Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zingakhale Bwanji Ngati Nditakumana ndi Winawake wa Kusukulu Kwathu?

Kodi Zingakhale Bwanji Ngati Nditakumana ndi Winawake wa Kusukulu Kwathu?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Zingakhale Bwanji Ngati Nditakumana ndi Winawake wa Kusukulu Kwathu?

“Nditapitanso kusukulu Lolemba, maganizo anga anangoti pwirikiti. Ngati mnzanga wina aliyense anandiona, ndinkangopeka bodza basi. Mwina kungowanamiza anzangawo kuti ndinali kutolera ndalama za chipani chotchedwa Labor Party,” anatero James, wochokera ku England.

“Anthu a kusukulu kwathu amene anandiona ankandinena. Ndinkasoŵa nazo mtendere kwambiri,” anatero Débora, wochokera ku Brazil.

N’CHIFUKWA chiyani achinyamata ameneŵa ankaopa kwambiri kuti anzawo asawaone? Kodi zimene ankachitazo zinali zosaloledwa? Ayi ndithu, iwo ankachita ntchito yolemekezeka ndiponso yofunika kwambiri imene ikuchitidwa padziko lonse masiku ano. Ankachita ntchito imene Yesu analamula kuti ichitidwe pamene anati: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.

Malingana ndi zimene gulu lina lofufuza lotchedwa Gallup ku America linapeza, akuti achinyamata opitirira 90 pa 100 alionse amakhulupirira Mulungu. Pafupifupi theka lawo amapita kutchalitchi mlungu uliwonse. Ndipo ngakhale kuti achinyamata ambiri amatanganidwa ndi zochitika za kutchalitchi kwawo monga kuimba makwaya, ochepa chabe ndiwo amene amakambirana za Mulungu ndi anzawo a kusukulu. Komabe Mboni za Yehova zimadziŵika padziko lonse chifukwa cha ntchito yawo yolalikira m’makomo a anthu. Mboni zachinyamata zambirimbiri zimachita nawo ntchito imeneyi.

Ngati muli Mboni yachinyamata, n’zosakayikitsa kuti nanunso mwakhala mukuchita nawo ntchito imeneyi yolalikira. Koma si ndiye kuti kuchita nawo zimenezi kumakuphwekerani. Monga achinyamata amene tawatchula poyamba paja, inunso mwina zokumana ndi mnzanu wa kusukulu kunyumba kwawo zimakusoŵetsani mtendere kwambiri. Mtsikana wina wa ku Britain dzina lake Jennie anavomereza kuti, “Chinthu chimene ndinkadana nacho kwambiri, chinali chakuti mnzanga wina wa kusukulu kwathu andione nditatchena bwinobwino, nditavala siketi, n’kunyamula chikwama cha mabuku, n’kumaoneka munthu wovala bwino kusiyana ndi mmene ndimaonekera kusukulu.”

Mantha okumana ndi wina wa kusukulu kwanu akhoza kukula kwambiri moti achinyamata ena achikristu amangoganiza zonena bodza basi. Mnyamata wina dzina lake Leon anati: “Ndikudziŵa mnyamata wina wa Mboni amene amavala jekete yokhala ndi chakumutu akamalalikira, kuchitira kuti akaona anzake a kusukulu azidzibisa nkhope.” Komanso achinyamata ena amangozemba kulalikira m’madera enaake. Mnyamata wina dzina lake Simon anati, “Ndikukumbukira kuti nthaŵi ina ndinkapempherera kuti tisakalalikire kumsewu wina wake chifukwa chakuti ndinkadziŵa kuti n’kumene kunkakhala anthu ambiri a kusukulu kwathu.”

Si zachilendo kumangika ukamaganiza zokumana ndi munthu winawake wodziŵana naye ngati ukulalikira. Komabe mukamangokhala ndi maganizo ameneŵa mungangodzipweteka nokha. Mtsikana wina wa ku Germany dzina lake Alicia anavomereza zimenezi motere: “Kulalikira ndinkadana nako kwambiri, mwakuti zimenezi zinkandipangitsa kuti ndisamakonde zinthu zokhudza Mawu a Mulungu.”

N’chifukwa chiyani nanga muyenera kulalikira, makamaka ngati zimakuvutani kutero? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione chifukwa chake Mulungu anakupatsani ntchito imeneyi. Kenaka tinena mmene zilili zotheka kuthetsa mantha anu pokhala wakhama ndiponso wofunitsitsa kutero.

Udindo wa Kulalikira

Choyamba, zingakuthandizeni kuganizira kuti palibe chachilendo ngakhale pang’ono kuuzako ena zachikhulupiriro chanu. Kuyambira kalekale, amuna ndi akazi oopa Mulungu akhala akuchita zomwezo. Mwachitsanzo, Nowa ndi munthu wodziŵika kwambiri chifukwa chomanga chingalawa chachikulu. (Genesis 6:14-16) Koma malingana ndi 2 Petro 2:5, akuti analinso “mlaliki wa chilungamo.” Nowa ankaona kuti anali ndi udindo wochenjeza ena za chiwonongeko chimene chinatsala pang’ono kuchitika.—Mateyu 24:37-39.

Kuchoka nthaŵi imeneyo, ngakhale kuti Ayuda anali asanapatsidwe kwenikweni malamulo olalikira kwa anthu amene sanali Ayuda, ambiri anauzako ena za chikhulupiriro chawo. Umu ndi mmene munthu wina amene sanali Myuda dzina lake Rute anadziŵira Yehova. Poyamikira apongozi ake dzina lawo Naomi, Rute anawauza kuti: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Kenakanso Mfumu Solomo inanena mawu osonyeza kuti anthu ambiri amene si Ayuda adzabwera kudzamva za ‘dzina lalikulu’ la Yehova ndi kudzalambira pa kachisi Wake.—1 Mafumu 8:41, 42.

Mwaonatu; ngati atumiki a Mulungu akale ameneŵa anauza ena chikhulupiriro chawo ngakhale kuti analibe lamulo lowauza mwatchutchutchu kuti atero, ndiye kuti n’kofunika kwambiri kwa Akristu masiku ano kuona kuti ali ndi udindo waukulu wolalikira! Ndiponsotu, ife tinalamulidwa kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Tili ngati mtumwi Paulo, mwanjira yakuti tili nacho chotikakamiza kulengeza uthenga uwu wabwino. (1 Akorinto 9:16) Ngakhale chipulumutso chathu chenichenicho chimadalira zomwezi. Aroma 10:9, 10 amati: “Ngati udzavomereza [pamaso pa anthu, NW] mkamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, . . . udzapulumuka: pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso.”

Kodi n’kuti kumene mungakalankhule “pamaso pa anthu”? Ngakhale kuti ndi bwinonso kulalikira mwamwayi, koma kulalikira m’makomo a anthu ndiko kumathandiza kwambiri pankhani ya kupezana ndi anthu. (Machitidwe 5:42; 20:20) Kodi simuli oyenera kuchita nawo ntchitoyi chifukwa chakuti ndinu wamng’ono? N’zosatheka zimenezo. Baibulo limapereka lamulo ili pa Salmo 148:12, 13: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova.”

Pamene Pagona Vuto Lolalikira Anzanu

Inde n’zoona kuti nthaŵi zina ngati ukulalikira n’kukumana ndi munthu wina amene amaphunzira pasukulu panu zimaumitsadi thupi. Ndiponsotu, aliyense amafuna kuti anthu ena azigwirizana naye. Palibe munthu amene amafuna kuti ena azim’seka, kum’tukwana kapena kum’chititsa manyazi. Ndipo monga ananenera mtsikana wina dzina lake Tanya, akuti “nthaŵi zina ana a kusukulu amachita zinthu za nkhanza kwambiri!” Choncho mukhozadi kukhala ndi nkhaŵa kuti kaya zikakutherani bwanji ngati anzanu a kusukulu atakuonani mutatchena bwinobwino muli ndi Baibulo m’manja. Tsoka ilo, iwo akhozadi kusachitira mwina koma kukusekani basi. Mnyamata wina wa ku Brazil dzina lake Felipe amakumbukira kuti, “M’kalasi mwathu munali mnyamata wina amene nyumba yawo ndi yathu zinali m’chinyumba chimodzi. Ankakonda kundinena kuti, ‘Uyo tamuonereni ndi Baibulo lakelo! Watenga chiyani m’chikwamacho?’”

Si nkhani yamaseŵera n’komwe anthu akamakunyodolani choncho. Baibulo limatiuza kuti Isake, mwana wa Abrahamu anasekedwa kwambiri ndi Ismayeli yemwe anali mchimwene wake koma wobadwa mwa mayi ena. (Genesis 21:9) Mtumwi Paulo sanaone nkhani yotereyi ngati yaing’ono ayi. Pa Agalatiya 4:29, mtumwiyo ananena molondola kuti zoterezi ‘n’kuzunza.’

Chimodzimodzinso Yesu anachenjeza kuti anthu ena adzadana ndi anthu om’tsatira iye. Iye anati: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti linada ine lisanayambe kuda inu. Mukanakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”—Yohane 15:18, 19.

Ndiye kuti pokhala Mkristu, muyenera kukhala wokonzeka kuzunzidwa mwanjira inayake. (2 Timoteo 3:12) Ngakhale mutangokhala chete osatchula mawu okhudza za m’Baibulo kwa anzanu, anzanu ena akhoza kukuzunzanibe chifukwa chakuti muli ndi makhalidwe abwino basi ndiponso kuti simugwirizana nawo pochita zinthu zopulupudza. (1 Petro 4:4) Komabe, Yesu akupereka mawu olimbikitsa awa: “Odala [achimwemwe, NW] muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine.” (Mateyu 5:11) Zingatheke bwanji kukhala wachimwemwe pamene anthu akukunyodolani kapena kukutukwanani? Zingatheke chifukwa chodziŵa kuti mukukondweretsa mtima wa Yehova Mulungu! (Miyambo 27:11) Ndipo mukasangalatsa Mulungu, ndiye kuti mumadzipatsa mwayi wokalandira mphoto ya moyo wosatha!—Luka 10:25-28.

Mwayi wake, si kuti anzanu a kusukulu onse, kapena ochuluka angakusekeni mukakumana nawo mukulalikira. Mtsikana wina wa ku Britain dzina lake Angela akutikumbutsa kuti: “Nthaŵi zambiri mumati mukam’peza mnzanu wa kusukulu ali pakhomo pawo, iyeyotu ndiye amakhala womangika kwambiri kuposa inuyo!” Ndiponsotu ena akhoza kuchita chidwi kwambiri pofuna kumva zimene munene. Mulimonsemo, Akristu achinyamata ambiri zinthu zikuwayendera bwino kwambiri polalikira kwa ana asukulu anzawo. Nkhani yathu yotsatira yotereyi idzakamba njira zina zimene inunso mungathe kuchita chimodzimodzi.

[Chithunzi patsamba 20]

Achinyamata ambiri amaopa kukumana ndi mnzawo wa kusukulu kwawo akamalalikira

[Chithunzi patsamba 22]

Musalole kuchita manyazi ndi chikhulupiriro chanu chifukwa chosekedwa