Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amayi Amachita Ntchito Zambiri

Amayi Amachita Ntchito Zambiri

Amayi Amachita Ntchito Zambiri

4:50 mmaŵa. Polira chifukwa cha tulo, khanda lina dzina lake Alex likukwerakwera amayi ake omwe dzina lawo ndi Helen. Ana ena aŵiri a Helen, Penny (wazaka 5) ndiponso Joanna (wazaka 12), komanso mwamuna wake dzina lake Nick, akugona. Helen akum’nyamula Alex n’kumuika pabedi ndipo akum’patsa bere. Helen akulephera kuti agonenso.

5:45 mmaŵa. Helen akum’zembera mwanayo kupita ku khichini kukaphika tiyi ndipo akuŵerenga zina n’zina.

6:15–7:20 mmaŵa. Mwamuna wake Nick akudzuka. Helen akudzutsa Penny ndi Joanna, kenaka akukonza kadzutsa ndiponso akukonzakonza pakhomo. Nthaŵi itakwana 7:15 mmaŵa, mwamuna wake Nick akunyamuka ulendo wakuntchito ndipo popita akum’tenga Joanna n’kukam’siya kusukulu. Amayi ake a Helen akufika kuti azimuyang’anira Alex amayi ake akachoka.

7:30 mmaŵa. Helen akukam’siya Penny kumene amaphunzira sukulu yamkaka. Ulendo wopita kuntchito ukupangitsa Helen kuona kuti kukhala mayi si zocheza. Iye akuti, “Ndi ntchito yovuta kwambiri kuposa ntchito zonse zimene ndinagwirapo.”

8:10 mmaŵa. Helen wangopeza ntchito zoti achite zitangoti mbwee pa desiki yake kuntchito. Nkhaŵa yake n’njakuti mwina akangokhalanso ndi pathupi pena akhoza kum’chotsa ntchito basi. Koma m’pofunikabe kuti nayenso azigwira ntchito chifukwa malipiro a mwamuna wake pawokha sangakwanire kusamalira banjalo.

10:43 mmaŵa. Helen atangoika pansi telefoni yomuuza za ana ake, mkazi wina dzina lake Nancy, amene amagwira naye ntchito akum’ziziritsa mtima kuti: “Ana ako ukuwalera bwino kwambiri.” Chifukwa cha mawuŵa, misozi yayamba kutsetsereka m’masaya a Helen.

12:05 masana. Helen akutenga mwakhamanikhamani buledi wopaka zokometsera n’kuyamba kudya kwinaku akuganizira zakale asanabereke mwana wake woyamba wamkazi. Nthaŵi imeneyo anali atalinganiza zinthu zoti azidzachita panthaŵi yake “yopuma.” ‘Ha, kumeneko kunali kulemba m’madzi ndithu!’ iye anatero.

3:10 madzulo. Atalandira mafoni ambirimbiri ochokera kunyumba omuuza zinthu zoseketsa zimene Alex akuchita, Helen akufotokoza kuti amakonda ana ake kwambiri ponena kuti: “Ndithudi, kale langa lonse sindinakondaneko ndi munthu wina ngati mmene ndimakonderana ndi ana angaŵa.” Kukhala ndi maganizo anzeru ameneŵa kunam’thandiza kuthetsa mavuto oyambirira amene sanawakonzekere n’komwe.

5:10 madzulo. Atapita kukam’tenga Joanna, Helen akupitanso ku timaulendo tingapo kukachita zinthu zina n’zina. Kenaka akumuimbira telefoni mwamuna wake Nick n’kumukumbutsa kuti asaiwale kuti ndiye amene akufunika kupita kukam’tenga Penny.

6:00–7:30 madzulo. Atafika kunyumba, Helen akuwalandira agogo ntchito yawo yoyang’anira Alex, ndiyeno atatero akugwira ntchito zina za pakhomo, kenaka n’kuphika chakudya chamadzulo. Atamufunsa zinthu zimene mwana amafuna, Helen akudzuma n’kunena kuti: “Khanda n’losautsa chifukwa limafuna chilichonse chokhudza mayi ake; limafuna kuti aziliyangata m’manja, limafuna kukhudza thupi lawo, kuyamwa ndiponso silifuna kuti mayi akewo agone tulo.”

8:30–10:00 usiku. Helen akum’thandiza mwana wawo Joanna kulemba za kusukulu ndipo akum’yamwitsa Alex. Pamene mwamuna wake Nick akuŵerengera mwana wawo Penny kwa mphindi 30, Helen akugwiragwira ntchito zina zapakhomo.

11:15 usiku. Penny ndi Joanna atapita kukagona, Alex adakali m’maso m’manja mwa amayi ake, koma kenaka akugona. “Ndikukhulupirira kuti wagona tsopano,” akutero Helen pouza mwamuna wake Nick yemwe wayamba kale kusinza.