Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mikaeli Mngelo Wamkulu Ndani?

Kodi Mikaeli Mngelo Wamkulu Ndani?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mikaeli Mngelo Wamkulu Ndani?

BAIBULO limanena kuti pali angelo mamiliyoni ambiri okhala kumalo auzimu. (Danieli 7:9, 10; Chivumbulutso 5:11) Kuyambira kuchiyambi mpaka kumapeto kwa Baibulo, Malemba ambirimbiri amasimba za angelo amene ali okhulupirikabe kwa Mulungu. Koma ndi angelo aŵiri okha amene Baibulo limachita kuwatchula mayina awo. M’modzi ndi mngelo Gabrieli, amene anapereka mauthenga ochokera kwa Mulungu kwa anthu atatu pa nthaŵi yotalikirana ndi zaka 600. (Danieli 9:20-22; Luka 1:8-19, 26-28) Mngelo wina amene anachita kutchulidwa dzina m’Baibulo ndi Mikaeli.

N’zoonekeratu kuti Mikaeli ndiye mngelo wapamwamba kwambiri. Mwachitsanzo, m’buku la Danieli, amalongosola kuti Mikaeli anali kumenyana ndi ziwanda pothandiza anthu a Yehova. (Danieli 10:13; 12:1) M’kalata youziridwa ya Yuda, akuti Mikaeli anam’tsutsa Satana pa mkangano wokhudza thupi la Mose. (Yuda 9) Buku la Chivumbulutso limasimba za Mikaeli akuchita nkhondo ndi Satana pamodzi ndi ziwanda zake ndi kuwathamangitsa kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-9) Kupatulapo iyeyu, Baibulo silisimba za mngelo winanso wokhala ndi mphamvu zambiri komanso ulamuliro waukulu chonchi pa adani a Mulungu. Motero, n’zosadabwitsa kuti Baibulo limati Mikaeli ndiye “mngelo wamkulu” kwa angelo ena onse.

Kusagwirizana Pankhani ya Amene Ali Mikaeli

Zipembedzo zambiri zachikristu, ngakhalenso za chiyuda ndi chisilamu, zili ndi ziphunzitso zotsutsana pankhani ya angelo. Zina n’zosamveka n’komwe. Mwachitsanzo buku lina lolongosola mawu a m’Baibulo lotchedwa The Anchor Bible Dictionary limanena kuti: “N’kutheka kuti pali mngelo m’modzi wapamwamba kapenanso pali kagulu ka angelo aakulu amene (nthaŵi zambiri amakhala anayi kapena asanu ndi aŵiri).” Buku linanso lotere lotchedwa The Imperial Bible Dictionary, limati Mikaeli ndi “dzina la munthu wauzimu, amene anthu akhala akutsutsana kuti mwina ndiye Ambuye Yesu Kristu, mwana wa Mulungu, kapena kuti ali m’gulu la angelo ena aakulu amene amati alipo asanu ndi aŵiri.”

Pankhani zakale za Ayuda angelo aakulu asanu ndi aŵiri ameneŵa ndi Gabrieli, Yeremieli, Mikaeli, Ragueli, Rafaeli, Sarieli, ndi Urieli. Komano Asilamu amakhulupirira kuti pali angelo aakulu anayi otchedwa, Jibril, Mikal, Izrail, ndi Israfil. Nawonso Akatolika amakhulupirira kuti pali angelo aakulu anayi, omwe amati ndi Mikaeli, Gabrieli, Rafaeli, ndi Urieli. Kodi Baibulo limati chiyani? Kodi pali angelo angapo aakulu?

Yankho la Baibulo

Baibulo silitchulapo mngelo wamkulu wina aliyense kupatulapo Mikaeli, ndiponso Malemba satchulapo mawu akuti “angelo aakulu” koma kuti mngelo wamkulu basi. Baibulo limanena kuti Mikaeli ndiye mngelo wamkulu, kusonyeza kuti alipo yekha amene amatchulidwa choncho. Motero, n’zomveka ndithu kunena kuti Yehova Mulungu anapereka udindo woyang’anira angelo ena onse kumwambako kwa mngelo m’modzi yekha basi.

Kuchotsapo Mlengi mwini, pali munthu m’modzi yekha wokhulupirika amene Baibulo limati amayang’anira angelo ndipo dzina lake ndi Yesu Kristu. (Mateyu 13:41; 16:27; 24:31) Mtumwi Paulo anachita kutchula mwachindunji za “Ambuye Yesu” ndi “angelo a mphamvu yake.” (2 Atesalonika 1:7) Ndipo Petro ananena za Yesu ataukitsidwa kuti: “Akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, ataloŵa m’mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zom’gonjera.”—1 Petro 3:22.

Ngakhale kuti m’Baibulo mulibe mawu alionse amene amachita kunena mwachimvekere kuti Mikaeli ndiye Yesu, muli lemba limene limam’khazika Yesu pamalo a mngelo wamkulu. M’kalata yake yopita kwa anthu a ku Tesalonika, mtumwi Paulo analosera kuti: “Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka.” (1 Atesalonika 4:16) Lemba limeneli likulongosola za Yesu atayamba kulamulira monga Mfumu ya Umesiya ya Ufumu wa Mulungu. Koma, likuti akulankhula ndi “mawu a mngelo wamkulu.” Onaninso kuti, likuti ali ndi mphamvu zoukitsa akufa.

Ali padziko lapansi monga munthu, Yesu anaukitsa anthu angapo. Kuti atero, anagwiritsa ntchito mawu ake pofuula molamulira. Mwachitsanzo, poukitsa mwana wamwamuna wa mayi wina wamasiye amene anafa mumzinda wa Nayini, iye anati: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.” (Luka 7:14, 15) Nthaŵi ina, atangotsala pang’ono kuukitsa mnzake Lazaro, Yesu ‘anafuula ndi mawu aakulu akuti, ‘Lazaro, tuluka!’’ (Yohane 11:43) Koma panthaŵiyi Yesu anali chabe kulankhula monga munthu wangwiro.

Yesu weniweniyo ataukitsidwa, “anam’kwezetsa” kumwamba kukhala cholengedwa chauzimu. (Afilipi 2:9) Simunthunso ayi, motero ali ndi mawu a mngelo wamkulu. Motero pamene lipenga la Mulungu linalira poitana “akufa mwa Ambuye” kuti aukitsidwe n’kupita kumwamba, Yesu anafuula molamulira ndipo panthaŵiyi anatero ndi “mawu a mngelo wamkulu.” Apa n’zomveka kwabasi kunena kuti mngelo wamkulu yekha ndiye amene angafuule “ndi mawu a mngelo wamkulu.”

Inde alipo angelo ena amaudindo apamwamba, monga aserafi ndi makerubi. (Genesis 3:24; Yesaya 6:2) Koma, Malemba amatchula kuti Yesu Kristu woukitsidwayo ndiye mngelo wamkulu pakati pa angelo ena onse. Mikaeli mngelo wamkulu ndiye ameneyu.