Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uphunzitsi Uli M’pokomera Pake

Uphunzitsi Uli M’pokomera Pake

Uphunzitsi Uli M’pokomera Pake

“Kodi mukufuna kudziŵa chimene chandipangitsa kupitiriza ntchito ya uphunzitsi? N’chifukwa chakuti ngakhale kuti ntchito ya uphunzitsi ndi yovuta komanso yotopetsa, kuona ana akusangalala ndi maphunziro ndiponso akukhoza, n’zimene zimandilimbikitsa kupitirizabe,” anatero Leemarys, mphunzitsi wa ku New York City.

NGAKHALE kuti pali mavuto, zopinga ndiponso zokhumudwitsa zonsezi, aphunzitsi ambiri padziko lonse lapansi akupitiriza ntchito imene anasankhayi. Kodi n’chiyani chimalimbikitsa ana asukulu ambiri kulimbikira kuti adzakhale aphunzitsi pamene akudziŵa kuti anthu sadzawayamikira kwenikweni? N’chiyani chimawapangitsa kupitiriza ntchitoyi?

Inna, mphunzitsi wa ku Russia akufotokoza kuti: “N’zosangalatsa kuona ana amene unawaphunzitsa atakula, kuwamva akunena kuti zimene unawaphunzitsa zinawapindulitsa kwambiri. Zimalimbikitsa kwambiri akamati amasangalala akamakumbukira zaka zimene unali kuwaphunzitsa.”

Giuliano, mphunzitsi amene tatchula zimene ananena m’nkhani yoyamba ija, anati: “Chokondweretsa china chachikulu ndicho kudziŵa kuti monga mphunzitsi wakwanitsa cholinga chokulitsa chidwi cha mwana pa phunziro linalake. Mwachitsanzo, nditalongosola mfundo inayake paphunziro la hisitole, ophunzira ena anati: ‘Musasiyire pomwepo. Tapitirizani! ’ Mawu ochokera mu mtima ameneŵa angathandize mphunzitsi kusangalala tsiku limene wapita kusukulu ali wokhumudwa, chifukwa amadziŵa kuti anawo wawapatsa maganizo ena atsopano. Umasangalala kwambiri kuona nkhope zawo zili zosangalala chifukwa chakuti amvetsa phunziro.”

Elena, mphuzitsi wa ku Italy, anati: “Ine ndimaona kuti nthaŵi zambiri munthu umasangalala ndi zinthu zing’onozing’ono za tsiku ndi tsiku, zinthu zazing’ono zimene ana akukhoza, osati ndi zinthu zikuluzikulu, zimene sizichitikachitika.”

Connie, mayi wa ku Australia amene ali ndi zaka zongopitirira 30, anati: “Zimasangalatsa zedi wophunzira amene unkam’phunzitsa akakulembera kalata yothokoza chifukwa cha ntchito imene unagwira.”

Oscar wa ku Mendoza, ku Argentina, ananena mawu ofananawo. Iye anati: “Ndimaona kuti ndinachita ntchito yaikulu ndikakumana ndi ophunzira anga panjira kapena kwinakwake n’kumandiyamikira zimene ndinawaphunzitsa.” Angel, wa ku Madrid, ku Spain, anati: “Ineyo mbali ya moyo wanga yathera kuchita ntchito yosangalatsa komanso yovuta imeneyi modzipereka ndipo ndikamaona ana amene ndinawaphunzitsa atasanduka azibambo ndi azimayi aulemu wawo, chifukwa chakuti ndinachita mbali yanga, ndithudi zimandikondweretsa kwambiri.”

Leemarys, amene wagwidwa mawu kumayambiriro kuja, anati: “Ndimaona kuti aphunzitsi ndi anthu ofunika kwambiri. Nthaŵi zina anthu amatidabwa kuti tinasankhiranji chintchito chachikulu ngati chimenechi. Koma ngati mungathandize mwana m’modzi kapena ana khumi ndiye kuti mwagwira ntchito, ndipo izi zimasangalatsa kwambiri. Mumagwira ntchito yanu mosangalala.”

Kodi Munawathokozapo Aphunzitsi Anu?

Kodi inu monga mwana wasukulu kapena kholo, munayamba mwathokozapo aphunzitsi chifukwa cha nthaŵi imene anawononga, khama ndiponso chidwi chimene anasonyeza pophunzitsa? Kapena kodi munawatumizirako khadi kapena kalata yothokoza? Arthur, wa ku Nairobi, ku Kenya, ananena mfundo yofunika, yakuti: “Aphunzitsinso amalimbikira akamayamikiridwa. Boma, makolo, ndiponso ophunzira ayenera kuwayamikira ndiponso kuthokoza ntchito imene amagwira.”

Wolemba mabuku wina LouAnne Johnson yemwenso ndi mphunzitsi anati: “Pakalata iliyonse yonyoza aphunzitsi imene ndimalandira, ndimalandiranso makalata ena 100 owayamikira aphunzitsi, kutsimikizira zimene ndimakhulupirira zakuti pali aphunzitsi abwino ambiri kuposa oipa.” Zosangalatsa n’zakuti, anthu ambiri mpaka amalipira anthu ofufuza kuti “awathandize kupeza mphunzitsi amene anawaphunzitsapo kale. Anthu akufuna kupeza aphunzitsi awo kuti awathokoze.”

Aphunzitsi amayala maziko abwino a maphunziro a munthu aliyense. Ngakhale mapulofesa apamwamba kwambiri a m’mayunivesite otchuka anafika pamenepo chifukwa cha aphunzitsi amene anataya nthaŵi yawo n’kuchita khama kuti awapatse chilakolako chofuna kuphunzira, kudziŵa, ndi kumvetsa zinthu. Arthur, wa ku Nairobi, akuti: “Akuluakulu aboma onse ndiponso amabungwe amene si aboma nthaŵi ina yake m’moyo wawo anaphunzitsidwako ndi mphunzitsi.”

Tiyenera kuyamikira kwambiri akazi ndi amuna ameneŵa amene anadzutsa chidwi chathu, amene anatilimbikitsa, amene anatisonyeza momwe tingakwaniritsire chikhumbo chathu cha kudziŵa ndi kumvetsa zinthu.

Chonchotu Tiyeneradi kuyamikira kwambiri Mphunzitsi Wamkulu, Yehova Mulungu, amene anauzira mawu a pa Miyambo 2:1-6, akuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kupfuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”

Onani mawu akuti “ukalandira,” “ukaitananso,” “ukaifunafuna,” amene akupezeka m’mawu ochititsa chidwi ameneŵa. Tangolingalirani kuti, ngati titafunitsitsadi kutero, titha “kum’dziŵadi Mulungu.” Ndithudi ameneŵa ndiwo maphunziro apamwamba koposa onse.

[Bokosi patsamba 13]

Kholo Losangalala

Iyi ndi kalata imene mphunzitsi wina ku New York City analandira:

“Ndikufuna kukuthokozani kuchokera pansi pamtima chifukwa cha zimene munachitira ana anga. Chifukwa chakuti munawasamalira, kuwakomera mtima, ndiponso chifukwa cha luso lanu, mwawathandiza kukhala anzeru kwambiri ndipo ndikukhulupirira kuti pakanapanda inu si bwenzi atafika pamenepa. Ndimanyadira ana anga kwambiri chifukwa cha zimene munawaphunzitsa ndipo sindidzaiŵala zimenezi. Ine wanu, S. B.”

Kodi alipo mphunzitsi aliyense amene mungam’limbikitse?

[Chithunzi patsamba 12]

‘N’zosangalatsa kuona nkhope za ophunzira zikusangalala chifukwa chakuti amvetsa phunzirolo, anatero GIULIANO, WA KU ITALY

[Zithunzi patsamba 13]

‘Zimasangalatsa kwambiri wophunzira akalemba kalata yothokoza, anatero CONNIE, WA KU AUSTRALIA