Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthana ndi Mavuto Obwera ndi Chivomezi

Kuthana ndi Mavuto Obwera ndi Chivomezi

Kuthana ndi Mavuto Obwera ndi Chivomezi

“TAKHALIRA KUYENDA M’MAŴA WONSEWU MPAKA PANO. TIKUTHAŴA KUTI TIPULUMUTSE MOYO. TILIBE MADZI AKUMWA, TILIBE CHAKUDYA. NYUMBA ZATHU ZONSE ZAGWA.”—ANATERO HARJIVAN, AMENE ANAPULUMUKA CHIVOMEZI CHACHIKULU 7.9 KU INDIA.

KUONA zinthu zikuwonongeka chifukwa cha chivomezi n’koopsa kwambiri. “Mabuku anali kugwa balalabalala kuchokera pakabati yaitali pafupifupi mamita aŵiri ndi theka,” munthu wina wopulumuka chivomezi chimene chinachitika ku Taiwan mu 1999 anakumbukira motero. Iye anawonjezera kunena kuti, ‘Chipeŵa changa cha njinga yamoto chomwe ndinangochigula kumene chinatsetsereka kuchokera pamwamba pa kabatiyo n’kugwera pafupi penipeni ndi mutu wanga ine ndili gone pabedi. Chipeŵachi n’chimenenso chikanandipha.’

Anthu Akapulumuka Chivomezi

Chivomezi chikagwedeza malo enaake iwe uli pomwepo koma n’kupulumuka, mantha amakugwira kwambiri. Koma kupulumuka chivomezicho n’chiyambi chabe cha zinthu zina zimene zimatsatira. Maola angapo akapita chivomezicho chitachitika, opulumutsa anthu amayesetsa molimba mtima kuti apeze ndiponso kuthandiza ovulala. Nthaŵi zambiri amatero mtima uli m’mwamba chifukwa pakachitika chivomezi choopsa kwambiri, chivomezi china chimatha kugwedezanso mwapang’onopang’ono. Chaposachedwapa ku El Salvador kutachitika chivomezi chimene chinakwirira dera linalake, munthu wina amene ankaganiza zokumba chimulu chadothi chimene chinakwirira deralo anati, “Tifunika kuti tikhale osamala kwambiri. Ngati nthakayi itangogwedezekanso mwadzidzidzi, chimulu chonsechi chingathe kugwa.”

Nthaŵi zina anthu amasonyezadi mtima woganizira ena kwambiri akamathandiza anthu ovutika ndi chivomezi. Mwachitsanzo, ku India kutachitika chivomezi chachikulu m’chaka cha 2001, gogo wina amene panopa akukhala ku United States dzina lake Manu, anabwerera kwawo ku India. Iye anaganiza kuti: “Ndiyenera kubwerera kwathu basi, kuti ndikathandize abale anga, komanso anthu ena onse amene akuvutika.” Manu anakapeza kuti m’madera onse amene anafikako zinthu zinafika poipa kwambiri. Komabe iye anaona kuti: “Anthu amalimba mtima mogometsa kwambiri.” Mtolankhani wina analemba kuti: “Sindikukhulupirira kuti alipo munthu wina amene sanathandizepo popereka chilichonse chimene akanatha kupatsa wina, ena anapereka ndalama zimene amalandira tsiku lonse, ena mlungu wonse, ena mwezi wonse, ena anakatapa ndalama zimene anasungitsa kubanki kapena kungopereka chilichonse chimene anatha kugaŵirako ena.”

N’zoona kuti kuchotsa zinthu zogumuka ndi kuthandiza ovulala si ntchito yovuta kwenikweni, koma kuthandiza anthu amene moyo wawo wasokonezekeratu chifukwa cha zoopsa zongochitika patimphindi tochepa kuti abwererenso mwakale n’kovuta kwambiri. Chitsanzo ndi cha Delores, mzimayi amene nyumba yake inagumuka pachivomezi ku El Salvador. Iye anati “Nkhondo ija inali nkhasakoni, chifukwa pogona pokha tinali napo.”

Monga tanenera m’nkhani yathu yoyamba ija, nthaŵi zina anthu amafunika kuwalimbikitsa kwambiri kuti asataye mtima osati kungowapatsa katundu wowathandiza basi. Mwachitsanzo, pamene chivomezi chinawonongeratu mzinda wa Armenia, chakumadzulo kwa dziko la Colombia kumayambiriro kwa chaka cha 1999, anthu oposa 1000 anaferatu, ndipo anthu enanso ambiri anagwidwa nthumanzi kwambiri ndiponso anasoŵa pogwira. Katswiri wina wa zamatenda a maganizo Roberto Estefan amenenso nyumba yake inagwa pachivomezicho ananena kuti, “Kulikonseko anthu akupempha kuti athandizidwe. Ndikapita ku lesitilanti anthu ambiri amene amandipatsa moni amapezerapo mwayi wondiuza kuti sakutha kugona ndiponso ali ndi chisoni chachikulu.”

Dr. Estefan amadziŵa bwino mmene munthu amasokonezekera chivomezi chowononga chikachitika. Mzimayi wina amene anadzipereka kuti akonze nawo msasa wa anthu ofuna chithandizo anaona kuti anthu ena amene ali pantchito safunanso kupita kuntchito chifukwa amangomva kununkhira kwa imfa basi.

Kuwalimbikitsa Anthu Amene Ataya Mtima

M’nthaŵi ya zovuta ngati zimenezi, Mboni za Yehova zimayesetsa kuthandiza opulumuka mwakuthupi komanso mwauzimu ndi mwamaganizo. Mwachitsanzo, chivomezi cha ku Colombia chija chitangochitika, ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova yakumeneko inakonza komiti yakomweko yoti ithandize pangoziyo. Mboni zongodzipereka zambirimbiri zochokera m’madera osiyanasiyana adzikolo zinapereka chakudya ndi ndalama. Pasanathe nthaŵi, zakudya zokwana matani 70 zinatumizidwa m’madera angoziwo.

Nthaŵi zambiri chithandizo chauzimu ndicho chimafunika kwambiri. M’maŵa wina chivomezi cha ku Colombia chitachitika, munthu wina wa Mboni za Yehova m’deralo anaona mzimayi amene ankaoneka wachisoni kwambiri akuyenda mumsewu wamumzinda wa Armenia womwe unali utawonongeka kwambiri. Ndiye anapita kumene kunali mzimayiyo n’kumupatsa thirakiti lakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? *

Mzimayiyo anatenga thirakitilo n’kupita nalo kunyumba n’kukaliŵerenga mwachifatse. Nthaŵi ina wina wa Mboni za Yehova anafika pakhomo pake ndipo mzimayiyo analephera kudzigwira motero anafotokoza zimene zinam’chitikira. Chinachitika n’chakuti chivomezi chija chinam’gumulira nyumba zake zingapo mumzindamo, zimene zinkam’thandiza kupeza ndalama. Tsopano anali paumphaŵi. Koma si zinali zokhazo ayi. Chivomezicho, chinagwetsa nyumba imene ankakhalamo pamodzi ndi mwana wake wamwamuna wazaka 25, ndipo mwanayo anafera momwemo. Mzimayiyo anauza Mboni imene inabwera kunyumba kwakeyo kuti sanachiteko chidwi ndi zachipembedzo koma kuti tsopano anali ndi mafunso ambiri. Thirakitilo linam’thandiza kutsimikiza kuti zabwino zili m’tsogolo. Posakhalitsa anayamba kuphunzira Baibulo panyumba pake.

Mboni za Yehova sizikayika n’komwe kuti ikudza nthaŵi imene anthu sadzaopanso masoka achilengedwe, kuphatikizapo zivomezi. Nkhani yotsatirayi ilongosola chifukwa chake.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 20]

KHALANI OKONZEKERATU!

▪ Onetsetsani kuti mathanki amagetsi otenthetsera madzi n’ngomangiriridwa bwinobwino ndiponso kuti zinthu zonse zolemera zili pansi kapena m’munsi mwa chinthu chimene tazisungirapo.

▪ Phunzitsani anthu a m’banja mwanu mmene angazimitsire magetsi komanso gasi ndi madzi.

▪ Pezani chida chozimitsira moto panyumba panu komanso zinthu zonse zofunika pothandiza munthu atangovulala kumene.

▪ Muzikhala ndi kawailesi ka m’manja pafupi ndiponso kazikhala ndi mabatire atsopano.

▪ Yesererani ndi banja lanu zimene mungachite pachivomezi, ndipo gogomezerani kwambiri kuti pachivomezi pamafunika kuti (1) musapupulume, (2) muzimitse zitofu ndi mbaula zamagetsi, (3) muime pakhomo kapena muloŵe kunsi kwa tebulo kapenanso desiki ndiponso (4) mukhale motalikirana ndi mawindo, magalasi odziyang’anirapo, ndiponso chumuni.

[Bokosi patsamba 21]

ZIVOMEZI KU ISRAEL

Dziko la Israel ndi limene “kuyambira kale kumakonda kuchitika zivomezi kuposa mayiko ena onse,” analemba choncho pulofesa Amos Nur. Chifukwa chake n’chakuti mbali ya chigwa chachikulu chotchedwa Great Rift Valley, chimene chinagaŵa pokumanira matanthwe apansi panthaka ku Mediterranean ndi Arabia, chimadutsa m’dziko la Israel kuchokera kumpoto mpaka kukaphera kumwera.

N’zochititsa chidwi kuti akatswiri ena ofufuza mbiri yakale pofukula mabwinja amakhulupirira kuti amisiri akale ankagwiritsa ntchito njira inayake yapadera kuti zinthu zisamawonongeke kwambiri ndi chivomezi. Zimenezi zikugwirizana ndi mmene Baibulo limalongosolera ntchito yomanga ya Solomo. Baibulo limati: “Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi likole la nyumbayo.” (1 Mafumu 6:36; 7:12) Umboni wosonyeza njira imeneyi yophatikiza milongoti ndi miyala wapezedwa m’malo osiyanasiyana kuphatikizapo chipata china cha ku Megido, chimene akuti mwina chinalipo m’nthaŵi ya Solomo kapena m’mbuyo mwake. Katswiri wina wamaphunziro David M. Rohl amakhulupirira kuti milongoti imeneyi mwina “ankailonga m’miyalamo n’cholinga chofuna kuteteza nyumbazo kuti zisawonongeke chifukwa cha zivomezi.”

[Chithunzi]

Bwinja lochitika chifukwa cha chivomezi, ku Bet Sheʼan, ku Israel

[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]

MPHINDI ZIŴIRI ZOOPSA—NKHANI IMENE WOPULUMUKA WINA ANASIMBA

Mumzinda wa Ahmadabad, ku India, banja lathu linali kukonzekera ukwati wa msuweni wanga. Pa January 26, 2001, ndinadzidzimuka kutulo, osati chifukwa cha kulira kwa wotchi ya alamu, koma chifukwa cha kugwedezeka kwamphamvu. Ndinamva makabati a zitsulo akukhwekhwerezeka, ndiye ndinadziŵa kuti kunja kwaipa. Bambo anga aang’ono anali kukuwa kuti, “Tulukani m’nyumbamo!” Titatuluka panja tinkatha kuona nyumbayo ili ndengundengu kugwedezeka. Chivomezicho chimangokhala ngati kuti sichileka n’komwe. Koma kwenikweni chinangochitika kwa mphindi ziŵiri zokha basi.

Zinandisokoneza maganizo kwambiri chifukwa zinangondidzidzimutsa. Tinaonetsetsa kuti anthu a m’banja mwathu onse ali bwino. Telefoni ndi magetsi zinali zitaduka, motero sitikanatha kudziŵa nthaŵi yomweyo kuti azibale athu amene amakhala kwina ali bwanji. Mmene timadziŵa kuti ali bwino n’kuti patatha ola limodzi tikungovutika ndi mtima kuti kaya ali bwanji. Si onse amene anachita mwayi choncho. Mwachitsanzo ku Ahmadabad, nyumba zopitirira 100 zinagwa, ndipo anthu opitirira 500 anaferatu.

Aliyense anagwidwa nthumanzi kwambiri kwa milungu ingapo. Tsiku lililonse anthu ankapita kokagona ali ndi mantha poopa chivomezi china chimene anati chichitikanso. Pang’onopang’ono zinthu zinayamba kubwerera mwakale komabe anthu ambiri analibe pogona. Chinachititsa zonsezi n’chivomezi chimene chinachitika kwa mphindi ziŵiri zokha koma chimene sitidzachiiwala mpaka kalekale.—Anasimba nkhani imeneyi ndi Samir Saraiya.

[Chithunzi pamasamba 21, 22]

Munthu wina wopulumuka chivomezi cha mu January 2001, ku India wanyamula chithunzi cha amayi ake amene anafa ndipo mtembo wawo akuuwotcha

[Mawu a Chithunzi]

© Randolph Langenbach/UNESCO (www.conservationtech.com)