Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malingaliro Oyenera a Ntchito

Malingaliro Oyenera a Ntchito

Malingaliro Oyenera a Ntchito

OFESALA wankhondo wodzipereka anapitiriza kugwira ntchito panthaŵi yopuma kuti amalize ntchito imene ofesala wamkulu ankaifuna mofulumira. Anzake a pantchitopo atabwerako kopuma, anapeza ofesala uja atasamira ntchito imene inali pa desiki lake atafa.

Pasanathe maola aŵiri, maofesala anzake anadabwa zedi bwana wawo atawaimbira telefoni n’kuwauza kuti: “Imfa ya———ndi yomvetsa chisoni, koma ndikufuna kuti pofika maŵa m’maŵa ndikhale nditapeza munthu wina amene angatenge malo ake!” Amene ankamva zimenezi anadzifunsa kuti, Kodi ntchito imene ofesalayo anali kugwira ndiyo inali chinthu chofunika kwambiri kwa bwanayo?

Nkhaniyi inachitikadi ndipo ikungosonyeza zinthu zimene zimachitikadi, zakuti nthaŵi zambiri munthu amakhala wofunika kwa bwana wake kokha chifukwa cha ntchito imene amagwira. Izi zingapangitse munthu kudzifunsa kuti: Kodi ntchito ndicho chofunika kwambiri m’moyo, kapena kodi ndimagwira ntchito kuti ndizipeza zinthu zofunika pamoyo? Kodi ntchito ikundiwonongera chiyani pa moyo wanga?

Kusankha Mwanzeru

Kaŵirikaŵiri zinthu ziŵiri zimene ena amati ndi zofunika kwambiri m’moyo amazichita mwaphuma. Zinthuzi ndizo kusankha wokwatirana naye ndiponso ntchito. Kale anthu ankaona ntchito ndiponso banja kuti n’zosayenera kutha. Choncho anthu ankasankha zinthu zimenezi mosamala kwambiri. Nthaŵi zambiri, anthu ankafunsira nzeru kwa anzawo kapena makolo achikulire.

Koma masiku ano, anthu ambiri amasankha wokwatirana naye kokha chifukwa cha kukongola pamaso, ndiponso amaganiza kuti ngati ukwati wawo suyenda bwino, adzapeza wina. Mofananamo, anthu ambiri amasankha ntchito chifukwa chakuti ndi yapamwamba, osalingalira n’komwe zoipa zimene zingakhalepo. Kapena zoipa zimene amaganiza kuti zingakhalepo, amazinyalanyaza mofulumira polingalira kuti, ‘ndikathana nazo.’

N’zachisoni kuti, kaŵirikaŵiri akazi a m’mayiko osauka amakopeka ndi makampani amene amalonjeza moyo wabwino kwinakwake. Koma nthaŵi zambiri akafika kudziko linalo, amawatumiza ku nyumba za mahule kumene moyo wawo umakhala woipa zedi kuposa moyo wawo wapoyamba. Malinga ndi magazini ya World Press Review, akuti mtundu woipa kwambiri wa ukapolo wamasiku anowu ndi “mliri umene sungathe panopo.”

Kodi n’zothekanso kuti anthu akopedwe kuloŵa ntchito yabwinobwino koma n’kudzapezeka ali paukapolo? Zimenezi zinachitikapo ndithu! Mwachitsanzo, makampani ena amalonjeza antchito awo zinthu zochuluka. Zina ndi monga zipinda zodyeramo za pa kampani pomwepo za banja lawo ndi anzawo, kuwatenga pagalimoto kwaulere, kuwachapira zovala, kukhala ndi dokotala wa mano pantchito pomwepo, kugwiritsa ntchito kwaulere zida zolimbitsira thupi, ndi kuwathandiza kulipira zakudya m’malesitiranti odula.

“Kampani ina mpaka imalinganiza zopezera zibwenzi antchito ake amene amagwira ntchito kwambiri,” anatero mtolankhani wotchedwa Richard Reeves. Koma chenjerani. Mtolankhaniyu anati: “Makampani ameneŵa amakusamalirani kuti musavutike, pokhapokha mukalola kuchita chinthu chimodzi chokha chakuti azikulamulirani, kuti muzigwira ntchito maola 18 patsiku komanso Loŵeruka ndi Lamlungu. Komanso muzidya, kuchita maseŵero olimbitsa thupi, ngakhale kugona mu ofesi kuti makampaniwo azipeza phindu.”

Kusankha Ntchito Ina Yabwino

Mwambi wina wakale umati: “Galu wamoyo aposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Mwambi umenewu ungam’pangitse munthu kudzifunsa kuti, Kodi ndifere ntchito kapena ndiwonongetse thanzi langa chifukwa cha ntchito? Poyankha, anthu ambiri asintha ntchito yawo ndipo apeza njira ina yopezera zofunika zokwanira pa moyo wawo komanso banja lawo ngati ali okwatira komanso kukhala ndi moyo wosangalatsa ndiponso wopindulitsadi.

Ndithudi, kuti zimenezi zitheke m’pofunika kusalira zambiri ndiponso kuona kuti n’chiyani chimene mumafuna kwenikweni, osati zinthu zosafunikira kwenikweni zimene mumangolakalaka. Anthu amene amafuna malo apamwamba ndiponso kutamidwa angakane ntchito zing’onozing’ono ndipo angati anthu amene amaloŵa ntchitozi ndi opusa. Koma kodi chofunika kwambiri m’moyo n’chiyani? Kodi mwalingalirapo zimenezi posachedwapa?

Mfumu yanzeru Solomo, imene inalemba mwambi walembedwa pamwamba uja, inali yolemera kwambiri mwina kuposa munthu wina aliyense. Koma mouziridwa ndi Mulungu inalemba mwachidule zimene zilidi zofunika, kuti: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.

Komanso Solomo ankakonda kugwira ntchito. Analemba kuti, “Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, nawonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake?” (Mlaliki 2:24) Yesu Kristu amene ali Solomo Wamkulu, amakondanso kugwira ntchito, monga amachitira Atate wake wakumwamba. “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.”—Yohane 5:17; Mateyu 12:42.

Pakalipano moyo wa anthu ndi wamasiku ochepa. (Salmo 90:10) Koma Kristu anadziŵa kuti moyo wosatha pa dziko lapansi udzakhalapo mu ulamuliro wa Ufumu, umene anaphunzitsa otsatira ake kuupempherera. N’chifukwa chake paulaliki wake wotchuka wa paphiri anapempha kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:9, 10, 33.

Kunena za moyo mu ulamuliro wa Ufumu umenewo, Baibulo limalonjeza kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; . . . osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.

Kudzasangalala ndi moyo wosatha komanso kudzagwira ntchito yokhutiritsa, ndi chiyembekezo chabwino kwambiridi. Titaiganizira bwino ntchito yathu mwamaganizo achikulu mwina tingaone kuti tikufunika kusiya mbali zina za ntchito yathu panopa kuti tipeŵe ngozi zimene zingakhalepo zomwe zingatilepheretseretu kudzasangalala ndi “moyo weniweniwo,” moyo wam’tsogolo mu Ufumu wa Mulungu. (1 Timoteo 6:19) Choncho tisonyeze mwa ntchito imene timagwira, kapena chilichonse chimene timachita, kuti timalemekeza amene anatipatsa moyo.—Akolose 3:23.

[Zithunzi pamasamba 27, 28]

Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzagwira ntchito zosawavulaza ndiponso zaphindu