Kodi Pali Vuto Ngati Nditachitako Chidwi Pang’ono Ndi Zamatsenga?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Pali Vuto Ngati Nditachitako Chidwi Pang’ono Ndi Zamatsenga?
KODI achinyamata amachitadi chidwi ndi zamatsenga? Gulu lina la ofufuza linayesa kufufuza zimenezi ku masukulu 115 pofunsa ana asukulu amene akuphunzira mu sitandadi 5 mpaka 8 ndiponso a kusekondale. Zimene anapeza atafufuza ndi izi: Ana opitirira theka la ana onse amene anawafunsa anangonena kuti amachita chidwi ndi zinthu zamizimu ndipo pafupifupi mmodzi pa anayi alionse ananena motsimikiza kuti “amachita nazo chidwi kwambiri.”
Ofufuza a payunivesite ya Alaska ku Anchorage analemba kuti: “Nkhani za m’manyuzipepala ndiponso m’magazini zokhudza kuchuluka kwa zochita zachipembedzo cha Satana . . . zawanda m’zaka zaposachedwapa.” Akatswiri akuti palibe umboni weniweni wakuti achinyamata ambiri akugwirizana ndi zinthu zausatana. Ngakhale zili choncho, si zoliranso kufunsa kuti achinyamata ambiri akuchita chidwi ndi zinthu zausatana ndiponso zamatsenga, ngakhale atamangochita nazo chidwi mwa apo ndi apo chabe.
Motero achinyamata ena angafunse kuti, ‘Kodi pali vuto ngati nditachitako chidwi pang’ono ndi zamatsenga? Kuti tiyankhe, tiyeni tione njira zina zimene achinyamata amayambira kuchita nawo zamatsenga.
Zamatsenga N’zokopa
Nkhani ina m’nyuzi yoona za ku United States ndiponso padziko lonse yotchedwa U.S.News & World Report inanena kuti “ana ndiponso achinyamata amasiku ano angathe kuona kapena kumva zinthu zochuluka, zimene kaŵirikaŵiri zimakhala zosokoneza maganizo komanso zimene sizikanatheka n’komwe kuziganizira ngakhale zaka 20 zapitazo.” Chidwi chofuna kudziŵa zinthu n’chimene chimawachititsa achinyamata ambiri kuŵerenga mabuku ndiponso magazini, kuonera mavidiyo kapena kufufuza pamene pali nkhani zamatsenga pa intaneti.
Malingana ndi nkhani za pa intaneti za bungwe lofalitsa nkhani la BBC, akuti mapulogalamu otchuka a pa TV amene amaonetsa zaufiti ndiponso za mizukwa “amalimbikitsa kuti ana azichita chidwi ndi zaufiti.” Nazonso nyimbo zolira mogunda kwambiri zimakhala ndi mawu olimbikitsa chiwawa kapena nkhani za ziwanda. Wolemba nyuzipepala wina ku Toronto dzina lake Tom Harpur analemba m’nyuzipepala yotchedwa The Sunday Star kuti: “Ndiyenera kunena chenjezo lamphamvu kwambiri la zomwe zikuchitika [pa nkhani ya nyimbo]. . . . Sindinaone chinthu china chilichonse choipa chonchi. Nyimbozi zimangotchula za misala, kuchita zinthu zoipa, za uchiwanda, kukhetsa mwazi, kutembererana, kuchita ziwawa zosiyanasiyana, kugwiririrana, kudzipundula, kuphana ndiponso kudzipha. Mitu ya nyimbozi imangokhala ya imfa ndiponso chiwonongeko, kulosera zatsoka, kukana zinthu zonse zimene zili zabwino n’kuvomereza zinthu zonse zimene zili zoopsa ndiponso zoipa kwambiri.”
Kodi kumvetsera nyimbo zamtunduwu kumachititsadi kuti munthu akhale ndi makhalidwe owononga? Zinaterodi nthaŵi inayake kwa wachinyamata wa zaka 14 ku United States amene anabaya amayi ake mpaka kufa kenaka n’kudzipha yekha. M’zipupa za m’chipinda mwake anamatamo zithunzi zambirimbiri za anthu oimba nyimbo zogunda kwambiri. Zimenezi zitachitika, abambo ake anachonderera kuti: “Chonde auzeni makolo asatope kuonetsetsa nyimbo zimene ana awo amamvera.” Iwo ananena kuti patatsala mlungu umodzi kuti mwana wawo aphe amayi ake, iye ankangoimba nyimbo ya chamba cha rock “imene imatchula zokhetsa mwazi ndiponso kupha amayi ako.”
Ndiye palinso maseŵera amene munthu amatsanzira munthu winawake, ndipo maseŵera ena otere amafunika kuti anthu amene akuseŵerawo achite zimene mfiti zimachita ndiponso zinthu zina zimene amatsenga amachita. Maseŵera ambiri otere amasonyeza zinthu zoopsa zochitidwa ndi ziwanda. *
Komabe bungwe la ofufuza lotchedwa Mediascope linati: “Umboni umasonyeza kuti kukonda nyimbo zolira mogunda kwambiri kungasonyeze kuti munthu wotere angathe kusanduka munthu wopatuka pagulu, wogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, wosokonekera mutu, woti angathe kudzipha . . . kapena wochita zinthu zoopsa paunyamata, koma si kuti nyimbozo ndizo zimayambitsa makhalidwe ameneŵa. Akuti mwina achinyamata amene panopa akulimbana ndi mavuto ameneŵa angatengeke ndi nyimbozi chifukwa chakuti mawu ake amatchula zinthu zimene zikuwavutitsadi iwowo.”
N’kutheka kuti ofufuza onse sangavomereze kuti munthu ukamamvetsera nyimbo zausatana pamakhala zotsatirapo zoipa. Koma kodi tinganenedi kuti kukonda mavidiyo, nyimbo kapena maseŵera amene amalimbikitsa zachiwawa kapena kudzipha si koopsadi? Komatu, kwa Akristu kuchita chidwi n’zamatsenga kungawabweretsere mavuto akulu.
Mmene Mulungu Amaonera Zamatsenga
Pa 1 Akorinto 10:20, mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.” Kodi ziwandazi ndani kwenikweni, ndipo n’chifukwa chiyani kugwirizana nazo kuli koopsa kwambiri? Kunena mosapita m’mbali, ziwandazi zinali angelo poyamba ndipo zinakonda kutsatira Satana Mdyerekezi. Satana amatanthauza kuti “Wotsutsa” ndipo Mdyerekezi amatanthauza kuti “Woneneza.” Baibulo limati mngelo ameneyu yemwe kale anali mwana wa Mulungu anadzipanga yekha wotsutsa ndiponso woneneza poukira Mulungu mwadala. Patapita nthaŵi, ananyengerera angelo ena kuti agwirizane naye maganizo ake oukirawo. Motero angelo amene anagwirizana nayeŵa anasanduka ziwanda.—Genesis 3:1-15; 6:1-4; Yuda 6.
Yesu anatchula Satana kuti “mkulu wa dziko ili lapansi.” (Yohane 12:31) Satana ndi angelo ake ali ndi “udani waukulu” podziŵa kuti atsala pang’ono kuwonongedwa. (Chivumbulutso 12:9-12) N’zosadabwitsa kuti anthu amene ayamba kukhudzidwa ndi ziwanda aona kuti ziwandazo n’zolusa kwambiri. Mkazi wina wa ku Suriname amene anakulira m’banja limene linkachita zamizimu anadzionera yekha mmene ziwanda “zimakondera kuzunza anthu amene sakufuna kuzimvera.” * Motero kugwirizana nazo zolengedwa zauzimu zankhanzazi mwa njira iliyonse n’koopsa kwambiri!
Ndiye n’chifukwa chake Mulungu analamula anthu ake akale, Aisrayeli kupewa zochita zonse zamatsenga. Deuteronomo 18:10-12 amachenjeza kuti, “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” Nawonso Akristu anachenjezedwa kuti “anthu amene amachita zamizimu” Mulungu adzawawononga. (Chivumbulutso 21:8, NW) Ngakhale kungochita chidwi pang’ono ndi zamatsenga n’koletsedwa ndi Mulungu. Baibulo limalamula kuti, “Musakhudza kanthu kosakonzeka.”—2 Akorinto 6:17.
Kusiyana Nazo Zamatsenga
Kodi munachitako chidwi pang’ono ndi zamatsenga musakudziŵa kuti mukulakwa? Ngati zili choncho, taonani zimene zinachitika mu zaka za zana loyamba mumzinda wa Aefeso. Anthu ambiri kumeneko ‘ankachita zamatsenga.’ Koma anthu ena anachita chidwi kwambiri ndi ntchito zamphamvu zimene mtumwi Paulo anachita pothandizidwa ndi mzimu woyera. Zitatero n’chiyani chinachitika? “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anaŵerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu. Chotero mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.”—Machitidwe 19:11-20.
Deuteronomo 7:25, 26) Tayani chinthu chilichonse chimene chingagwire ntchito poombeza, monga nsupa kapena namulondola. Ndiponso tayani nyimbo kapena mavidiyo amene amaonetsa zausatana.
Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Zikutiphunzitsa kuti ngati munthu akufuna kupewa mphamvu yaikulu ya ziwanda, ayenera kuwononga zinthu zonse zogwirizana ndi kulambira Satana! Zimenezi zikuphatikizapo zinthu zonse monga mabuku, magazini, zithunzi, mabuku a maseŵero, mavidiyo, zithumwa ndiponso zinthu zonse za uchiwanda zopezeka pa intaneti. (M’pofunika kulimba mtima ndiponso kutsimikiza ndithu kuti mutayedi zinthu zimenezi. Koma mukhoza kupindula kwambiri. Mkazi wina wachikristu dzina lake Jean * anagula maseŵera enaake a pakompyuta amene ankaoneka ngati abwinobwino poyamba. Atayamba kudziŵa bwino kuchita maseŵerawo, anatulukira kuti zochitika zina zamaseŵerawo zinkakhudza zamizimu. Posakhalitsa anayamba kulota maloto oopsa! “Ndinadzuka pakati pausiku, n’kuphwanyiratu zimbale zoika m’komputa zimene munali maseŵerawo,” anatero Jean. Ndiyeno chinachitika n’chiyani? “Kuyambira pamenepo palibenso chimene chinandivutitsa,” iye anatero.
Ngati mutasonyeza kuti mwatsimikizadi kusiyana nazo, zinthu zingakuyendereni bwino. Takumbukirani mmene Yesu anasonyezera kuti sakufunadi pamene Mdyerekezi anayesa kum’nyengerera kuti amulambire. “Yesu ananena kwa iye, ‘Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Yehova Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekha yekha udzam’lambira.”’ Pomwepo Mdyerekezi anamsiya iye.”—Mateyu 4:8-11.
Musalimbane Nazo Panokha
Mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti Akristu onse ‘ali nako kulimbana . . . ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’ (Aefeso 6:12, NW) Koma musayese kulimbana ndi Satana pamodzi ndi ziwanda zake muli nokha. Pemphani makolo anu ngati amaopa Mulungu ndiponso akulu a mumpingo wanu wachikristu kuti akuthandizeni. Zingakhale zochititsa manyazi kuti muulule zimene mwakhala mukuchita, koma kuteroko kungachititse kuti mulandire thandizo pamapeto pake.—Yakobo 5:14, 15.
Komanso musaiwale kuti Baibulo limati: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:7, 8) Inde, muli naye woti akuthandizeni, Yehova Mulungu! Iye angakuthandizeni kuti muwonjoke mumsampha wa zamatsenga.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Maseŵero Odziyerekeza Kukhala Munthu Wotchuka Angadzetse Ngozi Iliyonse?,” mu Galamukani! ya September 8, 1999.
^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Kuchotsa Goli la Kukhulupirira Mizimu” m’magazini inzake ya ino ya Nsanja ya Olonda ya September 1, 1987, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 20 Dzinali talisintha.
[Chithunzi patsamba 20]
Tayani zinthu zonse zimene zimagwirizana ndi kulambira Satana
[Chithunzi patsamba 20]
Chenjerani ndi zinthu za pa intaneti zimene zimalimbikitsa zamizimu