Kulimbana ndi Mavuto Okhala Mayi
Kulimbana ndi Mavuto Okhala Mayi
Popeza kuti ana amaimira nzika za m’tsogolo, ndiye kuti amayi awo ayeneradi kulandira ulemu waukulu ndiponso kuwathandiza. Ngakhale kuti anthu masiku ano amanena zinthu zosiyanasiyana pankhani ya kukhala mayi, Baibulo limatsimikiza kuti ana ndi madalitso ochokera kwa Mulungu ndipo akhoza kuchititsa makolo kukhala okondwa. (Salmo 127:3-5) Komabe si kuti m’Malemba mulibe nkhani zamavuto a amayi. M’Baibulo munalembedwa mavuto ambirimbiri a amayi.
Zimene makolo amaganizira kuti achite pa nkhani ya kulera ana ndiponso kukhala mayi zimakhudza kwambiri zochitika ndiponso moyo wa ana awo. Zikhoza kusintha kwambiri moyo wamakolowo, choncho m’pofunika kuziganizira mozama kwambiri. Ena mwa mafunso amene angawaganizire ndi onga akuti: Kodi mayi ayenera kumagwira ntchito yolembedwa? Ngati yankho litakhala lakuti inde, kodi ayenera kumagwira ntchitoyo kwanthaŵi yaitali bwanji? Kodi ndani amene azisamalira anawo mayiyo akakhala ali kuntchito? Chachikulu n’chakuti, makolo ayenera kuchita zimene akudziŵa kuti n’zothandizadi kwambiri kwa ana awo ndiponso zimene zili zoyenera pamaso pa Mulungu.
Komabe azimayi asamaone ngati alibe owathandiza akamayesa kuchita zinthu mwanzeru. Akhoza kupeza chilimbikitso chachikulu m’mawu a pa Yesaya 40:11 m’Baibulo la New World Translation amene amasonyeza kuti Mulungu amaganizira kwambiri za zinthu zimene amayi amene ali ndi makanda amafunikira, chifukwa iye ‘adzawachitira zinthu mosamala.’ Mulungu amasonyeza kuganizira amayi kumeneku mwakupereka malangizo ochuluka m’Baibulo amene amapangitsa kuti amayi azisangalala ndiponso kuti ntchito yawoyi iziwayendera bwino.
❖ Khalani wokhutira ndi zimene mungathe kuchita: Akristu ayenera kudziŵika chifukwa cha kukhutira ndi zimene amatha kuchita. (Afilipi 4:5) Mayi wina amene amalemba mabuku dzina lake Janet, anaona kufunika kwa mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinayamba kubereka ndili ndi maganizo odzithemba kwambiri. Ndinkangoti Ineyo ndikadzayamba kubereka, ndidzakhala mayi wabwino kuposa amayi onse. Ndinaŵerenga mabuku ambirimbiri okhudza amayi ndiponso ndinamvetsera zonena za alangizi ambirimbiri. Koma mmalo moona kuti zinthu zikundiyendera bwino ndiponso kuti ndafikapodi, ndinangoona kuti zikundikanika ndiponso zikungondipatsa maganizo.” Iye anati “kutsatira maimvaimva, n’kumalimbana n’kuti nawenso ufanane ndi zongomvazo kumangokuziziritsani nkhongono ndipo kumakubweretserani nkhaŵa ndi maganizo odziona ngati mwalakwa.”
❖ Osalira zambiri: Magazini yotchedwa Newsweek inalemba kuti: “Moyo wamasiku anoŵa woti aliyense amangokhala ali wotanganidwa ungachititse kuti kulera ana mwamtendere kutheretu ndiponso kuti moyo wa m’banja usamakhale wosangalatsa.” Ndiye chifukwa chake azimayi ambiri akulakalaka kukhala ndi moyo wosalira zambiri. Kodi mungakwanitse bwanji kuchita zimenezi? Choyamba, ganizirani zinthu zimene zili zofunika ndipo mukatero chitani kaye “zinthu zofunika kwambiri,” ndipo osaiwalanso kukhala ndi nthaŵi yocheza ndiponso kusamalira zofuna za ana anu. (Afilipi 1:10, 11, NW) Chachiŵiri, onani bwinobwino mmene mumakhalira. Mukhoza kusiya kuchita zinthu zina n’zina ndiponso kuchepetsa katundu wanu pochotsa wina amene ali wosafunika kwenikweni.
Kodi chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanu n’chiyani? Kodi n’kupeza zinthu zonse
zomwe mumalakalaka nthaŵi imodzi, kapena zinazo mukhoza kudzazipeza m’tsogolo muno koma panopa n’kumalimbana kaye ndi zamtundu wina. Mayi wina amene alibe chuma chambiri dzina lake Carolyn akusimba mmene amachitira kuti: “Sindilira kukhala n’zambiri ndipo sindigula zinthu wambawamba.” Mayi winanso amene ali ndi ana atatu dzina lake Gloria amakumbukira kuti: “Tinalibe ndalama zoti n’kumatha kugula zovala kusitolo, koma ndinkachita kuwasokera ana anga zovala n’kuwauza kuti zovalazo zinali zapamwamba kwambiri chifukwa chakuti palibenso wina amene anali ndi zovala zotero.”Mawu a Mulungu amati munthu “wosunga luntha adzapeza zabwino.” (Miyambo 19:8) Luntha n’lofunika kuti azimayi asankhe mwanzeru zinthu zambirimbiri monga zochita panthaŵi yopuma, katundu wina wothandiza pakhomo, ndiponso zizoloŵezi zina zimene zimazunzitsa azimayi ndi ana. Mayi wina wa ku South Africa dzina lake Judith anadandaula kuti: “Nthaŵi zonse amatitsatsa malonda a zinthu zatsopano, zinthu zaumisiri zamakono ndiponso zinthu zina zosiyanasiyana!” Mayi winanso amene ali ndi ana anayi dzina lake Angela wa ku Germany anati mavuto otere analimbana nawo motere: “Ndibwino kuona bwinobwino zinthu zofunika kwambiri komanso zimene zingakuthandizeni kwenikweni, ndipo mukatero ndibwinonso kuwathandiza ana anu kuchita chimodzimodzi.”
❖ Sinthani zinthu zimene zingatheke kusintha: “Muzigwiritsa ntchito mutu ndiponso kuganiza mwanzeru,” limalimbikitsa motero Baibulo la Contemporary English Version pa Miyambo 3:21. Ngati panopa mumagwira ntchito yolembedwa, kodi zingatheke kuti banja lanu lizidalira malipiro a mwamuna wanu yekha? Kuti muone mmene mungayankhire funso limeneli, onani kaye kuti mumatsala ndi ndalama zingati mukachotsera za misonkho, zofunika za mwana, zoyendera kuntchito, zogulira zovala, zogulira phoso ndi zinthu zina. Komanso n’kutheka kuti ndalama zimene amuna anu amapeza angazidule msonkho waukulu ngati mumati mukaphatikiza ndalama zanuzo zimaoneka kukhala zochuluka kwambiri. Mungakhumudwe kuona kuti mumatsala ndi ndalama zochepa kwambiri.
Azimayi ena amagwira ntchito kwa maola ochepa chabe kapena amagwirira pafupi ndi kunyumba kwawo, mwina n’kumalandira ndalama zochepa koma n’kumakhala ndi nthaŵi yambiri yokhala ndi ana awo. Ngati mwaganiza zosiya ntchito ndipo ngati ntchitoyo inali kukuthandizani kuti muzidziona kuti ndinu wofunika ndiponso waphindu ndiyetu muyenera kuganiza mmene mungakhalirebe wotero koma muli panyumba.
❖ Pezani thandizo: Mawu a Mulungu amasonyeza mobwerezabwereza kuti kupempha thandizo kuli ndi zotsatira zake. (Eksodo 2:23, 24; Salmo 34:15) Kupempha kwa mayi kuti athandizidwe kuyenera kuchititsa mwamuna wake kum’thandiza. Mukagwirizana chimodzi ndi mwamuna wanuyo mukhoza kupeza njira yothandizana ntchito zapakhomo kuti mukhale ndi nthaŵi yochitira pamodzi zolinga zanu, monga kukhala ndi nthaŵi yambiri muli ndi ana anu. Ngati zingatheke, mayi ayeneranso kupempha chithandizo kwa achibale ndiponso anzake apamtima amene amagwirizana zochitika.
Azimayi ambiri amapeza thandizo lofunika kwambiri kuchokera kwa okhulupirira anzawo a mumpingo wawo wachikristu. Mayi wina amene ali ndi ana atatu dzina lake María anaona kuti “kugwirizana kwambiri ndi mpingo” ndiko njira imodzi imene “Mulungu amatisonyezera chikondi komanso chifundo ndiponso imene amasonyezera kuti amatiganizira.”
❖ Khalani ndi nthaŵi yoti muzipumako: Ngakhale Yesu, munthu wangwiro wamphamvu zake, anawauza ophunzira ake kuti apite ‘padera ku malo achipululu kuti apumule kwa kamphindi.’ (Marko 6:30-32) Kuti zinthu zikuyendereni bwino monga mayi, ndiye kuti muyenera kuchitabe zinthu bwinobwino panthaŵi zovuta. Inde, n’zoona kuti ana anu amakufunani inuyo, koma amafunanso kuti muzikhala wokondwa ndiponso wokhutira. Mufunika kupumulako ndithu.
Mayi uja tam’tchula poyamba, Angela, ali ndi njira yake yopumulira. Iye anati: “Ndimapeza nthaŵi mmamaŵa yoti ndingokhala ndekha paphee. Mwina ndimakhala theka la ola kapena kuposa ndili ndekhandekha. Ndipo kamodzi kapena kaŵiri pa mlungu, ine ndi mwamuna wanga timakhala omasuka kuchitira zinthu limodzi madzulo, ana athu akafatsa kuchita zinthu zawo m’zipinda zina za m’nyumba momwemo. Motero timatha kukhala mpaka ola lathunthu.”
❖ Muzikonda kwambiri zinthu zauzimu kuposa china chilichonse: Akuti mavuto a kukhala mayi amakula kwambiri chifukwa cholephera kuona cholinga chake ndiponso kuona ubwino woyamba kaye kuchita zinthu zofunika kwambiri. Mabanja Achikristu amakhala n’chimwemwe akagwirizana chimodzi poyesetsa kuti choyamba m’moyo wawo azichita zimene Mulungu amafuna. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Banja limene limadzipereka kwa Mulungu ndipo limene limatsatira malangizo ake amene ali m’Baibulo lidzakhala lachimwemwe. Ndi bwino kukhala ndi munthu mmodzi m’banjamo amene amatsatira zimene Baibulo limanena, kuposa kukhala opandiratu aliyense wotere.
Mayi wina wachikristu amene amapita kuntchito dzina lake Adele, anaona ubwino wokhala munthu wokonda zauzimu. Iye anati: “Tili ndi malangizo ndiponso nkhani zambiri zedi zimene zili m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene amatidziŵitsa zinthu zimene ana athu akukumana nazo ndiponso mmene tingawathandizire. Zimakhala zonyaditsa kuona ana anu akutsatira zinthu zauzimu zimene mumawaphunzitsa. Mukamaona anawo akusintha khalidwe m’zochitika zina n’zina ndiponso m’kaganizidwe kawo, mumazindikira kuti akumvetsadi zimene mukuwaphunzitsa komanso kuti khama lanulo silikupita pachabe.” *
Inde, n’zotheka ndithu kugonjetsa mavuto a kukhala mayi. Mulungu mwini amatilimbitsa mtima potitsimikizira kuti khama lonse la azimayi odzipereka amene amam’khulupirira iye silidzapita pachabe. Azimayi amene amam’konda kwambiri Mulungu angapeze chowalimbitsa mitima poganizira lonjezo lake lakuti ‘adzalimbitsa olefuka.’—Yesaya 40:29.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 16 Mboni za Yehova zatulutsa mabuku angapo amene amafotokoza za m’Baibulo amene cholinga chake n’kuphunzitsira ana. Ena mwa mabukuŵa ndiwo Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza ndiponso Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
[Bokosi patsamba 10]
Kutengera Zochita za Amayi
Ngati muli mayi, n’kutheka kuti nthaŵi zina mumadzifunsa kuti kodi zimene mumachita zimakhudza motani moyo wa mwana wanu. Nthaŵi zina mungaone kuti mwana wanu akutengera kwambiri ana anzake, aphunzitsi, asangalatsi, maseŵera apavidiyo ndiponso nyimbo kuposa kutengera zochita zanu.
Taganizirani chitsanzo cha amayi ake a Mose dzina lawo Yokobedi. Iwo ankakhala m’nthaŵi yovuta kwambiri ndipo analibe mphamvu yonenapo chilichonse pa zatsogolo la mwana wawo. Komabe iwo anagwiritsa ntchito mipata imene anali nayo kuti mwanayo akamakula adzatengere zochita zawo. Poyamba penipeni, iwo anasonyeza chikhulupiriro molimba mtima kwambiri popangitsa kuti zisatheke kuti Mose aphedwe. Mulungu anawadalitsa chifukwa cha chikhulupiriro chawo pom’pulumutsa mwanayo komanso potheketsa kuti Yokobedi alere mwanayo monganso mayi ake.—Eksodo 1:15, 16; 2:1-10.
N’zoonekeratu kuti Yokobedi anam’thandiza mwana wake kuti akule bwino. Chimene chinam’pangitsa Mose kumadziona kuti ali mbali ya Ahebri ndiponso Mulungu wawo ngakhale kuti iye anali m’banja lachifumu ku Aigupto n’chimene chimasonyezadi kuti makolo ake anam’chititsa kuti atengere maganizo awo adakali wakhanda.—Ahebri 11:24-26.
N’kutheka kuti inu monga mayi, muli ndi mipata yambiri kuposa Yokobedi yom’chititsa mwana wanu kutengera zochita zanu. Kodi mukupezerapo mwayi pazaka zochepa chabe zimene mwana wanu amakhala adakali wamng’ono pom’phunzitsa zinthu zosaiwalika msanga zokhudza Mulungu? Kapena kodi mumangolekerera kuti mwana wanu azikula mogwirizana ndi mmene anthu ambiri masiku ano amaganizira?
[Zithunzi patsamba 10]
Gaŵiraniko ena ntchito zapakhomo ndipo ikani nthaŵi yapadera yokhala nokha ndipo muzikonda zinthu zauzimu kuposa china chilichonse