Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsiku Losangalatsa Kwambiri M’moyo Wathu”

“Tsiku Losangalatsa Kwambiri M’moyo Wathu”

“Tsiku Losangalatsa Kwambiri M’moyo Wathu”

TSIKU laukwati ndi nthaŵi yosangalatsa kwambiri. Mabanja ambiri amanena kuti: “Linali tsiku losangalatsa kwambiri m’moyo wathu.” Koma tsikuli lingathenso kukhala losautsa kwambiri. Mkwati ndi mkwatibwi komanso achibale awo angatheretu mphamvu chifukwa ayenera kuchita ndiponso kukonzekera zinthu zambiri, komanso patsikulo mkwati ndi mkwatibwi amakumana ndi anthu ochuluka.

Chikwati ndi chiyambi cha moyo watsopano wa anthu amene akukwatiranawo. Koma si chikhudza anthu okhawa. Nthaŵi zambiri abale a munthuyo amavutika maganizo chifukwa chakuti ukwati wa mwana wawo wamkazi, wamwamuna, wa achemwali kapena wa achimwene umatanthauza kuti wokondedwayo akuyambitsa banja lake.

Zochitika za pa chikwati zimasiyanasiyana m’mayiko onse, motero sitingathe kuzifotokoza zonse panopa. Nkhanizi zifotokoza zimene anthu a m’mayiko a azungu ndiponso m’mayiko ena amene amatsatira zochitika zimenezo akhala akuchita. Kumayikoŵa, kukwatira kapena kukwatiwa kumawonongetsa chuma chambiri. Anthu ena amawononga ndalama zochuluka kwambiri polipirira zinthu zodzagwiritsa ntchito patsiku laukwatiwo, monga kubwereka holo kapena lesitilanti yokachitirako madyerero. Akuti ku Italy kaŵirikaŵiri ukwati umadya ndalama zoposa madola 10,000. Koma ku Japan ndi kwinanso ndalamazo zimaposa pamenepo. Nthaŵi zambiri makolo ndi amene amapereka ndalama osati mkwati ndi mkwatibwi.

Mapwando aukwati amalemeretsa mabungwe ambiri. Mabungwe ambiri amalimbikitsa malingaliro akuti ukwati ukhale wa “mbambande,” wosasoŵa kanthu. Ndiponsotu, mabungweŵa amanyengerera anthu pomati, “ili ndi tsiku losangalatsa kwambiri m’moyo wanu!” Motero mabungweŵa amasatsa anthuŵa zinthu zimene amati ndi “zofunika kwambiri” kuti tsiku laukwati wanu likhale “lambambande.” Akhoza kukukonzerani makadi anuanu oitanira anthu, kayanso chovala chaukwati chimene “mumachiganizira” kwambiri kapena zovala za anyamata ndi atsikana operekeza paukwati. Ndiye palinso maluŵa, galimoto yapamwamba yokwera akwati, mwina pangakhalenso holo yokachitirako madyerero, munthu wojambula zithunzi, a bandi ndi zinthu zina ndi zina. Zinthu zimene mkwati ndi mkwatibwi angazifune paukwati wawo ndiponso ndalama zimene ayenera kuwonongera zinthuzo, zimapangitsa azibambo awo ambiri kuvutavuta.

M’zikhalidwe zosiyanasiyana, anthu amatsatira kwambiri mwambo wawo akamachita zinthu. Pamakhala njira imene amatsatira pochita zinthu zosiyanasiyana ndipo amafuna kuona kuti mkwati ndi mkwatibwi akuchita zimenezi. Inde, pamakhala zinthu zambiri zoyenera kuzikumbukira, komatu pamangokhala nthaŵi yochepa chabe yolinganiza zonsezo.

Ndiye kodi zimenezi n’zosangalatsa kapena n’zotopetsa? Kaya mukuganiza kuti n’zosangalatsa kapena kuti n’zotopetsa, kuganizira zinthu zonse zimene phwando laukwati lingakhale nazo kumabweretsa mafunso ambirimbiri. Kodi masiku ano akamati kukwatira kapena kukwatiwa ndiye kuti n’chiyani? Kodi munthu akachita zonsezi mpamene tingati wachitadi ukwati weniweni? Kodi munthu angathane nazo bwanji zinthu zosautsa zonsezi?

Ngakhale kuti pamakhala zinthu zosautsa zonsezi, anthu ambiri anakhoza bwinobwino kulinganiza zinthu zofunika ndipo zinthu zinawayendera bwino kwambiri patsikulo. Zimene anachita zingathandize ena amene akukonzekera kuchita ukwati woterowo. Ndiponso mfundo za m’Baibulo zingathandize pokonzekera phwando laukwati, kuti potero tsikulo lidzakhale losangalatsa kwambiri ndiponso lolimbikitsa kwa anthu onse.