Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Otetezeka Kumalo Anu Antchito

Kukhala Otetezeka Kumalo Anu Antchito

Kukhala Otetezeka Kumalo Anu Antchito

NGAKHALE kuti pali malamulo othandiza kuti ntchito zisamawononge thanzi la munthu ndiponso kumuvulaza, vuto la kuvulala ndiponso kufa pantchito likadali lalikulu kwambiri. Pamenepatu, n’zodziŵikiratu kuti anthu pantchito sangakhale otetezeka kokha chifukwa choti pali malamulo. Ndi udindo wa mabwana ndi antchito awo kudziteteza ndiponso kuteteza ena.

Choncho, apantchito onse ayenera kuona bwino malo awo antchito ndi kagwiridwe kawo kantchito. Mwachitsanzo, kodi mwaona kuti pantchito panu m’potetezekadi? Kodi mumagwiritsa ntchito mankhwala akupha? Ngati ndi choncho, kodi ndinu wotetezeka mokwanira? Kodi ntchito imakuchulukirani nthaŵi zonse? Kodi mumagwira ntchito maola oposa ovomerezeka ndi boma?

Mayankho a mafunso ngati ameneŵa angasonyeze ngati muli wotetezeka kuntchito.

Kusamala ndi Zoopsa

Kuyesetsa kugwira ntchito yochuluka kwambiri kungakhale kovulaza. Pulofesa Lawson Savery wa pa yunivesite ya Curtin ku Australia pamodzi ndi wochita kafukufuku wina, ataona zotsatira za kafukufuku wa anthu apantchito okwana 3.6 miliyoni ndi malo antchito okwana 37,200, analemba nkhani yam’chizungu yofotokoza kafukufukuyo yamutu wakuti “Kugwira Ntchito Maola Ochuluka: Kodi N’koopsa Ndipo Kodi Anthu Amagwirizana Nako?” Kunena mosapita m’mbali mayankho a mafunso onseŵa, ndi inde.

Indedi, amene amagwira ntchito atatopa sachita zinthu molongosoka ndipo amalakwitsalakwitsa. Pulofesa Savery ananena zofanana ndi zimene zinalembedwa mu nyuzipepala ya ku Australia komweko ya The Sun-Herald kuti: “Makampani ambiri ankalimbikitsa antchito kuti azikondetsetsa ntchito yawo ndipo ankayesetsa kupeza anthu otereŵa ndi kuwapatsa mphoto.” Zotsatira zake n’zoopsa. Mwinamwake palibenso kwina kumene vuto limeneli limaonekera kwambiri koposa m’makampani onyamula katundu, komwe madalaivala amauzidwa ngakhale kukakamizidwa kumene, kuti ayendetse galimoto maola ambiri popanda kupuma, zomwe zili zoletsedwa m’mayiko ena.

Kusagwira ntchito molongosoka, monga mosasamala ndi mwauve kumachititsanso ngozi. Kaŵirikaŵiri kusiya zida zili mbwee kapena nthambo za magetsi zili pamtunda kumachititsa ngozi ndipo ngakhale kuphetsa anthu kumene. Chimodzimodzinso kunyalanyaza njira zopeŵera ngozi pamene tikugwiritsa ntchito zida ndiponso makina amagetsi. Chinthu china chimene chimavulaza, ndiponso kupha, n’kusapukuta zinthu zimene zatayikira pansi—makamaka zakupha. Antchito ambiri avulala chifukwa choterereka pa mafuta kapena pasimenti ponyowa. Choncho tingati chiyambi cha ntchito yabwino ndicho kukhala waukhondo ndiponso wadongosolo.

Komabe, ambiri amanyalanyaza njira zopeŵera ngozi. Magazini ya Monthly Labor Review inati “Kuchuluka kwa ntchito kungachititse munthu kuganiza kuti ndi bwino kungochita chidule kuti zinthu ziyende.” Choncho, anthu ena anganyalanyaze malangizo opeŵera ngozi poganiza kuti, ‘Ineyo chikhalireni ndimanyalanyaza malangizo ameneŵa koma sindinakumanepo ndi vuto ayi.’ Pa nkhaniyi, manijala wodziŵa ntchito wa pa fakitale ina anati: “China mwa zinthu zoipitsitsa zimene munthu angachite pantchito ndicho kunyalanyaza njira zopeŵera ngozi ndiyeno osapeza vuto!” Chifukwa? Chifukwa chakuti izi zimapangitsa munthu kukhala wodzidalira kwambiri ndiponso wosasamala, zomwe zimachititsa ngozi zambiri.

Kaŵirikaŵiri anthu amanena kuti kuphulika kwa fakitale ina ku Chernobyl ku Ukraine mu 1986 inali “ngozi ya nyukiliya yoopsa kwambiri padziko lonse.” Kodi chinachititsa ngoziyi n’chiyani? Lipoti lina pa zangozi imeneyi linatchula kuti pafakitalepo ankagwiritsa ntchito “njira zogwirira ntchito mosasamala zambirimbiri” ndiponso “kunyalanyaza mobwerezabwereza njira zopeŵera ngozi.”

Bwana ndi wantchito wake angagwirizane kuoneratu zinthu zimene zingachititse ngozi. Mwambi wanzeru wa m’Baibulo umati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Inde, munthu wanzeru amaona patali zimene zingakhale zovulaza ndi kupeza njira zomwe angadzitetezere yekha ndi ena.

Mabwana akachita zimenezi, amapindula pamodzi ndi antchito awo. Mwachitsanzo, kampani imene inakonza ofesi yake pofuna kupeŵa “kukhala m’nyumba zodwalitsa” za ofesizo inapeza kuti mosakhalitsa zinthu zinali kuyenda bwino kwambiri ndipo antchito anali kusangalala zedi. Ndipo anapezanso kuti anthu sanali kujombajomba chifukwa chodwala. Kusamalira thanzi la anthu ena kumeneku sikuti kumapangitsa bwana ndi antchito ake okha kukhala pamtendere, koma, malinga ndi momwe taonera pamenepa, kungabweretse ndalama zambiri.

Monga taonera mu nkhani yoyamba ija, chiwawa n’chofala kuntchito. Kodi mungatani kuti mudziteteze?

Zomwe Mungachite

Kwapezeka kuti pantchito nkhani yaing’ono imakula n’kukhala nkhani yaikulu. Magazini ya Harvard Business Review inalangiza mwamphamvu kuti: “Pothetsa chiwawa pantchito, dziŵani kuti kaŵirikaŵiri anthu amene amaputa anzawo ndi nkhani zing’onozing’ono amapitiriza mpaka kuchita zazikulu.”

Mayi angakhale alibe maganizo okopa anzake pantchitopo, koma ngati mavalidwe, malankhulidwe ndi makhalidwe ake ali osayenera, ena angaganize kuti ndi wachiwerewere. Masiku ano, khalidwe limene cholinga chake si ndicho kudzutsa chilakolako chonyansa nthaŵi zina limathera m’mavuto aakulu monga kumangom’londola munthu pazifukwa zoipa, kugwiririrana, kapena ngakhale kuphana. Choncho onani bwino momwe mavalidwe ndi makhalidwe anu akukhudzira ena. Mverani langizo la m’Baibulo lakuti: ‘Dzivekeni nokha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chiletso.’1 Timoteo 2:9.

Magazini ya Monthly Labor Review inapeza chinthu china chimene chingadzetse mavuto, ndipo inati: “Anthu amene amagwira ntchito okhaokha usiku, kumalo akutali, timawadera nkhaŵa.” Choncho lingalirani izi: Kodi ndi nzeru kulolera kupeza mavuto amene nthaŵi zambiri amabwera chifukwa chogwira ntchito nokha, makamaka usiku kwambiri? Kodi ndalama zimene mungapeze zingagwirizane ndi mavutoŵa?

Ndibwinonso kulingalira zomwe timachita anzathu amene atopa ndi ntchito akatiputa. Kodi tingachite chiyani kuti tisakolezere moto pakabuka mkangano? Mwambi wa m’Baibulo umalangiza kuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Inde, poyankha mokoma mtima ndi mwaulemu, mungathandize kwambiri kuthetsa nkhaniyo ndi kupeŵa mkangano.

Masiku ano anthu amene amagwira ntchito mitima ili m’mwamba, kuputana n’kofala. Ngakhale kuti zingaoneke kuti munthuyo akulimbana ndi inuyo, iye kwenikweni angakhale akungophwetsa mkwiyo wake ndiponso kuthetsera mavuto ake pa inuyo. N’kutheka kuti zinangochitika kuti ifeyo tinapezeka pamalo olakwika komanso panthaŵi yolakwika imeneyi. Choncho m’pofunika kusamala mayankhidwe athu. Angachepetse kapena kukulitsa nkhaniyo.

Komanso mwina, n’kuthekadi kuti palidi zifukwa zenizeni zomwe mwasiyanirana maganizo. Buku lakuti Resolving Conflicts at Work [Kuthetsa Mikangano Pantchito] linanena mawu othandiza aŵa: “Tikamakangana, . . . nthaŵi zambiri sitikambirana momwe tikumveradi.” Kodi vuto limakhala chiyani? Bukuli linapitiriza kunena kuti: “Mikangano ingatisokoneze maganizo, ndipo tingaganize kuti sitingachitire mwina koma kumenyana basi.”

Kodi choyenera kuchita n’chiyani? MVETSERANI! Buku limene mawu ake ali pamwambaŵa limati: “ Mwakumvetseradi zonena za anthu amene sitikugwirizana nawo . . . , mtima ungaphwe, sitingafunenso kupitiriza mkanganowo ndipo tingapeze njira zouthetsera.” Ameneŵa ndi malangizo abwino opeŵera kusagwirizana kapena kukulitsa mikangano.

Choncho, dzitetezeni mwa kulingalira bwino. Ndiye kutinso muyenera kutsatira kwambiri malangizo a chitetezo a m’dera lanu. Kuchita zimenezi kungathandize kwambiri kuti mukhale otetezeka pamalo anu antchito.

N’zoona kuti momwe timaonera moyo, ntchito, ndi nthaŵi yongopuma zingakhudze mtundu wa ntchito imene tingasankhe komanso mmene timaonera nkhani ya chitetezo. Nkhani yotsatira ingatithandize kusankha bwino zimenezi.

[Chithunzi patsamba 25]

Pukutani bwinobwino pamene patayikira mafuta

[Chithunzi patsamba 26]

Kuyankha mofatsa kungaletse mkangano waukulu kubuka