Kodi Ndingalalikire Bwanji Anzanga a Kusukulu?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingalalikire Bwanji Anzanga a Kusukulu?
“Ndinali kolalikira ndipo mwadzidzidzi ndinakumana ndi munthu amene ndimadziŵana naye. Ndinatheratu mphamvu! Ndiye mnzanga amene ndinali kulalikira naye anangoloŵererapo n’kuyamba kulankhulana ndi munthuyo m’malo mwa ine,” anatero Alberto.
“Ndinkadziŵa kuti mnzanga wina amene tili m’kalasi limodzi amakhala msewu umenewu, motero ndinasiyira mchimwene wanga kuti ndiye azilankhula tikafika pakhomo lililonse. Koma kenaka nayenso anatopa ndiye anandipempha kuti ndilankhuleko pakhomo lotsatira. Ndinagogoda, ndipo ndinangolakalaka nditaloŵa pansi chifukwa yemwe anatsegula chitsekoyo anali mnzanga yemweyo! Thupi lonse linangoti zii chifukwa cha mantha!” anatero James.
NTHAŴI zambiri achinyamata amaona kuti kukambirana zachipembedzo si “udolo.” Komabe kwa Akristu oona, achinyamata amayamikira mwayi umene Mulungu anawapatsa womauza anzawo chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chake Mboni za Yehova zachinyamata zochuluka zimachita nawo ntchito yolalikira khomo ndi khomo. Koma ena amalalikira mwamantha poopa kukumana ndi munthu wodziŵana naye wakusukulu kwawo. Ngakhale kuti Jennifer anamaliza kalekale sukulu ya sekondale iye ananena kuti, “Ndimachitabe mantha ndikamakumana ndi anthu amene tinali limodzi kusukulu.”
Ngati ndinu Mkristu wachinyamata, nthaŵi zina mwina mumamvanso chimodzimodzi. Inde, palibe amene amafuna kuti anzake azimuthaŵa, motero si chinthu chodabwitsa kukhala n’timantha mukamaganiza zokambirana zachipembedzo ndi anzanu akusukulu. * Koma si ndiye kuti muzifika mpaka poumiratu thupi ndi mantha. Kodi mukum’kumbukira munthu amene Baibulo limamutcha kuti “Yosefe wa ku Arimateya”? Iye anakhulupirira zinthu zimene anaphunzira kwa Yesu. Komatu Baibulo limati Yosefe ameneyu anali “wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda.” (Yohane 19:38) Ndiye kodi inuyo mungamve bwanji ngati mutakhala ndi mnzanu amene safuna kuti ena adziŵe kuti mumagwirizana naye? (Luka 12:8, 9) Motero sizodabwitsa, kuti Mulungu amafuna kuti Akristu onse ‘alengeze kwa ena’ za chikhulupiriro chawo. (Aroma 10:10, NW) Ndiye kutinso muyenera kulankhula ndi achinyamata a kusukulu kwanu.
Yosefe wa ku Arimateya anathetsa mantha ake, mpaka anafika pokapempha chilolezo choti akaike m’manda mtembo wa Yesu. Kodi inuyo mungathetse bwanji mantha anuwo.
Kuphunzira Kulalikira Mofunitsitsa
Mtumwi Paulo sankachita manyazi n’komwe kuuza ena za chikhulupiro chake. Pa Aroma 1:15, iye analongosola kuti anali kuchita kufuna ndithu kulalikira uthenga wa m’Baibulo! Kodi n’chiyani chinam’chititsa kukhala wofunitsitsa kutero? Malingana ndi vesi 16 iye anati: “Uthenga wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira.” Nanga inuyo bwanji? Kodi choonadi mwachizindikiradi panokha. (Aroma 12:2) Kodi kuchokera pansi pamtima mumakhulupiriradi panokha kuti uthenga wa m’Baibulo ndi “mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa”?
Kungopita kumisonkhano yachikristu ndi makolo anu si kokwanira. Mtsikana wina dzina lake Deborah anati, “Kupita kumisonkhano sikunkandivuta, chifukwa makolo anga ankachita kundipangira. Koma anthu akamandifunsa mafunso okhudza Baibulo, zinkandivuta kuyankha.” Mtsikana winanso dzina lake Mi Young akuvomereza kuti: “Tiyenera kukhulupirira patokha kuchokera pansi pamtima kuti zoonadi ichi n’choonadi.”
Kodi n’chiyani chimene chingakulimbikitseni kuti muziuza ena zimene mukudziŵa m’Baibulo? Inuyo muziliŵerenga Baibulolo panokha. Mnyamata wina dzina lake Sean anati: “Mukayamba kuŵerenga Baibulo panokha, choonadi chimayamba kukhala chanuchanu chifukwatu mumadziŵerengera nokha.” N’zoona kuti si kuti aliyense amakonda kuŵerenga. Shevon ananena kuti: “Ine sindikonda kuŵerenga, motero poyamba zinkandivuta kwambiri kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Koma kenaka m’kupita kwa nthaŵi ndinayamba kutero.”
Kodi kuŵerenga kwakhama kotereku kumapindulitsa motani? Mtumwi Paulo anati: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” (Aroma 10:17) Chikhulupiriro chanu chikayamba kukula, mumayambanso kuona zinthu m’njira ina. Mtsikana wina wa ku Brazil wotchedwa Elisângela anaona kuti: “Kukhala Mkristu ndi chinthu chaulemu kwambiri, si chinthu chochititsa manyazi ayi.” N’zoonadi kuti chikhulupiriro chanu chikamakula, mumangofuna kuti muuzeko ena basi, ngakhalenso anzanu a m’kalasi mwanu. Paulo anati: “Tikhulupira, chifukwa chake tilankhula.” (2 Akorinto 4:13) Nanga mukapanda kutero, kodi mungakhale bwanji ‘opanda mwazi’ wa ena ngati simukuwadziŵitsa uthenga wopatsa moyo achinyamata amene mumaonana nawo tsiku lililonse?—Machitidwe 20:26, 27.
Komabe achinyamata ena achikristu amaona kuti sangakwanitse kuuza ena za m’Baibulo. Mnyamata wina wotchedwa Joshua ananena kuti, “Ngati sukudziŵa chonena, kulalikira si kusangalatsa n’komwe.” Apanso tinganene kuti ngati mutalidziŵa mozama Baibulo zingakuthandizeni kuti muligwiritse ntchito mwaluso. (2 Timoteo 2:15) M’mipingo ya Mboni za Yehova, achinyamata angathe kupempha akulu a mumpingomo kuti awaphunzitse maluso akuphunzitsa ena. Mnyamata wina wochokera ku Germany dzina lake Matthias anati: “Kulalikira kunayamba kundisangalatsa nditayamba kulankhulana zenizeni ndi anthu, osati kumangogaŵira chabe mabuku ofotokoza za m’Baibulo.”
Komanso osaiwala kuti mungathe kupemphera kuti Mulungu akuthandizeni kuti muzilankhula molimba mtima. (Machitidwe 4:29) Mtumwi Paulo anathandizidwa ndi Mulungu m’njira imeneyi. Pa 1 Atesalonika 2:2, iye anati: “Tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.” Malinga ndi zimene buku lina linanena, akuti mawu ameneŵa angathenso kulembedwa kuti: “Mulungu anachotsa mantha m’mitima mwathu.” Motero bwanji osam’pempha Mulungu kuti akuchotseni mantha m’mtima mwanu?
Kudzidziŵikitsa Kwa Ena
Mogwirizana ndi pemphero limenelo, mungachitenso chinthu china chofunika kulimba mtima kwambiri. Mtsikana wina wa ku Britain wotchedwa Chic anapereka malangizo akuti: “Uzani anzanu a kusukulu kuti ndinu Mkristu.” Sibwino kuti mukhale ‘wophunzira wobisika.’ Mtsikana wina wotchedwa Rebecca anavomereza kuti poyamba akamalalikira ankaopa kwambiri kukumana ndi munthu wom’dziŵa. Koma akuti anadzazindikira kuti “ukamuuziratu kuti ndiwe Mkristu ndi kuti umayenda khomo ndi khomo, nthaŵi zina amafunsa kuti, ‘Ndiye kwathu udzafikako liti?’”
Koma kodi mukuchita kudikira kuti mudzakumane naye mwamwayi basi? Ayi ndithu yesetsani kupeza mpata wouza ena chikhulupiriro chanu kusukulu. Kumbukirani mafunso amene mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:14) Inuyo ndi amene mungathe kuwathandiza mosavuta anzanu a m’kalasi lanu kuti amve zimenezi. Mtsikana wina wotchedwa Iraida ananena kuti: “Sukulu ndi gawo lolalikira limene ife tokha ndi amene tingafikeko.” Motero achinyamata ambiri amatengerapo mwayi umenewu polalikira mwamwayi.
Komabe nthaŵi zina pamakhala ntchito yoti muchite m’kalasi imene imakupatsani mpata wouza ena choonadi cha m’Baibulo. Mtsikana wina wa ku Britain dzina lake Jaimie ananena kuti: “Tsiku lina tikuphunzira phunziro lasayansi tinali kukambirana kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera kuzinthu zina, ndipo ine ndinanena zimene ndimakhulupirira. Mnyamata wina anandiseka n’kunena kuti Mboni za Yehova ndi anthu opanda nzeru ndipo si oyenera kuyimba sukulu. Koma nthaŵi yomweyo ana ena m’kalasimo anandikhalira kumbuyo.” N’zachionekere kuti zinthu zinam’yendera bwino chifukwa chodziŵika kuti ndi Mkristu. Jaimie akunenanso kuti: “Mapeto ake ndinapeza mwayi wom’siyira mtsikana wina wa m’kalasi lathu buku lonena za nkhaniyi lakuti Is There a Creator Who Cares About You? *
Mtsikana wina wazaka 14 wa ku Romania wotchedwa Roxana analongosolanso nkhani yangati yomweyi. Iye anati: “Aphunzitsi anga analengeza kuti kalasi yathu ikambirana za mowa, fodya, ndi mankhwala osokoneza bongo. Motero ndinatenga nkhani ya m’Galamukani! ya pa April 8, 2000 yakuti ‘Mmene Mungasiyire Kusuta Fodya.’ Mnzanga wina wa m’kalasi lathulo anaona magaziniyo n’kuitenga ndipo anakana kundibwezera. Ataiŵerenga, anati watsimikiza kuti asiya kusuta fodya.”
Sikuti nthaŵi zonse zinthu zingakuyendereni bwino chonchi. Koma Mlaliki 11:6 amatilimbikitsa kuti: “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino.” Ngakhale kuti anzanuwo sakusonyeza chidwi, kuwauza zimene mumakhulupirira kungachititse kuti nthaŵi ina mudzakambirane mosavuta ngati mutadzakumana nawo muutumiki woyendera nyumba ndi nyumba. Mtsikana wina wa ku Britain dzina lake Jessica anati: “Kulalikira kwa anthu amene munadziŵana nawo kusukulu n’kosavuta chifukwa mumakhala kuti mukudziŵana nawo kale.” Inunso mungadabwe kuona chidwi chimene anzanu ena akusukulu angakhale nacho pofuna kudziŵa zimene mumakhulupirira.
N’zoona kuti si onse amene angakulandireni bwino. Koma Yesu anapereka malangizo othandiza kwambiri akuti: “Yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo . . . sansani fumbi m’mapazi anu.” (Mateyu 10:14) Kapena tinganene kuti, akakana simuyenera kupsa nazo mtima. Ingochokani mwamtendere ndipo funani munthu wina amene angafune kwambiri kumvetsera. Mungathebe kupeza anthu ena oona mtima amene ali ndi njala ya choonadi ndiponso amene alidi ofunitsitsa kukumvetserani. Kodi sizingakhale zosangalatsa ngati wina wa anthuŵa atakhala mnzanu wakusukulu? Ngati ndi choncho, mungadzasangalale chifukwa chosiya kuopa kuuzako anzanu a m’kalasi lanu za chikhulupiriro chanu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Zingakhale Bwanji Ngati Nditakumana ndi Winawake wa Kusukulu Kwathu?,” yomwe ili mu magazini ya March 8, 2002.
^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 16]
“Mukayamba kuŵerenga Baibulo panokha, choonadi chimayamba kukhala chanuchanu,” anatero Sean
[Chithunzi patsamba 14]
Musachite mantha kudzidziŵikitsa kuti ndinu Mkristu
[Chithunzi patsamba 14]
Ntchito zoti muchite m’kalasi nthaŵi zambiri zimakupatsani mpata wouza ena choonadi cha m’Baibulo