Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziona Ngati Wolakwa N’koipa Nthaŵi Zonse?

Kodi Kudziona Ngati Wolakwa N’koipa Nthaŵi Zonse?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kudziona Ngati Wolakwa N’koipa Nthaŵi Zonse?

ANTHU ambiri masiku ano amaona kuti kudziona ngati wolakwa n’kosafunika. Iwo amaganiza ngati mmene ankaganizira munthu wina woganiza kwambiri dzina lake Friedrich Nietzsche, amene anati: “Kudziona ngati wolakwa ndiko matenda oopsa kwambiri amene sanalekepo kugwira anthu.”

Koma ofufuza ena ayamba kunena mosiyana ndi zimenezo. Susan Forward yemwe n’ngophunzira kwambiri komanso n’ngodziŵika padziko lonse kuti ndi dokotala ndiponso wolemba mabuku ananena kuti, “Kudziona ngati wolakwa n’kofunika pakuti kumasonyeza kuti chinachake chikachitika chimakukhudza monga munthu wabwinobwino komanso woganizira zochita zako. Kumakhala ngati ndi mbali ina ya chikumbumtima.” Nanga kodi pamenepa, ndiye kuti kudziona ngati wolakwa n’koipa nthaŵi zonse? Kodi zingatheke kuti nthaŵi zina kudziona ngati wolakwa kungathandize kwambiri?

Kodi Kudziona Ngati Wolakwa N’kutani?

Kudziona ngati wolakwa kumayambika tikazindikira kuti talakwira munthu winawake amene timam’ganizira kapenanso tikalephera kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene tikuonera kuti ndimo mmene zinayenera kukhalira. Buku lina lomasulira mawu linati, kudziona ngati wolakwa kumatanthauza “kuzindikira kulakwa kwako chifukwa cholephera kuchita chinachake, kupalamula, kuphwanya lamulo, kapena kuchita tchimo.”

M’malemba Achihebri, munthu wachiisrayeli ankakhala wolakwa ngati atalephera kuchita zimene Malamulo a Mulungu amanena ndipo ambiri mwa malamulo ameneŵa ali m’mabuku a m’Baibulo a Levitiko ndiponso Numeri. Komanso m’Malemba Achigiriki Achikristu nkhani ya kukhala wolakwa imakhudza zinthu zikuluzikulu zolakwira Mulungu.—Marko 3:29; 1 Akorinto 11:27.

Tsoka ilo, tikhoza kumadziona ngati olakwa pamene sizili choncho. Mwachitsanzo, munthu akakhala wosafuna kulakwitsa kanthu kalikonse ndiye akamadzipatsa zinthu zovuta kuchita, ndipo zikam’kanika akhoza kukhala ndi maganizo osayenera odziona ngati ndi wolakwa. (Mlaliki 7:16) Kapena tikhoza kuchititsa kuti maganizo oti talakwa akule n’kufika pokhala ndi manyazi aakulu mapeto ake n’kudzilanga n’zopanda pake. Ndiye nanga phindu lodziona ngati wolakwa lili pati kwenikweni?

Nthaŵi Zina Kudziona Ngati Wolakwa N’kwabwino

Kudziona ngati wolakwa kungakhale kothandiza m’njira zosachepera zitatu. Mbali yoyamba n’njakuti, kumasonyeza kuti tikudziŵa makhalidwe oyenera. Kumasonyeza kuti chikumbumtima chathu chikugwira ntchito. (Aroma 2:15) Kwenikweni buku limene linafalitsidwa ndi bungwe loona za matenda a misala lotchedwa American Psychiatric Association limati ngati munthu sadzionga ngati wolakwa, ndiye kuti ali ndi khalidwe limene lingathe kuvulaza anthu ena. Anthu amene chikumbumtima chawo sichigwira bwino ntchito yake amakhala ndi vuto lozindikira kusiyana kwa chinthu chabwino ndi choipa, ndipotu zimenezi n’zoopsa.—Tito 1:15, 16.

Mbali yachiŵiri n’njakuti tikakhala ndi chikumbumtima chomadziona kuti talakwa zimatithandiza kusachita zinthu zimene anthu safuna. Zili ngati mmene zimakhalira tikamamva kuŵaŵa penapake m’thupi, timadziŵa kuti mwina tikudwala matenda ena ake. Chonchonso tikamawawidwa maganizo chifukwa choona kuti talakwa, timadziŵa kuti sitilibwino pa nkhani ya khalidwe kapena moyo wathu wauzimu ndipo tikufunika chithandizo. Tikangodziŵa kuti penapake zinthu sizili bwino, timakhala ofunitsitsa kuti tisadzidandaulitse tokha kapena kudandaulitsa anzathu, kapenanso kudzadandaulitsa anthu ena mtsogolomo.—Mateyu 7:12.

Ndipo mbali yomaliza n’njakuti kuulula zimene talakwa kumathandiza munthu wolakwayo ngakhalenso wolakwiridwayo. Mwachitsanzo, Mfumu Davide italakwa inavutika kwambiri mumtima mwake. Iye analemba kuti, “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.” Koma pamapeto pake ataulula tchimo lake kwa Mulungu, Davide anaimba mokondwa kuti: “Mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.” (Salmo 32: 3, 7) Kuulula zolakwa kumam’chititsa wolakwiridwayo kutsitsa mtima pansi chifukwa chakuti kuvomereza cholakwa kukhoza kum’tsimikizira wolakwiridwayo kuti munthu amene wam’lakwirayo amam’konda kwambiri mwakuti zimamuwawa akam’chitira iyeyo zinthu zom’lakwira ngati zimenezo.—2 Samueli 11:2-15.

Maganizo Oyenera Pankhani Yodziona Ngati Wolakwa

Kuti mukhale ndi maganizo oyenera pankhani yodziona ngati wolakwa, taonani kusiyana kumene kunalipo pakati pa Yesu ndi Afarisi pankhani ya mmene ankaonera ochimwa ndiponso tchimo. Pa Luka 7:36-50 timaŵerengapo za mkazi wakhalidwe loipa amene analoŵa m’nyumba mwa Mfarisi winawake mmene Yesu anali kudya chakudya. Mkaziyo anafika pamene panali Yesu, n’kutsuka mapazi a Yesuyo ndi misozi yake, n’kuwapaka mafuta apamwamba onunkhira bwino.

Mfarisi wodzionetsera ngati munthu wopembedza kwambiriyo ananyoza mkaziyu kuti sanali woti munthu waulemu wake ngati iyeyo angayandikane naye n’kumataya nthaŵi yake pokambirana naye. Mfarisiyu analankhula chamumtima kuti, “Akadakhala mneneri uyu [Yesu] akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo wom’khudza iye, chifukwa ali wochimwa.” (Luka 7:39) Nthaŵi yomweyo Yesu anam’konza maganizo akewo. Yesuyo anati, “Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino. Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri.” N’zosakayikitsa kuti mawu ameneŵa anam’limbikitsa kwambiri mkaziyo ndipo anam’khazika mtima mmalo.—Luka 7:46, 47.

Apa sikuti Yesu ankalekerera khalidwe loipa ayi. Koma ankaphunzitsa Mfarisi wamatamayo kuti chikondi ndicho chili chofunikira kwambiri kuti munthu alimbikire potumikira Mulungu. (Mateyu 22:36-40) Inde, kunali koyeneradi kuti mkaziyo azidziona kuti anali wolakwa pa zochita zake zoipa zakale. N’zoonekeratu kuti analapa, chifukwa chakuti analira ndipo sanayese kudzilungamitsa pa zimene ankachita ndiponso sanazengereze kum’lemekeza Yesu pagulu. Poona zimenezi, Yesu anamuuza kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.”—Luka 7:50.

Komabe Mfarisiyo anapitirizabe kum’nyoza mkaziyo monga wochimwa. Mwinamwake ankafuna kuti mkaziyo akhale akuganizira kuti ali ndi mlandu kwa Mulungu ndi kutinso achite manyazi. Koma tikamafuna kuti nthaŵi zonse ena azidziona kuti ndi olakwa ngati sakuchita zinthu mmene ifeyo timafunira ndiye kuti tikusoŵa chikondi ndipo pamapeto pake zinthu siziyenda bwino n’komwe. (2 Akorinto 9:7) Zinthu zimakhala bwino tikamatsanzira Yesu, poonetsa chitsanzo chabwino, powayamikira ena kuchokera pansi pamtima, ndiponso powasonyeza kuti timawakhulupilira ngakhale kuti nthaŵi zina tikhoza kuwadzudzula kapena kuwapatsa uphungu.—Mateyu 11:28-30; Aroma 12:10; Aefeso 4:29.

Choncho, kudziona ngati wolakwa kungakhale kwabwino, mwinanso kofunika ngati tachita chinachake cholakwika. Lemba la Miyambo 14:9 (m’Baibulo la Knox) limati: “Zitsiru sizidandaula zikalakwa.” Chikumbumtima chodziona kuti talakwa chikhoza ndipo chiyenera kutilimbikitsa kuulula ndiponso kuchita zinthu zina zoyenerera. Komabe chifukwa chathu chachikulu potumikira Yehova, nthaŵi zonse sichiyenera kukhala choti tikuopa kupalamula, koma kuti tikum’konda. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Baibulo limatitsimikizira kuti anthu abwino akalimbikitsidwa ndiponso kutsitsimulidwa ndi mfundo imeneyi, amayesetsa kuchita chilichonse chimene angathe kuti atumikire Mulungu. Chofunikanso kwambiri n’chakuti iwo amakhala okondwa pochita zimenezi.