Uchi—Mankhwala Ozuna
Uchi—Mankhwala Ozuna
AKATSWIRI ena ofufuza mankhwala asangalala podziŵa kuti uchi uli ndi mphamvu yochepetsa tizilombo todwalitsa ndiponso yoletsa kutupa. Nyuzipepala ina ya ku Canada yotchedwa The Globe and Mail inati: “Uchi umapha tizilombo todwalitsa kusiyana ndi mankhwala ambirimbiri amene akukanika kupheratu tizilomboto.”
Kodi mu uchi muli chiyani chimene chimachititsa kuti uzichiritsa? Yankho lake likukhudza njuchi imene imagwira ntchito yotenga timadzi tam’maluŵa. M’malovu a njuchi muli mankhwala ena ake amene amathandiza kusungunula timadzi tam’maluŵato. Timadziti tikasungunuka timasanduka mankhwala ena ake amenenso anthu amatha kupanga paokha ndipo amatsukira zilonda. Kaŵirikaŵiri, paokha mankhwala ameneŵa akawaika pabala amathandiza kwa nthaŵi yochepa chabe; koma akaikapo uchi, zimathandiza kwambiri. Nyuzipepala ya Globe ija inati, “Uchi akauika pa chilonda umasungunuka pang’ono chifukwa cha timadzi tinatake tam’thupi, ndipo zikatero asidi amene amapezeka mu uchiwo amachepa mphamvu.” Timadzi tam’thupiti tikakumana ndi asidi wochepa mphamvuyu timayamba kugwira ntchito yake yolimbana ndi tizilomboto. Shuga amene amapezeka mu uchi amasungunuka pang’onopang’ono. Izi zikamachitika chonchi, timadzi tija timapanga mankhwala okwanira kuphera tizilombo timene tili pachilondacho popanda kukulitsa chilondacho.
Nyuzipepala ya Globe inanenanso kuti uchi uli ndi zinthu zingapo zimene zingathandize pochiritsa chilonda. Nyuzipepalayo inanena kuti: “Kambali kenakake kochepa kwambiri ka uchi kamathandiza kuti chilonda chikhale chofeŵa ndipo izi zimathandiza kuti chilondacho chisachite nkhanambo kapena kunyekera m’kati. Uchi umathandiza kuti timitsempha tonyamula magazi tilumikizanenso pachilondapo ndipo kenaka n’kupangitsa kuti pabwerenso chikopa china chotsekapo.” Komanso mankhwala ena ake amene amapezeka mu uchiwo ali ndi mphamvu “yoletsa kutupa, mphamvu yothandiza kuti magazi aziyendabe bwinobwino ndiponso kuti chilondacho ‘chisamangotulutsa madzi.’”
“Komabe si kuti uchi umathandiza munthu wina aliyense,” inatero nyuzipapalayo. Akuti mu uchi mumatha kupezekanso timapoizoni tinatake. Mabungwe ena oona za chakudya cha poizoni, monga bungwe la Health Canada’s Botulism Reference Service komanso mabungwe oona za matenda a ana amalangiza kuti si bwino kum’patsa uchi mwana amene sanakwanitse chaka chimodzi chifukwa chakuti “makanda amakhala alibe tizilombo tam’mimba tokwanira towateteza ku tizilombo timene timadwalitsa.”