Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbidzi—Hatchi ya mu Africa Yongodziyendera Mmene Ikufunira

Mbidzi—Hatchi ya mu Africa Yongodziyendera Mmene Ikufunira

MbidziHatchi ya mu Africa Yongodziyendera Mmene Ikufunira

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! MU AFRICA

MBIDZI zambirimbiri zikungodzithamangira m’dera la udzu la mu Africa. Thupi lawo lamizeremizere pamodzi ndi makosi awo okhala ndi bweya wambiri zikugwedezeka mogwirizana ndi chimdidi chawo. Mapazi a mbidzizo akamaponda pansi poumapo, m’chidikha chonsecho mukungomveka kuti likitilikiti. M’mbuyomu zikusiya chifumbi cha katondo chitangoti koboo m’mwamba ndipo chikuonekera kutali kwambiri. Zikungothamanga mwaphee, osatekeseka ndi china chilichonse.

Zikuyamba kuchepetsa liŵiro ngati kuti zamva chinachake chimene ife sitikuchiona ndipo kenaka zikuimiratu. Ndiyeno zikuyamba kumwetula udzu woumawo ndi mano awo amphamvu komanso ochindikala. Gulu la mbidzili n’latcheru, ndipo zikakhalakhala zikumadzutsa mitu, kumvetsera bwinobwino, ndiponso kununkhiza kumene kukuchokera mphepo. Kenaka chifukwa cha mphepo, zikumva kubangula kwa mkango womwe uli kutali, ndipo zikuchita mantha. Kulira kumeneku zimakudziŵa bwino. Mbidzizi zikuimitsa makutu awo, udzu uli lendelende kukamwa, n’kucheukira kumene kukumveka kubangulako. Poona kuti palibe choopsa chilichonse pafupi, zikuŵeramitsanso makosi awo n’kumapitiriza kudya.

Dzuŵa likayamba kutentha kwambiri ziyamba kusuntha. Pano tsopano zamva kununkhira kwa madzi, ndipo zikuloŵera kumene kuli mtsinje. Zikuima pamtunda n’kumayang’ana madzi akuda amene akuyenda pang’onopang’ono mumtsinjemo, ndipo zikufwentheza ndiponso kupalasa dothi loumalo. Zikuzengereza kaye, chifukwa zikudziŵa kuti ngakhale kuti kumtsinjeko kwangoti zii kumakhala chinthu chinachake choopsa. Koma ludzu lazipweteka kwambiri, ndipo zina zangoyambapo kupita kumtsinjeko. Kenaka zonse pamodzi zangoti ndondondo, kuthamangira kumtsinjeko. Ndipo mosiyiranasiyirana zonse zikumwa madziwo mpaka kuthetseratu ludzu lawo, basi n’kutembenuka kuloŵeranso m’chidikha chopanda malirecho.

Pofika madzulo gulu la mbidzilo likungoyenda mwachifatse m’maudzu aataliatali. Si kuchititsa kaso kwake mmene zikuonekera poyenda m’dera lokongola la maudzu la mu Africa, kwinakunso dzuŵa likuloŵa, litangoti psuu.

N’zamizeremizere Ndipo Zimakondana

Mbidzi zili ndi chizoloŵezi chimene zimachita tsiku lililonse. Nthaŵi zonse sizikhazikika pofunafuna chakudya ndi madzi. Zikamadya pamtetete zimaoneka kuti n’zaukhondo komanso n’zonenepa, ndiponso kuti chikopa chake chamizeremizere chimakuta bwinobwino thupi lake lojintcha bwinobwino. Mizere ya mbidzi n’njolembeka mosiyana, ndipo ena amati palibe mbidzi iliyonse imene mizere yake imafanana ndendende ndi ya mbidzi ina. Mizere yake yoyera ndi yakuda imaoneka kuti n’njosiyana kwambiri ndi ya nyama zina za m’chigwacho. Komabe imaoneka mokopa mtima ndiponso moyenereranadi ndi tchire la mu Africa.

Mbidzi ndi nyama zokondana kwambiri. Nyamazi zimakondana kwambiri mwakuti zingakhale paubwenzi kwa moyo wawo wonse. Ngakhale kuti pagulu lalikulu nyamazi zimakwana zikwi zambiri, gululo limakhalanso ndi timabanja tokhala ndi mbidzi yamphongo ya akazi angapo. Kabanja kameneka kamachita zinthu mwadongosolo pom’patsa aliyense m’banjamo udindo. Mbidzi yaikazi yolamulira gululo ndi imene imaona nkhani zokhudza kumene banjalo liloŵere. Iyo imatsogola, ndipo mbidzi zina zazimuna pamodzinso ndi mathole zimatsatira pamzere umodzi mogwirizana ndi udindo wawo. Komabe mbidzi yamphongo ndiyo imalamulira mbidzi zonsezo. Ngati ikufuna kuti banja lake liloŵere kwina, imapita kwa mbidzi yaikazi yotsogolera ija n’kuikankhira kumene ikufunako.

Mbidzi zimakonda kuchotsana fumbi kapena zitsotso zokanirira m’bweya wawo, ndipo kaŵirikaŵiri mungathe kuziona zikukhulana cha m’nthiti, m’mapewa, ndi kumsana. Zikuoneka kuti kukhulana kumachititsa kuti nyamazi zizikondana kwambiri ndipo zimayamba kuchita zimenezi zidakali mathole a masiku ochepa chabe. Ngati palibe mbidzi ina m’banjamo yoti ikande zinzake, mbidzi zimene zikumva kunyerenyetsa zimadzikanda zokha podzigubuduza padothi kapena podzikhulitsa kumtengo, kuchulu, kapena kuzinthu zina zolimba.

Kusunga Phukusi la Moyo Movutikira

Mbidzi zili ndi zinthu zambiri zoopseza moyo wawo. Mikango, nkhandwe, afisi, anyalugwe, ndiponso ng’ona zimafuna kugwira nyama yolemera makilogalamu 250 imeneyi. Mbidzi ingathamange mtunda wa makilomita 55 pa ola limodzi, koma nthaŵi zina imapezedwa mwadzidzidzi ndi nyama zoopsa zomwe zimangobwera modzidzimutsa ndiponso mobisalira. Mikango imazidikirira itabisala, ndipo ng’ona nazo zimangoti duu m’madzi akuda, komanso akambuku amazidikirira mumdima pamene izo sizikuona.

Mbidzi zimatetezedwa ngati m’gulu lawo muli mbidzi zatcheru ndiponso zochita zinthu mogwirizana. Ngakhale kuti mbidzi zina zimagona usiku, nthaŵi zonse pamakhala zina zimene zimakhala tcheru, n’kumamvetsera ndi kulondera. Mbidzi ina ikaona nyama yoopsa ikubwera poteropo, imafwenthera mochenjeza gulu lonselo. Nthaŵi zambiri, ngati mbidzi ina pagulupo ikudwala kapena ngati ili yokalamba mwakuti siingathamange ngati zinzakezo, mbidzi zinazo zimachepetsa dala liŵiro kapena zimadikirira mbidzi yochedwayo kuti ifikenso pali gululo. Zinthu zikaipa, mbidzi yaimuna ija imatchinjiriza mbidzi zazikazizo potchingira nyama yoopsayo, ndipo imakhala ngati ikufuna kuiluma ndi kuimenya mateche kuti gululo lipeze mpata wothaŵira.

Zimene anaona katswiri wina wa zinthu zachilengedwe wotchedwa Hugo van Lawick m’chidikha cha Serengeti mu Africa zikusonyeza kugwirizana kwa mabanja ambidzi. Iye analongosola kuti panali gulu la nkhandwe limene linkathamangitsa gulu la mbidzi, ndipo anati pagulu lambidzilo nkhandwezo zinatengetsa mbidzi ina yaikazi pamodzi ndi thole lake ndiponso mbidzi ina ya chaka chimodzi. Mbidzi zina zonse zitathaŵa, mbidzi yaikaziyi pamodzi ndi ya chaka chimodziyo zinalimbana ndi nkhandwezo mwachamuna. Posapita nthaŵi nkhandwezo zinalusa kwambiri, ndipo mbidzi yaikazi ija ndi mbidzi yachaka chimodziyo zinayamba kutha mphamvu. Zinali zokayikitsa kwambiri kuti mbidzizi zingapulumuke. Van Lawick amakumbukira zofoola zimene ankaonazo motere: “Mwadzidzidzi ndinayamba kumva likitilikiti ndipo nditaponya maso anga komweko, ndinadabwa kuona mbidzi khumi zikubwera poteropo mwaliŵiro la mtondo wadooka. Pakanthaŵi kochepa gulu limeneli linazungulira mbidzi yaikaziyo ndi ana ake aŵiri aja ndipo kenaka, mbidzi zonsezo zinatembenuka, n’kumathamanga pamodzi mothithikana, kuloŵera kumene kunachokera mbidzi khumi zija. Nkhandwezo zinathamangitsa mbidzizo mtunda wa mamita mwina 50 kapena kuposa pamenepo koma zinakanika kugwirapo mbidzi iliyonse pagulupo ndipo posapita nthaŵi nkhandwezo zinangoleka.”

Kulera Ana

Mbidzi yaikazi imateteza kwambiri mwana wake akangobadwa ndipo poyamba imam’patula m’gululo. Panthaŵi imene tholeli limakhala lokha ndi mayi wake yekha, limayamba kukondana naye kwambiri mayi wakeyo. Tholeli limaloweza mizere ya mayi wake yoyera ndi yakuda imene imakhala yosiyana ndi ya mbidzi ina iliyonse. Kenaka, limaloŵeza kulira kwa amayi ake akamaliitana, fungo lawo, ndiponso kalembedwe ka mizere yawo ndipo sililolanso mbidzi ina iliyonse yaikazi.

Mathole a mbidzi sabadwa ndi mizere yoyera ndi yakuda yangati ya makolo awo. Mizere yawo imakhala yofiirira ndipo imadzasanduka yakuda akamakula. Mathole ochokera m’mabanja osiyanasiyana a m’gulu lalikulu la mbidzizo amaseŵerera pamodzi. Amathamangitsana, amaponya miyendo ndiponso kuthamanga m’chigulu cha mbidzi zikuluzikuluzo, zimene nthaŵi zina zimachita nawo maseŵerawo. Matholeŵa amathamanga ndi timiyendo tawo tanthete, pochita maseŵera othamangitsa mbalame ndiponso nyama zina zing’onozing’ono. Ana a mbidzi ndi okongola kwambiri mukamawaona chifukwa amakhala ndi timiyendo tatitali ndiponso towonda, maso akuda aakulu, ndiponso ubweya wowala komanso wofewa bwino.

Zimangodziyendera Ndipo N’zosangalatsa

Masiku ano mungathebe kuona magulu aakulu a mbidzi akungodzithamangira m’dera lalikulu ndiponso lokongola la udzu wa mu Africa. Si mmene zimakongolera kuziona.

Mbidzi zili ndi mizere yosiyanasiyana yoyera ndi yakuda ndipo zimatetezana kwambiri m’banja mwawo ndiponso zimangodziyendera m’tchire zili phee. Nanga kodi ndani amene angatsutse kuti mbidzi ndi nyama zochititsa kaso kwambiri ndiponso zokongola? Mukaidziŵa bwino nyama imeneyi mungathe kudziŵa yankho la funso limene linafunsidwa zaka masauzande angapo m’mbuyomu, lakuti: “Ndani walola mbidzi ituluke yaufulu?” (Yobu 39:5) Yankho lake n’lachidziŵikire kuti, ndi amene anakonza zinthu zonse zamoyo, Yehova Mulungu.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi N’chifukwa Chiyani Mbidzi Zili ndi Mizeremizere?

Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zimasanduka zamoyo zina pakapita nthaŵi yaitali amalephera kulongosola chifukwa chimene mbidzi zilili ndi mizeremizere. Ena akhala akuganiza kuti mizereyi imateteza mbidzizi kunyama zina. Komabe pali umboni wakuti mikango ndiponso nyama zoopsa zina zikuluzikulu siziopa mizere ya mbidziyi ngakhale pang’ono.

Anthu ena amati mizereyi imakopa mbidzi zazimuna kapena zazikazi kuti zizifuna kukwerana. Komabe, pakuti mbidzi zonse zili ndi mizeremizere yofanana ndiponso sizitengera kuti ndi yaikazi kapena ndi yaimuna, zikuoneka kuti chimenechi n’chifukwa chosamveka.

Enanso amaganiza kuti mbidzi zinasanduka n’kukhala ndi mizere yoyera ndi yakuda n’cholinga choti zisamatenthedwe kwambiri ndi dzuŵa la mu Africa. Ngati zimenezi zili zoona nanga n’chifukwa chiyani nyama zina zilibe mizere yotere?

Enanso ambiri amaganiza kuti mbidzi zinasanduka zamizeremizere kuti zizivuta kuziona zikakhala m’tchire. Asayansi atulukira kuti kutentha kwambiri kwa m’zidikha za ku Africa kumabisadi maonekedwe a mbidzi, motero zimavuta kuziona ngati muli kutali. Komabe, mbidzizi sizipindula m’njira iliyonse posaoneka bwinobwino ngati zili kutali chifukwa chakuti mikango, imene ili mdani wamkulu kwambiri wa mbidzi, umagwira mbidzizi pokhapokha ukaziyandikira.

Akutinso mbidzizi zikamathamanga m’chigulugulu mizere yakeyo imasokoneza mikango imene imazisaka, motero imakanika kuthotha mbidzi imodzi yokha. Komatu, zoona zake n’zakuti kufufuza kumene anachita kokhudza nyama zakutchire kwasonyeza kuti mikango imatha kugwira mbidzi mosavutikira monga mmene imagwiriranso nyama zina.

Chinthu chinanso chovuta kwambiri kulongosola pa nkhaniyi n’chakuti mizere ya mbidzi nthaŵi zina imapweteketsanso mbidzizo. Usiku, m’chigwa chowala mbee chifukwa cha mwezi, mizere ya mbidzi yoyera ndi yakudayo imachititsa kuti zizionekera kutali kwambiri kuposa nyama zina zimene zili ndi mtundu umodzi wokha. Pakuti mikango imakonda kusaka usiku, ndiye kuti mizereyi ingapweteketse kwambiri mbidzizi.

Ndiye kodi mbidzi zinakhala bwanji za mizeremizere? Zimenezi tingazimvetse poganizira za mawu osapita m’mbali aŵa akuti: “Dzanja la Yehova lichita ichi.” (Yobu 12:9) Ndithudi, Mlengi anapanga zachilengedwe zapadziko lapansi kuti zikhale ndi zinthu zinazake zothandiza kuti zikhale ndi moyo pa zifukwa zimene anthu sangathe kuzidziŵa bwinobwino. Palinso chifukwa china chimene zinthu zamoyo anazipangira kukhala zokongola. Zimachititsa anthu kusangalala nazo kwambiri. Inde, chifukwa cha kukongola kwa zachilengedwe anthu ambiri masiku ano amaganiza mmene anaganizira Davide kalekale ponena kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24.