Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Limene Nyumba Zosanja Ziŵiri Zinagwa

Tsiku Limene Nyumba Zosanja Ziŵiri Zinagwa

Tsiku Limene Nyumba Zosanja Ziŵiri Zinagwa

ZIMENE zinachitika pa September 11, 2001, mumzinda wa New York, ku Washington, D.C., ndi ku Pennsylvania sizidzaiwalika m’maganizo mwa anthu ochuluka zedi padziko lonse. Kodi inuyo nkhani ya ndege zimene zinawomba Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse komanso nyumba ya likulu la zachitetezo ku America yotchedwa Pentagon imene ili ku Washington munaimvera kapena kuionerera muli kuti?

Anthu anangoti kakasi chifukwa cha mmene chuma chambiri ndiponso makamaka miyoyo yambiri ya anthu inapululukira pa kanthaŵi kochepa chabe.

Kodi taphunzirapo kuti zinthu zofunika kwambiri m’moyo wathu n’ziti ndipo tiyenera kusankha bwanji zinthu zoyenera kuchita? Kodi zinatheka bwanji kuti zoopsa zimenezi zichititse anthu kukhala ndi makhalidwe okoma a kudzipereka, chifundo, kupirira, ndiponso kuganizira ena? Nkhani inoyo komanso yotsatirayi ziyesa kuyankha funso lachiŵirili.

Nkhani Zimene Opulumuka Anasimba

Zoopsazo zitangochitika ku New York, sitima zoyenda pansi pa nthaka zinaleka kuyenda ndipo anthu miyandamiyanda anali kuyenda wapansi kutuluka m’dera la Manhattan la chakumwera ndipo ambiri anali kudutsa pa mlatho wa Brooklyn ndi mlatho winanso wa Manhattan. Ankatha kuona bwinobwino nyumba za maofesi ndiponso fakitale ya likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Mwamsanga anthu ena othaŵa pamalo pamene panachitika zoopsazo anayamba kuloŵera kunyumba zimenezi.

Alisha, (ali kumanjayu), yemwe ndi mwana wa Mboni, anali m’gulu la anthu oyamba kufikako. Anali fumbi ndi phulusa lokhalokha. * Iye analongosola kuti: “Ndinali m’sitima popita kuntchito, ndipo ndinaona utsi ukuchokera ku nyumba zosanjana zomwe munali Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse [World Trade Center]. Nditafika pamene panachitika zoopsazo, ndinapeza magalasi ali mbwee ndiponso panali thuu, kutentha. Anthu anali kuthaŵa kuloŵera mbali zosiyanasiyana kwinaku apolisi akuyesa kuchotsa anthu pamalowo. Zimangooneka ngati n’kunkhondo.

“Ndinathaŵira m’nyumba ina yapafupi kukabisala. Kenaka ndinamva chiphokoso cha kuphulika pamene ndege yachiŵiri inali kuwomba nyumba yosanja imene inali chakumwera. Zimene zinkachitika zinali zosasimbika, ndipo chiutsi chakuda bii chinadzaza dera lonselo. Anatiuza kuti tichoke kumalo oopsawo. Anandikweza m’boti lowolotsa anthu pamtsinje wa East n’kupita nane ku Brooklyn. Nditafika tsidya linalo, ndinakweza maso n’kuona chikwangwani chachikulu cholembedwa kuti, ‘WATCHTOWER’ Kumenekutu n’kulikulu kwa chipembedzo cha amayi anga! Nthaŵi yomweyo ndinapita ku maofesiwo. Ndinadziŵa kuti panalibenso kwina kumene ndikanathandizidwa koposa kuno. Ndinasamba bwinobwino ndipo kenaka ndinawaimbira telefoni makolo anga.”

Wendell (ali kumanjayu) ankagwira ntchito yokhala pakhomo la hotela ya Marriott n’kumathandiza anthu. Hotelayi inali pakati pa nyumba ziŵiri zosanjazo. Iye analongosola kuti: “Pamene ndege yoyamba inkawomba nyumbayo, ndinali ndikugwira ntchito pamalo ofikira alendo m’hotelayo. Ndinaona zinthu zogumuka kunyumbazo zikungoyoyokera paliponse. Ndinayang’ana tsidya lina la msewu n’kuona munthu atagwa pansi akuyaka moto. Mwamsanga, ndinangochotsa jekete ndi shati yanga n’kum’thamangira komweko kuti ndikamuzimitse. Munthu wina amene anali kudutsa anayamba kundithandiza. Malaya onse a munthu woyakayo anapseratu kupatulapo sokosi ndi nsapato zake zokha. Kenaka ozimitsa moto anabwera n’kumutenga kuti akalandire chithandizo kuchipatala.

“Pasanathe nthaŵi, Bryant Gumbel amene ndi mtolankhani wa wailesi ina ya kanema yotchedwa CBS anaimba telefoni kuti amve zimene tinaona zikuchitika. Abale anga omwe ali ku zilumba zotchedwa Virgin anamva zimenezi pa wailesi yawo yakanema ndipo motero anadziŵa kuti ndili moyo.”

Donald, yemwe ndi wamtali kwambiri komanso wojintcha bwino, amagwira ntchito m’nyumba ina yosanja ya zamalonda yam’dera lomwelo ndipo anali pansanja ya nambala 31, motero ankatha kuona bwinobwino nyumba zosanja ziŵirizo ndiponso hotela ya Marriott zili poteropo. Iye anati: “Ndinangoti kakasi ndiponso zimene ndinaona zinandiopsa kwambiri. Anthu anali kugwa ndiponso kudumphira panja kudzera m’mawindo a nyumba yosanja imene inali chakumpoto. Ndinagwidwa mantha osaneneka ndipo ndinayamba kutuluka m’nyumbayo mothamanga kwambiri.”

Nkhani inanso ndi ya mayi wina wa zaka za m’ma 60 pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri a zaka za m’ma 40. Ruth ndi mng’ono wake Joni anali kukhala ndi amayi awo, a Janice, pa hotela ina ya pafupi ndi nyumba zosanja ziŵirizo. Ruth, amene ali namwino wovomerezedwa ndi boma, akusimba nkhaniyo motere: “Ndinali kusamba m’bafa. Mwadzidzidzi amayi ndi mng’ono wanga anafuula kuti ndituluke m’bafamo. Tinali pansanja ya nambala 16, ndipo iwo ankaona zidutswa zogumukagumuka zikugwera pansi kudutsa cha pawindo pathu. Amayi anga anaonanso thupi la munthu lili peyupeyu kudutsa padenga la nyumba inayake ngati kuti lachita kuponyedwa mwamphamvu kuchokera kwinakwake.

“Ndinavala mwamsangamsanga, ndipo tinayamba kutsikira pansi panyumbayo. Tinkangomva anthu ambiri akukuwa chifukwa cha mantha. Tinatuluka n’kupita mumsewu. Tinamva zinthu zikuphulika ndipo tinaona moto wothetheka. Tinauzidwa kuti tithamangire cha kum’mwera kudera lotchedwa Battery Park, kumene kuli boti lowolotsa anthu la pa chilumba cha Staten. Tili m’njira, tinatayana ndi amayi, amene amadwala chifuwa cha mphumu chosatha. Kodi akhalabe ndi moyo pakati pautsi wonsewo, phulusa ndiponso fumbi lambiri chonchi? Tinawafunafuna kwambiri koma osawapeza. Komabe, poyamba sitinade nkhaŵa kwambiri chifukwa chakuti amayi ndi munthu wamphamvu zake ndiponso ndi wolimba mtima.

“Kenaka anatiuza kuti tidutse pa mlatho wa Brooklyn kuti tiolokere kutsidya linalo. Tangoganizirani mmene mitima yathu inakhalira pansi titafika kutsidya linalo n’kuona chikwangwani chachikulu cholembedwa kuti ‘WATCHTOWER’! Tinadziŵa kuti tsopano tapulumuka.

“Anatilandira bwino ndipo anatipatsa chakudya ndi pogona. Anatipatsanso zovala, pakuti tinangotsala ndi zam’thupi zokha. Koma kodi amayi athu anali kuti? Usiku wonse tinali kuyesa kufunsa kuzipatala koma sitinawapeze. Ndiye mmaŵa mwake cha m’ma hafu pasiti leveni, tinalandira uthenga wakuti amayi athu anali pansi m’chipinda chofikira alendo! Kodi chinawachitikira n’chiyani?”

Amayiwo, omwe dzina lawo ndi a Janice, akupitiriza nkhaniyi motere: “Titatuluka m’hotelayo, ndinayamba kudera nkhaŵa mnzanga wina wachikulire, amene sankatha kunyamuka nafe limodzi. Ndinafuna kubwerera kuti ndikangom’tulutsa ndekha. Koma kuteroko kunali kudziika pangozi yaikulu. Ndinatayana ndi ana anga m’chipwirikiti cha anthu osokonezeka ndi mantha. Komabe, sindinade nkhaŵa kwambiri, chifukwa chakuti ana anga n’ngochenjera ndipo Ruth ndi namwino woidziŵa bwino ntchito yake.

“Kulikonse kumene ndinkaponya maso kunali anthu ambirimbiri ofuna kuthandizidwa, makamaka ana achichepere ndi makanda. Ndinathandiza anthu onse amene ndikanatha. Ndinapita pamalo pamene anali kupatula ndiponso kuthandiza anthu malingana ndi mmene avulalira. Ndinathandiza apolisi ndiponso ozimitsa moto amene anali mbuu kutuwa ndiponso kuda chifukwa cha mwaye ndiponso fumbi powasambitsa m’manja ndi kumaso. Ndinakhala mpaka cha m’ma firi koloko mbandakucha wa tsiku lotsatira ndili komweko. Kenaka ndinakwera boti lotsiriza lowolotsa anthu kupita ku chilumba cha Staten. Ndinaganiza kuti mwina ana anga anali atathaŵira kumeneko. Koma sindinawapezeko.

“M’maŵa mwake ndinkati ndikwere nawo boti loyamba lopita ku Manhattan, koma sanandilole chifukwa sindinali m’gulu la anthu ogwira ntchito yopulumutsa anthu. Kenaka ndinaona wapolisi wina amene ndinam’thandiza. Ndinam’kuwira kuti: ‘John! Ndikufuna kubwerera ku Manhattan.’ Iye anandiyankha kuti: ‘Ingonditsatani.’

“Nditafika ku Manhattan, ndinabwerera ku hotela ya Marriott. Mwina panopa zikanatheka kuti ndim’thandize mnzanga wachikulire uja. Koma ayi ndithu! Hotelayo inangosanduka bwinja. Dera la kumwera kwa mzindawu linangoti zii, kopanda anthu ena alionse kungosiya apolisi ndi ozimitsa moto ofooka ndiponso andwii, ochita kuonekeratu kuti aona zoopsa.

“Ndinapitiriza ulendo wanga mpaka kukafika ku mlatho wa Brooklyn. Nditayandikira kutsidya linalo, ndinaona chikwangwani chimene ndimachidziŵa bwino chakuti, ‘WATCHTOWER.’ Mwina ana anga ndingawapeze kumeneko. N’zoonadi, iwo anabwera pofikira alendo n’kudzandilonjera. Tinakumbatirana ndi kutulutsa misozi ya chimwemwe posakhulupirira kuti takumananso!

“N’zodabwitsa kuti nthaŵi yonseyi sindinabanike ngakhale kamodzi chifukwa cha matenda anga a chifuwa cha mphumu, ngakhale kuti kunali utsi wambiri, fumbi, ndiponso phulusa. Ndinkangopemphera nthaŵi yonseyo, chifukwa chakuti ndinkafuna kuthandiza anthu osati kuti ineyo ndiwapatse chintchito.”

“Kulibe Malo Otera Ndege!”

Mkazi wina dzina lake Rachel ndipo ali ndi zaka za m’ma 20, anauza mtolankhani wa Galamukani! kuti: “Ndinamva kulira kwa ndege ikuuluka m’munsi mwenimweni uku ndikuyenda m’msewu wakwathu kumwera kwa dera la Manhattan. Inkasokosa kwambiri mwakuti ndinakweza maso m’mwamba. Sindinakhulupirire zimene ndinkaonazo, chifukwa ndinaona ndege ya jeti yaikulu kwambiri ikuoneka kuti ikukatera basi. Sindinamvetse kuti n’chifukwa chiyani imauluka m’munsi komanso n’kumathamanga kwambiri choncho. Kulibe malo otera ndege! Mwinatu woyendetsa ndegeyo wasokonezeka. Kenaka ndinangomva m’zimayi akukuwa amvekere, ‘Ndege yagunda nyumba!’ Chimoto chachikulu chinabuka pa nyumba yosanja imene inali chakumpoto. Ndinaona chibowo chachikulu chitangoti bii panyumbapo.

“Sindinaonepo zinthu zoopsa ngati zimenezi m’moyo wanga wonse. Zinkangooneka ngati ndikulota. Ndinangoima poteropo kukamwa kuli yasaa. Patangotha kanthaŵi kochepa, ndege ina inakawombanso nyumba yachiŵiri, ndipo nyumba zonsezo mapeto ake zinagwa. Ndinazunguzika mutu kwambiri. Ndinaona zosaona!”

“Kukakhala Kusambira, Ndisambira Basi”

Denise, mtsikana wa zaka 16, anali atangofika kumene kusukulu imene amaphunzirako yomwe inagundizana ndi nyumba ya za zamalonda yotchedwa American Stock Exchange, yomwe inali pafupi Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse. “Nthaŵi inali itangopitirira naini koloko m’maŵa. Ndinadziŵa kuti kwachitika chinachake, koma sindinadziŵe kuti n’chiyani makamaka. Ndinali pa nsanja ya nambala 11 m’nyumba imene munali sukuluyo, ndipo tinkaphunzira phunziro lokhudza za mbiri yakale. Ana onse m’kalasilo anagwidwa mantha. Aphunzitsi athu ankafunabe kutiyesa kuti aone ngati tinamva zimene anali atatiphunzitsa. Ifeyo tinkangofuna kuti tituluke n’kumapita kunyumba.

“Kenaka sukuluyo inagwedezeka pamene ndege yachiŵiriyo inagunda nyumba yosanja imene inali chakumwera. Koma sitinadziŵebe kuti chachitika n’chiyani. Kenaka ndinamva pa wailesimeseji ya aphunzitsi akunena kuti: ‘Ndege ziŵiri zawomba nyumba zosanja ziŵiri zija!’ Ndinaganiza mumtima mwanga kuti, ‘Si kwanzeru kukhalabe m’mwamba muno. Umenewu ndi uchigawenga basi, ndipo kenaka zigawengazi zigumulanso nyumba ya zamalonda tili nayo pafupiyi.’ Motero tinatuluka.

“Tinathamanga kuloŵera ku dera lotchedwa Battery Park. Ndinatembenuka kuti ndione zimene zinali kuchitika. Ndinaona kuti nyumba yosanja imene inali chakumwerayo igwa basi. Kenaka ndinaganiza kuti nyumbayo igwetsanso nyumba zosanja zina, mwakuti nyumba zosanja zonse zitalizitali zigwa nawo. Ndinabanika, chifukwa phulusa ndiponso utsi zinkanditseka mphuno ndi kukhosi. Ndinathamanga kuloŵera kumtsinje wa East, kwinaku ndikuganiza kuti, ‘Kukakhala kusambira, ndisambira basi.’ Ndili m’kati mothaŵa chonchi, ndinapemphera kuti Yehova andipulumutse.

“Kenaka, anandiloŵetsa m’boti lopita ku boma la New Jersey. Amayi anga anandipeza patatha maola asanu, koma chachikulu n’chakuti ndinali bwinobwino!”

“Kodi Lero ndi Tsiku Langa Lomaliza?”

Joshua, wa zaka 28, amachokera mumzinda wa Princeton, m’boma la New Jersey ndipo anali kuphunzitsa m’chipinda china chimene chili m’nsanja ya nambala 40 ya nyumba yosanja imene inali chakumpoto. Iye akukumbukira kuti: “Mwadzidzidzi kunamveka ngati kuti kwaphulika bomba. Nyumbayo inagwedezeka, ndipo ndinaganiza kuti ‘Ayi, koma ichi n’chivomezi.’ Ndinayang’ana kunja, ndipo ndinaona zoopsa kwambiri; utsi unangoti toloo ndipo zogumuka zinali kulakatika kuzungulira nyumba yonseyo. Ndinauza ana a m’kalasilo kuti, ‘Aliyense asatenge chilichonse. Tiyeni tizipita!’

“Tinayamba kutsika pa masitepesi, ndipo utsi unayamba kukula, ndiponso madzi ankatuluka m’mapaipi ozimitsira moto. Koma sitinasokonezeke maganizo chifukwa cha mantha. Ndinkangopempherera kuti tiloŵere kwabwino kuti tisakumanizane ndi motowo.

“Ndili m’kati motsika mothamanga chonchi, ndinkangodzifunsa kuti, ‘kodi lero ndi tsiku langa lomaliza?’ Ndinkangopemphera kwa Yehova, ndipo ndinayamba kumva mtendere winawake wodabwitsa mumtima mwanga. Sindinakhalepo ndi mtendere wotere kale lonse. Sindidzaiiwala n’komwe nthaŵi imeneyo.

“Kenaka titatuluka m’nyumbayo, apolisi anali kukusa anthu onse n’kumawachotsa pamalopo. Ndinayang’ana nyumba zosanja ziŵirizo ndipo ndinaona kuti zonse zinali zitabooledwa. Zinali ngati zochitika za m’maloto.

Kenaka ndinamva phokoso lochititsa nthumanzi kwambiri ndipo kunakhala bata lodabwitsa kwambiri ngati kuti anthu zikwizikwi angoti duu nthaŵi imodzi. Zinali ngati kuti mzinda wonse wa New York wangoti duu. Kenaka ndinamva kukuwa. Nyumba yosanja imene inali kumwera ija inayamba kugwa yokha! Ndiyetu chiutsi, phulusa, ndiponso chifumbi chosaneneka zinangoti koboo n’kumabwera kumene kunali ifeko. Zimangooneka ngati filimu basi. Koma ndithu zinali kuchitikadi. Fumbi lija litatipeza, tinangobanikiratu.

“Ndinakwanitsa kufika pa mlatho wa Manhattan ndipo ndinayang’ana m’mbuyo n’kuona nyumba yosanja imene inali chakumpoto, yomwenso inali ndi mlongoti waukulu wa TV ikugwa. Ndili m’kati mooloka mlathowo, ndinkangopempherera kuti ndikafike ku Beteli, ku likulu la Mboni za Yehova la padziko lonse. M’moyo wanga wonse sindinasangalalepo kwambiri chonchi chifukwa chofika pa malo ameneŵa. Ndipo pa khoma la nyumba ya fakitale ndinaona chikwangwani chimene anthu ochuluka amachiona tsiku lililonse cholembedwa kuti ‘Read God’s Word the Holy Bible Daily’! [‘Ŵerengani Mawu a Mulungu Baibulo Lopatulika Tsiku ndi Tsiku’!] Ndinaganiza mumtima kuti, ‘Apa ndiye ndafika kale. Ndisafooke ayi.’

“Ndikamaganizira zimene zinachitikazo, ndimaona kuti zinandilimbikitsa kwambiri kutsimikiza kuti ndiyenera kuchita kaye zinthu zofunikadi kwenikweni.”

“Ndinaona Anthu Akudumpha Kuchokera M’nyumba Yosanjayo”

Jessica, wa zaka 22, anaona zimenezi atangotsika sitima yoyenda pansi panthaka m’kati mwa mzindawu. “Nditatukula mutu ndinaona phulusa, zogumuka ndiponso zidutswa zosiyanasiyana za zitsulo zikugwa. Anthu anali kudikirira kuti aimbe telefoni zamumsewu ndipo anayamba kusakhazikika maganizo chifukwa zinkawachedwetsa. Ndinapemphera kuti ndikhazikike mtima. Kenaka tinamvanso kuphulika kwina. Zitsulo ndiponso magalasi anali kugwa kuchoka m’mwamba. Ndinamva anthu akukuwa kwambiri kuti, ‘Ndi ndege inanso!’

“Ndinakweza maso, ndipo ndinaona zoopsa kwambiri. Anthu anali kudumpha kuchokera m’zipinda za pamwamba pa zipinda zimene ndegeyo inagunda ndipo m’zipindazi munkatuluka utsi ndi malaŵi a moto. Zimene ndinaona sizinachokebe m’maganizo mwanga. Ndinaona mwamuna ndi mkazi. Analendewera pawindo kwa kanthaŵi ndithu. Kenaka atatopa anangodziponya kuchokera pamwamba kwambiri n’kungoti lengalenga mpaka kugwera pansi penipeni. Sizinali zoti n’kuyang’anako kaŵiri.

“Kenaka, ndinafika pa mlatho wa Brooklyn, pamene ndinavula nsapato zanga zomwe sindinkatha kuyenda nazo bwinobwino ndipo ndinathamangira tsidya linalo la mtsinjewo. Ndinayenda n’kukafika ku maofesi a Watchtower, kumene anandithandiza mwamsanga kuti ndikhazikitse mtima pansi.

Usiku wa tsiku limenelo kunyumba, ndinakaŵerenga nkhani za mu Galamukani! ya pa September 8, 2001, zakuti ‘Kulimbana ndi Vuto Lokhala ndi Mantha Mukamakumbukira Zoopsa.’ Kunali kofunikadi kwambiri kuti ndiŵerenge nkhani imeneyi!”

Kukula kwa ngoziyi kunachititsa anthu kuthandizapo m’njira ina iliyonse imene akanatha. Nkhani yotsatirayi ilongosola zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Atolankhani a Galamukani! analankhula ndi anthu ambirimbiri opulumuka mwakuti n’zosatheka kuwalemba onsewo m’nkhani yachidule ino. Iwo atithandiza kwambiri kuti tilembe bwinobwino ndiponso kutsimikizira nkhani zimenezi.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZOGWERATU

1 NYUMBA YOSANJA YA CHAKUMPUTO 1 Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse

2 NYUMBA YOSANJA YA CHAKUMWERA 2 Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse

3 HOTELA YA MARRIOTT 3 Likulu la Zamalonda la Padziko lonse

7 7 LIKULU LA ZAMALONDA LA PADZIKO LONSE

ZOWONONGEKA KWAMBIRI

4 4 LIKULU LA ZAMALONDA LA PADZIKO LONSE

5 5 LIKULU LA ZAMALONDA LA PADZIKO LONSE

L NYUMBA YOTCHEDWA ONE LIBERTY PLAZA

D BANKI YOTCHEDWA DEUTSCHE BANK imene ili pa 130 Liberty St.

6 NYUMBA YOTCHEDWA U.S. CUSTOMS HOUSE

N S MILATHO YA ANTHU OYENDA WAPANSI WACHAKUMPOTO NDI WACHAKUMWERA

ZOWONONGEKA PANG’ONO

2F 2 LIKULU LA ZACHUMA LA PADZIKO LONSE

3F 3 LIKULU LA ZACHUMA LA PADZIKO LONSE

W HOLO YOTCHEDWA WINTER GARDEN

[Mawu a Chithunzi]

As of October 4, 2001 3D Map of Lower Manhattan by Urban Data Solutions, Inc.

[Zithunzi]

Pamtundapo: Nyumba yosanja imene inali chakumwera ndi imene inayamba kugwa

Pamwambapa: Anthu ena anathaŵira ku nyumba za Watchtower

Kumanja: Anthu ambirimbiri ozimitsa moto ndi opulumutsa anthu anagwira ntchito mwakhama pa malo angoziwo

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/Jerry Torrens

Andrea Booher/FEMA News Photo

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

AP Photo/Marty Lederhandler

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

AP Photo/Suzanne Plunkett