Dziko Limene Aliyense Angaloledwe Kudzakhalamo
Dziko Limene Aliyense Angaloledwe Kudzakhalamo
“Popeza kuti vuto la anthu othaŵa kwawo n’lapadziko lonse, ndiye kuti mayiko onse ayeneranso kufunafuna njira zolithetsera.”—Anatero ndi Gil Loescher, pulofesa wa nkhani za kugwirizana kwa mayiko.
KABANJA kachinyamata kanayamba ulendo wawo pakati pausiku. Poopa kuika moyo wawo pachiswe mwamunayo sanafune kuzengereza, ngakhale kuti m’banjamo anali ndi kamwana. Iye anali atamva kuti wolamulira wankhanza wadzikolo anali kukonza chiwembu chopha anthu m’tauniyo. Banjalo linayenda movutikira mtunda wopitirira makilomita 160 ndipo kenaka linatuluka m’dzikolo n’kukabisala m’dziko lina.
Pambuyo pake banja losauka limeneli linadziŵika padziko lonse lapansi. Mwana wawoyo dzina lake anali Yesu, ndipo makolo ake anali Mariya ndi Yosefe. Anthu ameneŵa sanathaŵe kwawo pofuna chuma ayi. Koma anathaŵa kuti apulumutse moyo. Chifukwatu chiwembu chonsecho chinali chofuna kupha mwana wawoyo!
Monganso anthu ena ambiri othaŵa kwawo, Yosefe ndi banja lake pamapeto pake anabwerera kwawo ndale zitakhalako bwino. Koma ndithudi mwana wawo anapulumuka chifukwa chakuti iwo anathaŵa mwamsanga. (Mateyu 2:13-16) Dziko limene anathaŵira, la Aigupto, m’mbuyomo linali litalandirapo anthu othaŵa kwawo chifukwa chandale ndiponso umphaŵi. Zaka zambiri m’mbuyomo, azigogo akale a Yesu anathaŵira ku Aigupto m’dziko la Kanani mutakhala chilala choopsa.—Genesis 45:9-11.
Amathaŵadi Nkhondoyo Koma Sapeza Zimene Amafuna
Zitsanzo za m’Malemba komanso zamasiku ano zimaikira umboni wakuti munthu angapulumuke ngati atathaŵira kudziko lina. Komabe, anthu a m’banja lililonse amapwetekedwa mtima akachoka kunyumba kwawo. Ngakhale nyumba yawo itakhala yonyozeka motani, anaipeza atatayirapo nthaŵi ndiponso ndalama zambiri. Komanso n’kutheka kuti makolo awo ndi amene anasiyira banjalo nyumbayo motero imawakumbutsa zambiri zokhudza chikhalidwe chawo komanso malo awo. Kuphatikizanso apo, anthu othaŵa amangotenga katundu wochepa mwinanso satenga chilichonse. Motero, nthaŵi zonse anthu othaŵa kwawo amasanduka amphaŵi, ngakhale kuti poyamba anali anthu olemera kwambiri.
Maganizo amene amakhala nawo poyamba oti apumulako pamavuto awo amatha mwamsanga akangofika pa kampu n’kuona kuti moyo wawo wonse akhalira kuchita zimene anthu amachita m’kampumo. Ndipo moyo wa m’kampu umawawa kwambiri munthu akakhalitsako, makamaka ngati sachezerana ndi eni dzikolo. Anthu othaŵa kwawo, monganso munthu wina aliyense amafuna kukhala ndi malo oti akakhala aziti kuno ndiye kwathu. Ndithu kampu ya anthu othaŵa kwawo si malo akuti munthu angalerereko ana. Kodi zidzatheka m’tsogolo muno kuti aliyense adzakhale ndi malo owanena kuti kwathu?
Kodi Njira Yabwino Ndiyo Kuwabweza Kwawo?
M’zaka za m’ma 1990, mabanja osamutsidwa kwawo pafupifupi 9 miliyoni anabwereranso kwawo. Kwa ena imeneyi inali nthaŵi yachisangalalo, ndipo anayamba kuchita zinthu zosiyanasiyana kuti abwerere mwakale. Koma ena anafooledwa nkhongono. Anangobwerera chifukwa chakuti sakanathanso kukhala m’dziko limene anathaŵiralo. Mavuto amene anakumana nawo pamene anali kunja anali ochuluka zedi mwakuti anangoti ndi bwino kubwerera kwawo, ngakhale kuti zinali zodziŵikiratu kuti akakafika akakhala pamavuto aakulu.
Ngakhale zinthu zitayenda bwino motani,
kubwerera kwawo kumakhala ndi mavuto ena chifukwa amakayambiranso kuchita zinthu zimene anali atachita kale. Magazini yotchedwa The State of the World’s Refugees 1997-98 inalongosola kuti: “Nthaŵi iliyonse anthu akasamuka amataya zinthu zofunika m’moyo wawo, monga malo, ntchito, nyumba ndiponso ziweto zawo. Ndipo nthaŵi iliyonse anthu akasamuka amayamba ntchito yovuta yoti akhazikike bwinobwino.” Pakufufuza kwina kwa anthu obwerera kwawo a m’chigawo chapakati cha mu Africa anapeza kuti “anthu othaŵa nkhondo amene anali kuthandizidwa ali m’dziko lina, amaona kuti kubwerera kwawo n’kovuta kwambiri kuposa mavuto amene ankakumana nawo m’dziko limene anathaŵiralo.”Komabe vuto lopweteketsa mutu kwambiri ndi la anthu mamiliyoni ambiri othaŵa kwawo amene amawakakamiza kubwerera kwawo iwo asakufuna. Kodi amakakumana ndi zinthu zotani akabwerera? “Anthu obwerera kwawo amakapeza kuti m’dziko lawolo anthu satsatiranso malamulo aboma, amakapezanso kuti muli umbava ndiponso chiwawa chosaneneka, muli asilikali olandidwa zida amene amavutitsa anthu wamba ndiponso muli anthu ambiri okhala ndi zida zankhondo zonyamulika,” linatero lipoti la bungwe la United Nations. Ndithudi, m’malo otere anthu osamutsidwaŵa sangathe kupeza ngakhale chitetezo chenichenicho.
Kupanga Dziko Limene Aliyense Angakhale Wotetezeka
Kusamutsa anthu mowakakamiza kapena asakufuna kwenikweni sikudzathetsa mavuto a anthu a othaŵa kwawo ngati zifukwa zimene amasamutsira anthuwo zidakalipobe. Mu 1999, mayi Sadako Ogata, amene anali mkulu woyang’anira bungwe la anthu othaŵa kwawo la United Nations High Commission for Refugees, ananena kuti: “Zimene zachitika m’zaka khumizi, ngakhalenso zimene zangochitika chaka chathachi, zikusonyezeratu poyera kuti nkhani za anthu othaŵa kwawo sizingathe kukambidwa popanda kutchulapo nkhani zokhudza chitetezo.”
Ndipo anthu ochuluka zedi padziko lonse amakhala mtima uli m’mwamba chifukwa si otetezeka. A Kofi Annan, yemwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, analongosola kuti: “M’madera ena a padziko, mayiko awonongedwa kwambiri chifukwa cha nkhondo zosiyanasiyana zapachiweniweni zimene zimachititsa kuti nzika za mayikowo zisakhale zotetezeka n’komwe. M’madera enanso anthu amaopa maboma amene safuna kuchita zinthu zothandiza anthu ndipo amazunza anthu awo owatsutsa komanso kulanga anthu osalakwa amafuko onyozeka.”
Zifukwa zikuluzikulu zimene anatchula a Kofi Annan kuti ndizo zimachititsa anthu kukhala osatetezeka ndi nkhondo, kuzunza anthu, ndiponso kulimbana ndi mafuko ena ake ndipo nthaŵi zambiri zimayamba chifukwa cha udani, kusankhana mitundu, ndiponso kusoŵa chilungamo. Zinthu zoipa zimenezi n’zovuta kuzithetsa kwenikweni. Kodi ndiye kuti vuto la anthu othaŵa kwawo lizingokulabe?
Ngati zinthu zonse zitangosiyidwa m’manja mwa anthu, ndiye kuti zikhoza kuterodi. Koma m’Baibulo, Mulungu akulonjeza kuti “aletsa nkhondo kumalekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, iye analongosolanso nthaŵi imene anthu “adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.” (Yesaya 65:21-23) Mikhalidwe yotere ingathedi kudzachotseratu vuto la anthu othaŵa kwawo. Koma kodi mikhalidweyi ingadzakhalekodi?
“Pakuti nkhondo imayambira m’maganizo mwa anthu, chonchonso mtendere umene umachititsa kuti pasakhale nkhondo uyenera kuyambira m’maganizo momwemo,” anatero mawu oyamba a bungwe la United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization. Mlengi wathu amadziŵa bwino kuti m’pofunika kuti anthu asinthe maganizo. Mneneri yemwe uja akulongosola chifukwa chimene aliyense padziko lapansi adzakhalire wotetezeka motere: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Mboni za Yehova zinatulukira kale kuti kudziŵa Yehova kungathetse tsankho ndiponso udani. M’ntchito yawo yolalikira ya padziko lonse iwo amafuna kuphunzitsa anthu khalidwe la Chikristu limene limayambitsa chikondi m’malo mwa udani, ngakhale m’mayiko amene muli nkhondo. Iwonso amathandiza othaŵa kwawo m’njira iliyonse imene angathe.
Koma iwo amadziŵanso kuti amene adzathetse vuto la othaŵa kwawo ndi Mfumu imene inasankhidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu. Ndithu iye amamvetsa kuti mposavuta kuti chidani ndiponso chiwawa chiwononge moyo wa anthu. Baibulo limatitsimikizira kuti adzaweruza aumphaŵi molungama. (Yesaya 11:1-5) Iye polamulira ali kumwamba, zimene Mulungu amafuna zidzachitika padziko lapansi, monga zimachitikira kumwamba. (Mateyu 6:9, 10) Nthaŵi imeneyo ikadzafika, palibe munthu amene adzathaŵenso kwawo. Ndipo munthu aliyense adzakhala ndi malo omati ndiye kwawo.
[Bokosi patsamba 12]
Kodi Pakufunika Chiyani Kuti Vuto la Othaŵa Kwawo Lithe?
“Kupereka zofuna za anthu osamutsidwa kwawo, kaya ndi othaŵa dziko lawo kapena osamutsidwa koma ali m’dziko lawo lomwelo, si chinthu chapafupi monga kungowapatsa zinthu zowathandiza kwa kanthaŵi kochepa chabe. Pamafunikanso kuletsa kuzunza anthu, kupha anthu ndiponso nkhondo zimene zimayambitsa vuto loti anthu azichoka kwawo. Pamafunika kuzindikira ufulu woti azibambo, azimayi ndiponso ana azikhala mwamtendere, mwabata, ndiponso mopatsidwa ulemu popanda kuthaŵa kwawo,” linatero buku lotchedwa The State of the World’s Refugees 2000.
Bokosi/Chithunzi patsamba 13]
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzathetsa Bwanji Vutoli?
“M’dziko lonse anthu adzachita zinthu zabwino ndiponso zolungama. Chifukwa chakuti aliyense adzachita zabwino, padzakhala mtendere ndi bata kosatha. Anthu a Mulungu sadzakhalanso ndi nkhaŵa zilizonse, ndipo nyumba zawo zidzakhala zamtendere ndiponso zopanda choopsa chilichonse.”—Yesaya 32:16-18, Today’s English Version.