Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mdyerekezi Alikodi?

Kodi Mdyerekezi Alikodi?

Kodi Mdyerekezi Alikodi?

M’ZIPEMBEDZO zambiri, anthu amati Mdyerekezi ndi maganizo akale achabechabe amene anthu anangopeka basi. Choncho bishopu wamkulu wa mumzinda wa Genoa ku Italy dzina lake Dionigi Tettamanzi, yemwenso ali m’gulu la makadinala otchuka, anakwiyitsa anthu ndi kalata yake ya masamba 40 imene analembera atsogoleri amatchalitchi achikristu pankhani yolimbana ndi Mdyerekezi. Kalatayo inali ndi “malamulo khumi” aŵa:

Loyamba: “Musaiwale kuti mdyerekezi aliko,” chifukwa chakuti “bodza lake loyamba” ndi loti “atipangitse kukhulupirira kuti kulibe mdyerekeziyo.”

Lachiŵiri: “Musaiwale kuti mdyerekezi ndi wonyenga. . . . Musamadzione ngati mdyerekezi sangakuukireni kapena kuti sangakutheni.”

Lachitatu: “Musaiwale kuti mdyerekezi ndi wochenjera ndiponso wonyenga kwambiri. Iye akupitiriza kunyenga anthu powanyengerera ndi zinthu zokopa, monga mmene ananyengererera munthu woyambayo.”

Lachinayi: “Khalani tcheru: pa zoganiza zanu ndiponso pa zinthu zimene mumaona. Ndipo khalani wolimba: potsimikiza kwambiri kuchita zinthu zabwino.”

Lachisanu: “Khulupirirani kwambiri kuti Kristu amagonjetsa wonyengayu” chifukwa chakuti mukatero “mungakhale wotetezeka ndipo wosaopa china chilichonse ngakhale wina atachita kukuukirani motani.”

Lachisanu n’chimodzi: “Kumbukirani kuti Kristu amakugwiritsirani ntchito pogonjetsa woipayu.”

Lachisanu n’chiŵiri: “Pitirizani kumvera Mawu a Mulungu.”

Lachisanu n’chitatu: “Khalani wodzichepetsa ndiponso wosadandaula kwambiri mukachititsidwa manyazi.”

Lachisanu n’chinayi: “Pempherani nthaŵi zonse, osatopa,” kuti mugonjetse chiyeso.

Lakhumi: “Lemekezani Ambuye Mulungu wanu ndipo iye yekhayo muzim’lambira.”

Kodi zotsatirapo za kalatayi zinali zotani? Anthu apakoleji yophunzirako za Mulungu yotchedwa Milan’s Center of Theological Studies sanakonde kwenikweni malangizo a m’kalatayo. A pasukuluyo anatsutsa kuti “kuyambitsa chipembedzo kwa mtunduwu kukungokhala ngati kuganiza kwa munthu wachikale kwambiri.” Munthu wina amene analankhula mmalo mwa ena onse anati, “kuti tinene kuti amayambitsa machimo onse ndi mdyerekezi, ndiye kuti tingochititsa kuti anthu apeze podzikhululukira akamachitira dala zoipa.”

Ngakhale kuti Baibulo silichotsera anthu mlandu pa zochita zawo, ilo limalongosola momveka bwino kuti Satana Mdyerekezi ndiye “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” amene anam’yesa Yesu. Limaululanso za mphamvu ya Satana ndi cholinga chake cha ‘kuchititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.’—2 Akorinto 4:4; Mateyu 4:1-11.

Indedi, zimene mtumwi Petro analemba n’zoonadi kuti, Satana ali “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.” (1 Petro 5:8) Si zodabwitsa kuti mtumwi Yohane anakumbutsa okhulupirira kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) N’chanzeru kuti tisanyalanyaze machenjezo a m’Malembaŵa.