Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’kusankhiranji Uphunzitsi?

N’kusankhiranji Uphunzitsi?

N’kusankhiranji Uphunzitsi?

“Aphunzitsi ambiri amasankha ntchitoyi chifukwa imathandiza anthu. Ndi ntchito imene imasintha miyoyo ya ana.”—Linatero buku la Teachers, Schools, and Society.

NGAKHALE kuti aphunzitsi ena amapangitsa ntchito ya uphunzitsi kuoneka ngati yophweka, ntchitoyi ili ndi zopinga zambiri monga kuchuluka kwa ana m’kalasi ndiponso kuchuluka zolemba; kuchuluka malamulo, ana osamvera ndiponso kuchepa kwa malipiro. Pedro, mphunzitsi wa ku Madrid, ku Spain, anati: “Uphunzitsi si ntchito yamaseŵera. Imafunika kukhala wodzimana kwambiri. Komabe, ngakhale kuti ili ndi poipira pake, ndimaona kuti ntchito ya uphunzitsi n’njopindulitsa kwambiri kuposa ina iliyonse yokhudza zamalonda.”

M’mayiko ambiri, masukulu amene ali m’matauni akuluakulu ndi amene amakhala ndi mavuto aakulu kwambiri. Mankhwala osokoneza bongo, kulekerera khalidwe loipa, ndiponso nthaŵi zina kusasamala kwa makolo kumawononga kwambiri moyo ndi malangizo operekedwa kusukulu. Kupanduka n’kofala. Choncho, n’chifukwa chiyani anthu ambiri ophunzira amasankha ntchito ya uphunzitsi?

Leemarys ndi Diana ndi aphunzitsi ku New York City. Amaphunzitsa ana oyambira zaka 5 kulekeza 10. Akazi ameneŵa amalankhula zinenero ziŵiri (Chingelezi ndi Chispaniya) ndipo kwenikweni amaphunzitsa ana olankhula Chispanya. Funso lathu linali lakuti . . .

Kodi N’chiyani Chimalimbikitsa Aphunzitsi?

Leemarys anati: “Mukufuna mudziŵe chimene chimandilimbikitsa? N’kukonda anatu basi. Ndimadziŵa kuti pali ana ena omwe palibe wina amene amawathandiza zochita zawo koma ine ndekha.”

Diana anati: “Ndinkaphunzitsa padera mwana wa mchimwene wanga, wa zaka zisanu ndi zitatu, amene sakhoza kusukulu makamaka kuŵerenga. Zinkandisangalatsa kwambiri kumuona akukhoza pamodzinso ndi anzake ena. Choncho ndinasankha zoloŵa uphunzitsi, ndipo ndinasiya ntchito imene ndinkagwira ku banki.”

Galamukani! inafunsa funso lomweli aphunzitsi a m’mayiko angapo, ndipo nazi zina zimene anayankha.

Giuliano, wa ku Italy amene ali zaka za m’ma 40, anafotokoza kuti: “Ndinasankha ntchito imeneyi chifukwa ndili pasukulu (kudzanja lamanja) ndinkachita nayo chidwi. Ndinkaiona kuti imaphunzitsa munthu zinthu zambiri ndiponso imakupatsa mwayi waukulu wothandiza kwambiri anthu ena. Chidwi chimene ndinali nacho poyambacho chinandithandiza kupirira mavuto amene ndinkapeza nditangoyamba kumene ntchitoyi.”

Nick wa ku New South Wales, ku Australia, anati: “Ntchito yogwirizana ndi maphunziro anga ofufuza zamankhwala inali yosoŵa, koma ya uphunzitsi inali yosavuta kupeza. Kuyambira pamenepo ndinaona kuti ndikusangalala ndi uphunzitsi, ndipo ananso amasangalala ndi momwe ndimaphunzitsira.”

Kaŵirikaŵiri chitsanzo cha makolo kwenikweni n’chimene chimapangitsa ena kusankha uphunzitsi. William, wa ku Kenya, anayankha motere funso lathu lija: “Kuti ndikhale mphunzitsi anandilimbikitsa kwambiri ndi bambo anga, amene anali m’phunzitsi m’1952. Kudziŵa kuti ndikusula malingaliro a ana kwandipangitsa kupitirizabe ntchitoyi.”

Rosemary, wa ku Kenya komweko, anatiuza kuti: “Nthaŵi zonse ndinkafuna kuthandiza anthu ovutika. Choncho ndinkafuna kukhala nesi kapena mphunzitsi. Ntchito ya uphunzitsi ndi imene inapezeka msanga. Komanso ndimaikonda kwambiri ntchitoyi chifukwa chakuti ndine mayi.”

Berthold, wa ku Düren, ku Germany, chinamulimbikitsa kuloŵa uphunzitsi ndi chinthu china osati chimenechi. Iye anati: “Mkazi wanga anandiuza kuti uphunzitsi ungandiyenerere kwambiri.” Ndipo nditayamba ntchitoyi ndinaona kuti ankanena zoona. Anatinso: “Ntchito yanga tsopano imandisangalatsa kwambiri. Mphunzitsi akazindikira kufunika kwa maphunziro ndipo akakhala wokonda ana, sizingamuvute kukhala mphunzitsi wabwino, wopambana, wakhama ndi wokhutira.”

Masahiro, mphunzitsi wa ku Nakatsu City, ku Japan, anati: “Chimene chinandilimbikitsa kuloŵa uphunzitsi n’chakuti nditafika sitandade 5 ndinali ndi aphunzitsi abwino kwambiri. Ankatiphunzitsa modziperekadi. Ndipo chimene chandipangitsa kupitiriza ntchito imeneyi ndi chakuti ndimakonda ana.”

Yoshiya, yemwenso ndi wa ku Japan, amenenso tsopano ali ndi zaka 54, anali pantchito yamalipiro abwino pa fakitale inayake koma anaona kuti anali kapolo wantchitoyo ndiponso woyenda popita kuntchitoko. “Tsiku lina, ndinati chamumtima, ‘Kodi zimenezi ndichita mpaka liti?’ Ndinaganiza zofuna ntchito imene ndingamagwire kwambiri ndi anthu osati zinthu. Uphunzitsi ndi ntchito yapadera. Umagwira ntchito ndi ana. Imathandiza anthu ena.”

Valentina wa ku St. Petersburg, ku Russia, amaona kuti pamenepa m’pokomera pena pa uphunzitsi. Anati: “Uphunzitsi ndi ntchito ya kumtima kwanga. Ndakhala ndikuphunzitsa ku sukulu ya mkaka kwa zaka 37. Ndimasangalala kucheza ndi ana makamaka ang’onoang’ono. Ndimaikonda ntchitoyi, n’chifukwa chake mpaka pano sindinapumebe pantchito.”

William Ayers yemwe ndi mphunzitsi, analemba kuti: “Anthu amafuna uphunzitsi chifukwa chakuti amakonda ana ndi achinyamata, kapena chifukwa amakonda kucheza nawo, kuwaona akukula ndi kukhala odziŵa zinthu, otha kuchita zinthu bwino ndiponso amaudindo awo. . . . Anthu amaphunzitsa . . . mofanana ndi kudzipereka kwa ena monga mphatso. Ndimaphunzitsa pofuna kupanga dzikoli kukhala malo abwino.”

Inde, ngakhale kuti pali mavuto ndi zokhumudwitsa zambiri, akazi ndi amuna odzipereka ambiri amasangalatsidwa ndi ntchito ya uphunzitsi. Kodi ndi mavuto akuluakulu otani amene amakumana nawo? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.

[Bokosi patsamba 6]

Mfundo Zabwino Pankhani ya Kulankhulana kwa Aphunzitsi ndi Makolo

✔ Adziŵeni makolo. Kutero si kutaya nthaŵi ayi. N’kopindulitsa kwa nonsenu kugwiritsa ntchito nthaŵi mwanjira imeneyi. Ndi nthaŵi yanu yodziŵana ndi amene angakhale anzanu othandizana nanu ntchito.

✔ Lankhulani monga mukulankhula ndi kholo—musadzitukumule kapena kuwanyoza. Peŵani kugwiritsa ntchito mawu odziŵa aphunzitsi okha.

✔ Mukamakamba za ana awowo, tchulani kwambiri zinthu zabwino zimene anawo amachita. Kuyamikira kumathandiza kwambiri kusiyana ndi kuwanena. Fotokozani zimene makolowo angachite pothandiza mwana wawo kuti apambane.

✔ Apatseni mpata wolankhula makolowo, ndipo amvetsereni kwambiri.

✔ Zindikirani momwe ku nyumba kwa mwanayo kulili. Ngati mungathe, pitani kwawo komweko.

✔ Ikani tsiku loti mudzaonanenso. Izi n’zofunika. Zimasonyeza kuti mukuwafuniradi zabwino.—Zachokera m’buku lakuti Teaching in America.

[Chithunzi patsamba 6]

‘Bambo anga analinso mphunzitsi,’ anatero WILLIAM, WA KU KENYA

[Chithunzi patsamba 7]

“Ndimakonda kucheza ndi ana,” anatero VALENTINA, WA KU RUSSIA

[Chithunzi patsamba 7]

“Uphunzitsi ndi ntchito yapadera. Umagwira ntchito ndi ana,” anatero YOSHIYA, WA KU JAPAN