Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’Chifukwa Chiyani Timafunikira Aphunzitsi?

N’Chifukwa Chiyani Timafunikira Aphunzitsi?

N’Chifukwa Chiyani Timafunikira Aphunzitsi?

Mwambi wina wa ku Japan umati “Kuli bwino kukhala tsiku limodzi ndi mphunzitsi wabwino kusiyana ndi kukhala masiku 1000 ukuphunzira mwakhama pawekha.”

KODI mumakumbukira mphunzitsi amene anakugwirani mtima kwambiri muli pasukulu? Kapena ngati mudakali pasukulu, kodi muli ndi mphunzitsi amene mumam’konda kwambiri? Ngati alipo, n’chifukwa chiyani mumam’konda?

Mphunzitsi wabwino amawalimbitsa mtima ana ake asukulu ndipo amapangitsa maphunziro kukhala osangalatsa. Mwamuna wina wa ku England, amene ali ndi zaka 70 saiŵala mphunzitsi wake wa Chingelezi wa kusukulu ya ku Birmingham kumene ankaphunzira. “A Clewley anandithandiza kudziŵa luso limene sindin’kadziŵa kuti ndili nalo. Ndinali wamanyazi, koma anandilimbikitsa kuti ndikachite nawo mpikisano wa zisudzo wa kusukulu. M’chaka changa chomaliza maphunziro, ndinapambana mpikisano wa zisudzowo. Sindikadapambana, akadapanda kundilimbikitsa. Ndimadandaula kuti n’takula sindinakumane nawo kuti ndiwathokoze chifukwa cha kudzipereka kwawo pothandiza ana awo asukulu.”

Margit, mayi wansangala wa ku Munich ku Germany amene ali ndi zaka za m’ma 50, anati: “Panali mphunzitsi wina amene ndinkamukonda kwambiri. Zinthu zovuta ankazifotokoza bwino m’njira yosavuta kumva. Ankatilimbikitsa kuti tizifunsa ngati sitinamvetse. Anali womasuka ndiponso wochezeka. Zimenezi zinkapangitsa maphunziro kukoma kwambiri.”

Peter wa ku Australia, akukumbukira aphunzitsi ake a masamu, ndipo akuti, “anatithandiza kuona kufunika kwa zimene timaphunzira mwa kutipatsa zitsanzo zenizeni. Pamene tinali kuphunzira masamu a kakhotedwe ka zinthu za makona, anatiphunzitsa momwe tingadziŵire kutalika kwa nyumba popanda kuigwira n’komwe, koma mongogwiritsa ntchito mfundo za masamu ameneŵa. Ndikukumbukira, chamumtima kuti ndinati, ‘Koma ndiye n’zochititsa chidwi bwanji!’ ”

Pauline wa kumpoto kwa England, anauza aphunzitsi ake kuti: “Masamu amandivuta kwambiri.” Mphunzitsiyo anam’funsa kuti: “Kodi ukufuna kuti uzikhoza? Ndikhoza kukuthandizatu.” Pauline akupitiriza kunena kuti: “Kuyambira pamenepo, anayesetsa kundithandiza mwapadera kwa miyezi ingapo, ankandiphunzitsa ngakhale tikaŵeruka. Ndinadziŵa kuti ankafuna kuti ndizikhoza komanso kuti ankandifunira zabwino. Podziŵa zimenezi ndinalimbikira kwambiri, ndipo ndinayamba kukhoza.”

Angie wa ku Scotland, amene panopa ali zaka za m’ma 30 amakumbukira aphunzitsi ake a hisitole a Graham. Iye anati: “Ankapangitsa phunziro la hisitole kukhala losangalatsa kwambiri! Ankasimba zimene zinachitika ngati nkhani ndipo mutu uliwonse ankauphunzitsa mosangalatsa. Ankaphunzitsa zonse monga kuti zikuchitika nthaŵi yomweyo.” Saiwalanso mayi Hewitt, aphunzitsi ake achikulire akalasi lake loyamba ku pulaimale. “Anali okoma mtima ndi ofunira ena zabwino. Tsiku lina tili m’kalasi, ndinapita kukawafunsa funso. Anandinyamula. Ndinaona kuti ankandikondadi.”

Timothy wa kumwera kwa Greece, anayamikira ponena mawu otsatiraŵa: “Ndikukumbukirabe aphunzitsi anga a sayansi. Anasinthiratu maganizo anga a momwe ndinkaonera dziko ndi moyo. Ankapangitsa kuti tikakhala m’kalasi tizigoma ndi zimene timaphunzira. Anatithandiza kwambiri kukonda maphunziro.”

Chitsanzo china ndi cha mkazi wa ku California, ku United States of America, dzina lake Ramona. Iye anati: “Aphunzitsi anga a ku sekondale ankakonda kwambiri Chingelezi. Chifukwa cha khama lawo, ifenso tinayamba kukonda Chingelezi! Ngakhale mbali zovuta ankazipanga kuoneka ngati zophweka.”

Jane wa ku Canada, ananena mosangalala za mphunzitsi wake wa phunziro lolimbitsa thupi amene anali “wokonda kuchita zinthu zosangalatsa ndi kuphunzira. Ankapita nafe kumalo osangalatsa kwambiri panja ndi kutiphunzitsa maseŵera omayenda pa chipale chofeŵa ndiponso kuŵedza nsomba m’nyanja za madzi ouma mwa kuboola bowo pamadzi oumawo. Nthaŵi zina mpaka tinkasonkha moto tokha n’kuphika mtundu winawake wamkate wa Amwenye a ku America. Zonsezi zinali zinthu zosangalatsa kwa ineyo chifukwa ndinali mtsikana wokonda kungokhala panyumba n’kumaŵerenga. ”

Helen ndi mkazi wamanyazi amene anabadwira ku Shanghai ndipo anaimba sukulu ku Hong Kong. Akukumbukira kuti: “Ndili mu kalasi lachisanu ku pulayimale, aphunzitsi anga ena anali a Chan, amene ankaphunzitsa maseŵera olimbitsa thupi ndiponso kujambula zithunzi ndi penti. Ndinali wochepa thupi komanso sindinkatha n’komwe kuseŵera mpira wamanja womadumphitsa ukonde ndiponso mpira wamanja wonjanjitsa n’kumagoletsa pa chingerengere chopachikidwa pamwamba. Iwo sanandichititse manyazi. Ankandiloleza kuseŵera maseŵera ena ondiyenera. Anali wolingalira za ena ndiponso wokoma mtima.

“Chimodzimodzinso kujambula, sindinkadziŵa kujambula zinthu zina zilizonse kapena kujambula anthu ndi penti. Choncho anandiuza kuti ndizingojambula mizere ya maluŵa yokongoletsera zinthu ndipo izi sizinkandivuta. Popeza ndinali wamng’ono poyerekezera ndi ana ena, anandiuza kuti ndibwereze kalasi yomweyo. Apa m’pamene panasinthira zinthu m’maphunziro anga. Ndinaphunzira kukhala wodzidalira ndipo ndinapita patsogolo. Sindidzasiya kuthokoza mphunzitsi ameneyu.”

Kodi ndi aphunzitsi ati amene amathandiza kwambiri? William Ayers anayankha m’buku lake lonena za kuphunzitsa lakuti To Teach—The Journey of a Teacher kuti: “Kuphunzitsa bwino, choyamba kumafuna kuti mphunzitsi akhale woganizira za ena, ndi wodzipereka pa ntchito yothandiza ana ake asukulu. . . . Kuphunzitsa bwino sikuti kumalira kutsatira njira zakezake zophunzitsira, kapena zochita zinazake zapadera . . . Chofunika kwenikweni pa kuphunzitsa ndicho chikondi.” Chotero kodi mphunzitsi wabwino n’ndani? Iye akuti: “Mphunzitsi amene anakukhudzani mtima, amene ankakumvetsani kapena amene ankakuganizirani kwambiri, mphunzitsi amene anakuyambitsani kukonda zinthu zimene iye ankazikonda monga nyimbo, masamu, Chilatini, ndege za mapepala.”

Mosakayikira, aphunzitsi ambiri akhala akuyamikiridwa ndi ophunzira ngakhale makolo ndipo motero zimenezi zawalimbikitsa kupitiriza kuphunzitsa ngakhale akamakumana ndi mavuto. Chifukwa chimodzi chimene chachititsa anthu ambiri kuyamikira ndicho chidwi chenicheni ndiponso kukoma mtima kumene aphunzitsiwo anasonyeza kwa wophunzirayo.

N’zoona, si aphunzitsi onse amene amachita zimenezi. Koma tidziŵenso kuti kaŵirikaŵiri aphunzitsi amakumana ndi mavuto ambiri amene amabwezera m’mbuyo zimene angachitire ana awo asukulu. Izi zikutipangitsa kufunsa kuti, N’chifukwa chiyani anthu amasankha ntchito yovutayi?

[Chithunzi patsamba 4]

“Chofunika kwenikweni pa kuphunzitsa ndicho chikondi”