Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Anthu Amene Ataya Mtima Pakati pa Zoopsa

Kuthandiza Anthu Amene Ataya Mtima Pakati pa Zoopsa

Kuthandiza Anthu Amene Ataya Mtima Pakati pa Zoopsa

“KULIKONSE KUMENE NDINKAYANG’ANAKO, NYUMBA ZINKANJENJEMERA NDIPO MALAŴI A MOTO ANALI TOLOTOLO. NDILI M’KATI MOTHAMANGA, KULIKONSEKO ANTHU ANALI KULIRA, KUPEMPHERA NDIPONSO ANALI KUKUWA KUTI WINA AWATHANDIZE. NDINKANGOTI BASI MAPETO A DZIKO AJA AFIKA.”—ANATERO G.R., AMENE ANAPULUMUKA KUTAGWA CHIVOMEZI.

CHAKA chilichonse zivomezi zambirimbiri zimagwedeza dziko lathuli lomwe limakhalira kuyenda nthaŵi zonse. N’zoona kuti zivomezi zambiri zotere sitimazimva n’komwe. * Komabe, pafupifupi zivomezi 140 pachaka zimakhala zoopsa mwakuti anthu amatha kuzigaŵa patatu kuti ichi n’chivomezi “champhamvu,” “chowononga” kapenanso kuti “chosakaza kwambiri.” M’mbuyo monsemu, zivomezi zimenezi zaphetsa anthu ambirimbiri ndiponso zawonongetsa katundu wa ndalama zambirimbiri.

Zivomezi zimasautsanso kwambiri maganizo a anthu opulumuka. Mwachitsanzo, zivomezi ziŵiri zamphamvu zitachitika m’dziko la El Salvador kumayambiriro kwa chaka cha 2001, mkulu woyang’anira za matenda okhudza maganizo mu unduna wa zaumoyo m’dzikolo anati: “Anthu ayamba kuvutika maganizo motero kuti akumakhala okwiya, othedwa nzeru ndi aukali.” N’zosadabwitsa kuti ogwira ntchito ya zaumoyo ku El Salvador ananena kuti pa anthu 100 alionse odwala matenda ovutika maganizo pakuwonjezeka anthu enanso okwana 73. Kwenikweni ofufuza aona kuti mwa zinthu zina zofunika kwambiri m’misasa yothandizira anthu omwe zoterezi zawagwera, madzi ndiwo ali poyambirira kenaka mankhwala othandiza anthu amene ali ndi matenda amaganizo.

Koma chivomezi chimaonetsa anthu zinthu zina zambiri osati kokha zinthu monga imfa, kuwonongeka kwa zinthu, ndi kusoŵa pogwira. Nthaŵi zambiri ngozi zimenezi zimapangitsa anthu kusonyeza mtima wabwino kwambiri ndiponso kudzipereka kuthandiza ena. Ena afikadi pogwira chintchito chachikulu chokonza zinthu zowonongeka ndiponso kusamalira anthu ovutika. Zinthu zolimbikitsa zimenezi zachititsa anthu kusataya mtima ngakhale pangozi zoopsa kwambiri, monga mmene tionere m’nkhanizi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zivomezi zina zoterezi si zamphamvu kwambiri, ndipo zambiri zimachitika tsiku lililonse.

[Zithunzi pamasamba 17, 18]

Ku Athens, m’dziko la Greece, bambo wina chimwemwe chili chodzaza tsaya pozindikira kuti mwana wake wamkazi wa zaka zisanu wapulumutsidwa

[Mawu a Chithunzi]

AP Photos/Dimitri Messinis