ukusintha” (June 8, 2001) ndi “Kulimbana ndi Vuto Lokhala ndi Mantha Mukamakumbukira Zoopsa” (September 8, 2001). Nthaŵi zambiri Mbonizo zinkalongosola chiyembekezo cha m’Baibulo cha chiukiriro. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) N’kutheka kuti anthu mamiliyoni ambiri anauzidwa uthenga wolimbikitsa umenewu.
Ziyenera Kutipangitsa Kuganizirapo Bwino
Ngozi zokhala ngati imene inachitika mumzinda wa New York imeneyi ziyenera kutipangitsa kuganizira zimene tikuchita m’moyo wathu. Kodi timangokhalira kuganiza zatokha, kapena timayesa kuthandiza ena kukhala osangalala? Mneneri Mika anafunsa kuti: “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” (Mika 6:8) Kudzichepetsa kuyenera kutipangitsa kufufuza m’Mawu a Mulungu kuti tipeze chiyembekezo chenicheni cha akufa ndi kutinso tidziŵe zimene Mulungu adzachite posachedwa kuti padziko lapansi padzakhalenso mikhalidwe ya m’paradaiso. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri zokhudza malonjezo a m’Baibulo, tikukulimbikitsani kuti mukumane ndi Mboni za Yehova za kumene mukukhalako.—Yesaya 65:17, 21-25; Chivumbulutso 21:1-4.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 11]
PEMPHERO LA TATIANA
Mkazi wa malemu Calvin Dawson, dzina lake Lena, anauza mtolankhani wa Galamukani! zimene mwana wake wamkazi wa zaka zisanu ndi ziŵiri ananena m’pemphero patatha masiku angapo atadziŵa kuti bambo ake sabweranso kunyumba. Mayi ake, a Lena anali atangomaliza kupemphera, ndipo Tatiana anawafunsa kuti, “Amayi, mungandilole kuti nane ndipemphere?” Mayi akewo anavomera. Ndiyeno Tatiana anapemphera motere: “Yehova, Atate wathu wakumwamba, tikufuna kukuthokozani chifukwa chotipatsa chakudya ichi ndiponso chifukwa chotisunga tsiku lonse. Ndipo tikufuna kukupemphani kuti mzimu wanu ukhale ndi ine pamodzi ndi mayi anga kuti tikhale olimba mtima. Ndipo tikufunanso kukupemphani kuti mzimu wanu ukhale ndi bambo anga, kuti akamabwera adzakhale olimba mtima. Ndipo kuti akabwera, akhale munthu wabwino, wolimba mtima, ndiponso wosangalala komanso wathanzi, ndipo tionana nawonso. Kudzera m’dzina la Yesu . . . hii, musaiwale kuwalimbitsa mtima mayi anga. Ame.”
Pokayikira kuti Tatiana analidi atamvetsetsa, a Lena anati: “Tiana, wapemphera bwino kwambiri. Koma mwanawanga wokondedwa, kodi ukudziŵa kuti bambo ako sadzabweranso?” Nthaŵi yomweyo, nkhope ya Tatiana inasintha. “Mwati sadzabweranso?” anafunsa motero Tatiana. “Inde,” anayankha choncho amayi ake. “Kodi sindinakuuze iwe? Inetu ndimangoti unamvetsa bwinobwino kuti ndinati bambo ako sadzabweranso.” Tatiana anati: “Komatu inu nthaŵi yonseyi mwakhala mukundiuza kuti adzabweranso m’dziko latsopano!” Kenaka atamvetsa zimene mwana wakeyo anali kutanthauza, a Lena anati: “Pepa, Tatiana. Sindinakumvetse bwino ayi. Ndimangoti ukutanthauza kuti bambo abweranso maŵa.” A Lena anati: “Ndinasangalala podziŵa kuti iye amaonadi kuti dziko latsopano ndi lenileni.”